Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Asonkhezeredwa Kutumikira

Asonkhezeredwa Kutumikira

Asonkhezeredwa Kutumikira

KODI n’chiyani chingapangitse mabanja 24, amuna ndi akazi awo, omwe ali pachimake posangalala ndi moyo kusiya mabanja awo, mabwenzi awo, ndiponso malo omwe anawazoloŵera kuti akagwire ntchito yaumishonale kumayiko achilendo? N’chifukwa chiyani iwo angasangalale kupita ku madera monga Papua New Guinea ndi Taiwan, komanso ku mayiko a ku Africa ndi Latin America? Kodi chingakhale chifukwa chakuti amakonda kuyendayenda? Ayi. Koma kuti, iwo asonkhezereka chifukwa chakuti amakondadi Mulungu komanso anansi awo.​—Mateyu 22:37-39.

Kodi anthu ameneŵa ndani? Ndiwo omaliza maphunziro m’kalasi la 109 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Loŵeruka, pa September 9, 2000, anthu okwana 5,198 anasonkhana pa Likulu la Maphunziro a Watchtower​—lomwe lili ku Patterson, mu mzinda wa New York​—ndiponso m’malo ena a kanema kuti amvetsere uphungu wabwino kwambiri womwe ungathandize omaliza maphunzirowo kukhala amishonale opambana.

Tcheyamani wa pulogalamuyo anali Stephen Lett, yemwe ndi membala wa Komiti Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Anafutukula mawu ake amalonje kuchokera pa Mateyu 5:13, “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi.” Mbale Lett anafotokoza kuti mawu a Yesu akugwiradi ntchito kwa ophunzira omwe anamaliza maphunzirowo. Mwachitsanzo, mchere uli ndi mphamvu yokoleretsa zinthu. Choncho, nawonso amishonale ali ngati mchere mophiphiritsira, mwa ntchito yawo yolalikira yogwira mtima.

Chilimbikitso cha Panthaŵi ya Kulekana

Kenako, Mbale Lett anaitana ena mwa atumiki a Yehova amene akhala akum’tumikira kwa nthaŵi yaitali omwe anakamba nkhani za m’Malemba zifupizifupi koma zamphamvu kwambiri. Woyamba anali John Wischuk, yemwe akutumikira m’Dipatimenti Yolemba. Mutu wa nkhani yake wakuti, “Salmo Lalifupi Kwambiri Limalimbikitsa Mzimu Waumishonale,” unazikidwa pa Salmo 117. Lerolino, padziko lonse lapansi pali kufunika kwakuti umboni wokhudza Yehova ndi Ufumu wake uperekedwe kwa “amitundu” ndi “anthu.” Ophunzirawo analimbikitsidwa kukwaniritsa zimene Salmo 117, NW, limanena mwa kulimbikitsa ena kuti ‘atamande Yehova.’

Kenako, tcheyamani anaitana Guy Pierce wa Bungwe Lolamulira. Iye analankhula pa mutu wakuti “Khalani Ololera, Koma Osasunthika.” Mawu a Mulungu n’ngolimba. Pa Deuteronomo 32:4, Yehova Mulungu amatchedwa kuti Thanthwe, komabe Mawu ake amatipatsa ufulu wosonyeza kulolera m’lingaliro lakuti analembedwa kaamba ka anthu a zinenero zonse ndiponso makhalidwe​—inde, kaamba ka anthu onse. Ophunzirawo analimbikitsidwa kulalikira Mawu a Mulungu, kulola uthenga wake kukhudza mitima ndiponso chikumbumtima cha anthu. (2 Akorinto 4:2) “Mukhale osasunthika pa mfundo zamakhalidwe abwino, komabe khalani ololera. Osakanyoza anthu amene ali m’gawo lanu lomwe mwagaŵiridwa chifukwa chakuti chikhalidwe chawo ndi chosiyana ndi chanu,” analimbikitsa motero Mbale Pierce.

Karl Adams, mmodzi wa alangizi a Gileadi, amene wakhala akutumikira pa likulu la dziko lonse kwa zaka pafupifupi 53, analankhula pa mutu wochititsa chidwi kwambiri wakuti, “Kodi Mukachoka Pano Mupita Kuti?” Ndi zoona kuti, mabanja 24 amenewo analandira magawo aumishonale m’mayiko osiyanasiyana okwanira 20 padziko lonse, koma panadzutsidwa funso lakuti, Mukakafika ku magawo amenewo, ndipo mwaliona dziko lanu latsopano, kodi mukachita chiyani? Tikukhala m’dziko lotanganidwa kwambiri. Anthu amafuna kupita kumalo atsopano ndi kuchita zinthu zatsopano n’cholinga chofuna kuti asangalale. Mosiyana ndi zimenezo, ophunzirawo analandira ntchito yomwe Yehova anawapatsa, kudera limene iye akufuna kuti iwo akasamalire “nkhosa” zake mopanda dyera. Sayenera kukhala monga anthu a mu Israyeli wakale omwe chifukwa cha dyera anaphonya mwayi woti agwiritsidwe ntchito ndi Yehova kudalitsa anthu onse. M’malo mwake, iwo ayenera kutsanzira Yesu Kristu, yemwe nthaŵi zonse anachita chifuniro cha Atate wake mopanda dyera ndiponso yemwe anali womvera, zivute zitani.​—Yohane 8:29; 10:16.

“Sungani Zakuya za Mulungu” ndiwo unali mutu wa nkhani ya Wallace Liverance, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi. Mobwerezabwereza, Malemba amanena za Mawu a Mulungu mowafananitsa ndi chuma, ngale zamtengo wapatali, zitsulo zamtengo wapatali, ndi zinthu zapamwamba ndi zokhumbika kwambiri. Miyambo 2:1-5 imasonyeza kuti, kuti ‘tim’dziŵedi Mulungu,’ tiyenera kufufuza chidziŵitso chakecho ngati “chuma chobisika.” Wokamba nkhaniyo analimbikitsa ophunzirawo kuti akapitirizebe kukumba zinthu zakuya za Mulungu pamene akutumikira m’magawo awo atsopano. Mbale Liverance anati: “Zimenezi n’zothandiza kwambiri, chifukwa chakuti zimamanga chikhulupiriro komanso chidaliro mwa Yehova ndipo zidzalimbitsa kufunitsitsa kwanu kukhala omamatira ku utumiki wanu. Zidzakuthandizani kulankhula molimba mtima ndiponso kukhala mphunzitsi wogwira mtima pamene mukufotokoza kwa anthu ena za zifuno za Mulungu.”

Mogwiritsa ntchito zochitika za m’kalasi, mlangizi wa Sukulu ya Gileadi anapenda mmene Yehova wadalitsira ntchito ya mu utumiki wakumunda ya ophunzirawo m’miyezi isanu yapitayo. Lawrence Bowen anatchula mawu a mtumwi Paulo a pa Machitidwe 20:20 okhudza utumiki wake ku Efeso, kusonyeza kuti Paulo anagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti achitire umboni. Zokumana nazo za ophunzirawo zinasonyeza kuti, monga mtumwi Paulo, anthu amene asonkhezeredwa ndi chikondi cha kwa Mulungu ndiponso kwa mnansi m’nthaŵi yathu ino, saleka kulankhula za choonadi kapenanso kulola mphamvu ya Mawu a Mulungu kutsogolera anthu ena. Zimenezi zimadzetsa madalitso ochuluka a Yehova.

Anthu Oidziŵa Bwino Ntchitoyo Alankhulapo

Panyengo yawo ya sukulu, ophunzira a m’kalasi la Gileadi limeneli anapindula kwambiri makamaka mwa kuyanjana ndi mamembala a Makomiti Anthambi ochokera m’mayiko 23, amenenso anali pa Likulu la Maphunziro la Patterson kaamba ka maphunziro apadera. Leon Weaver ndi Merton Campbell a m’Dipatimenti Yoyang’anira Utumiki anafunsa mamembala osiyanasiyana a Makomiti Anthambi, omwe ena mwa iwo anamalizapo maphunziro a Gileadi. Kumvetsera kuchokera kwa amkhala kale pantchito yaumishonale ameneŵa kunali kolimbikitsa kwambiri kwa ophunzirawo, mabanja awo, komanso mabwenzi awo.

Uphungu womwe unaperekedwa kwa anthu omaliza maphunzirowo n’cholinga chofuna kuwathandiza kuti akazoloŵere magawo awo a kumayiko ena unaphatikizapo mawu monga aŵa: “Kakhaleni odekha. Ngati chinthu chinachake chachilendo kapena chimene simukuchimvetsa chakuchitikirani, osakasiya utumiki wanu. Kadalireni Yehova”; “phunzirani kukhala osangalala ndi zinthu zimene zilipo, ndipo kakhaleni ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzakupatsani zinthu zofunika m’moyo.” Ndemanga zina zinali zolimbikitsa ophunzirawo kukhalabe ndi chimwemwe m’ntchito yawo. Mawu ena ochepa chabe anali akuti: “Musakafananitse gawo lomwe mwagaŵiridwa ndi dera limene munachokera”; “kaphunzireni chinenero cha m’deralo ndipo kachilankhuleni molongosoka kotero kuti mukathe kumvana ndi anthu”; “kaphunzireni miyambo ndi chikhalidwe cha anthuwo, chifukwa chakuti zimenezi zidzakuthandizani kumamatira ku ntchito yanu.” Ndemanga zimenezi zinali zolimbikitsa kwambiri kwa amishonale atsopanowo.

Kufunsa kutatha, David Splane, yemwe anakhalapo mmishonale ndipo anachita nawo maphunziro a kalasi la 42 la Gileadi amene tsopano akutumikira monga membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anakamba nkhani yaikulu ya mutu wodzutsa chidwi wakuti “Kodi Ndinu Ophunzira Kapena Omaliza Maphunziro?” Anafunsa kalasi lomaliza maphunzirolo kuti: “Kodi muzidziona motani popita ku gawo lanu laumishonale? Monga omaliza maphunziro amene amadziŵa zilizonse zokhudza ntchito yaumishonale kapena monga ophunzira amene adakali ndi zinthu zambiri zoti aphunzire?” Mbale Splane anafotokoza kuti womaliza maphunziro wanzeru amadziona ngati wophunzira. Amishonalewo ayenera kukhala ndi malingaliro akuti aliyense amene akakumane naye m’gawo lawo laumishonale angathe kuwaphunzitsa kanthu kenakake. (Afilipi 2:3) Ophunzirawo analimbikitsidwa kukagwirizana kwambiri ndi amishonale anzawo, maofesi anthambi, ndi mipingo ya m’gawo lawo. “Mwapambana mayeso anu omalizira, koma sikuti mwasiya kukhala ophunzira. Kam’fotokozereni bwinobwino munthu aliyense kuti, mwapita kumeneko kukaphunzira,” analimbikitsa motero Mbale Splane.

Pambuyo pa nkhani imeneyi, ophunzirawo analandira madipuloma awo, ndiponso magawo awo analengezedwa kwa omvetsera. Kenako, inali nthaŵi yokhudza mtima kwa ophunzira omaliza maphunzirowo pamene woimira kalasiyo anaŵerenga mawu otsimikiza mtima onena za kufunitsitsa kwa omaliza maphunzirowo kulola zimene aphunzira kuchokera m’Mawu a Mulungu kuwalimbikitsa kuchita zinthu zikuluzikulu za utumiki wopatulika.

Onse amene anamvetsera nkhanizo angavomereze kuti uphungu womwe unaperekedwa unalimbitsa chosankha cha omaliza maphunzirowo chosonyeza chikondi kwa Mulungu ndiponso kwa mnansi. Unawathandiza kukhala ofunitsitsa kwambiri kusiyana ndi kale lonse, kuthandiza mwauzimu anthu a m’gawo lawo laumishonale.

[Bokosi patsamba 25]

ZIŴERENGERO ZA KALASI

Chiŵerengero cha mayiko kumene anachokera: 10

Chiŵerengero cha mayiko kumene anatumizidwa: 20

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Avareji ya zaka zakubadwa: 33.7

Avareji ya zaka m’choonadi: 16.2

Avareji ya zaka mu utumiki wanthaŵi zonse: 12.5

[Chithunzi patsamba 26]

Kalasi la 109 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo mayina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse.

(1) Collins, E.; Miles, L.; Alvarado, A.; Lake, J. (2) Van Dusen, L.; Biharie, A.; Heikkinen, H.; Koós, S.; Smith, H. (3) Ashford, J.; Ashford, C.; Boor, C.; Richard, L.; Wilburn, D.; Lake, J. (4) Chichii, K.; Chichii, H.; Ramirez, M.; Baumann, D.; Becker, G.; Biharie, S.; Ramirez, A. (5) Van Dusen, W.; Lemâtre, H.; Pisko, J.; Cutts, L.; Russell, H.; Johnson, R. (6) Becker, F.; Baumann, D.; Johnson, K.; Pifer, A.; Madsen, C.; Lemâtre, J.; Heikkinen, P. (7) Smith, R.; Russell, J.; Collins, A.; Pisko, D.; Wilburn, R.; Koós, G. (8) Cutts, B.; Boor, J.; Madsen, N.; Pifer, S.; Richard, E.; Miles, B.; Alvarado, R.