Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akuchita Mawu a Mulungu Amapeza Chimwemwe

Akuchita Mawu a Mulungu Amapeza Chimwemwe

Akuchita Mawu a Mulungu Amapeza Chimwemwe

“Timaona msonkhano uno monga chinthu chinanso chopatsidwa ndi Yehova, kutikonzekeretsa ntchito yowonjezereka ya Ufumu,” anatero wokamba nkhani wina kumayambiriro kwa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wamutu wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu.” Iye anapitiriza kuti: “Takonzekera kulangizidwa za moyo wabanja wachimwemwe, kulimbikitsidwa kumamatira kotheratu ku gulu la Yehova, kusonkhezeredwa kukhalabe achangu muutumiki wa Ufumu, ndi kukumbutsidwa kufunika kwa kukhalabe odikira.”

KUYAMBIRA kumapeto kwa May 2000, akuchita mawu a Mulungu miyandamiyanda pamodzi ndi anzawo, anakhamukira m’malo zikwi zambiri padziko lonse kuti akalandire maphunziro ofunika kwambiri a m’Baibulo. Kodi anaphunzira zotani pamsonkhano wamasiku atatuwo?

Tsiku Loyamba​—Kusaiŵala Zochita za Mulungu

M’nkhani yotsegulira, tcheyamani anapempha omvetsera kusangalala ndi madalitso ochokera m’kulambira Yehova mogwirizana pamsonkhanowo. Onse amene analipo anawatsimikizira kuti chikhulupiriro chawo chiwonjezeka ndi kuti unansi wawo ndi Yehova ulimbitsidwa.

“Mulungu wachimwemwe” amadziŵa zomwe ife timafuna kuti aliyense payekha akhale wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) N’chifukwa chake nkhani yakuti “Kuchita Chifuniro cha Mulungu Kumabweretsa Chimwemwe” inagogomeza kuti Mawu a Yehova, Baibulo, amapereka njira yabwino koposa yokhalira ndi moyo. (Yohane 13:17) Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho ndi ena amene akhala Mboni za Yehova nthaŵi yaitali, kunasonyeza mmene kuchita chifuno cha Mulungu m’mikhalidwe yosiyanasiyana kumawonjezera phindu ku miyoyo yathu. Nkhani yotsatira yakuti “Sangalalani ndi Ubwino wa Yehova” inagogomezera kuti, monga “akutsanza a Mulungu,” Akristu ayenera kusonyeza ‘ubwino wonse’ m’miyoyo yawo. (Aefeso 5:1, 9) Njira yapadera yochitira zimenezi ndiyo kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira.​—Salmo 145:7.

Nkhani yakuti “Khalanibe Osasunthika Ngati Oona Iye Wosaonekayo,” inafotokoza mmene chikhulupiriro cholimba chimatithandizira “kuona” Mulungu wosaonekayo. Wokamba nkhaniyo anafotokoza mmene anthu okhwima mwauzimu amazindikirira mikhalidwe ya Mulungu, kuphatikizapo mphamvu zake zodziŵa ngakhale zimene anthufe timaganiza. (Miyambo 5:21) Anthu amene anafunsidwa anasimba njira zomwe iwo atsatira kuti akulitse chikhulupiriro cholimba ndiponso kuika zinthu zauzimu patsogolo m’miyoyo yawo.

Chigawo cham’maŵa chinamalizira ndi nkhani yaikulu yakuti, “Tamandani Yehova​—Wochita Zinthu Zodabwitsa.” Nkhaniyo inathandiza omvetsera kuzindikira kuti pamene tikuphunzira zochuluka zokhudza Yehova m’pamene timapeza zifukwa zochuluka zom’tamandira monga Wochita zinthu zodabwitsa. Wokamba nkhaniyo anati: “Tikamalingalira za ntchito zozizwitsa za Mulungu za chilengedwe limodzi ndi zinthu zonse zodabwitsa zomwe akutichitira padakali pano, kuyamikira kochokera m’mtima kumatisonkhezera kum’tamanda. Pamene tikusinkhasinkha pa zinthu zozizwitsa zomwe wachitira anthu ake m’mbuyomu, timafunadi kum’tamanda. Ndipo pamene tikulingalira za malonjezo a zinthu zozizwitsa zomwe Yehova adzachita posachedwapa, timayesetsa kufunafuna njira zosonyezera kuyamikira.”

Chigawo chamasana chinayamba ndi nkhani yakuti “Musaleme Pakuchita Zabwino.” Nkhaniyo inakumbutsa omvetsera kuti mavuto a dziko lino akutsimikiza kuti mapeto ayandikira. (2 Timoteo 3:1) Komabe, mwa kupitirizabe osaleka tingasonyeze kuti ndife “a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.”​—Ahebri 10:39.

Kodi ndi malangizo otani a m’Baibulo a moyo wabanja amene anaperekedwa? Nkhani yoyamba yosiyirana pamsonkhanowo yamutu wakuti “Mverani Mawu a Mulungu,” inayamba ndi mbali yakuti “Posankha Wokwatirana Naye.” Kusankha wokwatirana naye ndiko chimodzi mwa zosankha zazikulu zomwe anthu amachita. N’chifukwa chaketu Akristu safulumira kukwatira kapena kukwatiŵa. Amadikira mpaka atakhwima, ndipo akatero amakwatira kapena kukwatiŵa kokha “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39) Mbali yotsatira ya nkhani yosiyiranayo inalongosola chifuno cha Yehova choti mabanja onse achikristu akhale olimba mwauzimu ndipo inapereka njira zothandiza kuti zimenezi zitheke. Mbali yothera ya nkhaniyo inakumbutsa makolo kuti kuphunzitsa ana kukonda Mulungu kumayamba ndi chikondi chomwe makolowo ali nacho kwa iye.

Mfundo zotulutsidwa m’nkhani yakuti “Chenjerani ndi Mphekesera ndi Miseche,” zinathandiza onse kuona kuti ngakhale kuti zinthu zina zochititsa chidwi zimachitika, tiyenera kuchita mwanzeru, osati motengeka maganizo, tikamva nkhani zochititsa chidwi. Akristu ali ndi mwayi chifukwa amalankhula za uthenga wabwino wa Ufumu umene akudziŵa kuti n’ngwoona. Ambiri anaona nkhani yotsatira yakuti “Kupirira ndi ‘Munga M’thupi,’” kukhala yotonthoza ndiponso yolimbikitsa kwambiri. Inawathandiza kuzindikira kuti ngakhale titakumana ndi ziyeso nthaŵi ndi nthaŵi, Yehova atha kutilimbikitsa ndi mphamvu yake ya mzimu woyera, Mawu ake, ndiponso ubale wathu wachikristu. Chilimbikitso chachikulu chinali zomwe mtumwi Paulo anakumana nazo pankhaniyi.​—2 Akorinto 12:7-10; Afilipi 4:11, 13.

Nkhani yomaliza m’tsiku loyamba inali yakuti “Kuyendera Limodzi ndi Gulu la Yehova.” Nkhaniyo inapenda makamaka mbali zitatu za momwe gulu la Mulungu lapitira patsogolo kwambiri: (1) kuzindikira kowonjezereka kwa kuwala kwauzimu kochokera kwa Yehova, (2) utumiki umene Mulungu watipatsa, ndipo (3) kusintha kwa njira zoyendetsera gulu kwapanthaŵi yake. Kenako wokamba nkhaniyo ananena motsimikiza kuti: “Tili ndi chidwi choona zomwe ziti zichitike.” Iye anafunsa kuti: “Kodi tingakayikirenso zoti pali zifukwa zabwino zokhalirabe ndi chidaliro chomwe tinali nacho poyamba mpaka titafika kumapeto?” (Ahebri 3:14) Yankho lake linali lodziŵikiratu. Kenako bulosha lakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! linatulutsidwa. Buloshali n’lothandiza kwambiri pophunzitsa ndi kuthandiza anthu amene sanaphunzire kwambiri kapena amene amavutika kuŵerenga kuti aphunzire za Yehova.

Tsiku Lachiŵiri​—Kupitirizabe Kulalikira Ntchito Zodabwitsa za Mulungu

Atakambirana lemba la tsiku, tsiku lachiŵirili linapitiriza ndi nkhani yosiyirana yakuti “Atumiki a Mawu a Mulungu.” Mbali yoyamba ya nkhaniyo inafotokoza za kupambana kwa ntchito yathu yolalikira yapadziko lonse masiku ano. Komabe, kupitiriza kwathu kuchita ntchitoyi kukutsutsidwa ndi anthu ambiri omwe amakana uthenga wa Ufumu. Anthu angapo amene akhala akufalitsa uthengawu kwanthaŵi yaitali anafotokoza mmene apitirizira kukhalabe achimwemwe mu utumiki mwa kulimbikitsa maganizo ndi mitima yawo kuti athane ndi kupanda chidwi kapena chitsutso. Mbali yachiŵiri inakumbutsa opezeka pamsonkhanowo kuti Mboni za Yehova zimayesetsa kufikira anthu kulikonse, zitakonzekera kapena mwamwayi. Ndipo mbali yomaliza inafotokoza njira zosiyanasiyana zomwe Akristu onse angafutukulire utumiki wawo aliyense payekha. Wokamba nkhaniyo anatsindika mfundo yakuti, kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo, ngakhale ngati kuchita zimenezo kukuphatikizapo mavuto ndiponso kudzimana.​—Mateyu 6:19-21.

Popeza tikukhala m’dziko losapembedza lodzala ndi kukondetsa zinthu zakuthupi, nkhani yakuti “Kulitsani Kudzipereka Kwaumulungu Limodzi ndi Kudzidalira” inalidi yapanthaŵi yake. Potchula ndemanga zina mwa kugwiritsa ntchito 1 Timoteo 6:6-10, 18, 19, wokamba nkhaniyo anafotokoza mmene kudzipereka kwaumulungu kumathandizira Akristu kupeŵa chikondi chapandalama, chomwe chingawasokeretse ndiponso kuwabweretsera zowawa zambiri. Iye anagogomezera kuti kaya ndife otani pachuma, chimwemwe chathu chimadalira pa unansi wathu ndi Yehova komanso mkhalidwe wathu wauzimu. Ambiri anachita chidwi kwambiri ndi mfundo zotulutsidwa m’nkhani yakuti “Kusachititsa Manyazi Mulungu.” Mfundo yakuti Mulungu saiŵala konse Mboni zake zokhulupirika inagogomezedwa. Chitsanzo chosayerekezereka cha Yesu Kristu, yemwe “ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthaŵi zonse,” chidzathandiza anthu ambiri kupitirizabe kuthamanga mpikisano wofuna moyo mwachipiriro.​—Ahebri 13:8.

Nkhani yothera m’chigawo cham’maŵa inali yaubatizo​—chimake chenicheni cha misonkhano ikuluikulu ya Mboni za Yehova nthaŵi zonse. Zinali zosangalatsatu kwabasi kuona odzipatulira kumene akutsatira m’mapazi a Yesu mwa kudzipereka ku ubatizo wam’madzi! (Mateyu 3:13-17) Onse amene amatsatira njirayi amakhala atakwaniritsa kale zambiri monga akuchita mawu a Mulungu. Komanso, akabatizidwa amakhala atumiki oikidwa a uthenga wabwino, akumapeza chimwemwe chochuluka podziŵa kuti akuchita nawo ntchito yoyeretsa dzina la Yehova.​—Miyambo 27:11.

Uphungu wogwira mtima unaperekedwa m’nkhani yakuti “Uchikulire N’ngwofunika ‘Kuti Tisiyanitse Chabwino ndi Choipa.’” Miyezo yadziko ya chabwino ndi choipa n’njopereŵera zedi. Choncho, tiyenera kudalira miyezo ya Yehova. (Aroma 12:2) Onse analimbikitsidwa kuchita khama kuti azindikire njira za Mulungu molondola ndiponso kuti akule kufika pauchikulire. Tikatero, pamodzi ndi kuyeserera, mphamvu zathu zakuzindikira zidzaphunzitsidwa “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”​—Ahebri 5:11-14.

Yotsatira inali nkhani yosiyirana yakuti “Limbikirani Kukulitsa Mkhalidwe Wauzimu.” Akristu oona amazindikira kufunika kokulitsa ndiponso kokhalabe ndi mkhalidwe wauzimu. Zimenezi zimafuna khama​—kuŵerenga, kuphunzira, ndiponso kusinkhasinkha. (Mateyu 7:13, 14; Luka 13:24) Anthu okhwima mwauzimu amapitirizabe ndi “pemphero lonse ndi pembedzero.” (Aefeso 6:18) Timazindikira kuti mapemphero athu amavumbula kuzama kwa chikhulupiriro chathu ndi kudzipereka kwathu, mlingo wa mkhalidwe wathu wauzimu, komanso zinthu zomwe timaziona monga “zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW) Kufunika kwa kukulitsa unansi wabwino ndi Yehova monga umene umakhalapo pakati pa mwana womvera ndi bambo wokoma mtima, anakugogomezeranso. Sikuti timangokhala ndi chipembedzo​—ngakhale kuti n’choona​—koma timafunikira kukulitsa chikhulupiriro cholimba, ‘ngati kuti tikuona Mulungu.’​—Ahebri 11:6, 27.

Nkhani ya kupita patsogolo mwauzimu inafotokozedwa mowonjezereka m’nkhani ina yakuti “Chititsani Kuti Kupita Patsogolo Kwanu Kuonekere.” Mbali zitatu za kupita patsogolo koteroko zinafotokozedwa: (1) kuwonjezeka kwa chidziŵitso, kuzindikira, ndiponso nzeru, (2) kusonyeza zipatso za mzimu wa Mulungu, ndipo (3) kuchita maudindo athu monga mamembala a banja.

Nkhani yotsiriza m’tsikulo inali yakuti, “Kuyenda M’kuunika Koŵaliraŵalirabe kwa Mawu a Mulungu.” Osonkhanawo anali osangalala kulandira buku latsopano lakuti Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse Gawo 1. Bukuli ndi gawo loyamba mwa magawo aŵiri ofotokoza chaputala ndi chaputala cha buku la m’Baibulo la Yesaya. “Buku la Yesaya lili ndi uthenga kwa ife lerolino,” anatero wokamba nkhaniyo. Iye anapitiriza kuti: “Inde, maulosi ake ambiri anakwaniritsidwa kalelo m’masiku a Yesaya. . . . Komabe, maulosi ambiri a Yesaya akukwaniritsidwabe lerolino, ndipo ena adzakwaniritsidwa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.”

Tsiku Lachitatu​—Kukhala Akuchita Mawu a Yehova

Tsiku lomaliza la msonkhano wachigawo linayamba ndi kukambirana lemba la tsikulo. Kenako panabwera nkhani yosiyirana yakuti “Ulosi wa Zefaniya Watanthauzo kwa Ochita Chifuniro cha Mulungu.” Mbali zitatu za nkhani yosiyiranayi zinafotokoza kuti, monga anachitira m’nthaŵi ya mtundu wopulupudza wa Yuda, Yehova adzabweretsa tsoka kwa anthu amene tsopano akukana kulabadira chenjezo lake. Chifukwa chakuti akuchimwira Mulungu, anthuŵa adzayenda punzipunzi ngati akhungu, ndipo sadzapeza chipulumutso. Komabe, Akristu oona amafunafunabe Yehova mokhulupirika ndipo adzabisika m’tsiku la mkwiyo wa Mulungu. Komanso, ngakhale tsopano lino, iwo akusangalala ndi madalitso ochuluka. Ali ndi mwayi wodalitsidwa wa kulankhula “chinenero choyera” cha choonadi cha Baibulo. (Zefaniya 3:9) Wokamba nkhaniyo anati: “Kulankhula chinenero choyera sindiko chabe kukhulupirira choonadi ndi kuchiphunzitsa kwa ena, koma kumaphatikizaponso kugwirizanitsa khalidwe lathu ndi malamulo ndi malangizo a Mulungu.”

Osonkhanawo anayembekeza mwachidwi seŵero lakuti “Zitsanzo Zotichenjeza M’nthaŵi Yathu.” Seŵeroli lomwe ochita ake anavala mogwirizana ndi m’nthaŵiyo, linasonyeza mmene Aisrayeli zikwi zambiri anatayira miyoyo yawo m’malire a Dziko Lolonjezedwa chifukwa choti anaiŵala Yehova ndipo ananyengedwa ndi akazi achikunja kuchita nawo zachiwerewere ndiponso kulambira konyenga. M’modzi mwa anthu a m’seŵeroli, wotchedwa Yamini, poyamba anagwira njakata pankhani ya akazi okongola zedi achimoabu ndi kudzipereka kwake kwa Yehova. Maganizo onama ndiponso onyenga a Zimiri wosapembedzayo anaonekera poyera monga mmene chinachitira chikhulupiriro ndiponso kudzipereka kwa Pinehasi. Kuopsa kogwirizana ndi anthu osakonda Yehova kunaonekera bwino lomwe.

Seŵerolo linalambula bwalo kaamba ka nkhani yotsatira yakuti “Musakhale Akumva Oiŵala.” Kufotokoza mwatsatanetsatane 1 Akorinto 10:1-10 kunasonyeza kuti Yehova amayesa kumvera kwathu kuti atsimikize kuyenerera kwathu kulandira choloŵa m’dziko latsopano. Kwa ena, zikhumbo zakuthupi zimakutabe zolinga zauzimu ngakhale tsopano pamene tatsala pang’ono kuloŵa m’dongosolo latsopano. Onse analimbikitsidwa kusataya mwayi wa ‘kuloŵa mpumulo wa Yehova.’​—Ahebri 4:1.

Nkhani yapoyera inali ndi mutu wakuti “Chifukwa Chake Tiyenera Kulingalira za Ntchito Zodabwitsa za Mulungu.” “Ntchito zodabwitsa” za Yehova zimasonyeza nzeru ndiponso ulamuliro wake pazinthu zonse analengazi. (Yobu 37:14) Mafunso ogometsa angapo ochokera kwa Yehova anakhutiritsa Yobu za mphamvu yaikulu ya Mlengi wamphamvuyonse. Yehova adzachitanso “ntchito zodabwitsa” kaamba ka atumiki ake okhulupirika m’tsogolomu. Wokamba nkhaniyo anamaliza n’kunena kuti: “Tili ndi zifukwa zokwanira zoganizira ntchito za Yehova zodabwitsa​—zimene wachita m’mbuyomu, zimene akuchita m’chilengedwe chotizinga lero, ndi zimene walonjeza kudzachita m’tsogolo.”

Chitatha chidule cha phunziro la Nsanja ya Olonda la mlunguwo, nkhani yomaliza ya msonkhanowo inali yamutu wakuti, “Yamikirani Kwambiri Mwayi Wanu Wokhala Wakuchita Mawu a Mulungu.” Nkhani yolimbikitsayo inagogomezera kuti ndi mwayi wapadera kukhala akuchita mawu a Mulungu. (Yakobo 1:22) Omvetsera anakumbutsidwa kuti mwayi wathu monga akuchita mawu a Mulungu n’ngwapadera kwambiri ndipo tikauchita kwanthaŵi yaitali, mpamene timauyamikira kwambiri. Onse omwe analipo analimbikitsidwa kusonyeza mangolomera opindulitsa amsonkhanowo m’chikhumbo chawo chofuna kukhala akuchita mawu a Mulungu kumlingo waukulu koposa. Imeneyi ndiyo njira yokhayo yopezera chimwemwe chochuluka koposa.

[Bokosi/​Chitunzi patsamba 25]

Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!

Pa lachisanu madzulo, bulosha latsopano lakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu! linatulutsidwa. Kufeŵetsa maphunziro a Baibulo m’madera ambiri a pa dziko lonse kukufunika kwambiri, ndipo bulosha limeneli lidzagwiritsidwa ntchito kuthandiza pambali imeneyi. Buloshali lidzakhala dalitso lalikulu kwa anthu amene amavutika kuŵerenga ndiponso amene sanaphunzire kwambiri.

[Bokosi/​Zitunzi patsamba 26]

Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse

Osonkhanawo anali okondwa kulandira gawo loyamba mwa magawo aŵiri a buku lakuti Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse. Buku limeneli likugogomezera za kufunika kwa ulosi wa Yesaya m’nthaŵi yathu ino.