Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira ndi Moyo Wonse Mosasamala Kanthu za Mayesero

Kutumikira ndi Moyo Wonse Mosasamala Kanthu za Mayesero

Mbiri ya Moyo Wanga

Kutumikira ndi Moyo Wonse Mosasamala Kanthu za Mayesero

YOSIMBIDWA NDI RODOLFO LOZANO

Ndinabadwira ku Mexico, mu m’zinda wa Gómez Palacio, ku Durango State pa September 17, 1917. Panthaŵi imeneyo n’kuti kuukira boma kutafika pachimake ku Mexico. Ngakhale kuti kuukirako kunatha mu 1920, kwa zaka zina pambuyo pake, chisokonezo chinapitirirabe m’dera limene tinali kukhala zomwe zinapangitsa moyo kukhala wovuta kwambiri.

NTHAŴI ina, pamene amayi anamva kuti kudzakhala nkhondo pakati pa gulu loukira ndi asilikali a boma, anatenga ine ndi abale anga atatu ndi alongo anga aŵiri n’kutibisa m’nyumba kwa masiku angapo. Tinalibe chakudya chokwanira ndipo ndikukumbukira nditabisala kunsi kwa bedi pamodzi ndi mlongo wanga wamng’ono. Pambuyo pake, amayi anaganiza zotitengera ku United States kuti bambo akatipeze pambuyo pake.

Tinafika ku California mu 1926, kutangotsala pang’ono kuti dziko la United States likhale pa Umphaŵi Waukulu. Tinali kuyendayenda kulikonse kumene tikanatha kupeza ntchito, kumalo monga ku San Joaquin Valley, Santa Clara, Salinas, ndi King City. Tinaphunzira kugwira ntchito m’minda ndiponso kukolola mitundu yonse ya zipatso ndi ya zamasamba. Ngakhale kuti unyamata wanga unali nthaŵi ya ntchito yakalavula gaga, unalinso nthaŵi yosangalatsa kwambiri pamoyo wanga.

Kumva za Choonadi cha Baibulo

Mu March 1928, mmodzi wa Ophunzira Baibulo, monga mmene Mboni za Yehova zinkadziŵikira panthaŵiyo, anafika kwathu. Anali mwamuna wachikalambire, wolankhula Chisipanya dzina lake Esteban Rivera. Mutu wa kabuku komwe anatisiyira wakuti, “Where Are the Dead?” (Kodi Akufa Ali Kuti?) ndiponso nkhani zake, zinandichititsa chidwi. Ngakhale kuti ndinali wamng’ono, ndinalimbikira kuphunzira Baibulo ndiponso kuyanjana ndi Ophunzira Baibulo. Pambuyo pake, amayi anga ndi mlongo wanga Aurora anakhalanso akhama potamanda Yehova.

Cha pakati pa ma 1930, Nyumba ya Ufumu ya mpingo wachingelezi inamangidwa ku San Jose. Chifukwa chakuti anthu ambiri achisipanya anali kugwira ntchito m’mafamu a m’deralo, tinayamba kulalikira kwa iwo ndi kupangitsakonso Phunziro la Nsanja ya Olonda. Tinachita zimenezi mothandizidwa ndi Mboni za chisipanya zochokera ku San Francisco mtunda wa makilomita 80. Pambuyo pake, anthu okwanira 60 anayamba kusonkhana nafe pamisonkhano ya Chisipanya pa Nyumba ya Ufumu ya San Jose.

Pambuyo pake, pa February 28, 1940, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi pa msonkhano wa ku San Jose. M’chaka chotsatira ndinaikidwa kukhala mpainiya, mtumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Kenako, mu April 1943, ndinapemphedwa kusamukira ku Stockton, mtunda wa makilomita 130, kukakhazikitsa mpingo wachisipanya. Panthaŵi imeneyo ndinali kutumikira monga woyang’anira wotsogolera wa mpingo wachingelezi ku San Jose, ndipo ndinalinso kuyang’anira Mboni za chisipanya kumeneko. Pambuyo popeza anthu ena kuti asamalire maudindo ameneŵa ndinasamukira ku Stockton.

Kukhulupirika Kuyesedwa

Kuyambira m’ma 1940, ndinali kuitanidwa kaŵirikaŵiri ndi bungwe lokakamiza anthu kuloŵa usilikali, koma nthaŵi zonse anali kumvetsetsa malingaliro anga okana kuchita zinthu zotsutsana ndi chikumbumtima changa. Dziko la United States litangoloŵa m’nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse mu December 1941, kukakamizidwa ndi bungwelo kunakula. Mapeto ake, ndinamangidwa mu 1941. Pamene ndinali kudikira kuŵeruzidwa, ndinaikidwa m’chipinda chapansi limodzi ndi akaidi. Atadziŵa kuti ndinali wa Mboni za Yehova, ambiri mwa iwo ankandifunsa za mmene Mulungu adzawachitira malingana ndi milandu yawo.

Mboni za ku San Jose zinandilipirira belo kuti ndimasulidwe ndi kumakadikira tsiku la kuzenga mlandu. Loya wa ku Los Angeles yemwe anandiimira pankhani za ufulu wa nzika anavomereza kutero popanda malipiro. Woŵeruza anati andimasula pokhapokha nditasiya upainiya, kuti ndikaloŵe ntchito ina, ndi kumakaonekera kwa akuluakulu a boma mwezi uliwonse. Sindinavomereze chigamulo chimenecho, choncho ndinaŵeruzidwa kukakhala m’ndende pachilumba cha McNeil ku Washington State kwa zaka ziŵiri. Kumeneko, ndinagwiritsa ntchito nthaŵi yanga kuphunzira Baibulo kwambiri. Ndinaphunziranso kutaipa. Zaka ziŵiri zisanathe, ndinamasulidwa chifukwa chakuti ndinali ndi khalidwe labwino. Nthaŵi yomweyo ndinakonzekera kupitiriza utumiki waupainiya.

Ntchito Yowonjezereka

M’nyengo yozizira ya mu 1947, ine ndi mpainiya mzanga, tinapatsidwa ntchito yokalalikira kwa anthu achisipanya a ku Colorado City, ku Texas. Koma kumeneko kunali kozizira kwambiri moti tinachita kupita ku San Antonio kuti tikasangalaleko ndi kutentha. Koma tili kumeneko, kunagwa mvula kwambiri mwakuti inasokoneza ulaliki wathu wa khomo ndi khomo. Posapita nthaŵi, ndalama zinatithera. Tinali kudya masangweji a kabichi wamuŵisi ndi tiyi kwa masabata angapo. Mnzanga uja anabwerera kupita kwawo, koma ine ndinatsalabe. Pamene Mboni zachingelezi zinadziŵa za kuvutika kwanga, zinayamba kundithandiza.

M’nyengo yotsatira yachilimwe, ndinabwerera ku gawo langa ku Colorado City ndipo pambuyo pake, mpingo waung’ono wachisipanya unakhazikitsidwa. Kenako ndinasamukira ku Sweetwater ku Texas kumene ndinakathandiza kukhazikitsa mpingo winanso wachisipanya. Pamene ndinali ku Sweetwater, ndinalandira kalata yondiitanira ku kalasi ya nambala 15 ya umishonale ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower yophunzitsa Baibulo yomwe inali kudzayamba pa February 22, 1950. Pambuyo pa mwambo womaliza maphunzirowo womwe unachitikira pa msonkhano wamayiko pa Yankee Stadium ku New York City, ndinakhalabe pa likulu lapadziko lonse la Mboni za Yehova ku Brooklyn kwa miyezi itatu. Kumeneko, ndinaphunzitsidwa za ntchito yanga ku ofesi yanthambi ya ku Mexico.

Kugwira Ntchito ku Mexico

Ndinafika ku Mexico City pa October 20, 1950. Patangotha pafupifupi milungu iŵiri, ndinasankhidwa kukhala woyang’anira ofesi ya nthambiyo ndipo ndinagwira ntchito imeneyi kwa zaka zinayi ndi theka. Zomwe ndinakumana nazo mu utumiki waupainiya, ku ndende, ku Gileadi, ndiponso ku Brooklyn zinandithandiza kwambiri. N’tangofika kumene ku Mexico, mwamsanga ndinaona kuti kunali kofunika kukonza mkhalidwe wauzimu wa abale ndi alongo athu a ku Mexico. Chomwe chinali kufunika kwenikweni, ndicho kuwathandiza kuti akhale mogwirizana ndi miyezo ya makhalidwe apamwamba ya m’Mawu a Mulungu.

M’mayiko a ku Latin America, kuphatikizapo la Mexico, chinali chizoloŵezi kuti anthu aŵiri osakwatirana azikhalira limodzi popanda ukwati walamulo. Matchalitchi Achikristu, makamaka Tchalitchi cha Katolika, ankalola mchitidwe wotsutsana ndi Malemba umenewu kupitirira. (Ahebri 13:4) Choncho, ena anali ataloŵa m’mipingo ya Mboni za Yehova ngakhale kuti sanakwatirane mwalamulo. Choncho, kunakonzedwa kuti anthu oterowo alembetse ukwati wawo isanathe miyezi isanu ndi umodzi. Akanapanda kutero sakanakhalanso a Mboni za Yehova.

Kwa anthu ambiri kukonza zinthu m’miyoyo yawo kunali kosavuta. Anangofunikira kulembetsa ukwati wawo basi. Kwa ena zinali zovuta. Mwachitsanzo, ena anali atakwatirapo kaŵiri, ngakhalenso katatu, koma analibe makalata ovomereza kutha kwa maukwati oyambawo. Pamene maukwati a anthu a Yehova anakhala mogwirizana ndi ziphunzitso za m’Mawu a Mulungu, mipingo inasangalala ndi madalitso abwino auzimu.​—1 Akorinto 6:9-11.

M’masiku amenewo, anthu ambiri a ku Mexico sanali ophunzira kwenikweni. Ngakhale ndisanapiteko mu 1950, ofesi yanthambi inali itayamba kukhazikitsa makalasi ophunzitsa kulemba ndi kuŵerenga m’mipingo. Tsopano makalasi ameneŵa anali kukonzedwanso ndipo dongosolo lakuti alembetsedwe kuboma linali m’kati. Kuyambira pamene kaundula anayamba kulembedwa mu 1946, Mboni m’makalasi awo zaphunzitsa anthu oposa 143,000 kulemba ndi kuŵerenga ku Mexico!

Malamulo okhudza zipembedzo ku Mexico anali okhwima kwambiri. Koma m’zaka zingapo zapitazi zinthu zasintha kwambiri mbali imeneyi. Mu 1992, lamulo latsopano lokhudza nkhani za zipembedzo linakhazikitsidwa, choncho mu 1993, Mboni za Yehova ku Mexico zinalembetsedwa monga chipembedzo.

Kwa ine, kusintha kumeneku n’kosangalatsa kwambiri, n’zomwe kale ndinkaganiza kuti sizingatheke. Kwa zaka zambiri, ndinali kupita ku maofesi a boma koma kulabadira kwawo kunali kogwetsa ulesi. Komabe, n’zokondweretsa kuona mmene zinthu zakhalira kudzera mu Dipatimenti ya Zamalamulo pa ofesi yathu yanthambi ndipo tsopano timakumana ndi zododometsa zochepa pantchito yolalikira.

Kutumikira Limodzi ndi Mmishonale Mzanga

Pamene ndinafika ku Mexico, ndinapezako amishonale ena ambiri omwe anamaliza kale maphunziro awo a ku Gileadi. Mmodzi wa iwo anali Esther Vartanian, Mboni ya ku Armenia yomwe inayambira upainiya wake ku Vallejo, ku California, mu 1942. Tinakwatirana pa July 30, 1955, ndipo pambuyo pake tinapitirizabe ntchito yathu ku Mexico. Esther anapitirizabe ntchito yake ya umishonale mu Mexico City, ndipo tikukhala pa ofesi ya nthambi komwe ndikupitiriza kutumikira.

Esther anafika m’gawo lake loyambirira la umishonale ku Monterrey, Nuevo León ku Mexico mu 1947. Panthaŵi imeneyo ku Monterrey kunali mpingo umodzi wokha wokhala ndi Mboni 40, koma pofika mu 1950, pamene anasamutsidwira ku Mexico City, n’kuti kuli mipingo inayi. Pa ofesi yathu pafupi ndi Mexico City, pali anyamata aŵiri ochokera ku mabanja omwe Esther anaphunzira nawo Baibulo pamene anali kutumikira ku Monterrey.

Kumbuyoko mu 1950, mbali yaikulu ya gawo lolalikira la amishonale ku Mexico City linali mzindawo. Anayendayenda mu gawo lawolo maulendo apansi kapena pa mabasi omwe amakhala odzaza ndi anthu. Pamene ndinafika chakumapeto kwa 1950, kunali mipingo isanu ndi iŵiri. Tsopano yachuluka kufikira pafupifupi 1,600, yokhala ndi ofalitsa Ufumu oposa 90,000 mu mzinda wotchedwa Mexico City, ndipo chaka chatha, anthu oposa 250,000 anasonkhana pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu kumeneko! M’zaka zimenezi, ine ndi Esther, takhala ndi mwayi wotumikira m’mipingo yochuluka mwa imeneyi.

Nthaŵi zonse pamene tayambitsa phunziro la Baibulo, ine ndi Esther timayesetsa kukopa chidwi cha bambo wa banjalo kotero kuti banja lonselo liphatikizidwe. Choncho taona mabanja akuluakulu ambiri akuyamba kutumikira Yehova. Ndikhulupirira kuti chimodzi mwa zifukwa zomwe kulambira koona kwafalikira kwambiri ku Mexico n’chakuti banja lonse kaŵirikaŵiri limagwirizana pa kulambira koona.

Yehova Wadalitsa Ntchito

Kuyambira mu 1950, kupita patsogolo kwa ntchito ku Mexico kwakhala kochititsa chidwi, pa kuwonjezereka kwa anthu, ndiponso pa kayendetsedwe ka zinthu. Ndili wosangalala kwambiri kuona kuti ndathandizako pang’ono pa chiŵerengerochi, pogwira ntchito ndi anthu ochereza ndiponso ansangala ameneŵa.

Karl Klein, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi mkazi wake Margaret, anadzacheza nafe panthaŵi yomwe anali pa tchuti zaka zingapo zapitazo. Mbale Klein anafuna kuti adzionere yekha mmene ntchito yathu ikupitira patsogolo ku Mexico. Choncho iye ndi Margaret anabwera ku mpingo wa San Juan Tezontla, pafupi ndi Mexico City komwe tinali kusonkhana panthaŵiyo. Holo yathu inali yaing’ono mamitala 4.5 m’lifupi ndi mamitala 5.5 m’litali. Pamene tinafika, tinapezamo anthu pafupifupi 70 atafika kale, ndipo munalibiretu malo ngakhale oti munthu n’kuimirira. Akuluakulu anali atakhala pa mipando, achinyamata anali atakhala pa mabenchi ndipo ana anakhalira njerwa kapena kukhala pansi.

Mbale Klein anachita chidwi kwambiri kuona ana onse ali ndi mabaibulo awo m’manja, akusanthula Malemba kutsatira wokamba nkhani. Pambuyo pa nkhani yapoyera, Mbale Klein anafotokoza Mateyu 13:19-23 ndipo anati, ku Mexico kuli “nthaka yabwino” kwambiri yomwe Yesu ananena. Pakadali pano, ana asanu ndi aŵiri mwa ana omwe analipo tsiku limenelo, akugwira nawo ntchito yaikulu yowonjezera ofesi yathu yanthambi pafupi ndi Mexico City. Wina, akutumikira ku Beteli ndipo ena angapo ndi apainiya!

Pamene ndinafika kuno ku Mexico City, pa ofesi yathu panali anthu 11 okha. Tsopano pali athu 1,350 ogwira ntchito ndipo pafupifupi anthu 250 mwa ameneŵa akugwira ntchito yomanga nyumba za nthambi zatsopano. Ntchito imeneyi ikadzatha makamaka mu 2002, tidzatha kukhala ndi anthu ena 1,200 m’nyumba zathu zowonjezerazi. Tangoganizirani! Mu 1950, tinali ndi ofalitsa Ufumu osakwana 7,000 m’dziko lonse lino la Mexico, koma tsopano tili ndi opitirira 500,000. Mtima wanga umadzala ndi chimwemwe pamene ndikuona mmene Yehova wadalitsira khama la abale athu odzichepetsa a ku Mexico, amene akugwira ntchito molimbika kum’tamanda.

Kukumana Ndi Vuto Lalikulu

Limodzi mwa mavuto akulu omwe ndakumana nawo posachedwapa ndilo matenda. Kwa nthaŵi yaitali, ndinali munthu wathanzi. Koma mu November 1988, ndinadwala sitiroko yomwe inakhudza thanzi langa kwambiri. Ndikuthokoza Yehova chifukwa maseŵera olimbitsa thupi ndiponso mankhwala, andithandiza kuti ndikhaleko bwino, komabe ziwalo za thupi langa sizingathe kuchita monga mmene ndikufunira. Ndikupitirizabe kulandira chithandizo ndi mankhwala kuti ndipewe kupweteka kwambiri kwa mutu ndi mavuto ena.

Ngakhale kuti sindingathenso kuchita zochuluka monga mmene ndingafunire, ndine wokhutira podziŵa kuti ndathandiza anthu ambiri kuphunzira zolinga za Yehova ndiponso kukhala atumiki ake odzipatulira. Ndimasangalalanso polankhula ndi abale ndi alongo achikristu ambiri pamene abwera kudzaona ofesi yathu; ndipo ndimaona kuti timalimbikitsana mwachikondi.

Kudziŵa kuti Yehova amathokoza kum’tumikira kwathu, ndiponso kuti zomwe tachita sizikhala zachabe, kwandilimbikitsa kwambiri. (1 Akorinto 15:58) Ngakhale ndine wolephera kuchita zambiri ndiponso wodwala, mawu a pa Akolose 3:23, 24 akhala apamtima: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi; podziŵa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphoto ya choloŵa; mutumikira Ambuye Kristu mwaukapolo.” Pogwiritsa ntchito mawu olimbikitsa ameneŵa, ndaphunzira kutumikira Yehova ndi mtima wonse mosamala kanthu za mayesero.

[Chithunzi patsamba 24]

Pamene ndinali mpainiya mu 1942

[Chithunzi patsamba 24]

Mkazi wanga anayamba ntchito yake ya umishonale ku Mexico mu 1947

[Chithunzi patsamba 24]

Limodzi ndi Esther lero

[Zithunzi patsamba 26]

Pamwamba kumanzere: Ine patsogolopo ndi banja la Beteli ku Mexico mu 1952

Pamwamba: Anthu oposa 109,000 anasonkhana pa msonkhano wachigawo m’bwalo ili lazamaseŵero mu mzinda wa Mexico City mu 1999

Pansi kumanzere: Nyumba zatsopano za ofesi yathu yanthambi zomwe zatsala pang’ono kumalizidwa