Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupemphera?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupemphera?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupemphera?

“MUPEMPHA, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa . . . Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:3, 8) Mawu amenewo a wophunzira wa Yesu Yakobo angatichititse kulingalira zifukwa zomwe ife timapempherera.

Pemphero silili chabe njira youzira Mulungu zomwe tikufuna. Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anati: “Atate wanu adziŵa zomwe muzisoŵa, inu musanayambe kupempha iye.” Komabe, Yesu ananenanso kuti: “Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu.” (Mateyu 6:8; 7:7) Chotero Yehova amafuna kuti timuuze zomwe tikuzifunadi. Komatu pemphero limakhudza zambiri zoposa zimenezo.

Mabwenzi okondanadi amalankhulana nthaŵi zonse osati pokhapokha pamene akufuna chinthu chinachake. Amachitirana chidwi wina ndi mnzake, ndipo ubwenzi wawo umakula akamauzana zakukhosi. Mofananamo, pemphero lili ndi cholinga chachikulu osati kungopempha chabe zinthu zofunika. Limapereka mwayi wakuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova mwa kusonyeza kudzipereka kwathu kwa iye kochokera m’mtima.

Inde, Mulungu watipatsa mwayi wa pemphero kotero kuti tithe kum’yandikira. Zimenezi zingatheke pokhapokha ngati tikumuuzadi Mulungu maganizo athu m’malo momangobwereza mapemphero oloŵeza pamtima. Ha! Kulankhula ndi Yehova m’pemphero si kunyaditsa kwake! Komanso, mwambi wa m’Baibulo umati: “Pemphero la owongoka mtima lim’kondweretsa.”​—Miyambo 15:8.

“Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu,” anaimba motero wamasalmo Asafu. (Salmo 73:28) Koma kuti tiyandikire kwa Mulungu, tiyenera kuchita zochuluka zoposa kungopemphera. Taonani mmene chochitika chotsatirachi chikusonyezera zimenezi:

“Wina wa ophunzira a [Yesu] anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.” Poyankha Yesu anati: “Mmene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwe; Ufumu wanu udze.” (Luka 11:1, 2) Kodi tingapereke pemphero latanthauzo ngati limeneli tisanaphunzire choyamba dzina la Mulungulo ndi mmene lidzayeretsedwera? Ndipo kodi tingapemphere mogwirizana ndi mawu ameneŵa a Yesu ngati sitikudziŵa chomwe Ufumu wa Mulungu uli? Tingathe kumvetsa zinthu zoterezi ngati titaŵerenga Baibulo mosamalitsa. Chidziŵitso chomwe tidzapeza chidzatithandiza kum’dziŵa Mulungu ndi kuzindikira njira zake. Komanso, kum’dziŵa Yehova Mulungu kudzatichititsa kudzimva kukhala oyandikana naye ndi odzipereka kwambiri kwa iye. M’malo mwake, zimenezi zidzatithandiza kulankhulana naye momasuka kwambiri m’pemphero.

Pemphero Lingathetse Mavuto

Kupanga ubwenzi wamphamvu ndi Yehova kudzatithandiza kuthetsa mavuto. Onani mmene zimenezo zinakhalira zoona m’chilichonse cha zochitika zotsatirazi. Zochitikazi zikusonyeza kuti mwa kupemphera ena anakhoza kulimbikitsa ubwenzi wawo ndi Yehova.

Ku Brazil mkazi wina wotchedwa Maria anapempha thandizo kwa Mulungu. Nthaŵi zonse anafuna kuchita mosemphana ndi makhalidwe omwe anthu ambiri amawavomereza mwazina chifukwa chakuti amaona chinyengo chochuluka mwa anthuwo. Chotero Maria anachoka kwawo ndi kusiya mwamuna ndi ana ake. Anayambanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma atalephera kupeza chimwemwe, anatula nkhaŵa zake kwa Mulungu ndi kum’pempha thandizo.

Posakhalitsa, Mboni ziŵiri za Yehova zinafika ndi kum’siyira Maria kope la Nsanja ya Olonda momwe munali nkhani ya phindu la kutsatira chitsogozo chaumulungu. Linam’gwira mtima kwabasi, ndipo tsiku lomwelo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mbonizo. Mapeto ake zimenezi zinakonzanso moyo wake wabanja. Pamene amaphunzira za Yehova, anafunanso kumam’sonyeza chikondi chake. “Ndinawongolera zochita zanga,” akutero Maria. “Poyamba mwamuna wanga ndi am’banja langa ankandinena chifukwa chakuti ndayamba kuphunzira Baibulo. Koma poona kuti ndayamba kusintha, anayamba kundilimbikitsa.” Patapita nthaŵi, Maria anapatulira moyo wake kwa Wakumva pemphero kuti am’tumikire.

Ngakhale kuti José anali ndi mkazi wokongola ndipo bizinesi yake inali kupita patsogolo ku Bolivia, sanali wokondwa. Mkazi wake anam’thaŵa chifukwa chakuti mwamunayu anali wachimasomaso. Anayamba kumwa mwauchidakwa ndi kumadziona ngati wopanda pake. José akuti: “Ndinayamba kupemphera ndi mtima wonse, kupempha chomwe ndingachite kuti ndikondweretse Mulungu. Mosapita nthaŵi Mboni za Yehova zomwe zimapereka maphunziro apanyumba aulere zinafika pamalo anga ochitira malonda koma ndinawapitikitsa. Zimenezi zinachitika katatu konse. Nthaŵi zonse ndikapempha thandizo, ndinkangozindikira afika. Potsirizira pake, ndinaganiza kuti tsiku lina akadzabweranso ndidzawamvetsere. Baibulo ndinali n’taliŵerengapo lonse ndipo ndinali ndi mafunso ambirimbiri, koma nthaŵi zonse anali kundiyankha mokhutiritsa. Kuphunzira za Yehova kunandipatsa cholinga chatsopano m’moyo, ndipo mabwenzi anga omwenso anali Mboni anali zitsanzo zolimbikitsa kwabasi! Ndinalekana ndi bwenzi langa lalikazi komanso anzanga omwe ndimamwa nawo moŵa. Posakhalitsa, tinagwirizananso ndi mkazi wanga ndi ana anga. Kumayambiriro a chaka cha 1999 ndinabatizidwa.”

Ku Italy, ukwati wa Tamara unali pavuto, chotero anapempherera nzeru. Atam’menya ndi kumuthamangitsa m’banja lamakolo ake ali ndi zaka 14, Tamara anayamba kumaputa anzake dala. Iye akuti: “Ndinapeza Baibulo ndi kuyamba kuliŵerenga. Tsiku lina usiku, ndinaŵerenga kuti ‘kupeza nzeru kuli ngati kupeza chuma chobisika.’ Ndinapempherera nzeru imeneyo. (Miyambo 2:1-6) M’maŵa kutacha, Mboni za Yehova zinafika. Ndinayamba kuphunzira nawo Baibulo, koma zinanditengera nyengo kuti ndiyambe kugwiritsa ntchito zomwe ndimaphunzirazo. Kenako, ndinaganiza zotsatira moyo wachikristu ndipo ndinabatizidwa. Panopo, ine limodzi ndi mwamuna wanga, tikuthandiza ena kupindula ndi nzeru ya Mulungu.”

Beatriz anali mmodzi wa anthu olemera a ku Caracas, Venezuela. Komatu, anasudzulidwa ndipo anavutika mumtima. Nkhaŵa itakula, nthaŵi inayake anapemphera mosaleka kwa maola ambiri. M’maŵa kutacha, belu lapachitseko linalira. Monyansidwa anasuzumira pakabowo ndi kuona anthu aŵiri atanyamula zikwama zonyamulira mabuku. Anangokhala duu, kuchita ngati panyumbapo palibe anthu, koma banjali lisanachoke, linasereza handibilu pansi pa chitseko. Handibilu imeneyi inali yakuti “Dziŵani Baibulo Lanu.” Kodi kubwera kwawoku kunali kogwirizana ndi mapemphero ake ausiku wapita? Anawaitana kunjira kuti abwerere. Posakhalitsa anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo pambuyo pake anabatizidwa. Mwachimwemwe, tsopano Beatriz amaphunzitsa ena mmene angapezere chimwemwe.

Polimbana ndi umphaŵi wadzaoneni, Carmen anapemphera kuti apeze thandizo. Mayiyu anali ndi ana khumi ndipo mwamuna wake Rafael anali chidakwa. Carmen anati: “Ndinkachapa zovala za anthu kuti ndipeze ndalama.” Koma chizoloŵezi cha Rafael choledzeracho chinaipiraipirabe. “Zinali zovuta zedi, komabe titayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mwamuna wangayu anayamba kusintha. Tinaphunzira za lonjezo la Ufumu​—lakuti posachedwa Yehova adzathetsa umphaŵi ndi mavuto. Ndithudi Mulungu anayankha mapemphero anga!” Kuphunzira njira za Yehova kunam’thandiza Rafael kuleka kumwa mowa, ndipo anavala “[u]munthu watsopano.” (Aefeso 4:24) Iye ndi am’banja lake anatha kusintha miyoyo yawo. Rafael anati: “Ngakhale kuti si ndife olemera, ndipo tilibe nyumba yathuyathu, koma zonse zofunika m’moyo tili nazo, ndipo ndife okondwa.”

Pamene Mapemphero Onse Adzayankhidwa

Kodi kupemphera kunawathandiza n’komwe anthu ameneŵa? Kunawathandiza kumene! Ndipo kodi mwaona kuti nthaŵi zambiri mapemphero awo amayankhidwa winawake wochokera kumpingo wachikristu atawathandiza kuyandikira kwa Yehova Mulungu mwa kuphunzira Baibulo?​—Machitidwe 9:11.

Chotero tilitu ndi zifukwa zabwino zopempherera. Posachedwapa, pemphero lakuti Ufumu wa Mulungu udze ndikuti chifuno chake chichitike padziko lapansi lidzayankhidwa. (Mateyu 6:10) Mulungu akadzayeretsa dziko mwa kuchotsa om’tsutsa onse, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova.” (Yesaya 11:9) Ndiyeno onse amene amam’konda Yehova adzasangalala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu”​—ndipotu mwachionekere mapemphero awo adzayankhidwa.​—Aroma 8:18-21.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mukudziŵa chifukwa chake tiyenera kupemphera?