Kuchiritsa Mabala a Nkhondo
Kuchiritsa Mabala a Nkhondo
ABRAHAM anali m’gulu lankhondo lazigawenga kwa zaka 20. * Koma tsopano anasiya nkhondo ndipo sadzamenyanso nkhondo. Komanso, ena mwa amene kale anali adani ake ali mabwenzi ake a pamtima tsopano. N’chiyani chinam’sintha? Baibulo. Baibulo linapatsa Abraham chiyembekezo ndi chidziŵitso, kum’thandiza kuona zochita za anthu monga momwe Mulungu amazionera. Baibulo linam’chotsera chilakolako chankhondo, ndipo linayamba kupukuta misozi yake, kuchiritsa chidani chake, ndi kuwawidwa mtima kwake. Anazindikira kuti Baibulo lili ndi mankhwala amphamvu a mtima wake.
Kodi Baibulo limam’thandiza motani munthu kuchiritsa mabala ake a mumtima? Silinasinthe zimene Abraham anakumana nazo. Komabe, kuŵerenga ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Mulungu kunagwirizanitsa maganizo ake ndi maganizo a Mlengi. Tsopano ali ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino, ndipo ali ndi zinthu zatsopano zimene akuzitsogoza. Zinthu zofunika kwa Mulungu zakhala zofunika kwa iye. Zimenezi zitayamba kuchitika, mabala a mumtima mwake anayamba kuchira. Ndimo mmene Abraham anathandizidwira kuti asinthe.
Kuloŵa M’nkhondo Yachiŵeniŵeni
Abraham anabadwa m’ma 1930 mu Africa. Nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse itatha, dziko lake linayamba kulamulidwa ndi dziko lamphamvu loyandikana nalo, koma anthu ochuluka a m’dziko la Abraham ankafuna ufulu wodzilamulira. Mu 1961, Abraham analoŵa m’gulu lomenyera ufulu lomwe linamenya nkhondo yauchigawenga polimbana ndi dziko lamphamvu lija loyandikana nalo.
“Anali adani athu. Ankafuna kutipha, chotero ifenso tinali kufuna kuwapha,” akutero Abraham.
Kaŵirikaŵiri moyo wa Abraham unali kukhala pangozi, chotero mu 1982, atamenya nkhondo kwa zaka 20, anathaŵira ku Ulaya. Panthaŵiyi anali ndi zaka zothamangira ku 50, ndipo atapeza mpata wabwino wosinkhasinkha, anapendanso moyo wake. Kodi zikhumbo zake zinam’fikitsa pati? Nanga tsogolo linali lotani? Abraham anakumana ndi ena a Mboni za Yehova ndipo anayamba kupita kumisonkhano yawo. Iye anakumbukira kuti zaka zakumbuyoko ali ku Africa, anaŵerengapo thirakiti limene Mboni ina inam’patsa. Thirakiti limenelo linalongosola za paradaiso wa m’tsogolo wa padziko lapansi ndi boma lakumwamba limene lidzalamulira anthu. Koma kodi nkhanizo zinalidi zoona?
Abraham akuti: “Baibulo linandiphunzitsa kuti zaka zonsezo zimene ndinathera m’nkhondo zinangopita pachabe. Boma lokhalo limene lidzachita chilungamo kwa aliyense ndilo Ufumu wa Mulungu.”
Posapita nthaŵi Abraham atangobatizidwa kumene monga Mboni ya Yehova, mwamuna wina dzina lake Robert anathaŵa kuchoka ku Africa kupita kumzinda wa ku Ulaya kumene kunali Abraham. Robert ndi Abraham anali atamenya nawo nkhondo imodzimodziyo kumbali zomenyanazo. Kaŵirikaŵiri Robert anali kusinkhasinkha za chifuno chenicheni cha moyo. Anali munthu wokonda kupemphera, ndipo ataŵerenga zigawo zina za m’Baibulo, anadziŵa kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova. Pamene Mboni zochokera mu mpingo wa Abraham zinadzipereka kuthandiza Robert kulimvetsa bwino Baibulo, iye anavomereza ndi mtima wonse.
Robert akulongosola kuti: “Kungoyambira pachiyambi, ndinasangalala ndi mmene Mboni zimagwiritsira ntchito mayina a Yehova ndi Yesu, kusonyezadi kuti ndi anthu aŵiri osiyana. Zimenezo zinali zogwirizana ndi zimene ndinali kudziŵa kale malinga ndi Baibulo. Mboni zimavalanso mwaudongo ndipo zimasonyeza kukoma mtima kwa ena, mosasamala kanthu kuti enawo ndi a mtundu wanji. Zinthu ngati zimenezi zinandikhudza kwambiri.”
Adani Akhala Mabwenzi
Robert ndi Abraham, omwe poyamba anali adani, tsopano ndi mabwenzi enieni. Iwo akutumikira monga alaliki a nthaŵi zonse mumpingo umodzi wa Mboni za Yehova. Abraham akulongosola kuti: “Tili m’nkhondo, nthaŵi zambiri sindinali kumvetsa kuti zimatheka bwanji kuti anthu ochokera m’mayiko oyandikana azidana, ochuluka otinso anali m’chipembedzo chimodzi. Ineyo ndi Robert tinali m’tchalitchi chofanana, koma tonse tinapita kunkhondo kukamenyana. Tonse tsopano ndife Mboni za Yehova, ndipo chikhulupiriro chathu chatiyanjanitsa.”
“M’pamene pali kusiyana pamenepo,” akuwonjezera motero Robert. “Tonse tsopano tili m’chikhulupiriro chomwe chatiloŵetsa mu ubale weniweni. Sitingapitenso kunkhondo.” Baibulo lakhala lamphamvu posonkhezera mitima ya anthu ameneŵa omwe kale anali adani. M’kupita kwa nthawi, udani ndi kuwawidwa mtima zaloŵedwa m’malo ndi kukhulupirirana ndi kukondana.
Panthaŵi yofananayo pamene Abraham ndi Robert anali kunkhondo, anyamata enanso aŵiri anali kumbali zomenyana m’nkhondo ya pakati pa mayiko oyandikana. Nawonso sipanapite nthaŵi kuti Baibulo likhale ngati mankhwala amphamvu ochiritsa mitima yawo. Zinali bwanji?
Kupha—Kenako Kufera Chikhulupiriro
Gabriel, yemwe anakulira m’banja lopembedza, anaphunzitsidwa kuti dziko lawo linali pankhondo yopatulika. Chotero, ali ndi zaka 19 zakubadwa, anadzipereka kukhala msilikali ndipo anapempha kuti atumizidwe kunkhondoko. Kwa miyezi 13 anali pakati pa kumenyana kowopsa zedi, moti nthaŵi zina anali kungotsala ndi mtunda wa kilomita imodzi ndi theka basi kuti aonane maso ndi maso ndi adani awo. “Ndikukumbukira chochitika chimodzi makamaka,” iye akutero. “Mkulu wa gulu lathu anatiuza kuti adani athu adzatidzidzimutsa usikuwo. Tinakhala chire kwambiri moti tinawombera mizinga yathu usiku wonse.” Iye anali kuona anthu a m’dziko loyandikanalo monga adani ake, oyenera kufa. “Ndinali kungofuna kuwapha monga momwe ndingathere. Kenako, mofanana ndi
anzanga ambiri, ndinali kufuna kufa monga munthu wofera chikhulupiriro.”Koma m’kupita kwa nthaŵi, Gabriel anayamba kuzindikira zenizeni zake. Anathaŵira kumapiri, n’kuloŵa mozemba m’dziko losakhudzidwa ndi nkhondoyo, ndipo anapita ku Ulaya. Iye anapitirizabe kufunsa Mulungu chifukwa chake moyo unali wovuta chotero, ngati mavutowo anali chilango cha Mulungu. Anakumana ndi Mboni za Yehova, amene anam’sonyeza m’Baibulo chifukwa chimene moyo ulili wokhuta ndi mavuto okhaoka lerolino.—Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5.
Pamene Gabriel anapitiriza kuphunzira zowonjezeka m’Baibulo, anazindikiranso mowonjezeka kuti ilo n’la choonadi. “Ndinaphunzira kuti tingathe kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Komanso zimenezo n’zimene ndinkalakalaka ndi kale ndili mwana wamng’ono.” Baibulo linam’tonthoza Gabriel potonthoza mtima wake womwe unali kuvutika panthaŵi imeneyo. Mabala ake aakulu a mumtima anayamba kuchira. Chotero podzafika nthaŵi imene anakumana ndi Daniel, yemwe kale anali mdani wake, Gabriel analibenso chidani chilichonse mumtima. Koma n’chiyani chinapangitsa Daniel kupita ku Ulaya?
“Ngati Mulikodi, Chonde N’thandizeni!”
Daniel analeredwa monga m’Katolika ndipo pamene anali ndi zaka 18 zakubadwa anaitanidwa kuusilikali. Iye anatumizidwa kunkhondo imodzimodziyo imene Gabriel anatumizidwako, koma tsono kumbali yomenyana ndi mbali ya Gabriel. Pamene Daniel anali kuyenda m’kasinja cha komwe kunkamenyedwera nkhondoyo, bomba linaphulitsa kasinjayo. Anzake anaphedwa, ndipo iyeyo anavulala ndipo anagwidwa nakhala wandende. Anakhala miyezi yambiri m’chipatala ndi mumsasa wina asanam’thamangitsire ku dziko losakhudzidwa ndi nkhondoyi. Kwayekhayekhako, wopandanso kena kalikonse, anafuna kudzipha. Daniel anapemphera kwa Mulungu nati: “Ngati mulikodi, chonde n’thandizeni!” M’maŵa mwake, Mboni za Yehova zinam’fikira ndipo zinam’yankha mafunso ake ambiri. Pomalizira pake, anapita ku Ulaya monga wothaŵa kwawo. Kumenekonso Daniel anapitiriza kucheza ndi Mboni ndi kuphunzira Baibulo. Zimene anaphunzira zinachepetsa nkhaŵa zake ndi kuŵaŵidwa mtima.
Gabriel ndi Daniel tsopano ndi mabwenzi enieni, ogwirizana mu ubale wauzimu monga Mboni zobatizidwa za Yehova. “Kukonda kwanga Yehova komanso kulidziŵa bwino Baibulo zandithandiza kuona zinthu monga momwe iye amazionera. Daniel salinso mdani wanga. Zaka zapitazo ndikanafuna kumupha. Baibulo landiphunzitsa zosiyana kwambiri ndi zimenezo—kuti ndizikhala wofunitsitsa kum’fera,” akutero Gabriel.
“Ndinaona anthu a m’zipembedzo zosiyana ndi a mitundu yosiyana akuphana,” akutero Daniel. “Panalinso ena a chipembedzo chofanana kumbali zomenyanazo ndipo anali kuphana. Nditaona zimenezi, ndinaimba mlandu Mulungu. Tsopano ndikudziŵa kuti Satana ndiye
wochititsa nkhondo zonse. Ineyo ndi Gabriel tili ndi chikhulupiriro chimodzi tsopano. Sitidzamenyananso!”“Mawu a Mulungu Ali Amoyo, ndi Amphamvu”
N’chifukwa chiyani Abraham, Robert, Gabriel, ndi Daniel anasinthiratu chotero? Anatha bwanji kufafaniza udani wozikika kwambiri ndi chisoni m’mitima mwawo?
Aliyense wa amunaŵa anaŵerenga Baibulo, kusinkhasinkha, ndi kuphunzira choonadi cha m’Baibulomo, limene lili ‘lamoyo ndi lamphamvu.’ (Ahebri 4:12, NW) Mlembi wa Baibulo ndiye Mlengi wa anthu, amene amadziŵa kusonkhezera mtima wa munthu yemwe akufuna kumvetsera ndi kuphunzira kuti ukhale wabwino. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” Munthu amene akuŵerenga Baibulo akalilola kuti lim’tsogolere, amakhala ndi zinthu zatsopano zimene amatsogoza ndipo amakhalanso ndi miyezo yatsopano. Amayamba kuphunzira mmene Yehova amaonera zinthu. Zimenezi zimadzetsa mapindu ochuluka, kuphatikizapo kuchiritsa mabala a nkhondo.—2 Timoteo 3:16.
Mawu a Mulungu amalongosola kuti palibe mtundu, fuko, kapena mfunda wabwino kwambiri kapena woipa kwambiri kuposa wina. “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” M’kupita kwa nthaŵi, woŵerenga amene amalabadira zimenezi amathandizidwa kuthetsa chidani chake pa fuko kapena mtundu wina.—Machitidwe 10:34, 35.
Maulosi a m’Baibulo amasonyeza kuti posachedwa pompa Mulungu adzachotsapo dongosolo lilipoli la ulamuliro wa anthu n’kuikapo Ufumu wake Waumesiya. Pogwiritsa ntchito bomali, Mulungu “aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” Magulu amene amachirikiza nkhondo ndi kuchemerera anthu kuloŵa m’nkhondozo adzachotsedwapo. Amene anafa chifukwa cha nkhondo adzaukitsidwa ndi kupatsidwa mpata woti akhale padziko lapansi la paradaiso. Palibe amene adzathaŵa chifukwa cha munthu wankhanza kapena wopondereza.—Salmo 46:9; Danieli 2:44; Machitidwe 24:15.
Ponena za anthu amene adzakhalako panthaŵiyo, Baibulo limati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo. . . . Iwo sadzagwira ntchito mwachabe, pena kubalira tsoka.” Kupwetekedwa kapena kuvulala kwamtundu wina uliwonse kudzachiritsidwa. Kukhulupirira chiyembekezo choterechi pang’onopang’ono kumachotsa chisoni ndi kulira mumtima wa munthu.—Yesaya 65:21-23.
Baibulo lilidi mankhwala amphamvu a mtima. Ziphunzitso zake zayamba kale kuchiritsa mabala a nkhondo. Amene kale anali adani akuyanjanitsidwa mu ubale wogwirizana wapadziko lonse. Kuchiritsidwa kumeneku kudzapitirizabe m’dongosolo latsopano la Mulungu mpaka sikudzakhalanso kudana ndi kuŵaŵidwa mtima, kulira ndiponso chisoni m’mitima ya anthu. Mlengi akulonjeza kuti “zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.”—Yesaya 65:17.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Mayina ena m’nkhaniyi asinthidwa.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“Baibulo linandiphunzitsa kuti zaka zonsezo zimene ndinathera m’nkhondo zinapita pachabe”
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Baibulo lili ndi mphamvu yosonkhezera mitima ya anthu amene kale anali adani
[Mawu Otsindika patsamba 6]
M’kupita kwa nthaŵi udani ndi kuŵaŵidwa mtima zinaloŵedwa m’malo ndi kukhulupirirana ndi kukondana
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Woŵerenga akangolola Baibulo kum’tsogolera, amakhala ndi zinthu zatsopano zimene amatsogoza ndipo amakhalanso ndi miyezo yatsopano
[Chithunzi patsamba 7]
Amene kale anali adani akuyanjanitsidwa mu ubale wapadziko lonse tsopano
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Msasa wa othaŵa kwawo: CHITHUNZI CHA UN 186811/J. Isaac