Kodi Muyenera Kuwakhulupirira?
Kodi Muyenera Kuwakhulupirira?
MWANA wa sukulu wa zaka 12 zakubadwa anali kuyesetsa kuti amvetse njira zoyambirira zopezera ansala m’masamu ogwiritsa ntchito zilembo. Mphunzitsi wake anali atapatsa kalasilo samu yooneka ngati yomvetsetseka.
“Tinene kuti x ndi y n’zofanana ndipo chilichonse chikhale choimira 1,” anayamba motero mphunzitsiyo.
‘Pamenepo m’pomveka,’ analingalira motero mwanayo.
Koma mphunzitsiyo atawonkhetsera samuyo m’mizere inayi mwa njira yooneka ngati yomvetsetseka ndithu, anapeza ansala yozunguza mutu, nati: “Ndiye kuti, 2 n’chimodzimodzi ndi 1!”
“Ndani angasonyeze ngati ansalayi n’njolakwika?” anafunsa ophunzira ake ozizwawo.
Pokhala ndi chidziŵitso chochepa kwambiri cha masamu ameneŵa, mwana wasukuluyo analephera kupereka umboni wosonyeza kuti ansalayo n’njolakwika. Njira yonse yowonkhetsera samuyo sinaoneke kulakwika pena paliponse. Chotero, kodi ayenera kukhulupirira ansala yachilendo imeneyi? Komanso mphunzitsi wake anali katswiri wa masamu kusiyana ndi iyeyo. Iyayi, sayenera kuikhulupirira! ‘N’zosafunanso kuti ndichite kupereka umboni,’ anaganiza motero mwanayo. ‘N’zoonekeratu kuti palibe kugwirizana pamenepa.’ (Miyambo 14:15, 18) Anadziŵa kuti mphunzitsi wakeyo ngakhalenso anzake onse a m’kalasilo sangapereke ndalama zokwanira madola aŵiri posinthanitsa ndi dola imodzi!
M’kupita kwa nthaŵi mwanayo anapapeza polakwika m’kawonkhetsedwe kaja. Podzafika nthaŵiyi, anali ataphunzirapo phunziro lofunika kwambiri. Ngakhale pamene munthu wachidziŵitso chochuluka kwambiri atchula mfundo yokonzedwa bwino yoonekanso ngati yosatsutsika, womvetsera sayenera kukhulupirira malingaliro opusa kungoti popeza sangathe kupereka umboni wotsutsa mfundozo panthaŵiyo. Mwana wasukulu uja analitu kutsatira mfundo yachikhalidwe yomveka yopezeka pa 1 Yohane 4:1—osafulumira kukhulupirira zilizonse zimene mukumva, ngakhale pamene zikuoneka kuti zikuchokera kwa winawake wachidziŵitso chachikulu.
Zimenezi sizitanthauza kuti muziumirira malingaliro amene munali nawo musanamve zowonjezeka. N’kulakwa kunyalanyalaza mfundo zimene zingawongolere malingaliro olakwika. Komanso simuyenera ‘kugwedezeka mtima msanga’ poumirizidwa ndi winawake yemwe amati akudziŵa zambiri kapena ali ndi udindo waukulu. (2 Atesalonika 2:2) Zoona, mphunzitsi uja anali kungofuna kuyesa ophunzira ake. Koma nthaŵi zina pamakhala zolinga zoipa. Anthu angakhale ‘onyenga zedi pofuna kusokeretsa’ ena.—Aefeso 4:14; 2 Timoteo 2:14, 23, 24.
Kodi Akatswiri Amanena Zoona Nthaŵi Zonse?
Kaya akhale ndi chidziŵitso chotani, akatswiri a ntchito iliyonse amatha kusiyana malingaliro ngakhalenso kusinthasintha malingaliro awo. Mwachitsanzo, tiyeni tinene za kutsutsana komwe kulipo pakati pa akatswiri a sayansi yopanga mankhwala pankhani yachidziŵikire yakuti chimayambitsa matenda n’chiyani. “Mgwirizano umene chibadwa, malo okhala, ndi zochitika zapamalopo zingakhale nawo ndi kudwala kwa munthu ndiyo mfundo yochititsa mkangano waukulu pakati pa asayansi,” analemba motero pulofesa wa zamankhwala pa Yunivesite ya Harvard. Awo amene amakhulupirira kuti zochitika ndi zochita zonse za munthu zimasonkhezeredwa ndi mphamvu zina zosaletseka amakhulupirira ndi mtima wonse kuti majini athu ndi amene kwenikweni amapangitsa kuti matupi athu azilowedwa matenda osiyanasiyana. Koma ena akutsutsa ndipo akuti malo okhala ndi zochita za munthu pamoyo wake ndizo kwenikweni zimene zimachititsa munthu kudwala. Magulu onse aŵiri ali ndi maumboni
ochirikiza mfundo zawo malinga ndi zimene anapeza pofufuza. Koma mtsutsowo ukupitirirabe.Anthu oganiza mozama otchuka koposa apezeka kuti analakwitsa pamfundo zambiri zosiyanasiyana, ngakhale kuti zophunzitsa zawo panthaŵiyo zinkaoneka ngati zosatsutsika. Wafilosofi Bertrand Russell anati Aristotle anali mmodzi mwa “afilosofi achisonkhezero chachikulu kwambiri.” Komano, Russell ananenanso kuti ziphunzitso zambiri za Aristotle zinali “bodza lokhalokha.” “M’nthaŵi yonseyi yamakono,” iye analemba motero, “kutsogola kwina kulikonse m’zasayansi, m’luso la kulingalira bwino, kapena m’filosofi kwachitika motsutsana kotheratu ndi ophunzira a Aristotle.”—History of Western Philosophy.
‘Chotchedwa “Chidziŵitso” Konama’
Akristu oyambirira ayenera kuti ankakumana ndi ophunzira ochuluka ophunzitsidwa ndi afilosofi otchuka achigiriki, monga Socrates, Plato, ndi Aristotle. Anthu ophunzira panthaŵiyo anali kudziona ngati anzeru kuposa Akristu ochuluka. Ophunzira a Yesu ochuluka sanali kuonedwa ngati “anzeru, monga mwa thupi.” (1 Akorinto 1:26) Inde, awo amene anaphunzira mafilosofi a m’tsikulo ankaganiza kuti zimene Akristu amakhulupirira zinali ‘zopusa’ kapena “zopanda pake.”—1 Akorinto 1:23; Phillips.
Inuyo mukanakhala pakati pa Akristu oyambirirawo, kodi mukanakopeka ndi mfundo zokopa za anthu ophunzira a m’tsikulo kapena kuchita chidwi chadzaoneni ndi nzeru zawo? (Akolose 2:4) Sipakanakhala chifukwa chochitira zimenezo, malinga ndi mtumwi Paulo. Iye anakumbutsa Akristu kuti Yehova amaona “nzeru za anzeru” ndi “kuchenjera kwa ochenjera” a m’tsikulo monga zopusa. (1 Akorinto 1:19) Iye anafunsa kuti: “Kodi wafilosofi, wolemba nkhani ndi wotsutsa wadziko lino akwaniritsapo chiyani ndi nzeru zawozo?” (1 Akorinto 1:20, Phillips) Ngakhale kuti anali ndi nzeru zochuluka chotani, afilosofiwo, olemba nkhani, ndi otsutsa a m’tsiku la Paulo sanapeze njira yeniyeni yothetsera mavuto a mtundu wa anthu.
Chotero Akristu anaphunzira kupeŵa zimene mtumwi Paulo anati “zotsutsana za ichi chitchedwa chizindikiritso [“chidziŵitso,” NW] konama.” (1 Timoteo 6:20) Chifukwa chimene Paulo anatchera chidziŵitsocho kuti ‘chonama’ n’chakuti chinalibe chinthu chimodzi chofunika kwambiri—umboni wochokera kwa Mulungu woyesera nkhani zawozo. (Yobu 28:12; Miyambo 1:7) Posoŵeka zimenezo, komanso panthaŵi imodzimodziyo pochititsidwa khungu ndi wonyenga wamkulu, Satana, awo amene anamamatira chidziŵitso chimenecho sakanayembekezera kupeza choonadi.—1 Akorinto 2:6-8, 14; 3:18-20; 2 Akorinto 4:4; 11:14; Chivumbulutso 12:9.
Baibulo—Buku Louziridwa Lotsogolera
Akristu oyambirira sanali kukayikira zonena kuti Mulungu anavumbula chifuniro chake ndi mfundo zake zachikhalidwe m’Malemba. (2 Timoteo 3:16, 17) Zimenezi zinawateteza kuti ‘asalandidwe ngati chuma, mwa kukonda nzeru, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu.’ (Akolose 2:8) Zilinso chimodzimodzi lerolino. Mosiyana ndi malingaliro osokoneza ndi otsutsana a anthu, Mawu ouziridwa a Mulungu ndiwo maziko olimba omwe tingazikepo zikhulupiriro zathu. (Yohane 17:17; 1 Atesalonika 2:13; 2 Petro 1:21) Popanda Mawuwo tingakhale mumkhalidwe wokhumudwitsa woyesa kumanga chinthu cholimba pamchenga wosakhazikika wa nkhani ndi mafilosofi a anthu.—Mateyu 7:24-27.
‘Koma taimani kaye,’ wina angatero. ‘Kodi paja si mfundo za sayansi zimene zasonyeza kuti Baibulo n’lolakwa, zimene zikutanthauza kuti nalonso n’losadalirika mofanana ndi mafilosi a anthu omwe amasinthasinthaŵa?’ Mwachitsanzo, Bertrand Russell ananena kuti “Copernicus, Kepler, ndi Galileo anayenera kutsutsa Aristotle limodzinso ndi Baibulo posonyeza kuti dziko lapansi silili pakatikati pa thambo.” (Tapendeketsa mawuwo ndife.) Ndiponso kodi si zoona kuti m’tsiku lathu lino, mwachitsanzo, okhulupirira nkhani ya kulengedwa kwa dziko lapansi amanena motsindika kuti Baibulo limaphunzitsa kuti dziko lapansi linalengedwa pamasiku asanu ndi limodzi a maola 24 lililonse, pamene maumboni onse akusonyeza kuti dziko lapansi lakhalapo kwa zaka mabiliyoni ambirimbiri?
Baibulotu silinena kuti dziko lapansi lili pakatikati pa thambo. Chimenecho chinali chiphunzitso cha atsogoleri achipembedzo amenenso sanali kutsatira Mawu a Mulungu mosamalitsa. Nkhani yonena za kulenga ya m’Genesis imasonyezadi Genesis 1:1, 5, 8, 13, 19, 23, 31; 2:3, 4) Kufufuza Baibulo moona mtima kumasonyeza kuti ngakhale kuti si buku lolongosola za sayansi, ilo ‘silopanda pake.’ Kwenikweni, limagwirizana bwino lomwe ndi zinthu zoona zimene sayansi yasonyeza. *
kuti dziko lapansi liyenera kuti lakhalapo kwa zaka mabiliyoni ambiri ndipo siisonyeza kuti tsiku lililonse la kulenga linali la maola 24 okha ayi. (‘Mphamvu ya Kulingalira’
Ngakhale kuti ophunzira a Yesu ochuluka anali amuna ndi akazi wamba, mwina osaphunzira kwambiri, iwo anali ndi chuma chinanso chopatsidwa ndi Mulungu. Mosasamala kanthu za makulidwe awo, onse anapatsidwa mphamvu za kulingalira ndi kuganiza. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti azigwiritsa ntchito mokwanira ‘mphamvu zawo za kulingalira’ kuti ‘akazindikire chifuniro cha Mulungu chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.’—Aroma 12:1, 2, NW.
Pokhala ndi ‘mphamvu zolingalira’ zopatsidwa ndi Mulungu, Akristu oyambirirawo anaona bwino lomwe kuti filosofi iliyonse kapena chiphunzitso chilichonse chosagwirizana ndi Mawu a Mulungu ovumbulidwa chinali chachabe. Kwenikweni, anthu anzeru a m’tsiku lawo nthaŵi zina anali ‘kukanikizira pansi choonadi’ ndi kunyalanyaza umboni wowazungulira wosonyeza kuti kuli Mulungu. “Pakunena kuti ali anzeru, anapusa,” analemba motero mtumwi Paulo. Pokana choonadi cha Mulungu ndi chifuno chake, “anakhala opanda pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira.”—Aroma 1:18-22; Yeremiya 8:8, 9.
Awo amene amati ndi anzeru amanena zinthu zonga zakuti “Kulibe Mulungu” kapena “Baibulo n’losadalirika” kapena “Anoŵa si ‘masiku otsiriza.’” Malingaliro ameneŵa ndi opusa m’maso mwa Mulungu mofanana ndi kunena kuti “2 n’chimodzimodzi ndi 1.” (1 Akorinto 3:19) Kaya anthu adzinenere kuti ali ndi ulamuliro wotani, simuyenera kumvera zonena zawo ngati n’zotsutsana ndi Mulungu, zonyalanyaza Mawu ake, ndiponso n’zoonekeratu kuti n’zolakwika. Chotero kumaliza kwake tinganene kuti, njira yanzeru nthaŵi zonse ndiyo kunena kuti “Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama.”—Aroma 3:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 20 Ngati mukufuna kudziŵa zambiri, onani mabuku akuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Is There a Creator Who Cares About You?, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Zithunzi patsamba 31]
Mosiyana ndi malingaliro osadalirika a anthu, Baibulo ndilo maziko olimba a zimene timakhulupirira
[Mawu a Chithunzi]
Kulamanzere, Epicurus: Chithunzi chotengedwa mwachilolezo cha British Museum; pakati chapamwamba, Plato: National Archaeological Museum, Athens, Greece; kulamanja, Socrates: Roma, Musei Capitolini