Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amapereka Malo Opumirapo kwa Anthu Ake

Yehova Amapereka Malo Opumirapo kwa Anthu Ake

Olengeza Ufumu Akusimba

Yehova Amapereka Malo Opumirapo kwa Anthu Ake

PANJIRA ya m’mapiri, malo amthunzi opumirapo amakhala osangalatsa kwambiri kwa wapaulendo wotopa. Ku Nepal, malo oterowo amatchedwa kuti chautara. Chautara weniweni amakhala pambali pa mtengo woŵirira wa mvunguti, pamthunzi poti mutha kukhalapo n’kupuma. Kukonza chautara kumasonyeza kukoma mtima kwa munthu ndipo ambiri mwa anthu amene amapindula nawo sadziŵika kwa iye.

Zochitika ku Nepal zikusonyeza mmene Yehova Mulungu wakhalira Gwero la chisangalalo ndi mpumulo wauzimu kwa “apaulendo” ambiri otopa m’dongosolo lino la zinthu.​—Salmo 23:2.

• Lil Kumari amakhala mu mzinda wokongola wa Pokhara, komwe nsonga za mapiri a Himalaya zokutidwa ndi chipale chofewa zimaonekera bwino kwambiri mochititsa kaso. Koma pokhala ndi nkhaŵa ya mavuto azachuma a pabanja, Lil Kumari anaona kuti analibe chiyembekezo chenicheni chokhala ndi moyo wabwino. Pamene wa Mboni za Yehova anadzamuchezetsa, anachita chidwi ndi chiyembekezo chabwino cha m’Baibulo ndipo nthaŵi yomweyo anapempha kuphunzira Baibulo.

Ngakhale kuti Lil Kumari anali kusangalala ndi phunzirolo, si kuti kunali kwapafupi kupitiriza chifukwa chakuti a m’banja lake anali kutsutsa mwamphamvu. Koma iye sanaleke. Anayamba kupezeka pamisonkhano yachikristu nthaŵi zonse ndi kugwiritsa ntchito zimene anali kuphunzira makamaka pa nkhani ya mkazi kugonjera mwamuna wake. Chotsatira chake chinali chakuti mwamuna wake ndi amayi ake a Lil, anazindikira kuti kuphunzira kwake Baibulo kunali kupindulitsa banja lonselo.

Mwamuna wake ndi achibale ake angapo, tsopano akuphunzira Mawu a Mulungu. Pamsonkhano waposachedwapa womwe unachitikira ku Pokhara, Lil Kumari anasangalala ndi msonkhanowo limodzi ndi achibale ake akwanira 15. Iye anati: “Nyumba yathu yakhala malo opumirapo chifukwa banja lathu tsopano ndi logwirizana pa kulambira koona, ndipo ndapeza mtendere wa m’maganizo.”

• Ngakhale kuti kusankhana mitundu n’koletsedwa ku Nepal, kumakhudzabe kwambiri miyoyo ya anthu. Chotero, ambiri amachita chidwi ndi zimene Baibulo limanena pankhani ya ufulu wofanana ndi kupanda tsankhu. Kuphunzira kuti “Mulungu alibe tsankhu” kunasintha kwambiri moyo wa Surya Maya ndi banja lake.​—Machitidwe 10:34.

Surya Maya anavutika maganizo ndi chisalungamo cha kusankhana mitundu komanso chifukwa cha chikhalidwe ndi miyambo yamphamvu. Monga mayi wopembedza, kwa zaka zambiri Surya Maya anapempha milungu yake ya mafano kuti imuthandize. Koma mapemphero ake sankayankhidwa. Tsiku lina pamene anali kulira popempha thandizo, mdzukulu wake Babita wa zaka zisanu ndi chimodzi anafika ndi kufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukupempha thandizo kwa mafano amene sangachite chilichonse?”

Kunapezeka kuti mayi ake a Babita anali kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova. Babita mwachimwemwe anaitanira agogo akewo ku msonkhano wachikristu. Pamene Surya Maya anafika pamsonkhanopo, anadabwa kuona kuti anthu a mitundu yosiyanasiyana anali kusangalala limodzi popanda kusankhana. Nthaŵi yomweyo anapempha kuti aziphunzira Baibulo. Ngakhale kuti zimenezi zinapangitsa kuti anzake asiye kuyanjana naye, iye sanataye mtima; ndiponso ngakhale kusadziŵa kwake kulemba ndi kuŵerenga sikunamulepheretse kupita patsogolo mwauzimu.

Zaka zisanu ndi zitatu zapita, ndipo anthu asanu ndi mmodzi a m’banja lake, kuphatikizapo mwamuna wake ndi ana ake atatu, ndi Mboni za Yehova. Tsopano Surya Maya ndi mlaliki wa nthaŵi zonse, mpainiya wokhazikika, ndipo akusangalala pothandiza ena kutula mitolo yawo yolemera pa malo opumulira enieni omwe amaperekedwa ndi Yehova yekha.