Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova Zikupitabe Patsogolo ndi Chitsimikizo Champhamvu!

Mboni za Yehova Zikupitabe Patsogolo ndi Chitsimikizo Champhamvu!

Mboni za Yehova Zikupitabe Patsogolo ndi Chitsimikizo Champhamvu!

Lipoti La Msonkhano Wapachaka

M’MASIKU ano okayikira zinthu, Mboni za Yehova zikuonekera kukhala zapadera monga Akristu okhala ndi chitsimikizo champhamvu. Zimenezi zinaonekera bwino lomwe pamsonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, umene unachitikira ku Holo Yosonkhanira Mboni za Yehova ku Jersey City, ku New Jersey, Loŵeruka, pa October 7, 2000. *

M’mawu ake otsegulira, tcheyamani, John E. Barr, membala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anati: “Mwa anthu mabiliyoni okhala padziko lapansi, ifeyo timadziŵa ndipo timakhulupirira kuti Mwana wokondedwa wa Yehova, Kristu Yesu, tsopano analongedwa ufumu kumwamba, ndipo akulamulira pakati pa adani ake.” Umboni wa kutsimikiza mtima koteroko unaoneka mwa malipoti osangalatsa asanu ndi limodzi ochokera kumadera osiyanasiyana a dziko lapansi.

Kugonjetsa Chikhulupiriro cha Mizimu ku Haiti ndi Choonadi cha m’Baibulo

Kukhulupirira mizimu n’kofala ku Haiti. Mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi John Norman, anasimba kuti: “Kaŵirikaŵiri, anthu amachita zamatsenga pofuna kudziteteza.” Sing’anga wina anayamba kukayikira pamene anaduka mwendo pangozi. Posamvetsa zimenezo iye anati: ‘Zimenezi zingatheke bwanji kwa ine ngati ndili wotetezedwa ndi mizimu?’ Mofanana ndi ena ambiri, mwamuna ameneyu anaphunzitsidwa choonadi ndi Mboni za Yehova ndipo anathandizidwa kuti amasuke ku chikhulupiriro cha mizimu. Mwayi wa kuwonjezeka ndi waukulu mu Haiti. Titha kuona zimenezi mwa unyinji wa anthu amene anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu pa April 19, 2000. Onse pamodzi anakwana kuŵirikiza kanayi chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu onse m’dzikolo.

Kukangalika M’gawo Lalikulu la Korea

Ku Korea, 40 peresenti ya Mboni za Yehova ali mu utumiki wa nthaŵi zonse. Mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, Milton Hamilton anati: “Pokhala ndi khamu lotereli, gawo lathu la anthu opitirira 47 miliyoni limafoledwa lonse kamodzi pamwezi.” Chiwonjezeko chikuonekeranso kwambiri m’mipingo yogwiritsa ntchito chinenero cha manja. M’dera lina la chinenero cha manja, maphunziro a Baibulo apanyumba okwanira 800 akuchititsidwa. Imeneyi ndi avareji ya phunziro limodzi pa wofalitsa aliyense. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti, abale achinyamata amamangidwabe ndi kuikidwa m’ndende chifukwa chosachita nawo ndale. Ngakhale ndi choncho, Akristu okhulupirika ameneŵa amasamalidwabe bwino, ndipo kaŵirikaŵiri amapatsidwa ntchito zofuna anthu okhulupirika.

Kukwaniritsa Zofunika za Chiwonjezeko ku Mexico

Chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu okwanira 533,665 anachitira lipoti utumiki wakumunda ku Mexico m’mwezi wa August 2000. Anthu oŵirikiza katatu chiŵerengero chimenechi anafika pa Chikumbutso. Mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, Robert Tracy, anati: “Cholinga chathu chaka chino ndicho kumanga Nyumba za Ufumu 240. Komabe, tikufunikira zoposa pamenepo.”

Achinyamata pakati pa Mboni za Yehova ku Mexico ali a chitsanzo chabwino kwambiri. Ponena za wachinyamata wina, wansembe wachikatolika anati: “Ndingofuna kukhala ndi mmodzi yekha wonga ameneyu pakati pa anthu anga. Anthuŵa ndimawasilira kwabasi, chifukwa amakhala anthu otsimikiza mtima kwambiri komanso amagwiritsa ntchito Baibulo mwanzeru. Iwo aikira kumbuyo Mulungu, ngakhale kutairapo miyoyo yawo.”

Kukhulupirika M’kati mwa Chipwirikiti ku Sierra Leone

Chiyambire mu April 1991, pamene nkhondo ya pachiŵeniŵeni inabuka ku Sierra Leone, zikwizikwi za anthu aphedwa, kuvulazidwa, kapena kulemazidwa. Mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, Bill Cowan, anati: “Nkhondo ndi zovuta zina zakhudza kwambiri maganizo a anthu. Ambiri amene sankafuna kumva uthenga wathu tsopano amamvetsera mwachidwi. Si chachilendo tsopano kuona anthu akupatuka panjira ndi kukaloŵa mu Nyumba za Ufumu kukamvera msonkhano kwa nthaŵi yoyamba. Kaŵirikaŵiri abale amaimitsidwa m’njira ndi kupemphedwa phunziro la Baibulo.” Ngakhale kuti m’dzikomo mwakhala chipwirikiti chosalekeza, ntchito yolalikira Ufumu ikubala zipatso mu Sierra Leone.

Ntchito Yaikulu Yomanga ku South Africa

Pakali pano, pakufunika Nyumba za Ufumu zikwi zingapo m’gawo losamalidwa ndi ofesi ya nthambi ya South Africa. Maholo ena mazana angapo amangidwa kale. Membala wa Komiti ya Nthambi, John Kikot, anati: “M’malo mosonkhanira mumsasa kapena pansi pa mtengo, ngati mmene amachitira kale, abale athu tsopano akusonkhana m’malo oyenerera a mipando yabwino. Ngakhale kuti Nyumba za Ufumu zambiri si zamamangidwe adzaoneni, kaŵirikaŵiri zimaoneka zolemekezeka koposa m’maderamo. Zomwe zachitika m’madera ena n’zakuti, Nyumba ya Ufumu ikamangidwa, mpingowo umaŵirikiza koposa kaŵiri m’chaka chotsatira.”

Mbadwo Watsopano wa Mboni ku Ukraine

M’chaka chautumiki cha 2000, dziko limeneli linali ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 112,720. Oposa 50,000 mwa ameneŵa aphunzira choonadi cha Baibulo m’zaka zisanu zapitazo. Mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi, John Didur, anati: “Ndithudi, Yehova wautsa mbadwo watsopano wa Mboni zachinyamata kuti ulengeze dzina lake! Pazaka ziŵiri zapitazo, tagaŵira magazini oposa 50 miliyoni, chiŵerengero chofanana ndi anthu onse m’dzikomo. Mwezi uliwonse, pa avareji, timalandira makalata chikwi chimodzi ochokera kwa anthu okondwerera ofuna kudziŵa zambiri.”

Mbali Zina Zogwira Mtima za Pulogalamuyo

Daniel Sydlik, membala wa Bungwe Lolamulira, anapereka nkhani yotenga mtima. Nkhani imene ili m’magazini ino yakuti “Mmene Bungwe Lolamulira Limasiyanirana ndi Bungwe Lalamulo,” yachokera pa nkhani yopatsa chidziŵitso imeneyo.

Theodore Jaracz wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yodzutsa maganizo yakuti “Oyang’anira ndi Atumiki Otumikira Amaikidwa Mwateokalase.” Nkhani inanso m’magazini ino yachokera pa nkhani imeneyi.

Msonkhano wapachakawo unalinso ndi nkhani yosangalatsa kwambiri imene inakambidwa ndi membala wa Bungwe Lolamulira, Davide Splane, pa lemba la chaka cha 2001. Kuchokera pa mawu a mtumwi Paulo, lembalo limati: “Imani amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.” (Akolose 4:12, NW) Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi zili zotsimikiza mtima kuchita zimenezo pamene zikulalikira mokhulupirika uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse.​—Mateyu 24:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Pulogalamuyo inalumikizidwa pamawailesi akanema kumalo osiyanasiyana, moti omvetsera anakwana 13,082.