Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtima Wamataya Umadzetsa Chimwemwe

Mtima Wamataya Umadzetsa Chimwemwe

Mtima Wamataya Umadzetsa Chimwemwe

MONGA woyang’anira wachikondi wachikristu, mtumwi Paulo amadera nkhaŵa kwambiri za okhulupirira anzake ndipo anali wofunitsitsa kuwathandiza. (2 Akorinto 11:28) Choncho, polinganiza zopereka ndalama zothandizira Akristu osoŵa m’Yudeya m’zaka za m’ma 50 za zana loyamba la Nyengo Yathu ino, iye anagwiritsa ntchito mwayi umenewu kuphunzitsa kanthu kena kofunika kwambiri kokhudza kuwoloŵa manja. Paulo ananenetsa kuti Yehova amayamikira kwambiri kupereka mokondwera, pamene anati: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.”​—2 Akorinto 9:7.

Aumphaŵi Wadzaoneni, Koma Osaumira

Akristu ambiri a m’zaka za zana loyamba sanali olemera. Paulo anati “ambiri [sanali] amphamvu.” Anali “zofooka za dziko lapansi,” “zopanda pake za dziko lapansi.” (1 Akorinto 1:26-28) Mwachitsanzo, Akristu a ku Makedoniya anali ‘osauka’ ndiponso anali ‘m’chisautso.’ Komabe, okhulupirira odzichepetsa a ku Makedoniya ameneŵa anapempha kuti nawonso awapatse mwayi wopereka chuma chochirikizira “utumiki wa kwa oyera mtima”; ndipotu Paulo anachitira umboni kuti anapereka “koposa mphamvu yawo”!​—2 Akorinto 8:1-4.

Komatu kupereka kumeneku kunali kowoloŵa manja osati chifukwa cha kuchuluka kwa zoperekazo. M’malo mwake, kusonkhezereka, kufunitsitsa kugaŵana ndi ena, komanso mtima wabwino n’zomwe zinali zofunika. Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti malingaliro komanso mtima zimakhudzidwa popereka mwaufulu. Iye anati: “Ndidziŵa chivomerezo chanu [cha maganizo, NW] chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amakedoniya, . . . ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.” Akristu a ku Korinto “anatsimikiza mtima” kupereka mowoloŵa manja.​—2 Akorinto 9:2, 7.

‘Mzimu Wawo Unawafunitsa’

Mtumwi Paulo ayenera kuti ankaganiza za chitsanzo choyambirira cha kupereka mowoloŵa manja, chomwe chinachitikira m’chipululu zaka zoposa 1,500 iye asanabadwe. Mafuko 12 a Israyeli anali atapulumutsidwa mu ukapolo ku Igupto. Tsopano anali mtsinde mwa Phiri la Sinai, ndipo Yehova anawalamula kumanga chihema cholambiriramo ndi kuikamo zipangizo zogwiritsa ntchito polambirapo. Ntchito imeneyi inafuna chuma chochuluka, kotero kuti anthu onsewo anawapempha kupereka mwaufulu.

Kodi Aisrayeliwo anachitanji? “Anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wam’funitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha ku ntchito ya chihema chokomanako.” (Eksodo 35:21) Kodi mtunduwo unaperekadi mowoloŵa manja? Kwabasinso! Mose anauzidwa lipoti lakuti: “Anthu alinkubwera nazo zochuluka, zakuposera zoyenera ntchito imene Yehova anauza ichitike.”​—Eksodo 36:5.

Kodi mkhalidwe wachuma wa Aisrayeliwo unali wotani m’nthaŵiyo? Osati kale kwambiri m’mbuyomo, anali akapolo osauka, ‘osautsidwa ponyamula akatundu,’ okhala ‘m’moyo woŵaŵitsa’ moyo wa “mazunzo.” (Eksodo 1:11, 14; 3:7; 5:10-18) Chotero, n’chachidziŵikire kuti analibe chuma chochuluka. N’zoona kuti Aisrayeli anali ndi zoŵeta zazing’ono ndi zazikulu potuluka m’dziko la ukapolo. (Eksodo 12:32) Komatu zimenezo ziyenera kuti zinali zochepa, chifukwa chakuti atangochoka mu Igupto, anayamba kudandaula kuti alibe nyama ngakhale mkate woti adye.​—Eksodo 16:3.

Tsono Aisrayeliwo anachitenga kuti chuma chomwe anapereka pochirikiza kumanga chihemacho? Kwa Aigupto omwe ankawatumikirawo. Baibulo limati: “Ana a Israyeli . . . [a]napempha Aigupto zokometsera zasiliva, ndi zagolidi, ndi zovala. . . . ndipo [Aigupto] sanawakaniza.” Kuwoloŵa manja kumeneku kwa Aigupto kunali dalitso lochokera kwa Yehova, osati kwa Farao. Mawu a Mulungu amati: “Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aigupto, ndipo sanawakaniza.”​—Eksodo 12:35, 36.

Ndiyeno tangoganizani mmene Aisrayeliwo anamvera. Mibadwo inali itavutika muukapolo wadzaoneni ndi umphaŵi wosaneneka. Tsopano anali omasuka ndipo anali nacho chuma chambiri. Kodi akanamva motani polingalira zochotsanso china mwa chuma chimenecho? Iwo akanatha kumalingalira kuti anali malipiro awo ndipo anayenera kuchisunga. Komabe, atawapempha kuti apereke chuma pochirikiza kulambira koyera, anaperekadi​—ndipotu osati mokakamizika kapena monyinyirika! Sanaiŵale kuti Yehova ndi amene anatheketsa kuti iwo akhale ndi chuma choterocho. Choncho, anapereka siliva ndi golidi wawo ndi zoŵeta zawo mowoloŵa manja. Anali ndi ‘mtima wofunitsitsa.’ ‘Mitima yawo inawafulumiza.’ ‘Mzimu wawo unawafunitsa.’ Ndithudi chinali ‘chopereka chofuna mwini, choperekedwa kwa Yehova.’​—Eksodo 25:1-9; 35:4-9, 20-29; 36:3-7.

Changu cha Kupereka

Ukulu wa chopereka susonyeza kwenikweni kuwoloŵa manja kwa woperekayo. Nthaŵi inayake Yesu Kristu anaonerera anthu akuponya ndalama m’chosungiramo ndalama cha m’kachisi. Anthu olemera ankaponyamo masiliva ambiri, koma Yesu anachita chidwi ataona mkazi wamasiye waumphaŵi akuponya momwemo timakobiri tiŵiri. Iye anati: “Wamasiye uyu waumphaŵi anaikamo koposa onse . . . [Mkaziyu] mwa kusoŵa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.”​—Luka 21:1-4; Marko 12:41-44.

Mawu a Paulo kwa Akorinto anali ogwirizana ndi malingaliro ameneŵa a Yesu. Ponena za kupereka mwaufulu pothandiza okhulupirira anzathu aumphaŵi, Paulo anati: “Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo [“ngati alinacho changu,” NW], munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chim’soŵa.” (2 Akorinto 8:12) Inde, sitipereka n’cholinga chopikisana kapena kudziyerekeza ndi ena. Munthu amapereka zomwe angathe kupereka, ndipo Yehova amakondwera ndi mzimu wosaumira.

Ngakhale kuti palibe amene angalemeretse Yehova, yemwe ndiye mwiniwake wa chilichonse, kupereka mwaufulu ndi mwayi wapadera womwe umapatsa om’lambira, mpata wosonyeza kuti amam’konda. (1 Mbiri 29:14-17) Kupereka osati n’cholinga chodzionetsera, kapena n’zolinga zina zadyera, koma ndi cholinga choyenera ndi kuchirikiza kulambira koona, kumadzetsa chimwemwe limodzi ndi madalitso a Mulungu. (Mateyu 6:1-4) Yesu anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Tingalandire nawo madalitso amenewo mwa kupereka mphamvu zathu muutumiki wa Yehova ndi mwa kupatula kenakake pachuma chathu kuti tichirikize nako kulambira koona ndi kuthandiza osoŵa.​—1 Akorinto 16:1, 2.

Changu cha Kupereka Lerolino

Lerolino, Mboni za Yehova n’zokondwa kuona kupita patsogolo kwapadziko lonse m’ntchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) M’zaka khumi zotsirizira za m’ma 1900, anthu oposa 3,000,000 anabatizidwa kusonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova Mulungu, ndipo mipingo yatsopano ngati 30,000 inakhazikitsidwa. Inde, umodzi pa mipingo itatu iliyonse ya Mboni za Yehova yomwe ilipo lerolino inakhazikitsidwa m’zaka khumi zapitazo! Mokulira, kuwonjezeka kotereku kwachitika chifukwa cha ntchito yaikulu ya Akristu okhulupirika, amuna ndi akazi omwe athera nthaŵi ndi mphamvu zawo kuchezera anansi awo ndi kuwauza zomwe Yehova adzachita. Kumbali ina, kuwonjezekaku kwachitika chifukwa cha ntchito ya amishonale, omwe amachoka m’dziko lakwawo ndi kupita ku mayiko akutali kukathandiza kumeneko m’ntchito yolalikira Ufumu. Kuwonjezekaku kwachititsa kuti madera atsopano akhazikitsidwe, zomwenso zachititsa kuti oyang’anira madera atsopano aikidwe. Kuwonjezera pamenepo, mabaibulo ambiri oti agwiritsidwe ntchito polalikira ndi popanga phunziro laumwini akhala akufunika. Mabuku ambiri akhalanso akufunika zedi. Ndipo m’mayiko ambiri, nyumba za nthambi zakuzidwa kapena kumanga kumene nyumba ndi maofesi anthambi aakulu atsopano. Ntchito zonse zowonjezerekazi zatheka chifukwa cha thandizo la zopereka zaufulu zochokera kwa anthu a Yehova.

Nyumba za Ufumu Zikufunika

Chinthu chofunika kwambiri chomwe chakhalapo chifukwa cha kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha Mboni za Yehova ndicho Nyumba za Ufumu. Kufufuza kochitidwa kumayambiriro a chaka cha 2000 kunasonyeza kuti pakufunika Nyumba za Ufumu zoposa 11,000 m’mayiko omwe akutukuka kumene, momwe kupeza chuma kuli kovuta. Lingalirani za Angola. Ngakhale kuti mwakhala nkhondo yachiŵeniŵeni kwa zaka zambiri ndithu, ofalitsa Ufumu m’dziko limeneli akuwonjezeka chaka chilichonse pa avareji ya pafupifupi 10 peresenti. Komabe, mipingo yochuluka mwa mipingo 675 m’dziko lalikululi la mu Africa imachitira misonkhano yawo pabwalo. M’dzikoli muli Nyumba za Ufumu 22 zokha, ndipo 12 zokha mwa zimenezi n’zomwe zili zofolera.

Zinthu zilinso chimodzimodzi ku Democratic Republic of Congo. Ngakhale kuti mu Kinshasa, likulu la dzikoli, muli mipingo 300, muli Nyumba za Ufumu 10 zokha. M’dziko lonseli, Nyumba za Ufumu zoposa 1,500 zikufunika mwamsanga. Chifukwa cha kuwonjezereka koŵirikiza m’mayiko a Kum’maŵa kwa Ulaya, mayiko a Russia ndi Ukraine onse pamodzi anapereka lipoti lakuti akufuna Nyumba za Ufumu zambirimbiri. Kuwonjezereka koŵirikiza ku Latin America kwaonekeratu mu Brazil, momwe muli Mboni zoposa 500,000 ndipo Nyumba za Ufumu zochuluka zikufunika kwambiri kumeneku.

Kuti zosoŵazo zikwaniritsidwe m’mayiko amenewo, Mboni za Yehova zikugwiritsa ntchito pulogalamu yomanga Nyumba za Ufumu mofulumira kwambiri. Thandizo lochirikiza pulogalamu imeneyi limapezeka kuchokera kwa abale padziko lonse omwe amapereka mowoloŵa manja, kotero kuti ngakhale mipingo yosauka kwambiri ithe kukhala ndi malo abwino olambirira.

Monga momwe zinalili m’nthaŵi ya Israyeli wakale, zambiri zingathenso kuchitika lerolino chifukwa chakuti Akristu okhulupirika ‘akulemekeza Yehova ndi chuma chawo.’ (Miyambo 3:9, 10) Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lafuna kupezerapo mwayi wothokoza aliyense amene mtima wake wam’sonkhezera kupereka mwaufulu. Ndipo tili ndi chikhulupiriro chonse kuti mzimu wa Yehova upitirizabe kusonkhezera mitima ya anthu ake kuti athandize mwa kupereka zofunika pa ntchito ya Ufumu yomwe ikuwonjezekayi.

Pamene kuwonjezeka kwa padziko lonse kukupitirizabe, tifunefunetu nthaŵi zonse mipata yakuti tisonyeze kusangalala ndi kufunitsitsa kwathu kupereka mphamvu zathu, nthaŵi yathu, ndi chuma chathu. Ndipotu tipeze chimwemwe chenicheni chomwe mzimu woterowo wa kupatsa umadzetsa.

[Bokosi patsamba 29]

“IGWIRITSENI NTCHITO MWANZERU!”

“Ndili ndi zaka khumi zakubadwa. Ndatumiza ndalamayo kuti mugule pepala kapena chilichonse chomwe m’magwiritsa ntchito popanga mabuku.”​—Cindy.

“Ndakonda kukutumizirani ndalama iyi kuti mutipangire mabuku ambiri. Ndalama imeneyi ndinaipeza pothandiza abambo anga kuchita ntchito ina yake. Choncho igwiritseni ntchito mwanzeru!”​—Pam, wazaka zisanu ndi ziŵiri.

“Ndinamva chisoni pakumva za chimvula cha mkuntho. Ndikukhulupirira kuti mulibwino tsopano. Ndalama iyi [$2, U.S.] ndi yokhayo yomwe ndinali nayo.”​—Allison, wazaka zinayi.

“Dzina langa ndine Rudy, ndipo ndili ndi zaka 11 zakubadwa. Mbale wanga Ralph ali ndi zaka zisanu ndi chimodzi. Ndipo mchemwali wanga Judith ali ndi zaka ziŵiri ndi theka. Takhala tikusunga ndalama zomwe amatipatsa kwa miyezi itatu kuti tithandize abale athu [kudera komwe kuli nkhondo]. Ndalama zomwe timasungazo zakwana $20 yomwe tatumizayo.”

“Ndimamva chisoni chifukwa cha abale [omwe anavutika ndi chimvula cha mkuntho]. Nditagwira ntchito ndi bambo anga anandipatsa ndalama zokwana $17. Sindikutumiza ndalama imeneyi kuti ithandize pambali inayake imene ndikufuna, choncho mudzadziŵa chochita nayo ndinuyo.”​—Maclean, wazaka zisanu ndi zitatu.

[Bokosi patsamba 31]

Njira Zimene Ena Amasankha Popereka

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse​—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku likulu la dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yakwawo.

Ndalama zoperekedwa modzifunira zingatumizidwenso mwachindunji ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso yeniyeni iyenera kutsagana ndi zoperekazo.

MAKONZEDWE APADERA OPEREKERA

Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society pamakonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo akuzifunanso chifukwa cha kusoŵa kwinakwake, zoperekazo zidzabwezeredwa kwa iye. Kuti mudziŵe zambiri, chonde lemberani ku Accounting Office pa adiresi yosonyezedwa m’munsimu.

KUPATSA KOLINGANIZA

Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi ndalama zoperekedwa pamakonzedwe apadera, palinso njira zina zoperekera zopindulitsa utumiki wa Ufumu wapadziko lonse. Zimenezi zikuphatikizapo:

Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni.

Maakaunti a ku Banki: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikizidwe kapena mwiniwake atamwalira angalipiridwe ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanuko.

Chuma ndi Ndalama Zoikizidwa: Chuma ndi ndalama zoikizidwa m’malonda ena zingaperekedwe kukhala za Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni.

Malo: Malo okhoza kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo mwiniwake, amene angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Munthuyo ayenera kulankhula ndi Sosaite asanailoŵetse m’pangano la malo alionse.

Chuma cha Masiye ndi Choikizira: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwalamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzalandira mapindu a pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma chopindulitsa gulu lachipembedzo lingakhale ndi mapindu ena a kuchepetsa msonkho.

Monga mwa tanthauzo la mawuwo “kupatsa kolinganiza,” zopereka zoterezi zimafunadi kuti woperekayo alinganize bwino. Accounting Office iyenera kudziŵitsidwa ndi kulandira makope a zikalata zilizonse zofunika za makonzedwe alionse ameneŵa. Ngati mukufuna kudziŵa zambiri ponena za alionse mwa makonzedwe a kupatsa kolinganiza kumeneku, lankhulani ndi Accounting Office, kaya mwa kuwalembera kalata kapena pafoni, paadiresi yosonyezedwa pansipa kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu.

ACCOUNTING OFFICE

Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

P. O. Box 30749, Lilongwe 3

Telefoni: 762111