Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chikondi Chanu N’chosefukira Motani?

Kodi Chikondi Chanu N’chosefukira Motani?

Kodi Chikondi Chanu N’chosefukira Motani?

“Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”​—MATEYU 22:39.

1. Ngati Yehova timam’konda, n’chifukwa chiyani tiyeneranso kukonda anzathu?

YESU atafunsidwa kuti lamulo lalikulu ndi liti, anayankha kuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” Kenako, anagwira mawu lamulo lachiŵiri lofanana ndi loyambali, akumati: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” (Mateyu 22:37, 39) Inde, Mkristu amadziŵika chifukwa cha kukonda anzake. Ndithudi, ngati Yehova timam’konda, tiyenera kukondanso anzathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti timasonyeza kuti timakonda Mulungu mwa kumvera Mawu ake, ndipo Mawu akewo amatilamulira kukonda anzathu. Chotero, ngati abale ndi alongo athu sitiwakonda, ndiye kuti chikondi chathu pa Mulungu sichingakhale chenicheni.​—Aroma 13:8; 1 Yohane 2:5; 4:20, 21.

2. Kodi anansi athu tiyenera kuwakonda ndi chikondi chamtundu wanji?

2 Yesu ponena kuti tizikonda anzathu, anali kunena zoposa ubwenzi chabe. Ndipo anali kutanthauza chikondi chosiyana ndi chomwe mwachibadwa chimapezeka m’mabanja kapena chomwe mwamuna ndi mkazi amasonyezana. Anali kunena za mtundu wa chikondi chomwe Yehova alinacho kwa atumiki ake odzipatulira komanso chomwe atumikiwo alinacho kwa iye. (Yohane 17:26; 1 Yohane 4:11, 19) Mlembi wachiyuda​—yemwe, malinga n’kuona kwa Yesu, anali kulankhula mwanzeru​—anavomerezana ndi Yesu kuti munthu ayenera kukonda Mulungu “ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse.” (Marko 12:28-34) Ananena zoona. Chikondi chomwe Mkristu amakulitsa ponse paŵiri kwa Mulungu ndi kwa anzake chimakhudza mtima komanso nzeru zathu. Chimamveka mumtima ndipo malingaliro amachitsogolera.

3. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa motani mwamuna “wachilamulo” kuti athe kulingalira mofutukuka za yemwe mnansi wake ali? (b) Kodi fanizo la Yesuli limakhudza motani Akristu lerolino?

3 Monga momwe Luka akunenera, Yesu atanena kuti tiyenera kukonda anansi athu, mwamuna wina “wachilamulo” anafunsa kuti: “Ndipo mnansi wanga ndani?” Yesu anayankha mwa fanizo. Mwamuna wina anam’kwapula achifwamba, namulanda katundu wake, ndipo anam’siya m’mphepete mwa msewu ali wofuna kufa. Choyamba wansembe anadutsa pomwepo kenako Mlevi. Onseŵa anam’nyalanyaza. Potsirizira pake, Msamariya anafika, anaona mwamuna wovulazidwayo, ndipo anam’chitira zambiri mwachifundo. Ndani wa atatuwo yemwe anali mnansi wa wovulazidwayo? Yankho lake linali lachidziŵikire. (Luka 10:25-37) Mwinamwake mwamuna wachilamulo ameneyu anadabwa kwambiri kumva Yesu akunena kuti Msamariya angakhoze kukhala mnansi wabwino kuposa wansembe ndi Mlevi. Mwachionekere, Yesu anali kuthandiza munthu ameneyu kukonda anansi ake m’njira yapadera kwambiri. Akristu nawonso chikondi chawo n’chotero. Lingalirani za onse omwe amapindula ndi chikondi chawocho.

Chikondi M’banja

4. N’kuti komwe Mkristu amayambira kusonyeza chikondi?

4 Akristu amakonda am’banja lawo​—akazi amakonda amuna awo, amuna amakonda akazi awo, makolo amakonda ana awo. (Mlaliki 9:9; Aefeso 5:33; Tito 2:4) Zoonadi, m’mabanja ambiri muli mgwirizano wachikondi chachibadwa. Komabe, malipoti a mabanja osweka, kuchitirana nkhanza kwa okwatirana, ndi kunyalanyaza kapena kuchitira nkhanza ana akusonyeza kuti banja lili m’vuto lalikulu lerolino, ndipo chikondi chachibadwa cha m’banja sichingathe kuligwirizanitsa. (2 Timoteo 3:1-3) Kuti moyo wawo wam’banja ukhaledi wopambana, Akristu afunikira kusonyeza mtundu wachikondi chomwe Yehova ndi Yesu alinacho.​—Aefeso 5:21-27.

5. Kodi makolo amayang’ana kwayani kaamba ka thandizo polera ana awo, ndipo ochuluka akhala ndi zotsatirapo zotani?

5 Makolo achikristu amaona ana awo monga chuma chamtengo wapatali chomwe Yehova waikiza mwa iwo, ndipo amayang’ana kwa iye kuti awathandize kuwalera bwino. (Salmo 127:3-5; Miyambo 22:6) Mwanjira imeneyi amakulitsa chikondi chachikristu, chomwe chimawathandiza kuteteza ana awo ku zisonkhezero zovulaza zomwe achinyamata angagwemo. Chotsatirapo chake n’chakuti, makolo ambiri achikristu apeza chimwemwe chofanana ndi chomwe mayi wina ku Netherlands anapeza. Ataonerera kubatizidwa kwa mwana wake wamwamuna​—mmodzi wa anthu 575 omwe abatizidwa mu Netherlands chaka chathachi​—iye analemba kuti: “Panopa, chuma chomwe ndinaikiza m’zaka 20 zapitazo chatulutsa phindu tsopano. Nthaŵi ndi mphamvu zonse​—limodzi ndi ululu, khama, ndi chisoni​—zaiŵalika tsopano.” N’ngwosangalalatu kwabasi kuti mwakufuna kwake, mwana wake wamwamunayo, anasankha kutumikira Yehova. Chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 31,089 omwe anaperekera lipoti mu Netherlands chaka chathachi chikuphatikizapo ambiri omwe anaphunzira kukonda Yehova kuchokera kwa makolo awo.

6. Kodi chikondi chachikristu chingathandize motani kulimbitsa ukwati?

6 Paulo anati chikondi “ndicho chomangira cha mtima wamphumphu,” ndipo chingateteze mgwirizano wa banja ngakhale m’nthaŵi zamavuto. (Akolose 3:14, 18, 19; 1 Petro 3:1-7) Mwamuna wina ku Rurutu, kachilumba kakang’ono ka makilomita ngati 700 kuchokera ku Tahiti, atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mkazi wake anam’tsutsa mwamphamvu. Pambuyo pake, mkaziyo anatenga ana awo, anasiya mwamuna wakeyo ndi kuchoka kukakhala ku Tahiti. Komabe, mwamunayu anasonyeza chikondi chake mwa kumam’tumizira ndalama nthaŵi ndi nthaŵi komanso kumamuimbira telefoni kuti amufunse ngati pali china chilichonse chomwe iye kapena anawo akusoŵa. Pochita izi anayesetsa mbali yake kukwaniritsa udindo wake wachikristu. (1 Timoteo 5:8) Nthaŵi zonse anali kupemphera kuti banja lake ligwirizanenso, ndipo pambuyo pake mkazi wake anabwerera. Atabwerera, anachita naye mwa “chikondi, chipiriro, chifatso.” (1 Timoteo 6:11) M’chaka cha 1998, anabatizidwa ndipo pambuyo pake anali ndi chimwemwe chodzala tsaya mkazi wake atavomera kuphunzira Baibulo. Phunziro limenelo linali limodzi mwa maphunziro 1,351 omwe anachitidwa m’dera limenelo loyang’aniridwa ndi nthambi ya Tahiti chaka chathachi.

7. Malinga ndi kunena kwa mwamuna wina ku Germany, n’chiyani chomwe chinalimbitsa ukwati wake?

7 Ku Germany mwamuna wina anatsutsa kwambiri chidwi cha mkazi wake pa choonadi cha Baibulo ndipo anali wotsimikizira kuti Mboni za Yehova zikufuna kugwiritsa mkazi wakeyo fuŵa lamoto. Komabe, pambuyo pake iye analembera kalata wa Mboni yemwe anafikira mkazi wakeyo kwanthaŵi yoyamba kuti: “Zikomo kwambiri podziŵitsa mkazi wanga za Mboni za Yehova. Poyamba ndinkaopa chifukwa chakuti ndinamva zinthu zambiri zoipa zokhudza Mboni. Koma pano, pambuyo popita m’misonkhano limodzi ndi mkazi wanga, ndazindikira kuti ndimalakwitsa. Ndadziŵa tsopano kuti ndikumva choonadi, ndipo chalimbitsa kwambiri ukwati wathu.” Mboni za Yehova zokwana 162,932 m’Germany​—komanso zokwana 1,773 m’zilumba zomwe zikuyang’aniridwa ndi nthambi ya Tahiti​—zikuphatikizapo mabanja ambirimbiri ogwirizana m’chikondi chaumulungu.

Chikondi cha pa Abale Athu Achikristu

8, 9. (a) Ndani amatiphunzitsa kukonda abale athu, nanga chikondi chimatisonkhezera kuchita chiyani? (b) Perekani chitsanzo cha momwe chikondi chingathandizire abale kukhala othandizana.

8 Paulo anauza Akristu a ku Tesalonika kuti: “Wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 4:9) Inde, awo amene ‘akuphunzitsidwa ndi Yehova’ amakondana. (Yesaya 54:13) Chikondi chawocho amachisonyeza m’zochita zawo, monga momwe Paulo anasonyezera pamene anati: “Mwa chikondi chitiranani ukapolo.” (Agalatiya 5:13; 1 Yohane 3:18) Amachitadi zimenezi, mwachitsanzo, mwa kukachezera abale ndi alongo odwala, kulimbikitsa otaya mtima, ndi kuchirikiza ofooka. (1 Atesalonika 5:14) Chikondi chathu chenicheni chachikristu chimachirikiza kukula kwa paradaiso wathu wauzimu.

9 Mu Mpingo wa Ancón​—umodzi wa mipingo 544 mu Ecuador​—abale anasonyeza chikondi chawo m’njira yothandiza kwambiri. Mavuto a zachuma anawaika m’vuto losoŵa ntchito kapena ndalama, choncho ofalitsa anaganiza zopeza ndalama mwa kugulitsa chakudya kwa asodzi akomweko pamene asodziwo abwerera kunyumba atatha kusodza usiku. Aliyense anachirikiza ntchitoyo, ngakhalenso ana. Ankayamba nthaŵi ya 1:00 a.m. n’cholinga chakuti pomafika 4:00 a.m. pamene asodziwo amabwerera, akhale atatsiriza kukonza chakudya. Ndalama zomwe abalewo amapeza amagaŵana malinga ndi zosoŵa zawo. Kuthandizana kotereku kunasonyeza chikondi chenicheni chachikristu.

10, 11. Kodi tingasonyeze motani chikondi kwa abale omwe sitikuwadziŵa?

10 Komabe, chikondi chathu sitimachisonyeza kwa Akristu okhawo omwe tikuwadziŵa ayi. Mtumwi Petro anati: ‘Khalani ndi chikondi kwa gulu lonse la abale.’ (1 Petro 2:17, NW) Abale ndi alongo athu onse timawakonda chifukwa chakuti onsewo ndi olambira anzathu a Yehova Mulungu. Nthaŵi za mavuto zingatipatse mpata wosonyeza chikondi chimenechi. Mwachitsanzo, m’kati mwa chaka cha utumiki cha 2000, madzi osefukira anawononga zinthu mochititsa mantha ku Mozambique, komanso nkhondo yosatha yapachiŵeniŵeni ya ku Angola yaika anthu ambiri paumphaŵi wadzaoneni. Chiŵerengero chochuluka cha abale 31,725 ku Mozambique ndi abale 41,222 ku Angola akhudzidwa ndi zochitika zimenezi. Chotero, Mboni za m’dziko loyandikana nalo la South Africa zatumiza zinthu zochuluka kuti zikathandize kuchepetsa mavuto a abale awo m’mayiko amenewo. Kufunitsitsa kwawo kupereka mwaufulu ‘zochuluka’ zawo kwa abale awo osoŵa kunasonyeza chikondi chawo.​—2 Akorinto 8:8, 13-15, 24.

11 Chikondi chimaonekeranso, pamene abale m’mayiko ambiri apereka mwaufulu pochirikiza ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Msonkhano m’mayiko osauka. Chitsanzo ndi cha pa zilumba zotchedwa Solomon Islands. Ngakhale kuti zinthu n’zosokonekera kwambiri kumeneku, chiŵerengero cha ofalitsa pa Solomon Islands chinawonjezeka ndi 6 peresenti chaka chathachi, ndi chiŵerengero chapamwamba cha 1,697. Analinganiza zomanga Nyumba ya Msonkhano. Ngakhale kuti anthu ambiri okhala m’zilumbazo amathaŵa m’dziko lawoli, antchito odzifunira anabwera kuchokera ku Australia kudzathandiza kumangako. Kenako antchito odzifunirawo anachoka, koma ataphunzitsa kaye abale akomweko mmene adzamalizira maziko a nyumbayo. Zitsulo zoduliratu kale zogwiritsa ntchito pomanga nyumbayi zimabwera pasitima yapamadzi kuchokera ku Australia, ndipo kumalizidwa kwa nyumba yokongola yolambiriramo imeneyi​—panthaŵi yomwe malo ambiri omwe amati amangepo nyumba anyalanyazidwa​—kudzakhala umboni wamphamvu ku dzina la Yehova komanso ku chikondi cha abale.

Monga Mulungu, Timakonda Dziko Lapansi

12. Kodi timatsanzira motani Yehova pa momwe timaonera ena omwe sali achikhulupiriro chathu?

12 Kodi chikondi chathu timachisonyeza m’banja lathu lokha ndi kwa abale basi? Ayi, ngati ndife “akutsanza a Mulungu” sititero. Yesu anati: ‘Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.’ (Aefeso 5:1; Yohane 3:16) Mofanana ndi Yehova Mulungu, timachitira onse mwachikondi​—kuphatikizapo awo amene sali ofanana nafe chikhulupiriro. (Luka 6:35, 36; Agalatiya 6:10) Makamaka pa mbali imeneyi, timalalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuuza ena za ntchito zazikulu za chikondi zomwe Mulungu wawachitira. Zimenezi zingadzetse chipulumutso kwa aliyense womvetsera.​—Marko 13:10; 1 Timoteo 4:16.

13, 14. Pali zochitika zina zotani za abale omwe anasonyeza chikondi kwa anthu omwe si Mboni, ngakhale kuti kwa iwonso zinali zovuta kwambiri?

13 Talingalirani za atumiki anayi omwe akuchita upainiya wapadera ku Nepal. Abale ameneŵa anatumizidwa ku mzinda wina kumwera chakumadzulo kwa dzikoli, ndipo kwa zaka zisanu zapitazi, asonyeza chikondi chawo mwa kuchitira umboni moleza mtima m’mzindawo ndi m’midzi yozungulira. Kuti athe kufola gawo lawolo, kaŵirikaŵiri amayenda panjinga kwa maola ambiri m’nyengo yotentha kwambiri kuposa 40°C. Chikondi chawo ndi “kupirira pa ntchito zabwino” kunatulutsa zotsatira zabwino pamene gulu la phunziro labuku linakhazikitsidwa mu umodzi mwa midziyo. (Aroma 2:7) M’mwezi wa March 2000, anthu okwana 32 anabwera kudzamvetsera nkhani yapoyera yomwe woyang’anira dera amene anakawachezera anakamba. Nepal anali ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 430 chaka chathachi​—kuwonjezeka ndi 9 peresenti. N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa changu ndi chikondi cha abale m’dziko limenelo.

14 Ku Colombia apainiya apadera ogwirizira anapita kukalalikira Amwenye Achiwayuu. Kuti achite zimenezo, anafunikira kuphunzira chinenero chatsopano, koma chidwi chawo chachikondicho chinafupidwa pamene anthu 27 anamvetsera nkhani yapoyera ngakhale kuti kunagwa chimvula chadzaoneni. Changu chachikondi monga chomwe apainiyaŵa anasonyeza chinathandizira kuwonjezeka kwa 5 peresenti mu Colombia ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 107,613. Ku Denmark mlongo wina wachikulire ankafunitsitsa kugaŵana uthenga wabwino ndi ena, koma amalephera chifukwa cha ukalamba. Mosagwa mphwayi, analankhulana ndi anthu achidwi mwa kulemberana nawo makalata. Padakali pano, amalemberana makalata ndi anthu 42 ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo okwana 11. Iye ndi mmodzi mwa chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 14,885 omwe anapereka malipoti m’Denmark chaka chathachi.

Kondani Adani Anu

15, 16. (a) Kodi Yesu anati chikondi chathu chiyenera kukhala chosefukira motani? (b) Kodi abale anachita motani m’njira yachikondi ndi munthu yemwe ananena nkhani yabodza yokhudza Mboni za Yehova?

15 Yesu anauza mwamuna wachilamulo uja kuti Msamariya angamuone ngati mnansi. Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anaposa pamenepo pomwe anati: “Munamva kuti kunanenedwa, uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nawo adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa kumwamba.” (Mateyu 5:43-45) Ngakhale ngati winawake akutitsutsa, timayesa ‘kugonjetsa choipa’ pogwiritsa ntchito “chabwino.” (Aroma 12:19-21) Ngati n’kotheka, timagaŵana naye chuma chathu chamtengo wapatali koposa, choonadi.

16 Ku Ukraine nkhani ina m’nyuzipepala yotchedwa Kremenchuk Herald inati Mboni za Yehova ndi kagulu koopsa kampatuko. Imeneyi inali nkhani yaikulu kwambiri chifukwa chakuti ku Ulaya ena amaneneza Mboni za Yehova m’njira imeneyi n’cholinga chofuna kusonkhezera anthu kuti apondereze ntchito za Mboni kapena kuziletseratu kuchita chilichonse. Choncho mkonzi wake anam’fikira ndi kumupempha kusindikiza nkhani yowongolera nkhani imeneyi. Iye anavomera, koma potulutsa nkhani yowongolerayo, mkonzi ameneyu anasindikizanso mawu akuti nkhani yoyamba ija inali yoona. Choncho abale omwe amayendetsa nkhani imeneyi anam’fikiranso kachiŵiri ndi chidziŵitso chochuluka. Potsirizira pake, mkonzi ameneyu anazindikira kuti nkhani yoyamba ija sinali yoona, ndipo anasindikiza nkhani yovomereza kuti inali yabodza. Kuchita naye moona mtima ndi mwachifundo inali njira yachikondi yothetsera vuto limeneli, ndipo kunadzetsa zotsatira zabwino.

Kodi Chikondi Tingachikulitse Motani?

17. N’chiyani chomwe chimasonyeza kuti sichingakhale chapafupi nthaŵi zonse kuchitira ena mwachikondi?

17 Mwana akabadwa, mwamsanga makolo ake amam’konda. Kuchita mwachikondi ndi anthu aakulu si kumangochitika mwachibadwa nthaŵi zonse. Mwachionekere chimenecho n’chifukwa chake Baibulo limatiuza mobwerezabwereza kuti tikondane wina ndi mnzake​—ndi chinthu chomwe tiyenera kukulitsa. (1 Petro 1:22; 4:8; 1 Yohane 3:11) Yesu anadziŵa kuti chikondi chathu chidzayesedwa pamene anati tiyenera kukhululukira mbale wathu “kufikira makumi asanu ndi aŵiri.” (Mateyu 18:21, 22, NW) Paulo nayenso akutilimbikitsa kupitirizabe “kulolerana wina ndi mnzake.” (Akolose 3:12, 13) N’chifukwa chaketu tikuuzidwa kuti: “Tsatani chikondi”! (1 Akorinto 14:1) Kodi zimenezi tingazichite motani?

18. N’chiyani chomwe chingatithandize kukulitsa chikondi chathu kwa ena?

18 Choyamba, tiyenera kukumbukira nthaŵi zonse momwe timam’kondera Yehova Mulungu. Chikondi chimenechi n’chisonkhezero champhamvu cha kukonda anansi athu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti pamene tichita zimenezo, zimasonyeza kuti tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo zimenezi zimadzetsa ulemerero ndi chitamando kwa iye. (Yohane 15:8-10; Afilipi 1:9-11) Chachiŵiri, tingayese kuona zinthu monga momwe Yehova amazionera. Tikachimwa nthaŵi zonse, timachimwira Yehova; koma nthaŵi ndi nthaŵi amatikhululukira ndi kupitirizabe kutikonda. (Salmo 86:5; 103:2, 3; 1 Yohane 1:9; 4:18) Ngati titakulitsa mmene Yehova amaonera zinthu, tidzasonkhezereka kukonda ena ndi kuwakhululukira zomwe atichimwira. (Mateyu 6:12) Chachitatu, tingachitire ena monga momwe ife tikufunira kuti iwo atichitire. (Mateyu 7:12) Popeza kuti ndife opanda ungwiro, timafuna kukhululukidwa nthaŵi zonse. Mwachitsanzo, tikanena zinthu zomwe ena zawapsetsa mtima, timayembekezera kuti adzakumbukira kuti aliyense amachimwa polankhula nthaŵi ndi nthaŵi. (Yakobo 3:2) Ngati tikufuna kuti ena azichita nafe mwachikondi, nafenso tiyenera kuchita nawo mwachikondi.

19. Kodi tingafunefune motani thandizo la mzimu woyera pokulitsa chikondi?

19 Chachinayi, tingafunefune thandizo la mzimu woyera chifukwa chakuti chikondi ndi mbali ya chipatso cha mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Maubwenzi, kukondana m’banja, chikondi cha mwamuna ndi mkazi kaŵirikaŵiri zimakhala zachibadwa. Koma tifunikira thandizo la mzimu wa Yehova kuti tikulitse chikondi chomwe Yehova alinacho, chikondi chomwe ndi chomangira cholimba cha mgwirizano. Tingafunefune thandizo la mzimu woyera mwa kuŵerenga Baibulo louziridwa. Mwachitsanzo, tikaphunzira mbiri ya moyo wa Yesu, tidzaona momwe anali kuchitira ndi anthu, ndipo tidzaphunzira kumutsanzira. (Yohane 13:34, 35; 15:12) Komanso, tingapemphe mzimu woyera kwa Yehova, makamaka m’mikhalidwe yomwe imatilepheretsa kuchita zinthu mwachikondi. (Luka 11:13) Chotsirizira, tingakulitse chikondi mwa kuyandikira kwambiri mpingo wachikristu. Kukhalira limodzi ndi abale ndi alongo achikondi kumatithandiza kukulitsa chikondi.​—Miyambo 13:20.

20, 21. Kodi ndi motani momwe Mboni za Yehova zinasonyezera mwapadera chikondi m’chaka chautumiki cha 2000?

20 Chaka chatha, panali chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa a uthenga wabwino 6,035,564 padziko lonse lapansi. Mboni za Yehova zinathera chiwonkhetso cha maola 1,171,270,425 kufunafuna anthu ndi kuwauza uthenga wabwino umenewo. Chinali chikondi chomwe chinawachititsa kupirira kutentha, mvula, ndi kuzizira pamene anali kugwira ntchito imeneyi. Chinali chikondi chomwe chinawasonkhezera kulankhula kwa anzawo akusukulu ndi anzawo ogwira nawo ntchito limodzi komanso kufikira anthu osawadziŵa n’komwe m’misewu ndi m’malo ena osiyanasiyana. Ambiri omwe Mbonizo zinawafikira anali amphwayi, oŵerengeka anali otsutsa. Komabe, ena anasonyeza chidwi, chotero maulendo obwereza okwana 433,454,049 anachitika, ndipo maphunziro a Baibulo omwe anachititsidwa anali okwana 4,766,631. *

21 Zonsezi zinalitu chisonyezero cha chikondi chomwe Mboni za Yehova zili nacho pa Mulungu wawo ndi pa mabwenzi awo! Chikondi chimenechi sichidzazirala. Tili ndi chikhulupiriro kuti umboni wokulira uperekedwa kwa anthu m’chaka cha utumiki cha 2001. Madalitso a Yehova apitirizetu kutsanulidwa pa olambira ake okhulupirika ndi achangu pamene ‘akuchita zawo zonse m’chikondi’!​—1 Akorinto 16:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 20 Kuti mumve zonse zokhudza Lipoti la Chaka Chautumiki cha 2000, onani tchati chomwe chili patsamba 18-21.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi mwa kukonda anzathu timakhala tikutsanzira yani?

• Kodi chikondi chathu chiyenera kusefukira kwayani?

• N’zochitika zina zotani zomwe zikusonyeza chikondi chachikristu?

• Kodi chikondi chachikristu tingachikulitse motani?

[Mafunso]

[Tchati pamasamba 18-21]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2000 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi patsamba 15]

Chikondi chachikristu chingagwirizanitse banja

[Zithunzi patsamba 17]

Chikondi chimatisonkhezera kuuza ena za chiyembekezo chathu