Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabala a Nkhondo

Mabala a Nkhondo

Mabala a Nkhondo

“PANKHONDO palibe amene amapambana,” anatero winawake yemwe kale anali msilikali m’nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse. “Nonse mumaluza.” Ambiri angavomerezane naye. Mfupo ya nkhondo n’njoopsa; ogonjetsa komanso ogonjetsedwa amavutikira limodzi ndi zotsatira zake zoŵaŵa. Ngakhale pambuyo poti kumenyanako kwalekeka, anthu mamiliyoni ambiri amapitiriza kuvutika ndi mabala ochititsa mantha a nkhondo.

Mabala otani? Nkhondo ingasakaze mtundu, kusiya ana ndi akazi ambiri ali amasiye. Opulumuka nkhondo ochuluka amakhala ndi mabala enieni ochititsa chisoni, pamodzinso ndi zipsera zosiyidwa mumtima. Anthu mamiliyoni ambiri amaluza katundu wawo yense kapena amakakamizika kuthaŵira kumalo achilendo. Kodi tingayerekeze chidani chimene anthu opulumuka nkhondozo ayenera kuti amakhala nacho mumtima kuwonjezera pa chisoni chawo?

Zilonda Zotukusira

Mabala amene anthu amakhala nawo m’mitima yawo amamka natukusira patapita nthaŵi yaitali pambuyo pa kutha kwa nkhondoyo, mfuti zitasiya kumveka, asilikali atabwerera kwawo. Mibadwo yotsatira ingakhale paudani waukulu m’mitima mwawo. Mwa njira imeneyi mabala a nkhondo imodzi angakhale maziko oyambitsa nkhondo inanso.

Mwachitsanzo, Pangano la Versailles, lomwe linasainidwa mu 1919 pothetsa nkhondo yoyamba ya padziko lonse mwalamulo, linaikira dziko la Germany malamulo ena amene nzika za dzikolo zinawaona kukhala okhwimitsa zinthu ndi owakhaulitsa. Malinga n’kunena kwa buku lamaumboni la The Encyclopædia Britannica, mfundo za m’panganolo “zinapangitsa Ajeremani kunyansidwa nalo ndipo zinawonjezera chilakolako chawo chofuna kubwezera.” Patapita zaka zingapo, “kuipidwa ndi pangano lamtenderero kunakhala maziko a Hitler” ndipo ndiwo chimodzi mwa zinthu zimene zinayambitsa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inayambira ku Poland ndipo inafikanso kumayiko a ku Balkan. Mabala amene mafuko akumeneko anapwetekana nawo m’ma 1940 anatsegulira njira ya nkhondo ya m’mayiko a Balkan m’ma 1990. “Udani woyambitsa kupwetekana ndi kubwezerana wakhala vuto losatha lomwe lafikanso m’nthaŵi yathu ino,” inatero nyuzipepala ya Die Zeit pothirira ndemanga.

Kuti anthu akhale pamtendere, ndithudi mabala a nkhondo ayenera kuchiritsidwa. Kodi zimenezo zingatheke bwanji? Choyenera kuchita n’chiyani kuti udani ndi chisoni zifafanizike? Ndani angachiritse mabala a nkhondo?

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

CHIKUTO: Fatmir Boshnjaku

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Chithunzi cha U.S. Coast Guard; CHITHUNZI CHA UN 158297/​J. Isaac