Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu
Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu
“[Iye] amalimbika nthaŵi zonse m’mapemphero ake chifukwa cha inu, kuti potsirizira pake mukaime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.”—AKOLOSE 4:12, NW.
1, 2. (a) Kodi anthu akunja anaonanji mwa Akristu oyambirira? (b) Kodi buku la Akolose limasonyeza motani chidwi chachikondi?
OTSATIRA a Yesu anali ndi chidwi chozama mwa alambiri anzawo. Tertullian (wolemba mabuku wa m’zaka za m’ma 100 ndi m’ma 200 C.E.) ananenapo za kukoma mtima kumene iwo anasonyeza kwa ana amasiye, anthu osauka, ndi okalamba. Maumboni a chikondi amenewo anawakhudza kwambiri osakhulupirira moti ena anati za Akristu, ‘Onani mmene amakonderana.’
2 Buku la Akolose limasonyeza chidwi chachikondi choterocho chimene mtumwi Paulo ndi mnzake Epafra anali nacho kwa abale ndi alongo a ku Kolose. Paulo anawalembera kuti: Epafra “amalimbika nthaŵi zonse m’mapemphero ake chifukwa cha inu, kuti potsirizira pake mukaime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.” M’chaka cha 2001, Mboni za Yehova zidzakhala ndi lemba limeneli la Akolose 4:12, NW monga lemba lawo lachaka, ndipo limati: “Imani amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.”
3. Kodi Epafra anapempherera zinthu ziŵiri ziti?
3 Mutha kuona kuti mapemphero a Epafra m’malo mwa okondedwa ake anali ndi mbali ziŵiri: (1) kuti ‘potsirizira pake akaime amphumphu’ ndipo (2) kuti akaime “otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.” Mawu ameneŵa anaphatikizidwa m’Malemba kuti ife tipindule nawo. Chotero dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo pandekha n’chiyani chomwe ndifunikira kuchita kuti potsirizira pake ndikaime wamphumphu ndi wotsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu? Ndipo
pamene ndikuchita zimenezo, kodi chidzatsatirapo n’chiyani? Tiyeni tione.Yesetsani ‘Kuima Wamphumphu’
4. Kodi Akolose anafunikira kukhala “amphumphu” m’lingaliro lotani?
4 Epafra anafunitsitsa kuti abale ndi alongo ake auzimu a ku Kolose ‘potsirizira pake akaime amphumphu.’ Mawu amene Paulo anagwiritsa ntchito, omwe pano atembenuzidwa kuti “amphumphu,” angatanthauze angwiro, aakulu msinkhu, kapena kuti okhwima. (Mateyu 19:21; Ahebri 5:14; Yakobo 1:4, 25) Inu mukudziŵa bwino kuti kukhala Mboni yobatizidwa ya Yehova, mwa iko kokha sikutanthauza kuti munthu ndi Mkristu wamkulu msinkhu ayi. Paulo analembera Aefeso, okhala kumadzulo kwa Kolose, kuti abusa ndi aphunzitsi amayesa kuthandiza ‘onse kufikira pa umodzi m’chikhulupiriro ndi m’chidziŵitso cholondola cha Mwana wa Mulungu, ndi kukhala munthu wamkulu msinkhu, ku muyeso wa msinkhu wonse wa Kristu.’ Penapake Paulo analimbikitsa Akristu kuti akhale “aakulu misinkhu mu luso la kuzindikira.”—Aefeso 4:8-13, NW; 1 Akorinto 14:20, NW.
5. Kodi tingachite motani kuti cholinga chathu chachikulu chikhale kukhala amphumphu?
5 Ngati ena ku Kolose anali asanakulebe msinkhu mwauzimu, kapena kuti kukhwima mwauzimu, anafunikira kuchitapo kanthu. Kodi si mmenenso ziyenera kukhalira lerolino? Kaya tinabatizidwa zaka zochuluka m’mbuyomo kapena tangobatizidwa kumene, kodi tikutha kuona bwinobwino kuti tapita patsogolo m’maluso athu a kulingalira ndi mmene timaonera zinthu? Kodi timayamba talingalira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo tisanasankhe chochita? Kodi nkhani zokhudza Mulungu ndi mpingo zikukhala ndi mbali yomakulakulabe m’moyo wathu, m’malo moziona ngati zosafunika kwenikweni? Pano sitingathe kufotokoza njira zonse zomwe tingasonyezere kukula kumeneku kofikira kukhala wamphumphu, koma nazi zitsanzo ziŵiri.
6. Kodi ndi mbali iti yomwe munthu angathe kupitira patsogolo kufikira atakhala wangwiro, monga momwe Yehova alili?
6 Chitsanzo choyamba: Tiyerekeze kuti tinakulira m’dera lotchuka ndi tsankhu kapena kudana ndi anthu amtundu wina, a dziko lina, kapena a chigawo china. Tsopano tikudziŵa kuti Mulungu alibe tsankhu ndi kuti nafenso sitiyenera kuchita tsankhu. (Machitidwe 10:14, 15, 34, 35) Mu mpingo kapena m’dera lathu, muli anthu amitundu inayo, chotero ife tili pakati pawo. Komabe, kodi anthu amtundu umenewo timakhalabe nawo pachidani mumtima kapena kuwakayikira pamlingo wotani? Kodi ndife amtopola, ofulumira kum’ganizira molakwa wina wa m’mtundu umenewu akalakwitsa kapena ngati watilakwira pa kanthu kakang’ono? Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndifunikira kuwongolera kwambiri kuti ndikhale ndi maganizo opanda tsankhu mofanana ndi a Mulungu?’
7. Kukhala wamphumphu monga Mkristu kungaphatikizepo kuona ena motani?
7 Chitsanzo chachiŵiri: Malinga n’kunena kwa Afilipi 2:3, tisachite “kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake om’posa.” Kodi tikupita patsogolo motani pambali imeneyi? Munthu aliyense ali ndi zofooka zake komanso ali ndi mbali zina zomwe amachita bwino. Ngati m’mbuyomu timafulumira kuona zofooka za ena, kodi tasintha, mwakuti sitiwayembekezeranso kukhala ngati ‘angwiro’? (Yakobo 3:2) Tsopano lino, kuposa ndi kale lonse, kodi tikutha kuona—ngakhale kufufuza kumene—mbali zomwe ena amatiposa? ‘Kunena zoona mlongo uyu n’ngwoleza mtima mondiposa.’ ‘Koma iye uja ali ndi chikhulupiriro cholimba kwabasi kundiposa.’ ‘Kunena moona mtima, iye uja ndi mphunzitsi wabwino kundiposa.’ ‘Mlongo amene uja sindingafanane naye pobweza mkwiyo.’ Mwinamwake Akolose ena anafunikira kuwongolera pambali imeneyi. Kodi ife tikutero?
8, 9. (a) Kodi Epafra anapempherera Akolose kuti ‘aime’ amphumphu m’lingaliro lotani? (b) Kodi ‘kuima wamphumphu’ kunaphatikizapo chiyani chokhudza m’tsogolo?
8 Epafra anapempherera Akolose kuti ‘aime amphumphu.’ Mwachionekere, Epafra anali kupemphera kwa Mulungu kuti pamlingo womwe Akolose analili Akristu amphumphu, okhwima, aakulu msinkhu, ‘aime,’ kapena kuti apitirizebe kukhala otero.
9 Sitinganene kuti aliyense amene wakhala Mkristu, ndi kufikira pokhwima, adzakhalabe wotero. Yesu ananena kuti mwana waungelo wa Mulungu “sanaima m’choonadi.” (Yohane 8:44) Ndipo Paulo anakumbutsa Akorinto za ena omwe m’mbuyomo anatumikira Yehova kwakanthaŵi ndithu kenako n’kugwa. Anachenjeza abale odzozedwa ndi mzimu kuti: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” (1 Akorinto 10:12) Zimenezi zikuwonjezera mphamvu ku pemphero lakuti Akolose ‘potsirizira pake akaime amphumphu.’ Atakhala amphumphu, aakulu msinkhu, anafunikira kulimbikira, osabwerera m’mbuyo, osatopa, kapena kutengeka. (Ahebri 2:1; 3:12; 6:6; 10:39; 12:25) Kotero kuti m’tsiku la kuyang’anira ndi kuvomereza kotsiriza adzakhale “amphumphu.”—2 Akorinto 5:10; 1 Petro 2:12.
10, 11. (a) Kodi Epafra anatipatsa chitsanzo chotani chokhudza pemphero? (b) Mogwirizana ndi zomwe Epafra anachita, kodi mungatsimikizire mtima kuchitanji?
10 Takambirana kale kufunika kwa kupempherera ena mwa kutchula dzina lawo, kutchula mwachindunji popempha Yehova kuti awathandize, awatonthoze, awadalitse, ndi kuwapatsa mzimu woyera. Mapemphero a Epafra opempherera Akolose anali otero. Ndipo ife tingathe—kwenikweni tiyenera—kupeza mfundo yothandiza kwambiri m’mawu amenewo yokhudza zinthu zathu zaumwini zomwe timamuuza Yehova m’mapemphero. Mosakayikira, tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize ifeyo patokha kuti ‘potsirizira pake tikaime amphumphu.’ Kodi m’matero?
11 Bwanji osafotokoza mavuto anu m’pemphero? Lankhulani ndi Mulungu za momwe mwapitira patsogolo pakukhala ‘wamphumphu,’ wamkulu msinkhu, wokhwima. M’chonderereni kuti akuthandizeni kuzindikira mbali zomwe mufunikirabe kukulitsa mwauzimu. (Salmo 17:3; 139:23, 24) Mosachita kufunsa, n’zodziŵikiratu kuti muli nazo zina mwa mbali zoterozo. Chotero, m’malo mokhumudwa ndi zimenezi, m’pembedzereni Mulungu momveka bwino, mosapita m’mbali kuti akuthandizeni kupita patsogolo. Chitani zimenezi mobwerezabwereza. Kwenikweni, bwanji osatsimikiza mtima kuti mlungu ukudzawu mupemphera moŵirikiza kuti “potsirizira pake mukaime amphumphu.” Ndipo linganizani zoti mudzichita zimenezo mochulukira pamene mukupenda lemba la chaka. M’mapemphero anuwo, sumikani pa zizoloŵezi zomwe zingakuchititseni kubwerera m’mbuyo, kufooka, kapena kuleka kutumikira Mulungu ndi mmene mungapeŵere kuchita zimenezo.—Aefeso 6:11, 13, 14, 18.
Pempherani Kuti Mukhale Wotsimikiza Kotheratu
12. N’chifukwa chiyani kwenikweni Akolose anafunikira kukhala “otsimikiza kotheratu”?
12 Epafra anapemphereranso chinthu chinachake chomwe chinali chofunika kwambiri kuti Akolose apezeke ataima movomerezeka ndi Mulungu potsirizira pake. N’chofunikanso kwa ife. Kodi chimenecho chinali chiyani? Anawapempherera kuti athe kuima “otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.” Anali atazingidwa ndi mpatuko ndi mafilosofi owononga kwambiri, ndipo ena mwa ameneŵa anali ndi maonekedwe achinyengo a kulambira koona. Mwachitsanzo, iwo anaumirizidwa kusunga masiku ena ake apadera mwa kusala kudya kapena kuchita mapwando adzaoneni, monga momwe zinkafunikira pa kulambira kwachiyuda. Aphunzitsi onyenga ankaika maganizo awo onse kwa angelo, mizimu yamphamvu imene inagwiritsidwa Agalatiya 3:19; Akolose 2:8, 16-18.
ntchito kupereka Chilamulo kwa Mose. Tangoganizani kukhala pampanipani wa zinthu ngati zimenezo! Kunali chipwirikiti chosokoneza cha ziphunzitso zotsutsana.—13. Kodi Akolose akanathandizidwa mwa kuzindikira chiyani, nangano zimenezo zingatithandize motani ife?
13 Paulo anapereka mfundo zake mwa kugogomeza mbali yomwe Yesu Kristu ali nayo. “Monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa Iye, ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa.” Inde, (Akolose ngakhalenso ifeyo) anafunikira kutsimikiza mokwanira mbali ya Kristu m’chifuno cha Mulungu ndi m’moyo wathu. Paulo anafotokoza kuti: “Mwa Iye chikhalira chidzalo cha Umulungu m’thupi, ndipo muli odzazidwa mwa Iye, ndiye mutu wa ukulu wonse ndi ulamuliro.”—Akolose 2:6-10.
14. N’chifukwa chiyani chiyembekezo chinali chenicheni kwa Akolose amenewo?
14 Akolose anali Akristu odzozedwa ndi mzimu. Anali ndi chiyembekezo chapadera, cha moyo wakumwamba, ndipotu anali ndi chifukwa chomveka chosungira chiyembekezo chimenecho chili choŵala. (Akolose 1:5) Chinali ‘chifuniro cha Mulungu’ kuti akhale otsimikiza kotheratu kuti chiyembekezo chawocho chinali chodalirika. Kodi aliyense wa iwo anayenera kukayika za chiyembekezo chimenecho? M’pang’ono pomwe! Kodi ziyenera kukhala zosiyana lerolino kwa omwe ali ndi chiyembekezo chopatsidwa ndi Mulungu cha moyo m’dziko lapansi la paradaiso? Ndithudi ayi! Chiyembekezo chodalirika chimenecho chilidi mbali ya ‘chifuniro cha Mulungu.’ Tsopano lingalirani mafunso aŵa: Ngati mukuyesetsa kuti mukhale wa “khamu lalikulu” lomwe lidzapulumuke “chisautso chachikulu,” kodi chiyembekezo chanu n’chenicheni motani? (Chivumbulutso 7:9, 14) Kodi chili mbali ya ‘kutsimikiza kwanu kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu’?
15. Kodi Paulo anatchula mndandanda uti womwe ukuphatikizapo chiyembekezo?
15 Tikati “chiyembekezo” sitikutanthauza kungolakalaka chabe kapena kungoyerekeza. Tingaone zimenezi mu mndandanda wa mfundo zomwe Paulo anazipereka kwa Aroma poyambapo. Mu mndandanda umenewo, chinthu chilichonse chotchulidwamo chikugwirizana ndi chinzake kapena kutsogolera ku chinzake. Onetsetsani pomwe Paulo anaika “chiyembekezo” potchula mfundo zakezo kuti: “Tikondwera m’zisautso; podziŵa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizoloŵezi [“chiyanjo,” NW]; ndi chizoloŵezi [“chiyanjo,”] chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera.”—Aroma 5:3-5.
16. Kodi munapeza chiyembekezo chotani pophunzira choonadi cha Baibulo?
16 Mboni za Yehova zitakuuzani uthenga wa m’Baibulo kwanthaŵi yoyamba, mwinamwake munachita chidwi ndi choonadi chinachake, monga mkhalidwe wa anthu akufa kapena chiukiriro. Koma ochuluka, chinthu chatsopano chomwe anadziŵa kwanthaŵi yoyamba chinali kuthekera kwa moyo m’dziko lapansi la paradaiso kotchulidwa m’Baibulo. Kumbukirani nthaŵi yoyamba yomwe munamva za chiphunzitso chimenechi. N’chiyembekezotu chapamwamba kwabasi—matenda ndi ukalamba sizidzakhalako, mudzatha kumangokhalabe ndi moyo ndi kusangalala ndi zipatso za ntchito yanu, ndipo nyama zidzakhala pamtendere ndi anthu! (Mlaliki 9:5, 10; Yesaya 65:17-25; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 21:3, 4) Munapezatu chiyembekezo chabwino kwabasi!
17, 18. (a) Kodi mndandanda wa zinthu zomwe Paulo anauza Aroma zimatsogolera motani ku chiyembekezo? (b) Kodi ndi chiyembekezo chamtundu wanji chomwe chikutchulidwa pa Aroma 5:4, 5, nanga inuyo muli nacho chimenecho?
17 M’kupita kwa nthaŵi, mungakhale mutayang’anizana ndi chitsutso kapena kuzunzidwa m’njira inayake. (Mateyu 10:34-39; 24:9) Ngakhale m’nthaŵi zamakono, Mboni m’mayiko osiyanasiyana zalandidwa nyumba kapena kuumirizidwa kuthaŵa kwawo. Ena avulazidwa, alandidwa mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, kapena kunenezedwa mabodza m’zofalitsira nkhani. Kaya chizunzo chanu chinali chamtundu wanji, monga momwe Aroma 5:3 akunenera, munakondwera m’chisautso, ndipo chinadzetsa zotsatira zabwino. Monganso momwe Paulo analembera, chisautso chinadzetsa chipiriro mwa inu. Kenako chipirirocho chinadzetsa chiyanjo. Munadziŵa kuti munali kuchita chabwino, kuchita chifuniro cha Mulungu, chotero munali wotsimikiza kuti anali kukuyanjani. Monga mwa mawu a Paulo, munazindikira kuti munali ndi “chiyanjo” chake. Popitiriza, Paulo analemba kuti “chizoloŵezi [“chiyanjo,” ] chichita chiyembekezo.” Zimenezo zingaoneke zodabwitsa. N’chifukwa chiyani Paulo anaika “chiyembekezo” kumapeto kwenikweni pa mndandanda umenewu? Kodi chiyembekezo chanucho simunali nacho kale m’mbuyomo, mutamva za uthenga wabwino kwa nthaŵi yoyamba?
18 Mwachionekere, pano Paulo sakunena za malingaliro athu oyambirirawo a chiyembekezo cha moyo wangwiro. Chimene iye akutanthauza n’choposa pamenepo; n’chakuya, ndi chosonkhezera kwambiri. Pamene tikupirira mokhulupirika ndiyeno n’kuzindikira kuti ndife oyanjidwa ndi Mulungu, zimenezi zimawonjezera kwambiri ndi kulimbitsa chiyembekezo chathu choyambirira. Chiyembekezo chomwe tinali nacho tsopano chimakhala chenicheni, cholimba kwambiri, chathuchathu. Chiyembekezo chozamachi chimaŵala mowonjezereka.
Chimadzaza mbali iliyonse ya moyo wathu. “Ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi; chifukwa chikondi cha Mulungu chinatsanulidwa m’mitima mwathu mwa Mzimu Woyera.”19. Kodi chiyembekezo chanu chingakhale motani mbali ya pemphero lanu nthaŵi zonse?
19 Epafra ankapemphera moona mtima kuti abale ndi alongo ake a ku Kolose akhalebe osonkhezereka ndi okhutira ndi zomwe zinali patsogolo pawo, ali “otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.” Mofananamo aliyense wa ife apempheretu kwa Mulungu nthaŵi zonse mokhudzana ndi chiyembekezo chathu. M’mapemphero anu aumwini, tchulanimo za chiyembekezo chanu chokhudza dziko latsopano. M’fotokozereni Yehova mmene mukulilakalakira, motsimikiza kotheratu kuti lidzafikadi. M’pembedzereni kuti akuthandizeni kuzamitsa ndi kufutukula kutsimikiza kwanu. Monga momwe Epafra anapempherera kuti Akolose akhale “otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu,” chitaninso chimodzimodzi. Chitani zimenezo mobwerezabwereza.
20. Ngati ena oŵerengeka achoka panjira yachikristu, n’chifukwa chiyani zimenezo siziyenera kutifooketsa?
20 Musapatutsidwe kapena kufooka ndi mfundo yakuti si onse amene amaima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu. Ena angalephere, angapatutsidwe, kapena kungoleka. Zimenezo zinachitikapo kwa amene nthaŵi zonse sanali kusiyana ndi Yesu, atumwi ake. Koma Yudase atapereka Yesu kwa adani, kodi atumwi enawo anagwa mphwayi kapena kuleka? Ndithudi ayi! Petro anagwiritsa ntchito Salmo 109:8 kusonyeza kuti winawake adzatenga malo a Yudase. Wina wom’loŵa m’malo anasankhidwa, ndipo okhulupirika a Mulungu anapitirizabe mokangalika ndi ntchito yawo yolalikira. (Machitidwe 1:15-26) Anali otsimikiza mtima kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu.
21, 22. Kodi kuima kwanu wamphumphu ndi wotsimikiza kotheratu kudzaonedwa m’lingaliro lotani?
21 Mosakayika konse, dziŵani kuti kuima kwanu amphumphu komanso otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu sikudzagwa padera. Kudzaonedwa ndi kuyamikiridwa. Ndi yani?
22 Eya, abale ndi alongo anu, omwe akukudziŵani ndi kukukondani, adzaona. Ngakhale ngati ambiri sadzakuuzani mwachindunji, zotsatira zake zidzakhalabe zofanana ndi zomwe timaŵerenga pa 1 Atesalonika 1:2-6 kuti: “Tiyamika Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse, ndi kukumbukira inu m’mapemphero athu; ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu . . . Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu . . . Ndipo munayamba kukhala akutsanza athu, ndi a Ambuye.” Akristu okhulupirika omwe akuzungulirani adzamva mofananamo pamene adzaona kuti inu ‘mukuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’—Akolose 1:23.
23. M’chaka chikudzachi, kodi muyenera kutsimikiza mtima kuchitanji?
23 Mosakayika konse, Atate wanu wakumwamba adzaona ndipo adzakondwera. Khalani otsimikiza zimenezo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mukuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu “za chifuniro chonse cha Mulungu.” Paulo analembera Akolose mowalimbikitsa ponena za kuyenda kwawo “koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo.” (Akolose 1:10) Inde, n’zotheka kwa anthu opanda ungwiro kum’kondweretsa kwambiri. Abale ndi alongo anu a ku Kolose anachita zimenezo. Akristu omwe akuzunguliraniwo panopa akuchitanso zomwezo. Inunso mungachite zimenezo! Chotero, m’kati mwa chaka chikudzachi, mapemphero anu atsiku ndi tsiku ndi zochita zanu nthaŵi zonse zisonyeze kuti mwatsimikiza mtima kuti “potsirizira pake mukaime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.”
Kodi Mungakumbukire?
• Kodi ‘kuima kwanu amphumphu’ kumaphatikizapo chiyani?
• N’zinthu ziti zaumwini zomwe muyenera kuziphatikiza m’pemphero lanu?
• Malinga ndi Aroma 5:4, 5, kodi ndi mtundu uti wa chiyembekezo chomwe mukufuna kukhala nacho?
• Kodi phunziro lathuli lakusonkhezerani kukhala ndi cholinga chotani m’chaka chikudzachi?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 20]
Epafra anapemphera kuti abale ake aime amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za Kristu ndi chiyembekezo chawo
[Zithunzi patsamba 23]
Anthu ena mamiliyoni ambiri alinso ndi chiyembekezo chotsimikizirika ndiponso n’ngotsimikiza kotheratu ngati inuyo