Kodi Meleniyamu Yatsopano Ikhala Yamtendere?
Kodi Meleniyamu Yatsopano Ikhala Yamtendere?
PA September 14, 1999, linali tsiku la mwambo wokhazikitsa chaka cha khalidwe la mtendere padziko lonse wotchedwa The International Year for the Culture of Peace, womwe unachitikira ku Paris ndi ku New York City. Izi zinalengezedwa ndi bungwe la United Nations lotchedwa General Assembly, pokambirana za chaka cha 2000. Yemwe kale anali mtsogoleri wamkulu wa UNESCO, Federico Mayor, mwamphamvu anapempha “kuti padziko lonse pakhazikitsidwe bungwe loona za khalidwe lamtendere ndi lopanda chiwawa.”
Bungwe la UNESCO limakhulupirira kuti; pakuti “nkhondo zimayambira m’mitima mwa anthu, n’kofunika kuti chitetezo cha mtendere chikhazikitsidwe m’mitima mwa anthu.” Mogwirizana ndi zimenezi, bungweli likukonza zolimbikitsa mtendere kudzera “m’maphunziro, kukambirana pakakhala kusiyana maganizo, ndiponso mgwirizano.” Bambo Mayor anati sikokwanira “kukhala anthu a mtendere, ngakhalenso kukhala anthu odana ndi nkhondo, koma kukhala anthu okhazikitsa mtendere.”
N’zomvetsa chisoni kuti chaka cha 2000 sichinakhale chaka cha mtendere m’pang’ono pomwe. Mbiri yamakono, kuphatikizapo zochitika m’chaka cha 2000, zatsimikizira kulephera kwa anthu kuthetsa nkhondo ndi ziwawa ngakhale kuti ayesetsa moona mtima.
Koma n’kofunikadi kudziŵa kuti mtendere umagwirizanadi ndi maphunziro. Zaka 2,700 zapitazo, mneneri Yesaya analosera kuti: ‘Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.’ (Yesaya 54:13) Mneneri yemweyo, anaoneratu nthaŵi yomwe anthu amitundu yonse adzakhamukira ku kulambira koona kwa Yehova Mulungu kuti akaphunzire njira Zake. Kodi zotsatira zake zidzakhala zotani? ‘Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:2-4) Mogwirizana ndi ulosi umenewo, Mboni za Yehova zikugwira ntchito yophunzitsa anthu padziko lonse yomwe yathandiza kale mamiliyoni a anthu kugonjetsa tsankho la mitundu lomwe ndi maziko enieni a nkhondo zambiri.
Nkhondo sizidzakhalakonso mu Ufumu wa Mulungu, womwe udzakhazikitsa mtendere wosatha ndi chitetezo padziko lapansi. (Salmo 72:7; Danieli 2:44) Pamenepo, mawu a wamasalmo akuti: “Penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi” adzakwaniritsidwa.—Salmo 46:8, 9.