Mmene Amakanira Kusonkhezeredwa ndi Anzawo
Mmene Amakanira Kusonkhezeredwa ndi Anzawo
KUFUNA kuyanjidwa, kumasonkhezera anthu ambiri kutengera malingaliro ndi zochita za anzawo. Makamaka achinyamata amafunika kulimba mtima kuti akane makhalidwe oipa monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi chiwerewere. Kodi angakane motani kusonkhezeredwa ndi anzawo?
Posachedwapa, atsikana aŵiri ku Poland analemba kuti: “Mzimu wa dziko umaonekera bwino mwa anzathu ambiri. Amabera mayeso, kutukwana, ndiponso amakonda kuvala zovala za masitayelo oipa, ndi nyimbo zoipa. Ndifetu osangalala kwambiri chifukwa cha nkhani zofotokoza za ife achinyamata ndiponso zotiteteza kuti tisasonkhezeredwe ndi achinyamata osakhutira ndi moyo ndiponso opanduka!
“Sitingathe kuthokoza ndi mawu nkhani za mu Nsanja ya Olonda zokhudza ifeyo kuti monga achinyamata, ndife ofunika ndi kuti amatiyamikira. Uphungu wa m’Baibulo womwe tapeza, watithandiza kuwongola mayendedwe athu kuti tipitirizebe kusangalatsa Yehova Mulungu. Ndife otsimikiza kuti kutumikira Yehova mokhulupirika, ndiyo njira yabwino yokhalira ndi moyo.”
Inde, achinyamata akhoza kukana kusonkhezeredwa ndi anzawo. Mwa kuphunzitsa “mphamvu zawo za kuzindikira,” Akristu achinyamata amaphunzira kusankha zinthu mwanzeru zomwe sizisonyeza “mzimu wa dziko lapansi,” koma “Mzimu wa kwa Mulungu.”—Ahebri 5:14, NW; 1 Akorinto 2:12.