Kulani M’chikondi
Kulani M’chikondi
“Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” —MATEYU 22:37.
1. (a) Kodi zina mwa zinthu zomwe Mkristu amakulitsa ndi ziti? (b) Kodi mkhalidwe wofunika kwambiri wachikristu ndi uti, nanga n’chifukwa chiyani?
MKRISTU amakulitsa zinthu zambiri n’cholinga chakuti akhale mtumiki wogwira mtima. Buku la Miyambo limasonyeza kufunika kwa chidziŵitso, kuzindikira, ndi nzeru. (Miyambo 2:1-10) Mtumwi Paulo anafotokoza za kufunika kwa chikhulupiriro cholimba ndi chiyembekezo champhamvu. (Aroma 1:16, 17; Akolose 1:5; Ahebri 10:39) Kupirira ndi kudziletsa n’zofunikanso kwambiri. (Machitidwe 24:25; Ahebri 10:36) Komabe, pali chinthu china chimene, ngati chikusoŵa, mikhalidwe ina yonseyo imasokonezeka ndipo ingaoneke kukhala yopanda phindu. Chinthu chimenecho ndicho chikondi.—1 Akorinto 13:1-3, 13.
2. Kodi Yesu anasonyeza motani kufunika kwa chikondi, ndipo zimenezi zimabutsa mafunso otani?
2 Yesu anasonyeza kuti chikondi n’chofunika pamene anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Popeza kuti chikondi n’chomwe chimam’dziŵikitsa Mkristu weniweni, tingafunse mafunso monga akuti, Kodi chikondi n’chiyani? N’chifukwa chiyani chili chofunika kwambiri mwakuti Yesu n’kufikira ponena kuti, kuposa china chilichonse, ndicho chimadziŵikitsa ophunzira ake? Kodi chikondi tingachikulitse motani? Kodi ndani yemwe tiyenera kum’sonyeza chikondi? Tiyeni tipende mafunso ameneŵa.
Kodi Chikondi N’chiyani?
3. Kodi chikondi tingachifotokoze motani, nanga n’chifukwa chiyani chimakhudza malingaliro ndi mtima womwe?
3 Tanthauzo limodzi la chikondi n’lakuti ndicho ‘malingaliro aubwenzi wolimba ochokera pansi pamtima, kusangalatsidwa kwambiri ndi munthu wina.’ Ndi mkhalidwe womwe umasonkhezera anthu kuchitira ena zabwino, nthaŵi zina umafuna kudzimana kwambiri. Chikondi, monga momwe Baibulo lachifotokozera, chimakhudza malingaliro ndi mtima womwe. Malingaliro, kapena kuti nzeru, zimachita mbali yofunika chifukwa chakuti munthu wosonyeza chikondi, amachita zimenezi mozindikira, akumadziŵa kuti iyeyo limodzi ndi anthu ena omwe akuwasonyeza chikondiwo, onse ali ndi zofooka komanso mikhalidwe yochititsa chidwi. Nzeru zimakhudzidwa mowonjezeka chifukwa chakuti Mkristu angakonde ena—mwinamwake, nthaŵi zina osati mwachibadwa chake—chifukwa chakuti mwa kuŵerenga Baibulo wadziŵa kuti Mulungu akufuna kuti achite zimenezo. (Mateyu 5:44; 1 Akorinto 16:14) Komabe, kwenikweni chikondi chimachokera mumtima. Chikondi chopanda mpeni kumphasa monga momwe Baibulo lachivumbulira si nzeru wamba. Chimaphatikizapo kuona mtima kwenikweni ndi kudzipereka ndi mtima wonse.—1 Petro 1:22.
4. Kodi chikondi chili chomangirira champhamvu m’njira iti?
4 Anthu a mtima wodzikonda nthaŵi zambiri n’zosatheka kuti apange ubwenzi weniweni wachikondi chifukwa chakuti munthu wachikondi n’ngwokonzeka kuika zofuna za ena patsogolo pa zake. (Afilipi 2:2-4) Mawu a Yesu akuti “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira” n’ngoona makamaka ngati kuperekako kwasonkhezeredwa ndi chikondi. (Machitidwe 20:35) Chikondi n’chomangira champhamvu. (Akolose 3:14) Kaŵirikaŵiri chimaphatikizapo ubwenzi, koma zomangira za chikondi n’zolimba kuposa zomangira za ubwenzi. Ubwenzi wapakati pa mwamuna ndi mkazi wake nthaŵi zina amautchanso chikondi; komabe, chikondi chomwe Baibulo limatilimbikitsa kukulitsa n’chokhalitsa kuposa kungokopeka chabe mwakuthupi. Ngati okwatirana amakondanadi, amapitirizabe kukhalira limodzi ngakhale ngati kupereka mangaŵa am’banja sikungatheke chifukwa cha kufooka kwa thupi kodza ndi ukalamba kapena chifukwa chakuti mmodzi wa iwo sangathenso kutero.
Chikondi—Mkhalidwe Wofunika Kwambiri
5. N’chifukwa chiyani chikondi chili mkhalidwe wofunika kwa Akristu?
5 N’chifukwa chiyani chikondi chili mkhalidwe wofunika kwa Mkristu? Choyamba, chifukwa chakuti Yesu analamulira otsatira ake kuti azikondana wina ndi mnzake. Iye anati: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Zinthu izi ndilamulira inu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (Yohane 15:14, 17) Chachiŵiri, chifukwa chakuti Yehova ndiye chikondi, chotero monga olambira ake tiyenera kumutsanzira. (Aefeso 5:1; 1 Yohane 4:16) Baibulo limati kumudziŵa Yehova ndi Yesu ndiwo moyo wosatha. Tinganene bwanji kuti timam’dziŵa Mulungu ngati sitim’tsanzira? Mtumwi Yohane anati: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.”—1 Yohane 4:8.
6. Kodi chikondi chingalinganize motani zochitika zosiyanasiyana za m’moyo wathu?
6 Chikondi n’chofunika pachifukwa china chachitatu: Chimatithandiza kuika pamlingo woyenera zochitika zosiyanasiyana za m’moyo wathu ndipo chimawonjezera cholinga chabwino ku zomwe timachita. Mwachitsanzo, n’chofunika kwambiri kuti tipitirizebe kuloŵetsa chidziŵitso cha Mawu a Mulungu m’malingaliro mwathu mosalekeza. Kwa Mkristu, chidziŵitso choterocho chili ngati chakudya. Chimam’thandiza kufika pauchikulire ndi kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Salmo 119:105; Mateyu 4:4; 2 Timoteo 3:15, 16) Komabe, Paulo anachenjeza kuti: “Chidziŵitso chitukumula, koma chikondi chimangirira.” (1 Akorinto 8:1) Ayi, palibe cholakwika chilichonse ndi chidziŵitso cholondola. Vuto lili ndi ifeyo—tili ndi zizoloŵezi zauchimo. (Genesis 8:21) Ngati mphamvu yolinganiza zinthu ya chikondi ikusoŵa, chidziŵitso chingam’chititse munthu kudzitukumula, kudziona ngati kuti iyeyo n’ngwabwino kuposa ena. Zimenezo sizingachitike ngati kwenikweni chikondi chikum’sonkhezera. “Chikondi . . . sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” (1 Akorinto 13:4) Mkristu wosonkhezereka ndi chikondi sachita zinthu monyada ngakhale atapeza chidziŵitso chakuya. Chikondi chimam’chititsa kukhala wodzichepetsa ndi kumuteteza kuti asadzipangire dzina.—Salmo 138:6; Yakobo 4:6.
7, 8. Kodi chikondi chimatithandiza motani kusumika maganizo athu pa zinthu zofunika kwambiri?
7 Paulo analembera Afilipi kuti: “Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziŵitso, ndi kuzindikira konse; kuti mukayese inu zinthu zosiyana [“kuti mutsimikizire zinthu zofunika kwambiri,” NW].” (Afilipi 1:9, 10) Chikondi chachikristu chidzatithandiza kutsatira chilimbikitso chimenechi kuti titsimikizire zinthu zofunika kwambiri. Kungopereka chitsanzo, lingalirani mawu a Paulo kwa Timoteo akuti: “Ngati munthu akhumba udindo wa woyang’anira, aifuna ntchito yabwino.” (1 Timoteo 3:1) M’chaka chautumiki cha 2000, chiŵerengero cha mipingo padziko lonse chinawonjezeka ndi 1,502, n’kufika pa chiwonkhetso chatsopano cha 91,487. Pachifukwa chimenecho, akulu ochuluka akufunika kwambiri, ndipo omwe akukalamira udindo tikuwayamikira.
8 Komabe, awo amene akukalamira udindo wa woyang’anira adzakhalabe ndi kaonedwe kabwino ngati adzakumbukira cholinga cha udindo umenewo. Kungokhala ndi ulamuliro kapena kutchuka sindiko chinthu chofunika. Akulu omwe amakondweretsa Yehova amasonkhezereka ndi chikondi chawo kwa Mulungu ndi kwa abale awo. Sakufuna kutchuka kapena kusonyeza mphamvu zaulamuliro. Mtumwi Petro, atatsiriza kulangiza akulu ampingo kuti asunge khalidwe labwino, anagogomeza kufunika kwa “kudzichepetsa.” Analangiza onse mumpingo kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.” (1 Petro 5:1-6) Aliyense amene akukalamira adzachita bwino kulingalira chitsanzo cha akulu osaŵerengeka padziko lonse lapansi omwe ndi akhama pantchito, odzichepetsa, ndipo pa chifukwa chimenecho ali dalitso ku mipingo yawo.—Ahebri 13:7.
Zolinga Zabwino Zimatithandiza Kupirira
9. N’chifukwa chiyani Akristu amakumbukira madalitso a Yehova olonjezedwawo?
9 Kufunika kosonkhezereka ndi chikondi kumaoneka m’njira inanso. Kwa omwe atsata kudzipereka kwaumulungu chifukwa cha chikondi, Baibulo likulonjeza madalitso ochuluka tsopano lino ndi madalitso osaneneka amtengo wapatali m’tsogolo. (1 Timoteo 4:8) Mkristu yemwe amakhulupirira kwambiri malonjezo ameneŵa ndipo ndi wotsimikizira kuti Yehova “ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye” amathandizidwa kukhala wolimba m’chikhulupiriro. (Ahebri 11:6) Ambiri a ife tikufunitsitsa malonjezo a Mulungu atakwaniritsidwa ndipo timalingalira ngati mtumwi Yohane yemwe anati: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.” (Chivumbulutso 22:20) Inde, ngati ndife okhulupirika, kusinkhasinkha za madalitso omwe ayandikirawo kumatilimbitsa kuti tipirire, monga momwe kukumbukira “chimwemwe choikidwacho pamaso pake” kunathandizira Yesu kupirira.—Ahebri 12:1, 2.
10, 11. Kodi kusonkhezereka ndi chikondi kumatithandiza motani kupirira?
10 Bwanji ngati chisonkhezero chathu chimodzi chokha chotumikira Yehova ndicho chikhumbo chathu chodzakhala m’dziko lapansi latsopano? Pamenepo tingataye mtima mosavuta kapena kunyinyirika ngati zinthu zikupitiriza kuvuta kapena ngati sizikuchitika monga momwe timafunira kapena m’nthaŵi yomwe timayembekezera. Tingakhale pangozi yaikulu yobwerera m’mbuyo. (Ahebri 2:1; 3:12) Paulo ananena za mnzake woyamba wotchedwa Dema kuti anam’thaŵa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti “a[n]akonda dziko lino lapansi.” (2 Timoteo 4:10) Aliyense amene akutumikira pazifukwa zadyera ali pangozi yochita zomwezo. Angakopeke ndi mwayi womwe dziko lingawapatse mwamsanga ndi kuyamba kuzengereza kudzimana lerolino poyembekezera madalitso alinkudza.
11 Ngakhale kuti n’koyenera komanso n’kwachibadwa kukhala ndi chikhumbo chodzalandira madalitso am’tsogolo ndi mpumulo wa ziyeso woyembekezeredwawo, chikondi chimamangirira kuzindikira kwathu ponena za chomwe tiyenera kuchiika patsogolo m’moyo wathu. N’chifuno cha Yehova chomwe chili chofunika kwambiri, osati chathu. (Luka 22:41, 42) Inde, chikondi chimatimangirira. Chimatisonkhezera kuyembekezera pa Mulungu moleza mtima, kukhutira ndi madalitso alionse omwe akutipatsa ndi kutsimikizira kuti m’nthaŵi yake yoikika tidzalandira chilichonse chimene walonjeza—ndi zina zambiri. (Salmo 145:16; 2 Akorinto 12:8, 9) Padakali pano, chikondi chimatithandiza kupitirizabe kutumikira mopanda dyera chifukwa chakuti “chikondi . . . sichitsata za mwini yekha.”—1 Akorinto 13:4, 5.
Kodi Akristu Ayenera Kukonda Yani?
12. Malinga ndi zomwe Yesu ananena, kodi tiyenera kukonda yani?
12 Yesu anapereka lamulo losasankha ponena za yemwe tiyenera kum’konda pamene anagwira mawu ziganizo ziŵiri kuchokera m’Chilamulo cha Mose. Iye anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako Mateyu 22:37-39.
wonse, ndi nzeru zako zonse,” ndi kuti, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”—13. Kodi tingaphunzire motani kukonda Yehova, ngakhale kuti sitingathe kumuona?
13 Kuchokera m’mawu a Yesuwo, n’zoonekeratu kuti choyambirira tiyenera kukonda Yehova. Komabe, sitibadwa okhoza kumukonda kwambiri Yehova. N’chinthu chomwe tiyenera kuchikulitsa. Titamva za iye kwa nthaŵi yoyamba, tinakopeka naye chifukwa cha zomwe tinamvazo. Pang’ono ndi pang’ono, tinaphunzira momwe analengera dziko kuti anthu akhalemo. (Genesis 2:5-23) Tinaphunzira momwe wakhala akuchitira ndi anthu, sanatinyalanyaze pamene tchimo linaloŵa m’banja la anthu, koma anachitapo kanthu kuti atiwombole. (Genesis 3:1-5, 15) Omwe anali okhulupirika anawachitira chifundo, ndipo pambuyo pake anapereka Mwana wake wobadwa yekha kuti machimo athu athe kukhululukidwa. (Yohane 3:16, 36) Chidziŵitso chowonjezeka chimenechi chinakulitsa chiyamiko chathu kwa Yehova. (Yesaya 25:1) Mfumu Davide inati inakonda Yehova chifukwa cha chisamaliro Chake chachikondi. (Salmo 116:1-9) Lerolino, Yehova amatisamalira, kutitsogolera, kutilimbitsa, ndi kutilimbikitsa. Tikamaphunzira zambiri za iye, m’pamene chikondi chathu chimazama.—Salmo 31:23; Zefaniya 3:17; Aroma 8:28.
Kodi Chikondi Chathu Tingachisonyeze Motani?
14. Kodi tingasonyeze m’njira iti kuti Mulungu timam’kondadi moona mtima?
14 Inde, ambiri padziko lonse lapansi amati amamukonda Mulungu, koma zochita zawo zimasemphana ndi zimenezo. Kodi tingadziŵe bwanji kuti timam’kondadi Yehova? Tingalankhule naye m’pemphero ndi kumuuza malingaliro athu. Ndipo tingachite zinthu mosonyeza chikondi chathucho. Mtumwi Yohane anati: “Iye amene akasunga mawu [a Mulungu], mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. Mmenemo tizindikira kuti tili mwa Iye.” (1 Yohane 2:5; 5:3) Mwazina, Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizisonkhana pamodzi ndi kukhala ndi moyo waukhondo, ndi wa makhalidwe abwino. Timapeŵa chinyengo, timalankhula zoona, ndi kusunga malingaliro athu ali oyera. (2 Akorinto 7:1; Aefeso 4:15; 1 Timoteo 1:5; Ahebri 10:23-25) Timasonyeza chikondi mwakupereka thandizo kwa osoŵa. (1 Yohane 3:17, 18) Ndipotu sitizengereza kuuza ena za Yehova. Zimenezi zikuphatikizamo kutenga nawo mbali m’ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse. (Mateyu 24:14; Aroma 10:10) Kumvera Mawu a Mulungu m’zinthu ngati zimenezo ndi umboni wokwanira wakuti Yehova timam’kondadi moona mtima.
15, 16. Kodi chikondi cha pa Yehova chinakhudza motani miyoyo yambiri chaka chatha?
15 Kukonda Yehova kumathandiza anthu kusankha chabwino. Chaka chathachi, chikondi choterocho chinasonkhezera anthu 288,907 kupatulira miyoyo yawo kwa iye ndi kusonyeza chosankha chimenecho mwa ubatizo wam’madzi. (Mateyu 28:19, 20) Kudzipatulira kwawo kunali kwatanthauzo. Kunasonyeza kusintha kwa miyoyo yawo. Mwachitsanzo, Gazmend anali mmodzi wa akatswiri otchuka a maseŵero a basketball ku Albania. Kwa zaka zingapo, iye ndi mkazi wake anakhala akuphunzira Baibulo ngakhale kuti panali zopinga, iwo pambuyo pake anakwaniritsa ziyeneretso ndi kukhala olengeza Ufumu. Chaka chathachi, Gazmend anabatizidwa, anali mmodzi wa anthu 366 obatizidwa mu Albania m’chaka cha utumiki cha 2000. Nyuzipepala ina inalemba nkhani ya iyeyu ndipo inati: “Moyo wake uli ndi chifuno, ndipo pa chifukwa chimenechi, iye ndi banja lake ali m’masiku osangalatsa kwambiri a moyo wawo. Kwa iyeyu, kuona momwe moyo ungam’pindulitsire si chinthu chofunikanso tsopano, m’malo mwake, zomwe angapereke kuti athandize anthu ena ndizo zofunika.”
16 Mofananamo, mlongo wina wobatizidwa chatsopano yemwe amagwira ntchito pa kampani yogulitsa mafuta ku Guam anapatsidwa mwayi woyesa chikhulupiriro kwambiri. Atagwira ntchito m’maudindo ang’onoang’ono kwa zaka zingapo, kenako anapatsidwa mwayi wokhala mkazi woyamba kulandira udindo wa wachiŵiri kwa pulezidenti m’mbiri ya kampaniyo. Komabe, tsopano anali atapatulira moyo wake kwa Yehova. Choncho atakambirana nkhaniyo ndi mwamuna wake, mlongo wachatsopano ameneyu anakana kulandira udindowo ndipo mmalo mwake analinganiza zopeza ntchito ya maola ochepa n’cholinga chofuna kupita patsogolo ndikuti afikire pakukhala mtumiki wanthaŵi zonse, mpainiya. Kukonda Yehova kunam’sonkhezera kufunitsitsa kumutumikira monga mpainiya mmalo molondola chuma cha dziko lino. Kwenikweni, chikondi choterechi chinasonkhezera anthu 805,205 padziko lonse kuchita nawo mbali zosiyanasiyana za utumiki wa upainiya m’chaka cha utumiki cha 2000. Apainiya amenewo anasonyezatu chikondi ndi chikhulupiriro chawo chamtengo wapatali!
Kusonkhezereka Kukonda Yesu
17. Ndi chitsanzo chabwino chotani cha chikondi chomwe timaona mwa Yesu?
17 Yesu ndi chitsanzo chapadera cha amene anasonkhezereka ndi chikondi. Asanadzakhale munthu, anakonda Atate wake ndiponso anakonda anthu. Pokhala nzeru iyeyo, anati: “Ndinali pambali [pa Yehova] ngati mmisiri; ndinam’sekeretsa tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse; ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.” (Miyambo 8:30, 31) Chikondi cha Yesu chinam’sonkhezera kusiya malo ake okhala akumwamba ndi kudzabadwa monga khanda losakhoza kudziteteza. Ofatsa ndi odzichepetsa anachita nawo moleza mtima ndi mwachifundo ndipo anazunzidwa m’manja mwa adani a Yehova. Pamapeto pake, anafera anthu onse pamtengo wozunzirapo. (Yohane 3:35; 14:30, 31; 15:12, 13; Afilipi 2:5-11) Chitsanzotu chabwino kwabasi cha kusonkhezereka kwabwino!
18. (a) Kodi timakulitsa motani chikondi chathu pa Yesu? (b) Timasonyeza m’njira ziti kuti Yesu timam’konda?
18 Awo amene ali ndi mtima wabwino akaŵerenga nkhani za moyo wa Yesu m’Mauthenga Abwino 1 Petro 1:8) Chikondi chathu chimaonekera pamene tikhulupirira iye ndi kutsanzira moyo wake wodzimanawo. (1 Akorinto 11:1; 1 Atesalonika 1:6; 1 Petro 2:21-25) Pa April 19, 2000, anthu 14,872,086 anakumbutsidwa zifukwa zomwe Yesu timam’kondera pamene anafika pa Chikumbutso cha imfa yake chomwe chimachitika chaka chilichonse. Chinalitu chiŵerengero chachikulu chimenecho! Ndipotu n’kolimbikitsa kudziŵa kuti ochuluka chotere akufuna kudzalandira chipulumutso kudzera m’nsembe ya Yesu! Kunena zoona, timamangiririka ndi chikondi cha Yehova ndi cha Yesu pa ife komanso ndi chikondi chathu pa iwo.
ndi kulingalira za kuchuluka kwa madalitso omwe njira yake yokhulupirikayo yawadzetsera, zimenezi zimachititsa chikondi chawo chakuya kukula mumtima mwawo. Ife lerolino tili ngati anthu omwe Petro ankawauza kuti: “Mungakhale simunamuona [Yesu] mum’konda.” (19. Ndi mafunso ati onena za chikondi omwe tidzakambirane m’nkhani yotsatira?
19 Yesu anati tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, nzeru zathu zonse, ndi mphamvu zathu zonse. Koma ananenanso kuti tizikonda anansi athu monga momwe timadzikondera ife eni. (Marko 12:29-31) Kodi anansi athuwo akuphatikizapo ndani? Nanga kukonda mnansi wathu kumatithandiza motani kukhalabe olinganizika bwino ndi a zolinga zoyenera? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani chikondi uli mkhalidwe wofunika?
• Kodi tingaphunzire motani kukonda Yehova?
• Kodi khalidwe lathu limasonyeza motani kuti timakonda Yehova?
• Kodi timasonyeza motani kuti Yesu timam’konda?
[Mafunso]
[Zithunzi pamasamba 10, 11]
Chikondi chimatithandiza kudikira mpumulo moleza mtima
[Chithunzi patsamba 12]
Nsembe yaikulu ya Yesu imatisonkhezera kum’konda