Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungakhalebe ndi Khalidwe Loyera

Mungakhalebe ndi Khalidwe Loyera

Mungakhalebe ndi Khalidwe Loyera

“Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: Ndipo malamulo ake sali olemetsa.”​—1 YOHANE 5:3.

1. Kodi khalidwe la anthu lerolino n’losiyana motani?

KALEKALE, mneneri Malaki anauziridwa kuti alosere za nthaŵi pamene khalidwe la anthu a Mulungu lidzakhala losiyana kwambiri ndi khalidwe la anthu osatumikira Mulungu. Mneneriyo analemba kuti: “Adzabwera ndi kuzindikira [“anthu inu mudzaonanso kusiyana,” NW] pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.” (Malaki 3:18) Ulosi umenewo ukukwaniritsidwa lerolino. Kusunga malamulo a Mulungu, kuphatikizapo onena za kukhala ndi khalidwe loyera, ndiyo njira yanzeru ndiponso yoyenera m’moyo. Koma nthaŵi zina imeneyo ndi njira yovuta. Ndiye chifukwa chake Yesu ananena kuti Akristu ayenera kuyesetsa kuti apeze chipulumutso.​—Luka 13:23, 24.

2. Ndi zisonkhezero zotani zimene zimachititsa kuti kudzisunga kukhale kovuta kwa ena?

2 N’chifukwa chiyani kudzisunga kukuvuta? Chifukwa chimodzi n’chakuti pali zinthu zosonkhezera maganizo. Opanga malonda a zosangalatsa amapereka chithunzi chakuti kuchita chiwerewere n’kutsogola, n’kosangalatsa, ndiponso ndiko kukula, koma amanyalanyaza zotsatira zake zoipa. (Aefeso 4:17-19) Anthu ochuluka amene amasonyezedwa akugonana amakhala osakwatirana. Mafilimu ochuluka ngakhalenso a pa wailesi yakanema amasonyeza anthu amene ndi mabwenzi wamba akugonana ngati kuti kugonana ndi nkhani yongocheza. Nthaŵi zambiri, pamakhala palibe chikondi chenicheni ndi kulemekezana. Ambiri aona uthenga umenewu m’mafilimu kuyambira ali ana aan’gono. Komanso, pali chisonkhezero champhamvu cha mabwenzi choti titsatire khalidwe lodzitayirira lamakonoli, ndipo nthaŵi zina awo amene amakana kulitsatira amasekedwa ngakhalenso kunyozedwa.​—1 Petro 4:4.

3. Kodi pali zifukwa zina zotani zimene ena amachitira chisembwere?

3 Thupinso nalo limachititsa kuti kudzisunga kukhale kovuta. Yehova analenga anthu ndi chikhumbo cha kugonana, ndipo chikhumbo chimenecho chingakhale champhamvu kwambiri. Chikhumbo chimasonkhezeredwa kwambiri ndi zimene timaganiza, ndipo pali kugwirizana kwina pakati pa chisembwere ndi maganizo osemphana ndi malingaliro a Yehova. (Yakobo 1:14, 15) Mwachitsanzo, malinga ndi zimene kufufuza kwaposachedwapa kofalitsidwa m’magazini ya British Medical Journal kunapeza, ochuluka mwa amene anagonana ndi munthu wina kwa nthaŵi yoyamba anangochita chidwi chofuna kudziŵa kuti kugonana kumakhala bwanji. Ena anali kuona kuti anthu ambiri a msinkhu wawo anali kugonana, chotero iwonso anafuna kutaya unamwali wawo. Enanso ananena kuti anangotengeka maganizo kapena anali ‘oledzera pang’ono panthaŵiyo.’ Ngati tikufuna kusangalatsa Mulungu, tiyenera kukhala ndi maganizo osiyana ndi amenewo. Kodi ndi maganizo otani amene adzatithandiza kukhalabe ndi khalidwe loyera?

Khalani Wotsimikizira Kotheratu Mumtima

4. Kuti tikhalebe odzisunga, kodi tiyenera kuchitanji?

4 Kuti tikhalebe ndi khalidwe lodzisunga, tiyenera kuzindikira kuti moyo woterowo n’ngwaphindu. Zimenezi n’zimenenso mtumwi Paulo analembera Akristu ku Roma kuti: “Mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Kuzindikira kuti khalidwe loyera n’laphindu kumaphatikizaponso zina kuwonjeza pa kudziŵa kuti Mawu a Mulungu amatsutsa chisembwere. Kumaphatikizapo kumvetsa kuti chiwerewere chimaletsedwa pa zifukwa ziti komanso mmene timapindulira mwa kuchipewa. Zina mwa zifukwa zimenezi zinatchulidwa m’nkhani yoyambayo.

5. Kodi Akristu amafuna kudzisungira khalidwe labwino pachifukwa chachikulu chiti?

5 Kunena zoona, zifukwa zamphamvu kwambiri kwa Akristu zopewera chiwerewere n’zokhudzana ndi unansi wathu ndi Mulungu. Taphunzira kuti amadziŵa zimene zingatipindulitse. Chikondi chathu pa iye chidzatithandiza kudana nacho choipa. (Salmo 97:10) Mulungu ndiye Wopereka “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Amatikonda. Mwa kum’mvera iye, timasonyeza kuti timam’konda ndi kutinso tikuyamikira zonse zimene watichitira. (1 Yohane 5:3) Sitikufuna kukhumudwitsa Yehova ndi kum’pweteketsa mtima mwa kuswa malamulo ake olungama. (Salmo 78:41) Sitikufuna kuchita kalikonse kamene kangachititse njira yake yolungama ndi yopatulika ya kulambira kuneneredwa zamwano. (Tito 2:5; 2 Petro 2:2) Mwa kudzisungira khalidwe labwino, timakondweretsa Wamkulukuluyo.​—Miyambo 27:11.

6. Kodi kuuza ena za miyezo yathu pankhani ya khalidwe kumathandiza motani?

6 Titatsimikizira mumtima kuti tikufuna kudzisunga, chitetezo chowonjezera ndicho kuuzanso ena za chosankha chathucho. Lolani kuti anthu adziŵe kuti ndinu mtumiki wa Yehova Mulungu ndi kuti mwatsimikiza mtima kutsatira miyezo yake yapamwamba. Ndi moyo wanu, thupi lanu, kusankha n’kwanu. Mukufuna kuteteza chiyani? Unansi wanu wamtengo wapatali ndi Atate wanu wakumwamba. Choncho auzeni ena mosapita m’mbali kuti zivute zitani simungalolere kutaya khalidwe lanu lodzisungalo. Nyadirani kuimira Mulungu mwa kuchirikiza mfundo zake zamakhalidwe. (Salmo 64:10) Musachite manyazi kukambirana ndi ena za zimene mumakhulupirira pankhani ya khalidwe. Kulankhula molimba mtima kungakulimbitseni, kukutetezani, ndi kulimbikitsa ena kuti atsatire chitsanzo chanu.​—1 Timoteo 4:12.

7. Kodi tingakhalebe motani m’chosankha chathu cha kusunga khalidwe labwino?

7 Kenako, titatsimikizira kuti tidzasunga miyezo yapamwamba ya khalidwe ndiponso tauzako ena za chosankha chathu, tiyenera kuchitapo kanthu kuti tisachoke pachosankha chathucho. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndiyo mwa kusamala posankha anzathu. Baibulo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” Chezani kokha ndi anthu amene ali ndi malingaliro ofanana ndi anu pankhani ya khalidwe; adzakulimbitsani. Lembali limanenanso kuti: “Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Mulimonse mmene mungathere, peŵani anthu amene angafooketse chosankha chanu.​—1 Akorinto 15:33.

8. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudyetsa malingaliro athu zinthu zabwino? (b) Kodi tiyenera kupeŵa chiyani?

8 Ndiyeno, tiyenera kudyetsa malingaliro athu zinthu zoona, zolemekezeka, zolungama, zoyera, zokongola, zokoma, zabwino, ndi zotamandika. (Afilipi 4:8) Timachita zimenezi mwa kusamala posankha zinthu zimene timaonera ndi kuŵerenga komanso nyimbo zomwe timamvetsera. Kunena kuti mabuku osonyeza khalidwe lachiwerewere sangapotole malingaliro a munthu n’chimodzimodzi ndi kunena kuti mabuku osonyeza khalidwe labwino n’ngosathandiza. Kumbukirani kuti anthu opanda ungwiro angagwere m’chisembwere mosavuta. Chotero mabuku, magazini, mafilimu, ndi nyimbo zoyambitsa malingaliro a kugonana zimayambitsa chikhumbo choipa, ndipo m’kupita kwa nthaŵi chikhumbochi chimatsogolera ku uchimo. Kuti tikhalebe ndi khalidwe loyera, tiyenera kudzaza malingaliro athu ndi nzeru yaumulungu.​—Yakobo 3:17.

Zochitika Zotsogolera ku Chisembwere

9-11. Monga momwe Solomo anasimbira, kodi ndi zochitika zotani zimene pang’ono ndi pang’ono zinapangitsa mnyamata wina kuchita chisembwere?

9 Kaŵirikaŵiri, pamakhala zochitika zodziŵikiratu zotsogolera ku chisembwere. Chochitika chilichonse chimapangitsa kuti kubwerera kukhale kovuta kwambiri. Taonani mmene zimenezi zikulongosoledwera pa Miyambo 7:6-23. Solomo akuona zochitika za “mnyamata wopanda nzeru,” kapena wopanda zolinga zabwino. Mnyamatayo “alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo [hule], ndi kuyenda panjira ya ku nyumba yake; pa madzulo kuli sisiro.” Eya, kulakwitsa kwake koyamba kumeneko. Madzulo, mtima wake wam’tsogolera, osati m’khwalala lina lililonse, koma m’khwalala limene akudziŵa kuti angapezemo hule.

10 Kenako tikuŵerenga kuti: “Taona, mkaziyo anam’chingamira, atavala zadama wochenjera mtima.” Mnyamatayo wamuona tsopano mkaziyo! Akanatha kupotoloka ndi kubwerera kunyumba, koma zimenezo n’zovuta kwambiri kusiyana ndi poyambapo, makamaka popeza kuti mnyamatayo alibe maganizo a khalidwe lapamwamba. Mkaziyo akugwira mnyamatayo ndi kum’psopsona. Povomereza kupsopsonedwako, tsopano akumvetsera mawu ake okopa koma achinyengo akuti: “Nsembe za mtendere [zoyamika] zili nane,” mkaziyo akutero. “Lero ndachita zoŵinda zanga.” Nsembe zoyamika zinkaphatikizapo nyama, ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 19:5, 6; 22:21; Numeri 15:8-10) Mwa kutchula zimenezo, mwina anali kupereka lingaliro lakuti alibe vuto ndi mkhalidwe wake wauzimu komanso, panthaŵi imodzimodziyo, mwina anali kumuuza kuti kunyumba kwake kuli zakudya ndi zakumwa zambiri zabwino. Ndiye akum’chonderera kuti: “Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamaŵa; tidzisangalatse ndi chiyanjano.”

11 Chotsatira chake n’chodziŵikiratu. “Am’patutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.” Mnyamatayo akutsatira mkaziyo kunyumba kwake “monga ng’ombe ipita kukaphedwa” monganso “mbalame yothamangira msampha.” Solomo akumaliza ndi mawu ogwira mtima akuti: “Osadziŵa kuti adzawononga moyo wake.” Adzawonongetsa moyo wake chifukwa chakuti “adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.” (Ahebri 13:4) Palitu phunziro lamphamvu kwa amuna ndi akazi pamenepa! Sitiyenera kuyamba n’komwe kuchita kalikonse kamene kadzatsogolera ku kusayanjidwa ndi Mulungu.

12. (a) Kodi mawu akuti “wopanda nzeru” akutanthauzanji? (b) Kodi nyonga ya khalidwe labwino tingaikulitse motani?

12 Onani kuti mnyamata wa m’nkhaniyi anali “wopanda nzeru.” Mawu ameneŵa akutisonyeza kuti maganizo ake, zikhumbo zake, zomwe ankakonda, mtima wake, ndi zolinga zake m’moyo sizinali zogwirizana ndi zimene Mulungu amasangalala nazo. Posakhala ndi maganizo a khalidwe lapamwamba, anaphula ngozi. Mu “masiku otsiriza” ano ovuta chonchi, pamafunika khama kuti tikhale ndi nyonga ya khalidwe labwino. (2 Timoteo 3:1) Mulungu amapereka makonzedwe otithandiza. Amapereka misonkhano ya mpingo wachikristu kuti itilimbikitse kuyenda m’njira yoyenera ndi kutisonkhanitsa pamodzi ndi ena amene ali ndi cholinga chofananacho. (Ahebri 10:24, 25) Pali akulu a mumpingo amene amatisamalira monga abusa ndi kutiphunzitsa njira zachilungamo. (Aefeso 4:11, 12) Tili ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, otilangiza ndi kutitsogolera. (2 Timoteo 3:16) Ndiponso nthaŵi zonse, tili ndi mwayi wopempherera mzimu wa Mulungu kuti utithandize.​—Mateyu 26:41.

Kuphunzirapo Kanthu pa Machimo a Davide

13, 14. Kodi Mfumu Davide inaloŵa motani mu uchimo waukulu?

13 Ngakhale zili motero, n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale atumiki okhulupirika kwambiri a Mulungu agwera m’chisembwere. Mmodzi mwa anthu oterowo anali Mfumu Davide, amene kwa zaka zambiri anali atatumikira Yehova mokhulupirika. M’posakayikitsa kuti ankakonda Mulungu ndi mtima wonse. Koma, anadzaloŵerera mu uchimo. Mofanana ndi mnyamata amene Solomo anam’longosola, panali zochitika zina zimene zinatsogolera Davide mu uchimo kenakonso n’kuuwonjezera.

14 Panthaŵiyo, Davide anali wazaka zapakati, mwinamwake za kuchiyambiyambi kwa ma 50. Ali padenga lake, iye anaona Bateseba wokongolayo akusamba. Atafufuza za iye, Davide anauzidwa za mkaziyo ndipo anadziŵanso kuti mwamuna wake, Uriya, anali mmodzi mwa asilikali omwe anapita kukazinga Raba, mzinda wina wa Aamoni. Davide anamuitanitsa kunyumba yake yachifumu ndipo anagona naye. Pambuyo pake, zinthu zinavuta​—Bateseba anazindikira kuti ali ndi mimba ya Davide. Davide anaitanitsa Uriya kunkhondoko poyembekeza kuti akabwera adzagona ndi mkazi wake. Mwa njira imeneyo, zikanaoneka ngati kuti Uriya ndiye tate wa mwana wa Bateseba. Koma Uriya sanapite kunyumba kwake. Pofunitsitsa kubisa tchimo lake, Davide kenako anabweza Uriya ku Raba atam’patsira kalata yopita kwa kazembe wa gulu lankhondo yonena kuti Uriya aikidwe pamalo poti aphedwe. Uriya anatayadi moyo wake, ndipo Davide anakwatira mkazi wamasiyeyo zisanadziŵike kwa anthu kuti ali ndi mimba.​—2 Samueli 11:1-27.

15. (a) Kodi tchimo la Davide linavumbulidwa motani? (b) Kodi Davide anatani atamva chidzudzulo chaluso cha Natani?

15 Zinaoneka ngati kuti njira ya Davide yobisira tchimo lake yagwiradi ntchito. Miyezi inadutsa. Mwana wamwamuna anabadwa. Ngati Davide anali kuganizira nkhaniyi polemba Salmo 32, ndiye kuti mosakayikira chikumbumtima chake chinam’vutitsa. (Salmo 32:3-5) Komabe, tchimo limenelo silinabisike kwa Mulungu. Baibulo limati: “Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.” (2 Samueli 11:27) Yehova anatumiza mneneri Natani, amene mwaluso anauza Davide zimene anachita. Pomwepo, Davide anavomereza tchimo lake napempha Yehova kuti am’khululukire. Anayanjidwanso ndi Mulungu chifukwa chakuti analapadi moona mtima. (2 Samueli 12:1-13) Davide sanaipidwe podzudzulidwa. M’malo mwake, anasonyeza malingaliro otchulidwa pa Salmo 141:5 akuti: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati n’chifundo: Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane.”

16. Ndi chenjezo komanso uphungu wotani umene Solomo anapereka ponena za machimo?

16 Solomo, amene anali mwana wachiŵiri wa Davide ndi Bateseba, ayenera kuti anasinkhasinkha za nthaŵi ya chivuto chimenechi m’moyo wa atate wake. Anadzalemba kuti: “Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.” (Miyambo 28:13) Ngati tachita tchimo lalikulu, tiyenera kutsatira uphungu wouziridwa umenewu, womwe ndi chenjezo komanso ndi uphungu. Tiyenera kuvomereza tchimo lathu kwa Yehova ndi kufikira akulu mumpingo kuti atithandize. Ntchito yaikulu ya akulu ndiyo kuthandiza kuwongolera amene achita tchimo.​—Yakobo 5:14, 15.

Kupirira Zotsatira za Uchimo

17. Ngakhale kuti Yehova amakhululukira machimo, kodi satitchinjiriza ku chiyani?

17 Yehova anakhululukira Davide. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Davide anali munthu wokhulupirika, chifukwa chakuti anali kukhululukira ena, ndiponso chifukwa chakuti kulapa kwake kunali kochokeradi mumtima. Komabe, si kuti Davide anatchinjirizidwa ku zotsatira zoipa za machimo ake. (2 Samueli 12:9-14) Zilinso chimodzimodzi lerolino. Ngakhale kuti Yehova sadzetsa masoka pa anthu olapa, iye sawatchinjiriza ku zotsatira zachibadwa za zolakwa zawo. (Agalatiya 6:7) Pakati pa zotsatira zina za chisembwere pangakhalenso chisudzulo, mimba zapathengo, matenda opatsirana mwa kugonana, ndi kutha kwa kudaliridwa ndi ulemu.

18. (a) Kodi Paulo anauza mpingo wa ku Korinto kuchita motani ndi munthu amene anali kuchita chigololo choipitsitsa? (b) Kodi Yehova amasonyeza motani chikondi ndi chifundo chake kwa ochimwa?

18 Ngati ifeyo tachita tchimo lalikulu, titha kutaya mtima mosavuta pamene tikuvutika ndi zotsatira za zolakwa zathu. Komabe, sitiyenera kulola chilichonse kutiletsa kulapa ndi kutitsekereza kuti tisayanjanenso ndi Mulungu. M’zaka za zana loyamba, Paulo analembera Akorinto kuti achotse mumpingo mwamuna wina amene anali kuchita chigololo ndi munthu wachibale. (1 Akorinto 5:1, 13) Mwamunayo atalapa moona mtima, Paulo analangiza mpingowo kuti: “Mum’khululukire ndi kum’tonthoza [komanso] mum’tsimikizire ameneyo chikondi chanu.” (2 Akorinto 2:5-8) Mu uphungu wouziridwa umenewu, tikuona chikondi ndi chifundo cha Yehova kwa ochimwa amene alapa. Angelo kumwamba amakondwera pamene wochimwa alapa.​—Luka 15:10.

19. Kuchita chisoni moyenera pacholakwa kungadzetse mapindu otani?

19 Ngakhale ngati tikuchita chisoni ndi kulakwa kwathu, chisoni chimene tikumvacho chingatithandize kuti ‘tikhale ochenjera kuti tisadzachitenso mphulupulu.’ (Yobu 36:21) Ndithudi, zotsatira zoŵaŵa za uchimo ziyenera kutithandiza kuti tisadzachitenso cholakwacho. Komanso, Davide anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira pa khalidwe lake lauchimolo polangiza ena. Iye anati: “Ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.”​—Salmo 51:13.

Chimwemwe Chimadza mwa Kutumikira Yehova

20. Kodi kutsatira miyezo yolungama ya Mulungu kuli ndi mapindu otani?

20 “Odala iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga,” anatero Yesu. (Luka 11:28) Kutsatira miyezo yolungama ya Mulungu kumadzetsa chimwemwe tsopano komanso m’tsogolo mosatha. Ngati takhalabe ndi khalidwe loyera, tiyeni tipitirize kuyenda m’njira imeneyo mwa kugwiritsa ntchito zonse zimene Yehova watigaŵira kuti zitithandize. Ngati tagwera m’chisembwere, tiyeni tipeze chitonthozo chakuti Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu amene alapadi moona mtima, ndipo tiyeni tidzitsimikizire mumtima kuti sitidzabwerezanso tchimolo.​—Yesaya 55:7.

21. Kodi ndi kugwiritsa ntchito uphungu uti wa mtumwi Petro kumene kungatithandize kukhalabe ndi khalidwe loyera?

21 Posachedwapa dziko losalungamali lidzachoka, pamodzi ndi maganizo ndi zochitika zake zonse zachiwerewere. Mwa kudzisunga, tidzapindula panopa komanso kosatha. Mtumwi Petro analemba kuti: “Okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema. . . . Pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osayeruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu.”​—2 Petro 3:14, 17.

Kodi Mungalongosole?

• N’chifukwa chiyani kusunga khalidwe loyera kungakhale kovuta?

• Kodi kutsimikiza mtima kwathu kuti tidzatsatira miyezo yapamwamba ya khalidwe tingakuchirikize mwa njira zina ziti?

• Kodi ndi maphunziro otani amene tingatenge pa machimo a mnyamata wotchulidwa ndi Solomo?

• Kodi chitsanzo cha Davide chikutiphunzitsanji ponena za kulapa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kudziŵitsa ena za malingaliro anu pankhani ya kudzisunga kungakutetezeni

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Chifukwa chakuti Davide analapa moona mtima, Yehova anam’khululukira