Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi mkazi wokhulupirika wachikristu angakane kusudzulidwa ndi mwamuna wake mpaka pamlingo wotani?

Pamene ukwati wa anthu unali kuyamba, Mulungu anati mwamuna ndi mkazi ayenera ‘kuphatikana’. (Genesis 2:18-24) Anthu anataya ungwiro, ndipo chotsatirapo chake ndicho mavuto ochuluka m’mabanja ambiri, komabe chifuno cha Mulungu n’chakuti okwatirana adzikhalirabe limodzi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ayi, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna, komanso ngati am’siya akhale osakwatiŵa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.”​—1 Akorinto 7:10, 11.

Mawu amenewo akusonyeza kuti monga anthu opanda ungwiro nthaŵi zina mwamuna kapena mkazi angaganize zolekana ndi mnzake. Mwachitsanzo, Paulo ananena kuti ngati mmodzi muukwati achoka, onse aŵiriwo “akhale osakwatiŵa.” Chifukwa chiyani? Inde, mwamuna ndi mkazi wake angalekane, koma kwa Mulungu aŵiriwo amapitirizabe kukhala thupi limodzi. Mwinamwake Paulo ananena izi chifukwa chakuti Yesu anali ataikiratu muyezo wa ukwati wachikristu wakuti: “Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo [mu Chigiriki, por·neiʹa], nadzakwatira wina, achita chigololo.” (Mateyu 19:9) Inde, maziko okhawo a chisudzulo omwe amavomereza kuthetsa ukwati mwa Malemba ndiwo “chigololo,” kapena kuti chiwerewere. Zikuoneka kuti m’chochitika chimene Paulo anatchulacho, aliyense wa aŵiriwo sanachite chigololo, choncho ngati mwamuna kapena mkazi angachoke, kwa Mulungu ukwatiwo umakhalabe usanathe.

Kenako Paulo ananena za chochitika china chakuti Mkristu woona angakhale ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira. Lingalirani malangizo a Paulo akuti: “Koma ngati wosakhulupirayo achoka, achoke. M’milandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo. Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.” (1 Akorinto 7:12-16) Kodi mkazi wokhulupirika angachitenji ngati mwamuna wake wosakhulupirira amusiya, mwinanso kumuumiriza kuti am’sudzule mwalamulo?

Mwina mkazi angakonde kuti asalekane ndi mwamuna wake. Angakhale akum’kondabe, angazindikire zosoŵa za mumtima za aliyense wa iwo ndi mangaŵa a muukwati, ndikuti angazindikire kuti iyeyo ndi ana aang’ono ngati alinawo adzafunikira zinthu zowathandiza mwakuthupi. Angakhalenso n’chiyembekezo chakuti, m’kupita kwa nthaŵi, mwamuna wake angadzakhale wokhulupirira ndi kudzapulumuka. Komabe, ngati mwamuna angalimbikire kuti ukwatiwo uthe (pazifukwa zina zosakhala za m’malemba), mkaziyo angamulole “achoke,” monga momwe Paulo analembera. Momwemonso ngati mwamuna wokhulupirira wanyalanyaza kaonedwe ka Mulungu ka ukwati ndi kuumirira zakuti achoke.

Komabe, zinthu zikafika pamenepa, mkaziyo angafunikire kudziteteza komanso kuteteza ana ake mwalamulo. Motani? Angafune kupitiriza kulera ana ake okondedwawo kotero kuti apitirize kuwasonyeza chikondi cha mayi, kuwaphunzitsa makhalidwe abwino, ndi kukhomereza mwa anawo chikhulupiriro chozikika pa ziphunzitso zabwino za m’Baibulo. (2 Timoteo 3:15) Chisudzulo chingasokoneze ufulu wake. Choncho, sayenera kuzengereza kupeza wokam’chitira umboni moyenerera kwa akuluakulu a zamalamulo n’cholinga chofuna kuteteza ufulu wake wotenga ana ake ndikuti akatsimikizire kuti mwamuna wake wapatsidwa udindo wochirikiza banja lomwe amalinyalanyazalo. M’madera ena, mkazi amene akukana kum’sudzula angasaine zikalata zaboma zomwe zingam’theketse kutenga ana ndi kumalandira thandiza lazachuma, popanda kuvomereza chisudzulo chomwe mwamuna wake akufuna. Penapake, chikalatacho chingalembedwe mawu osonyeza kuti mkaziyo wagwirizana ndi chisudzulocho; chotero, ngati mwamuna wake anachitadi chigololo, ndiyeno mkaziyu n’kusaina zikalatazo, zingatanthauze kuti akukana mwamunayo.

Anthu ambiri m’dera lomwe akukhala ndiponso mumpingo angakhale asakudziŵa ndondomeko zake, monga yakuti chisudzulocho chinachitika mwa Malemba kapena ayi. Choncho zinthu zisanafike poipa choncho, angachite bwino ngati mkaziyo atadziŵitsa woyang’anira wotsogolera komanso mkulu wina mumpingo zoona zake zenizeni (makamaka mwa kulemba kalata). Mwanjira imeneyo padzakhala umboni ngati patabuka funso lililonse​—panthaŵiyo kapena m’tsogolo mwake.

Tiyeni tionenso ndemanga ya Yesu ija: “Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo.” Ngati mwamuna anachitadi chigololo koma akufuna kupitiriza kukhalira limodzi ndi mkazi wake monga banja, mkaziyo (wosachimwa malinga ndi chitsanzo cha Yesu) ayenera kusankha ngati angafune kum’khululukira ndi kupitiriza kukhala naye monga mwamuna wake kapena kumukana. Ngati wafunitsitsa kumukhululukira ndi kupitiriza ukwati ndi mwamuna wake walamulo, mkaziyu sanachite chigololo ngati atero.​—Hoseya 1:1-3; 3:1-3.

Ngati mwamuna wachiwerewere akufuna chisudzulo, mkazi angafunitsitsebe kumukhululukira, n’chiyembekezo chakuti adzabwerera pambuyo pake. Zili kwa mkaziyo kulingalira, malinga ndi chikumbumtima ndi mikhalidwe yake, ngati adzakana chisudzulocho. M’madera ena mkazi yemwe akukana kum’sudzula angathe kusaina zikalata zomwe zingam’vomereze kutenga ana ake ndi kuti azitha kumalandira thandizo lachuma popanda kusonyeza kuti akuvomera kusudzulidwa; kusaina kwake mapepala ngati amenewo mwa iko kokha sikudzasonyeza kuti akukana mwamunayo. Komabe, m’madera ena mkazi amene akukana kum’sudzula angam’pemphe kusaina zikalata zosonyeza kuti akugwirizana ndi chisudzulocho; ngati atasainadi zikalata zimenezo adzasonyeza kuti akukana mwamuna wake wolakwayo.

Pofuna kupeŵa kusamvetsana kulikonse komwe kungabuke, pamenepa n’chinthu chanzeru kuti mkazi apereke kalata kwa oimirira mpingo yofotokoza njira zomwe zikutsatiridwa ndi mmene akuzionera. Angatchulemo kuti anauza mwamuna wake kuti n’ngokonzeka kum’khululukira ndi kukhalabe mkazi wake. Zimenezi zidzatanthauza kuti mkaziyu sanafune kuti asudzulane; m’malo mokana mwamuna wake, anali wokonzeka ndithu kukhululuka. Atafotokoza momveka bwino choncho kuti anali wofunitsitsa kukhululuka ndi kupitirizabe kukhalira limodzi monga banja, kusaina kwake mapepala omwe akungosonyeza chabe mmene angalinganizire nkhani zachuma kapena zokhudza kutenga ana sizidzasonyeza kuti amakana mwamuna wakeyo. *

Atasonyeza kuti n’ngwofunitsitsa kukhululuka ngakhale pambuyo pa chisudzulo, mkazi ngakhalenso mwamuna wake sadzakhala waufulu kukwatirana ndi wina. Ngati mkazi, wosalakwa amene kukhululuka kwake kunakanidwa ndi mnzake uja, pambuyo pake angaganize zomukana chifukwa chakuti mwamunayu n’gwachiwerewere, pamenepo onse aŵiriwo adzakhala omasuka. Yesu anasonyeza kuti mwamuna kapena mkazi wosalakwayo ali ndi ufulu wochita chosankha chimenecho.​—Mateyu 5:32; 19:9; Luka 16:18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Kayendetsedwe ka zinthu ndi mapepala aboma n’kosiyanasiyana malinga ndi malo ake. Kayendetsedwe ka zinthu zosudzulira zofotokozedwa m’mzikalata zaboma ziyenera kupendedwa mosamala musanasaine. Ngati mwamuna kapena mkazi wosalakwa wasaina mapepala omwe akusonyeza kuti sakutsutsa malingaliro a mnzake akuti asudzulane, zikatanthauza kuti akugwirizana ndi chisudzulocho.​—Mateyu 5:37.