Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo—Buku Lophunzitsa Mokhalira ndi Moyo

Baibulo—Buku Lophunzitsa Mokhalira ndi Moyo

Baibulo​—Buku Lophunzitsa Mokhalira ndi Moyo

“MAWU a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” (Ahebri 4:12) Mawuŵa onena zimene Mawu a Mulungu angachite akusonyezadi kuti Baibulo si buku longolembedwa bwino chabe ayi.

“Uthenga wake ndi wofunika kwambiri pa moyo wathu monga mmene kupuma mpweya kulili,” winawake wolemba zachipembedzo analongosola motero mosapita m’mbali. Ndiyeno anatinso: “Munthu akaganizira nkhani ya chikhumbo chathu cha kuchiritsidwa komanso kufunika kwa kuchiritsidwako lerolino ndiyeno n’kuŵerenga Baibulo poganizira zimenezo, pamakhala zotsatira zodabwitsa.” Monga nyali yowala, Baibulo limatithandiza kumvetsa nkhani ndi mavuto ambiri aakulu a moyo wamakono.​—Salmo 119:105.

Ndithudi, nzeru zomwe zili m’Baibulo zili ndi mphamvu youmba maganizo athu, kutithandiza kuthetsa mavuto ena, kuwongolera moyo wathu, ndi kutipatsa maluso ofunika polimbana ndi mikhalidwe imene sitingaisinthe. Komanso chofunika kwambiri n’chakuti Baibulo limatithandiza kum’dziŵa Mulungu ndi kum’konda.

Buku Lopereka Chifuno

Wolemba Baibulo, Yehova Mulungu, ‘amadziŵa njira zathu zonse.’ Iye amadziŵa bwino lomwe zosoŵa zathu zakuthupi, zamumtima, ndi zauzimu kuposanso mmene ifeyo timazidziŵira. (Salmo 139:1-3) Mosamala, amaika malire oonekeratu pakhalidwe la anthu. (Mika 6:8) Ndi nzeru yabwino kufuna kumvetsa malire ndi zitsogozo zimenezo ndi kuphunzira kuzitsatira. Wachimwemwe ali iye amene “m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake,” anatero wamasalmo. “Zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:1-3) Chiyembekezo chimenecho chitisonkhezera kulipenda.

Maurice, mphunzitsi wapasukulu yemwe anapuma pantchito, anali kudziŵa kuti Baibulo n’lopindulitsa pophunzira mbiri yakale komanso monga buku lamfundo zabwino zophunzitsa. Komabe, anali kukayikira zonena kuti n’louziridwa ndi Mulungu. Atamvetsera malongosoledwe onena za chifukwa chimene Mulungu anapatsira anthu Mawu ake olembedwa, Maurice anapenda maulosi a m’Baibulo osiyanasiyana. Pamene anali mnyamata, anaphunzira mbiri yamakedzana, mabuku osiyanasiyana, sayansi, ndi maphunziro a chilengedwe cha dziko lapansi ndi zamoyo zake. Iye akuvomereza kuti ankadziyesa wanzeru kwambiri moti sanathe kuona zitsanzo zambirimbiri zochirikiza Baibulo. “Ndinali wotanganitsidwa kwambiri ndi kufunafuna moyo wa phee, chuma, ndi zosangalatsa za m’moyo. N’zomvetsa chisoni kuti sindinadziŵe za kukongola ndi choonadi cha buku loposa mabuku ena onse omwe analembedwapo.”

Tsopano pomwe ali ndi zaka za m’ma 70, Maurice, akunena moyamikira pogwirizanitsa mawu ake ndi nkhani yosimba za kuonekera kwa Yesu kwa mtumwi Tomasi, kuti: “Dzanja langa latsogozedwa ku ‘bala’ limene lidzachotseratu kwamuyaya chikayiko chilichonse pamfundo yakuti Baibulo ndi choonadi chokhachokha.” (Yohane 20:24-29) Monga momwe mtumwi Paulo ananeneradi, Baibulo limavumbula zolinga za mumtima, ndipo limapangitsa moyo kukhala watanthauzo. Lilidi buku lophunzitsa mokhalira ndi moyo.

Kulimbitsa Moyo Wovutika

Baibulo limaperekanso uphungu wothandiza anthu kusiya zizoloŵezi zoipa. Daniel anakwanitsa kusiya chizoloŵezi chodetsa cha kusuta fodya, ndi kusiyanso kupita kumapwando a zochitika zosadziletsa komanso kumwetsa mowa. (Aroma 13:13; 2 Akorinto 7:1; Agalatiya 5:19-21) Kunena zoona, kusiya zizoloŵezi zimenezi ndi kuvala “[u]munthu watsopano” kumafuna chamuna. (Aefeso 4:22-24) “Inali nkhondo,” akutero Daniel, “chifukwa chakuti ndife opandiratu ungwiro.” Koma anapambana. Daniel tsopano amaŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, ndipo amam’pangitsa kukhala woyandikana ndi Yehova.

Pamene anali kukula, Daniel anali kulilemekeza kwambiri Baibulo​—ngakhale kuti sanali kuliŵerenga​—ndipo anali kupemphera kwa Mulungu usiku uliwonse. Komabe, chinachake chinali kusoweka. Sanali kupeza chimwemwe. Zinthu zinasintha pamene anaona dzina la Mulungu m’Baibulo kwa nthaŵi yoyamba. (Eksodo 6:3; Salmo 83:18) Zitatero, popemphera anali kugwiritsa ntchito dzina la Yehova, ndipo mapemphero ake anakhaladi oti akuyankhulana ndi munthu wina. “Yehova anakhala bwenzi lapamtima kwambiri kwa ine, ndipo ndiye bwenzi langa lapamtima kwambiri mpaka pano.”

Asanaphunzire za Baibulo, Daniel analibe chiyembekezo cholimbikitsa cha m’tsogolo. “Sizochita kufuna kuganiza mozama kuti uone zimene zikuchitika padziko lapansi,” akutero. “Ndinkachita mantha, ndipo ndinayesa kudzitanganitsa kuti mwina ndingaziiwale.” Kenako anaphunzira kuti Mulungu adzakhazikitsa chilungamo kwa anthu onse padziko loyeretsedwa, pamene anthu omvera adzakhala ndi mtendere wokhalitsa ndi chimwemwe. (Salmo 37:10, 11; Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4) Daniel tsopano ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika. Chilimbikitso cha m’Baibulo chimenechi chimam’thandiza kukhala wosangalala ndi moyo.

Thandizo Pothetsa Mavuto a Mumtima

George anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa pamene amayi ake anamwalira. Iye ankachita mantha kuti agone usiku, poganizira kuti mwina m’maŵa mwake sadzukanso. Ndiye anadzaŵerenga zimene Yesu ananena zokhudzana ndi kuukitsidwa kuti: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Yesu], nadzatulukira.” Mawu enanso a Yesu omwe anam’gwira mtima ndi akuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo: wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo.” (Yohane 5:28, 29; 11:25) Malingaliro ngati ameneŵa anaonekadi kukhala abwino, omveka, ndi otonthoza. “Choonadi chimenechi,” akutero George, “n’chosangalatsadi kuchiganizira, komanso n’chogwira mtima.”

Nayenso Daniel, yemwe tam’tchula poyamba paja, anali ndi mantha ena ake. Amayi ake sakanatha kum’lera paokha, chotero anam’tumiza kukakhala m’nyumba zambiri zosamalira ana osoŵa makolo owasamalira. Nthaŵi zonse anali kumva ngati wotayidwa ndipo ankalakalaka kukhala wotetezeka m’banja lachikondi. Pamapeto pake, anapeza zomwe anali kufunazo mwa kuphunzira kwake Baibulo. Daniel anayamba kuyanjana ndi mpingo wachikristu wa Mboni za Yehova ndipo anakhala m’banja lauzimu, mmene anayamba kumva kuti ndi wolandiridwa ndiponso ndi wokondedwa ndi anthu a m’banjamo. Ndithudi, Baibulo limapindulitsa mokhutiritsa ndi mothandiza pamavuto a mumtima.

Kumbukirani kuti Yehova amaona zomwe zili mumtima mwathu ndiponso amadziŵa zimene tikufunafuna. Mulungu “ayesa mitima,” ndipo amapereka kwa “yense monga mwa njira zake.”​—Miyambo 21:2; Yeremiya 17:10.

Uphungu Wothandiza M’moyo Wabanja

Ponena za maunansi a anthu, Baibulo limapereka uphungu wothandiza. George akuti: “Kusiyana umunthu kapena kumvana molakwa ndizo zina mwa zinthu zosoŵetsa mtendere koposa m’moyo.” Kodi iye amathana nazo motani? “Ndikaona kuti winawake ali nane mlandu, ndimatsatira uphungu wolunjika wa pa Mateyu 5:23, 24 wakuti: ‘Yanjana ndi mbale wako.’ Kungoyankhula kokhako za vuto limene lilipo kumakhala ndi zotsatira. Ndimamva mtendere wa Mulungu umene Baibulo limanena. Uphunguwo umagwiradi ntchito. Ndi wothandiza kwambiri.”​—Afilipi 4:6, 7.

Mwamuna ndi mkazi wake akasemphana maganizo, onse aŵiri ayenera kukhala ‘otchera khutu, odekha polankhula, odekha pakupsa mtima.’ (Yakobo 1:19) Mawu anzeru ameneŵa amasonkhezera kulankhulana kwabwino. George akuwonjezera kuti: “Ndikatsatira uphungu wakuti ndizikonda ndi kusamala mkazi wanga momwe ndimadzikondera ndi kudzisamalira ine mwini, nthaŵi yomweyo ndimaona zotsatira zake. Savutika kundilemekeza.” (Aefeso 5:28-33) Inde, Baibulo limatiphunzitsa mmene tingazindikirire zophophonya zathu ndi kulimbana nazo komanso mmene tingapambanire popirira zophophonya za ena.

Uphungu Wokhalitsa

Mfumu Solomo yanzeruyo inati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Mawu amenewotu ndi osavuta kumva, koma n’ngofunika kwambiri!

Baibulo ndilo mphamvu yosonkhezera zabwino. Limapangitsa okonda Mulungu kusintha moyo wawo kuti ugwirizane ndi chifuniro chake ndi kuti akhale achimwemwe ‘poyenda m’chilamulo cha Yehova.’ (Salmo 119:1) Kaya tili mumkhalidwe wotani, Baibulo lili ndi zitsogozo ndi uphungu womwe tikufunikira. (Yesaya 48:17, 18) Liŵerengeni tsiku ndi tsiku, sinkhasinkhani pa zimene mwaŵerenga, ndipo litsatireni. Lidzawongolera maganizo anu ndi kuwakhazikitsa pa zinthu zoyera ndi zabwino zokhazokha. (Afilipi 4:8, 9) Kuwonjezera pa kukhala ndi moyo ndi kusangalala ndi moyo, mudzaphunziranso mmene mungakondere Mlengi wa moyowo.

Mwa kutsatira njira imeneyo, kwa inu​—monga momwe zakhalira kwa anthu enanso mamiliyoni ambiri​—Baibulo silidzangokhala buku lolembedwa bwino chabe ayi. Lidzakhaladi buku lophunzitsa mokhalira ndi moyo!

[Chithunzi patsamba 6]

Baibulo lingakulimbikitseni mukatsimikiza mtima kugonjetsa zizoloŵezi zovulaza

[Chithunzi patsamba 7]

Baibulo limakuphunzitsani mmene mungayandikirire kwa Mulungu