Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kupemphera Kumathandizadi?

Kodi Kupemphera Kumathandizadi?

Kodi Kupemphera Kumathandizadi?

PAFUPIFUPI aliyense imam’fikira nthaŵi yomwe amaona kuti m’pofunika atapemphera. Kwenikweni, pafupifupi anthu a m’gulu lililonse la chipembedzo amapemphera mwakhama. Mwachitsanzo, Mbuda amapemphera mobwerezabwereza tsiku lililonse pemphero lakuti “Ndiika chikhulupiriro changa mwa Amida Buddha.”

Poona mavuto omwe afala padziko lonse, m’pomveka kufunsa kuti: Kodi anthu akamapemphera amayembekezera kuti apindula chiyani? Kodi mapemphero onseŵa amawathandizadi?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera?

Anthu ambiri akum’maŵa amapemphera kwa makolo awo akale ndi kwa milungu yawo ya Shinto kapena Tao. Amachita zimenezo akumayembekezera kukhoza mayeso kusukulu, kukolola mbewu zochuluka, kapena kupeŵa matenda. Abuda amakhulupirira kuti mwa khama lawo, angathe kuloŵa m’mkhalidwe wa mtendere wokhawokha. Ahindu amapemphera modzipereka kwa milungu yawo yaimuna ndi yaikazi yapamtima kuti iwapatse chidziŵitso, chuma, ndi kuwateteza.

Akatolika ena amakhulupirira kuti angapindulitse anthu mwa kudzipereka kuti akhale amonke kapena avirigo m’nyumba zawo zosafikamo anthu wamba akumapemphera mosalekeza. Akatolika mamiliyoni ambiri amapempha chifundo kwa Mariya mwa kutchula mapemphero oloŵeza pamtima, mwinamwake pogwiritsa ntchito mikanda ya kolona. M’mayiko a Kum’maŵa, anthu ambiri amagwiritsa ntchito magudumu opempherera. Apulotesitanti amabwereza mawu a m’Pemphero la Ambuye, ngakhale kuti nthaŵi zina angafotokoze malingaliro awo kwa Mulungu m’mawu awoawo. Ayuda ambiri amayenda maulendo ataliatali kupita kukapemphera ku Western Wall (Khoma la Kumadzulo) mu Yerusalemu, n’chiyembekezo chakuti kachisi yemwe anali m’Yerusalemumo adzamangidwanso ndikuti nyengo yatsopano ya ulemerero ndi mtendere idzayamba.

Ngakhale kuti mamiliyoni onseŵa amalimbikira kupemphera, anthu akanthidwa mowonjezereka ndi mavuto a umphaŵi, kumwerekera, kutha kwa mabanja, upandu, ndi nkhondo. Kodi tingati n’chifukwa chakuti anthu onseŵa sakupemphera m’njira yoyenera? Mmene zililimu, kodi tingati kulidi aliyense amene amamva mapemphero?

Kodi Pali Aliyense Amene Amamva Mapemphero?

Mapemphero sangakhale othandiza m’njira iliyonse pokhapokha ngati akumvedwa. Pamene munthu akupemphera, n’zodziŵikiratu kuti amakhulupirira kuti winawake wosaoneka, wauzimu akum’mvetsera. Komabe, mapemphero samangoperekedwa ndi mawu chabe. Anthu ambiri amakhulupirira kuti winawake angathe kudziŵa ngakhalenso zomwe zili m’malingaliro a munthu amene akupempherayo. Kodi ameneyu angakhale ndani?

Ofufuza sakudziŵa n’komwe mmene malingaliro amapangidwira m’manyuroni mabiliyoni ochuluka omwe amapanga mbali inayake yapamwamba pa ubongo wathu yotchedwa cerebral cortex. Ndithudi, m’pomveka kuti Amene anapanga ubongowo angadziŵe malingaliro otereŵa. Ndipotu ameneyu si winanso ayi koma Mlengi wathu, Yehova Mulungu. (Salmo 83:18; Chivumbulutso 4:11) Ndi iyeyu woyenera kulandira mapemphero. Koma kodi Yehova amamvetsera mapemphero onse angati ameneŵa?

Kodi Amamva Mapemphero Onse?

Mfumu Davide wa Israyeli wakale anali munthu wokonda kupemphera. Monga wamasalmo wouziridwa ndi Mulungu, anaimba kuti: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.” (Salmo 65:2) Yehova amamva mapemphero operekedwa m’chilichonse cha zinenero masauzande ambirimbiri zomwe anthu amalankhula. Ngakhale kuti palibe munthu amene angamve ndi kusunga nkhani zochuluka chomwecho, sizikutanthauza kuti Mulungu sangamvetsere kwa onse amene amapemphera kwa iye m’njira yovomerezeka.

Komabe, Yesu Kristu​—yemwenso anali munthu wokonda kupemphera​—ananena kuti si mapemphero onse amene amakondweretsa Mulungu. Tamvani zomwe Yesu ananena zokhudza chomwe panthaŵiyo chinali chizoloŵezi chofala chobwereza mapemphero oloŵeza pamtima. Malinga n’kunena kwa Baibulo la Akatolika la Jerusalem Bible, iye anati: “M’mapempero anuwo musabwerezebwereze mawu monga amachitira anthu akunja, pakuti iwo amaganiza kuti mwa kuchulukitsa mawu choncho adzawamvera.” (Mateyu 6:7) Sitingayembekezere Yehova kumvetsera mapemphero omwe sakusonyeza malingaliro athu enieni ochokera pansi pamtima.

Posonyeza chifukwa chake mapemphero ena sakondweretsera Mulungu, mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Wopeŵetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.” (Miyambo 28:9) Mwambi winanso umati: “Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.” (Miyambo 15:29) Nthaŵi inayake pamene atsogoleri a Yuda wakale anali ndi liwongo lalikulu, Yehova anati: “Pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.”​—Yesaya 1:1, 15.

Mtumwi Petro anatchula chinthu chinachakenso chomwe chingapangitse kuti mapemphero akhale osavomerezeka kwa Mulungu. Petro analemba kuti: “Momwemonso amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Mapemphero a munthu amene amanyalanyaza malangizo ngati ameneŵa sangamveke n’komwe!

N’chachidziŵikire kuti pali zina zofunika kuzikwaniritsa kuti mapemphero azimvedwa. Komabe, ambiri amene amapemphera salabadira kwenikweni kuchita zimene Mulungu amafuna kuti tichite. N’chifukwa chaketu kupemphera mwakhama konseku sikunapange dzikoli kukhala labwinopo.

Nanga n’chiyani tsono chimene Mulungu amafuna kuti mapemphero athu azimvedwa? Yankho lake likukhudza chifukwa chomwe timapempherera. Kwenikweni, ngati tikufuna kudziŵa ngati mapemphero ali othandizadi, tiyenera kuzindikira cholinga chake. N’chifukwa chiyani Yehova wakonza njira yakuti tizitha kulankhula naye?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

G.P.O., Yerusalemu