Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo—Lokondedwa ndi Loponderezedwa

Baibulo—Lokondedwa ndi Loponderezedwa

Baibulo​—Lokondedwa ndi Loponderezedwa

“Ndimalakalaka mabuku opatulikawa atatembenuzidwa m’zinenero zonse,” analemba motero Desiderius Erasmus, katswiri wamaphunziro wotchuka wachidatchi wa m’zaka za m’ma 1500.

CHIYEMBEKEZO chachikulu cha Erasmus chinali chodzaona anthu onse akuŵerenga ndi kumvetsa Malemba. Komabe, otsutsa Baibulo anakaniratu lingaliro limenelo kwamtu wa galu. Ndipotu panthaŵi imeneyo, Ulaya anali malo oopsa kwambiri kwa aliyense wochita chidwi ndi Baibulo, ngakhale chidwi chochepetsetsa. Ku England nyumba ya malamulo inapanga lamulo lomwe linalamula kuti “aliyense amene adzaŵerenga Malemba m’Chingelezi adzalandidwa malo ake, katundu wake yense, ndi moyo . . . ndi kuti, ngati aumirirabe zimenezo, kapena ngati achitanso zimenezo nthaŵi inayake pambuyo poti wakhululukidwa, ayenera kunyongedwa kaye pogalukira mfumu, kenako kuwotchedwa popandukira Mulungu.”

M’mayiko ochuluka a Ulaya, khoti la kafukufuku la Akatolika linali kufunafuna magulu omwe ankati ndi opanduka, monga Awadensi a ku France, ndi kuwazunza chifukwa cha chizoloŵezi chawo cholalikira “pogwiritsa ntchito mauthenga abwino ndi makalata a m’Baibulo ndi malemba ena opatulika, . . . popeza kuti kulalikira ndi kulongosola malemba oyera [kunali] koletsedweratu kwa anthu wamba.” Amuna ndi akazi osaŵerengeka anazunzidwa koopsa ndi kuphedwa chifukwa cha kukonda kwawo Baibulo. Anali pangozi yolandira chilango chowawa koposa chifukwa chonena Pemphero la Ambuye kapena Malamulo Khumi ndi kuphunzitsa ana awo zinthu zimenezo.

Kudzipereka kumeneku pa Mawu a Mulungu kunakhazikikabe m’mitima ya atsamunda omwe anakakhala ku North America. Pachiyambi ku America, “kuŵerenga ndi chipembedzo zinali zogwirizana zedi, kuyambitsa chikhalidwe cha anthu chozikidwa pa chidziŵitso cha Baibulo,” limatero buku lakuti A History of Private Life​—Passions of the Renaissance. Komanso ngakhale ulaliki womwe unafalitsidwa ku Boston mu 1767 unati: “Chitani khama poŵerenga malemba oyera. M’maŵa uliwonse ndi madzulo alionse muyenera kuŵerenga chaputala chimodzi m’Baibulo.”

Malinga ndi zomwe a Barna Research Group ku Ventura, California, anapeza, anthu a ku America oposa 90 peresenti ali ndi avareji ya mabaibulo oposa atatu. Komabe, kufufuza kwaposachedwapa kwasonyeza kuti ngakhale kuti anthu kumeneko amalemekezabe Baibulo, “kuliŵerenga, kuliphunzira ndi kulitsatira . . . n’chinthu chakale.” Ochuluka sadziŵa kuti kwenikweni limanena chiyani. Winawake wolemba nkhani m’nyuzipepala anati: “Lingaliro lakuti [Baibulo] lingakhalebe lofunika kwambiri pamavuto ndi nkhaŵa zamasiku ano n’losoŵa.”

Kuwonjezeka kwa Maganizo Adziko

Ambiri amakhulupirira kuti tingapeze chipambano m’moyo mwa kungoganiza bwino ndi kugwirizana monga anthu. Baibulo amaliona monga limodzi mwa mabuku ambirimbiriwo onena za malingaliro achipembedzo ndi zokumana nazo za anthu ena, osati monga buku lonena zenizeni ndi choonadi.

Ndiye anthu ochuluka akutani ndi nkhani zazikulu ndi zovuta za m’moyo? Akukhala popanda mkhalidwe wauzimu, popanda makhalidwe ndi chipembedzo choti n’kuwalangiza ndi kuwatsogolera m’njira yothandiza. Angokhala ngati sitima zapamadzi zopanda chiwongolero, “otengekatengeka uku ndi uko ndi kugwedezeka ndi mpweya uliwonse wa ziphunzitso za anthu, . . . ndi chinyengo ndi machenjera a anthu.”​—Aefeso 4:14, The Twentieth Century New Testament.

Chotero tiyeni tifunse kuti, Kodi Baibulo langokhala buku lachipembedzo lofanana ndi ena ambirimbiri? Kapena kodi ndi Mawu a Mulungu oonadi, okhala ndi nkhani zothandiza ndiponso zofunika? (2 Timoteo 3:16, 17) Kodi ifeyo tiyenera kulipenda? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Chithunzi patsamba 3]

Desiderius Erasmus

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzi chotengedwa m’buku lakuti Deutsche Kulturgeschichte

[Chithunzi patsamba 4]

Awadensi anazunzidwa chifukwa chakuti anali kulalikira za m’Malemba

[Mawu a Chithunzi]

Stichting Atlas van Stolk, Rotterdam