Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“N’takhala ndi Chikhulupiriro Chosafooka”!

“N’takhala ndi Chikhulupiriro Chosafooka”!

Mbiri ya Moyo Wanga

“N’takhala ndi Chikhulupiriro Chosafooka”!

YOSIMBIDWA NDI HERBERT MÜLLER

Patapita miyezi yochepa yokha gulu la nkhondo la Hitler litalanda dziko la Netherlands, Mboni za Yehova anaziletsa. Pasanapite nthaŵi, dzina langa linaoneka pandandanda ya anthu amene a chipani cha Nazi anali kuwafuna kwambiri, ndipo anandisaka ngati nyama.

NTHAŴI ina, ndinatopa kwambiri n’kubisalabisala komanso kuthaŵathaŵa moti ndinauza mkazi wanga kuti kukanakhala bwino kuti gulu la nkhondolo lingondigwira. Kenaka ndinakumbukira mawu a nyimbo akuti: “N’takhala ndi chikhulupiriro chosafooka, ngakhale adani onse atandizunza.” * Maganizo a nyimbo imeneyo anandilimbitsa ndipo ndinakumbukira makolo anga ku Germany komanso tsiku limene anzanga anaimba nyimbo imeneyo potsazikana nane. Kodi ndingakuuzeni zina zimene ndikukumbukira?

Chitsanzo cha Makolo Anga

Pamene ndinabadwa mu 1913 ku tauni ya Copitz ku Germany, n’kuti makolo anga ali m’tchalitchi chotchedwa Evangelical Church. * Mu 1920, patatha zaka zisanu ndi ziŵiri, bambo analeka tchalitchicho. Pa April 6, anapempha Kirchenaustrittsbescheinigung (Kalata Yovomereza Kusiya Tchalitchi). Mkulu wa boma wolembera tauniyo anawalembera kalatayo. Komabe, patatha mlungu umodzi, bambo anapitanso ku ofesi ija kukanena kuti dzina la mwana wawo wamkazi sanalilembe pa kalatayo. Mkuluyo analemba kalata yachiŵiri kuti nayenso Martha Margaretha Müller wasiya tchalitchi chimenecho. Panthaŵi imeneyo, achemwali anga a Margaretha anali ndi chaka chimodzi ndi theka. Pankhani yotumikira Yehova, bambo sankafuna zinthu zimene sanakhutire nazo!

Chaka chomwecho, makolo anga anabatizidwa ndi Ophunzira Baibulo, mmene ankatchulira Mboni za Yehova panthaŵi imeneyo. Bambo anatilera anafe mokhwimitsa zinthu, koma kukhulupirika kwawo kwa Yehova kunachititsa kuti tisavutike kutsata malangizo ake. Kukhulupirika kunawachititsanso makolo anga kusintha. Mwachitsanzo, sankatilola kukaseŵera kunja Lamlungu lililonse. Komabe, tsiku lina Lamlungu mu 1925, makolo athu anatiuza kuti tikupita kokayenda. Tinanyamula todyaidya tathu ndipo tinasangalala. Kunali kusinthatu kumeneko kusiya kukhala obindikira m’nyumba tsiku lonse! Bambo ananena kuti anaphunzira mfundo zina pamsonkhano wachigawo umene unangochitika kumene zimene zinawathandiza kusintha malingaliro awo pazochita za Lamlungu. Nthaŵi zina, ankasonyezanso mzimu womwewo wofunitsitsa kusintha.

Ngakhale makolo anga anali odwaladwala, sanaleke ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, kuti tigaŵire thirakiti lamutu wakuti Ecclesiastics Indicted, tinakwera sitima yapamtunda tsiku lina usiku pamodzi ndi mpingo wonse n’kupita kutauni ya Regensburg, makilomita 300 kuchoka ku Dresden. Tsiku lotsatira, tinagaŵira mathirakitiwo m’tauni yonseyo, ndipo pamene tinamaliza, tinabwereranso ndi sitima yapamtunda. Pafupifupi maola 24 anali atatha pamene tinafikanso kunyumba.

Kuchoka Kunyumba Kwathu

Kukhala kwanga m’gulu la Jugendgruppe (Gulu la Achinyamata) mumpingo wathu kunandithandizanso kukula mwauzimu. Mlungu uliwonse, achinyamata azaka zopitirira 14 ankakumana ndi abale ena achikulire a mumpingowo. Tinkachita maseŵera komanso kuimba nyimbo ndi zida zoimbira, kuphunzira Baibulo, ndi kukambirana za chilengedwe ndi sayansi. Komabe, mu 1932, ndili ndi zaka 19, ndinachoka m’gululo.

Mu April chaka chomwecho, Bambo analandira kalata yochokera ku ofesi ya Watch Tower Society ku Magdeburg. Sosaite inkafuna munthu wodziŵa kuyendetsa galimoto komanso wofuna kuchita upainiya. Ndinali kudziŵa kuti makolo anga ankafuna kuti ndichite upainiya, koma ndinkaona kuti sindingathe. Popeza kuti makolo anga anali osauka, ndinayamba ndili ndi zaka 14 kukonza njinga ndi makina osokera, komanso mataipilaita, ndi zipangizo zina za muofesi. Ndikanachoka bwanji kwathu? Iwo amadalira ine kuwathandiza. Komanso, ndinali ndisanabatizidwe. Bambo anakhala nane pansi n’kundifunsa mafunso kuti aone ngati ndinamvetsetsa zimene ubatizo umafuna. Pamene anakhutira ndi mayankho anga kuti ndinali nditapita ndithu patsogolo mwauzimu kuti ndibatizidwe, iwo anati: “Uyenera kudzipereka kuti uchite ntchito imeneyi.” Ndinaterodi.

Patatha mlungu umodzi, anandiitana kupita ku Magdeburg. Nditawauza anzanga m’Gulu la Achinyamata, anakonda kutsazikana nane ndi nyimbo yabwino kwambiri. Anadabwa ndi nyimbo imene ndinasankha chifukwa chakuti anaitenga kukhala yaulemu kwambiri. Ngakhale zinali choncho, ena anatenga zoimbira zawo zotchedwa violin, mandolin, ndi magitala ndipo onse anaimba nyimbo yakuti: “N’takhala ndi chikhulupiriro chosafooka, ngakhale adani atandizunza; chimene sichingagwedezeke chifukwa cha masoka ochitika padziko.” Tsiku limenelo, sindinadziŵe kuti mawu amenewo adzandilimbitsa kangati m’zaka zimene zinali kudza.

Chiyambi Chovuta

Abale ku Magdeburg atayesa luso langa loyendetsa galimoto, anandipatsa galimoto pamodzi ndi apainiya ena anayi, ndipo tinapita ku Schneifel, dera lakufupi ndi Belgium. Tinadziŵa msanga kuti galimoto lathu linali chinthu chofunika. Tchalitchi cha Akatolika m’dera limenelo chinakwiya chifukwa cha kufikako kwathu, ndipo nthaŵi zambiri ansembe ankalimbikitsa anthu akumidzi kudikirira kuti atithamangitse. Nthaŵi zambiri, galimotolo limatithandiza kuthaŵa kuti asatipweteke ndi makasu ndi ntchokhotho zawo.

Mwambo wa Chikumbutso utatha mu 1933, woyang’anira chigawocho, Paul Grossmann, anatiuza kuti ntchito ya Sosaite ku Germany inaletsedwa. Posakhalitsa, ofesi ya nthambi inandiuza kuti ndipite ndi galimoto ku Magdeburg kuti ndikanyamuleko mabuku kupita nawo ku boma la Saxony, pafupifupi makilomita 100 kuchoka ku Magdeburg. Komabe, pamene ndinafika ku Magdeburg, a Gestapo (apolisi achinsinsi a Nazi) anali atatseka kale ofesi ya Sosaite. Ndinasiyira galimoto mbale ku Leipzig n’kubwerera kunyumba​—koma sindinakhalitseko.

Anandiitana ku ofesi ya Sosaite ku Switzerland kuti ndikayambe upainiya ku Netherlands. Ndinaganiza zopitako pakati pa mlungu umodzi kapena milungu iŵiri. Komabe, bambo anandilangiza kuti ndipite nthaŵi yomweyo. Ndinamvera, ndipo patangotha maola ochepa okha, ndinanyamuka. Tsiku lotsatira, apolisi anafika kunyumba kwa bambo kuti andimange chifukwa chothaŵa. Anali atachedwa.

Kuyamba Upainiya ku Netherlands

Pa August 15, 1933, ndinafika kunyumba ya apainiya ku Heemstede, tauni imene inali makilomita 25 kuchoka ku Amsterdam. Tsiku lotsatira ndinapita kukalalikira osadziŵa n’komwe chinenero cha Chidatchi. Ndinayamba kulalikira nditanyamula khadi laumboni, limene analembapo ulaliki. Zinandilimbitsa mtima kwambiri pamene mkazi wachikatolika analandira buku lamutu wakuti Reconciliation! Ndinagaŵiranso timabuku 27 tsiku lomwelo. Pakutha kwa tsiku loyamba limenelo, ndinali ndi chimwemwe chosefukira chifukwa chakutha kulalikiranso mwaufulu.

Masiku amenewo, apainiya analibe njira ina iliyonse yopezera ndalama kuposa zopereka za anthu zimene ankalandira akagaŵira mabuku. Ndalamayo imagwira ntchito yogulira chakudya ndi zinthu zina zofunika. Ndalamayo ikatsalako pang’ono pakutha kwa mwezi, tinkagaŵana molingana apainiya onse kuti tigule zimene tikufuna. Tinali ndi zinthu zochepa, koma Yehova anatithandiza kwambiri moti mu 1934, ndinali nawo pamsonkhano wachigawo ku Switzerland.

Mnzanga Wokhulupirika

Pamsonkhano wachigawowo, ndinaonana ndi Erika Finke wa zaka 18. Ndinam’dziŵa kuyambira panthaŵi imene ndinkakhala kwathu. Anali mnzake wa mchemwali wanga, Margaretha, ndipo Erika ankandisangalatsa nthaŵi zonse chifukwa chakuti ankalimbikira choonadi kwambiri. Sipanatenge nthaŵi yaitali atangobatizidwa mu 1932, munthu wina anakauza a Gestapo kuti Erika anakana kunena kuti “Heil Hitler!” A Gestapo anam’funafuna ndipo anafuna kudziŵa chifukwa chake anakana kutero. Erika anaŵerengera wapolisi kupolisiko Machitidwe 17:3 n’kufotokoza kuti Mulungu anasankha munthu mmodzi yekha kukhala Mpulumutsi, Yesu Kristu. “Kodi pali enanso amene amakhulupirira chimodzimodzi ngati iweyo?” wapolisiyo anafuna kuti adziŵe. Erika anakana kupereka mayina alionse. Pamene wapolisiyo anamuopseza kuti am’manga, Erika anamuuza kuti kuli bwino kuti afe kuposa kuti apereke mayinawo. Anam’yang’anitsitsa n’kukuwa kuti: “Ndichokere pano. Pita kwanu. Heil Hitler!”

Msonkhanowo utatha, ndinabwerera ku Netherlands pamene Erika anatsala ku Switzerland. Koma tonse aŵirife, tinakopeka ndi mnzake, moti ubwenzi wathu unakula. Erika adakali ku Switzerland, anamva kuti a Gestapo ankam’funafuna kunyumba. Anaganiza zongokhala ku Switzerland ndi kuchita upainiya. Patapita miyezi yochepa, Sosaite inamuuza kuti apite ku Spain. Anachita upainiya ku Madrid, kenaka ku Bilbao, ndiyeno ku San Sebastián, kumene chifukwa cha chizunzo chimene anayambitsa atsogoleri a matchalitchi achikristu, iye ndi mnzake amene ankachita naye upainiya anamangidwa. Mu 1935, anawalamula kuti achoke ku Spain. Erika anabwera ku Netherlands, ndipo chaka chomwecho tinakwatirana.

Nkhondo Yoopsa Inali Pafupi Kuyamba

Titakwatirana, tinachita upainiya ku Heemstede, ndipo tinachoka kupita ku mzinda wa Rotterdam. Mwana wathu wamwamuna, Wolfgang, anabadwira kumeneko mu 1937. Chaka chotsatira tinachoka kupita ku mzinda wa Groningen, kumpoto kwa Netherlands, kumene tinakhala m’nyumba imodzi ndi apainiya a ku Germany, Ferdinand ndi Helga Holtorf ndi mwana wawo wamkazi. Sosaite inatiuza mu July 1938 kuti boma la Dutch linachenjeza kuti Mboni zimene zinali za ku Germany sakuzilolanso kulalikira. Kukhala ngati nthaŵi yomweyo, anandiika kukhala mtumiki wadera (woyang’anira dera), ndipo banja lathu linasamuka n’kukhala m’boti lotchedwa Lichtdrager (Wonyamula Kuunika) la Sosaite limene linkagwira ntchito ngati nyumba ya apainiya amene ankalalikira dera la kumpoto kwa Netherlands. Nthaŵi zambiri, ndinkasiya banja langa, kumayenda panjinga kuchoka pampingo wina kumka ku mpingo winanso kukalimbikitsa abale kuti apitirize kulalikira. Ndipo abale ankachitadi zomwezo. Ndipo ena anawonjezera zochita zawo. Amene anali chitsanzo chabwino ndi Wim Kettelari.

Pamene ndinakumana ndi Wim, anali mnyamata amene ankadziŵa choonadi koma anali wotanganidwa kwambiri monga wogwira ntchito pafamu. “Ngati ukufuna kukhala ndi nthaŵi yotumikira Yehova,” ndinam’langiza, “uyenera kufuna ntchito ina.” Anaterodi. Ndiyeno pamene tinakumananso, ndinam’limbikitsa kuti achite upainiya. “Koma ndiyenera kugwira ntchito kuti ndidye,” anayankha choncho. “Udzadya,” ndinam’tsimikizira. “Yehova adzakusamala.” Wim anayamba kuchita upainiya. Pambuyo pake, ngakhale panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anachita ntchito ya woyang’anira woyendayenda. Lerolino, pamene Wim ali ndi zaka za m’ma 80, ndi Mboni yolimbikirabe. Yehova anam’yang’aniradi.

Nthaŵi ya Chiletso Komanso Kufunidwa

Pafupifupi chaka chitatha mwana wathu wachiŵiri, Reina atabadwa, mwezi wa May 1940, gulu lankhondo la Dutch linagonja ndipo a Nazi anatenga dziko la Netherlands. Mu July a Gestapo analanda ofesi ya Sosaite ndi makina osindikizira. Chaka chotsatira, kunali chipwirikiti chogwira Mboni, ndipo anandigwira. Pokhala Mboni komanso Mjeremani wazaka zoyenerera kuitanidwa kupita ku nkhondo, zinali zosavuta kuganizira zimene a Gestapo akanandichita. Ndinaganiza kuti basi sindidzalionanso banja langa.

Ndiye mu May 1941, a Gestapo ananditulutsa m’ndende n’kundiuza kuti ndipite ku nkhondo. Sindinakhulupirire zimenezo. Tsiku lomwelo ndinayamba kuzembazemba, ndipo mwezi womwewo ndinayambiranso ntchito yadera. A Gestapo anandiika pandandanda ya anthu amene ankawafuna kwambiri.

Mmene Banja Langa Linazoloŵerera

Mkazi wanga pamodzi ndi ana anali atasamukira ku mudzi wa Vorden chakum’maŵa kwa dzikolo. Komabe, powachepetsera mavuto, ndinali kupita kunyumbako kamodzikamodzi. (Mateyu 10:16) Abale sankatchula dzina langa lenileni chifukwa chofuna kunditeteza, koma ankatchula dzina lopeka lakuti Duitse Jan (John Mjeremani). Ngakhale mwana wanga wamwamuna wazaka zinayi, Wolfgang, sankamulola kunena kuti “Bambo” koma kungoti “Ome Jan” (Amalume John). Zimenezi zinali zom’vutitsa maganizo kwambiri.

Pamene ndimathaŵathaŵa, Erika anayang’anira ana komanso anapitirizabe kulalikira. Pamene Reina anali ndi zaka ziŵiri, Erika anali kumuika monyamulira katundu panjinga n’kupita naye kukalalikira kumidzi. Ngakhale kuti kupeza chakudya kunali vuto, Erika sanasoŵerepotu chakudya cha banja lathu. (Mateyu 6:33) Mlimi wina Mkatolika, amene ndinam’konzera makina ake osokera nthaŵi inayake, ankam’patsa mbatata. Ankaperekanso uthenga wanga kwa Erika. Nthaŵi inayake, iye analipira gulden imodzi imene ndi ndalama ya kuno ku Netherlands pogula chinthu chinachake m’sitolo yogulitsa mankhwala. Mwinisitolo, podziŵa kuti iye ankakhala mobisala ndipo sankatha kupeza makadi ogulira zakudya, anam’patsa chinthucho komanso ma gulden aŵiri. Anthu achifundo ngati amenewo anam’thandiza kuti apulumuke.​—Ahebri 13:5.

Kugwira Ntchito Pamodzi ndi Abale Olimba Mtima

Panthaŵi imeneyo, ndinapitiriza kuyendera mipingo​—ngakhale ndinali kukumana ndi abale amene anali ndi udindo okhaokha m’mipingo. Sindinkatha kukhala maola angapo pamalo amodzimodzi chifukwa chakuti a Gestapo ankandilondalonda kwambiri. Abale ndi alongo ambiri sankawalola kuti aonane nane. Ankadziŵana ndi Mboni za m’kagulu kawo ka phunziro la Baibulo basi. Choncho, akazi ena aŵiri pachibale pawo amene ankakhala mbali zosiyana mumzinda umodzi anadzadziŵa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha kuti onse anakhala Mboni m’kati mwa nkhondoyo.

Ntchito yanga inanso inali kupeza malo obisa mabuku a Sosaite. Tinkabisanso mapepala, makina osindikizira, ndi mataipilaita olembera makope a Nsanja ya Olonda, kuchitira kuti mwina akanadzafunika. Nthaŵi zina, tinkachotsa mabuku amene Sosaite inasindikiza pamalo amene tinawabisa kukawabisa kwina. Ndikukumbukira nthaŵi inayake tikunyamula makatoni 30 odzaza mabuku tikuyesetsa kuti anthu asatizindikire​—ntchitotu yochititsa mantha!

Komanso, tinalinganiza kanyamulidwe ka chakudya kuchoka ku mafamu a kum’maŵa kwa Netherlands kupita ku mizinda ya kumadzulo kwake, ngakhale kuti zimenezi zinali zoletsedwa. Tinali kupakira chakudya m’ngolo yokokedwa ndi mahachi n’kuloŵera kumadzulo. Tikafika pamtsinje, sitinkawolokera pamlatho chifukwa asilikali amalonderapo. Komano, tinkatsitsira katunduyo m’timabwato, n’kumawolotsa chakudyacho pamtsinjewo, kenaka n’kupakiranso katunduyo m’ngolo ina. Tikafika kumzinda womwe tinali kupitako, tinali kudikira mpaka kutachita mdima, n’kuveka nsokosi kumapazi a mahachiwo, n’kupitano mwakachetechete kumalo a mpingo obisako chakudya. Tinkatumiza chakudyacho kwa abale osoŵa kuchokera kumeneko.

Ngati asilikali a German akanatulukira malo amenewo, wina akanafa. Komabe, abale angapo anadzipereka kuti athandize. Mwachitsanzo, banja la a Bloemink m’tauni ya Amersfoort linalola kuti chipinda chawo chochezera chigwire ntchito yosungira chakudya, ngakhale kuti nyumba yawoyo inali pafupi ndi kampu ya asilikali a German! Mboni zolimba mtima ngati zimenezo zinaika moyo wawo pachiswe chifukwa cha abale awo.

Yehova anandithandiza ine ndi mkazi wanga kukhalabe okhulupirika zaka zonsezo zachiletso. Mu May 1945 asilikali a German anagonja, ndipo moyo wanga wokhala chobisala unathera pomwepo. Sosaite inandipempha kuti ndipitirize kugwira ntchito ya woyang’anira woyendayenda mpaka pamene abale ena anapezeka. Mu 1947, Bertus van der Bil anatenga udindo wanga. * Panthaŵi imeneyo n’kuti mwana wathu wachitatu atabadwa, ndipo tinakhazikika dera la kum’maŵa kwa dzikolo.

Chisoni Komanso Chimwemwe

Nkhondo itatha, ndinamva kuti bambo anamangidwa pafupifupi chaka chitatha nditachoka kunyumba kupita ku Netherlands. Anawamasula kaŵiri chifukwa cha kufooka kwa thanzi, ndipo nthaŵi iliyonse akawamasula, amawamanganso. Mwezi wa February mu 1938, anawapititsa kumsasa wachibalo wa Buchenwald kenaka wa Dachau. Abambo anga anamwalira kumeneko pa May 14, 1942. Anakhalabe wolimba komanso wokhulupirika mpaka mapeto.

Amayi anga anawapititsanso ku msasa wa Dachau. Anakhalabe konko mpaka pamene anawamasula mu 1945. Popeza kuti chitsanzo cholimba cha makolo anga onse chinandithandiza kwambiri kupeza madalitso auzimu amene ndinakhala nawo, unali mwayi wathu kuti amayi anadzakhala nafe mu 1954. Mchemwali wanga Margaretha​—amene ankachita upainiya ku Communist East Germany kuyambira mu 1945​—anabwera nawo. Ngakhale amayi ankadwala komanso sankadziŵa kulankhula chinenero cha Chidatchi, anapitirizabe kuchita nawo utumiki wakumunda mpaka pamene anamaliza moyo wawo wa padziko lapansi mu October 1957.

Msonkhano wachigawo wa mu 1955 ku Nuremberg, ku Germany, unakhaladi wapadera. Titafika kumeneko, abale ochokera ku Dresden anauza Erika kuti amayi ake analiponso pamsonkhano wachigawowo. Popeza kuti panthaŵi imeneyo mzinda wa Dresden unali kulamulidwa ndi East German, Erika anali asanaone amayi ake kwa zaka 21. Anakonza zoti akumane, ndipo atakumana, amayi ndi mwana wawo wamkazi anakumbatirana. Kunali kukumananso kosangalatsatu kwambiri kumeneko!

Patatha nthaŵi yaitali, banja lathu linakula kukhala ndi ana asanu ndi atatu. Mwatsoka, mwana wathu wamwamuna mmodzi anafa pangozi ya galimoto. Komabe, timasangalala kwambiri kuona ana athu amene alipo akutumikira Yehova. Ndife okondwa kuti mwana wathu wamwamuna Wolfgang ndi mkazi wake amachita ntchito yadera ndi kuti mwana wawo wamwamuna nayenso akugwira ntchito yoyang’anira dera.

Ndili wokondwa kuti ndaona kupita patsogolo kwa ntchito ya Yehova ku Netherlands. Pamene ndinayamba kuchita upainiya kunoko mu 1933, kunali Mboni pafupifupi 100. Lerolino, kuli Mboni zoposa 30,000. Ngakhale mphamvu zathu zikutha tsopano, ine ndi Erika ndife otsimikiza kuchitabe mogwirizana ndi mawu a nyimbo ija yamakedzana akuti: “N’takhala ndi chikhulupiriro chosafooka.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Nyimbo 194.​—Songs of Praise to Jehovah (1928).

^ ndime 7 Tauni ya Copitz, imene masiku ano ikutchedwa Pirna, ili m’mbali mwa mtsinje wa Elbe, makilomita 18 kuchoka ku mzinda wa Dresden.

^ ndime 38 Onani Nsanja ya Olonda ya January 1, 1998, pankhani ya mbiri ya moyo wa mbale Van der Bil yakuti, “Kulibe Chinthu Chabwino Choposa Choonadi.”

[Chithunzi patsamba 23]

Gulu la “Jugendgruppe” panthaŵi yopuma litamaliza utumiki wakumunda

[Chithunzi patsamba 24]

Ine ndi apainiya anzanga tinafola gawo la Schneifel. Ndinali ndi zaka 20

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi Erika ndi Wolfgang mu 1940

[Chithunzi patsamba 26]

Kuchoka kulamanzere mpaka kulamanja: Mdzukulu wanga Jonathan ndi mkazi wake, Mirjam; Erika, ineyo, mwana wanga Wolfgang ndi mkazi wake, Julia

[Chithunzi patsamba 26]

Mbale wina amene anali limodzi ndi bambo kundende anajambula chithunzi chawo chimenechi mu 1941