Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Bungwe Lolamulira Limasiyanirana ndi Bungwe Lalamulo

Mmene Bungwe Lolamulira Limasiyanirana ndi Bungwe Lalamulo

Mmene Bungwe Lolamulira Limasiyanirana ndi Bungwe Lalamulo

MISONKHANO yapachaka ya Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania yakhala ikuchitika chiyambire mwezi wa January 1885. Pamene kusonkhanitsa Akristu odzozedwa kunali m’kati chakumapeto kwa ma 1900, madailekitala ndi maofesala a bungwe limeneli anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Umu ndi mmene zinalili m’mbuyo monsemu.

Koma panthaŵi imodzi yokha zinachitikapo mosiyana. Mu 1940, Hayden C. Covington​—amene panthaŵiyo anali phungu wa Sosaite pankhani zamalamulo, wa “nkhosa zina,” wokhala ndi chiyembekezo cha padziko lapansi​—anasakhidwa kukhala dailekitala wa Sosaite. (Yohane 10:16) Iye anatumikira monga wachiŵiri kwa pulezidenti wa Sosaite kuchokera mu 1942 mpaka 1945. Panthaŵi imeneyo, Mbale Covington anatula pansi udindo wake monga dailekitala pofuna kugwirizana ndi chimene panthaŵiyo chinaoneka kukhala chifuniro cha Yehova​—kuti madailekitala ndi maofesala onse a bungwe la Pennsylvania anayenera kukhala Akristu odzozedwa. Lyman A. Swingle analoŵa m’malo mwa Hayden C. Covington pabungwe la madailekitala, ndipo Frederick W. Franz anasankhidwa kukhala wachiŵiri kwa pulezidenti.

Kodi n’chiyani chinachititsa atumiki a Yehova kukhulupirira kuti madailekitala ndi maofesala onse a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania anayenera kukhala Akristu odzozedwa? Chifukwa panthaŵiyo, bungwe la madailekitala ndi maofesala a bungwe la Pennsylvania analinso a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, limene nthaŵi zonse lakhala la amuna odzozedwa ndi mzimu okhaokha.

Msonkhano Wapachaka Wosaiŵalika

Pamsonkhano wapachaka umene unachitika pa October 2, 1944, ku Pittsburg, mamembala a bungwe lalamulo la ku Pennsylvania anakhazikitsa mfundo zisanu ndi imodzi zimene zinasintha chikalata cha mgwirizano cha bungwelo. Chikalatacho chinali ndi mfundo yakuti mavoti anayenera kugaŵidwa kwa anthu amene ankapereka chithandizo cha ndalama ku ntchito ya Sosaite, koma mfundo yatsopano yachitatu inathetsa mfundo imeneyo. Lipoti la msonkhano umenewo linati: “Sosaite tsopano izikhala ndi mamembala osapitirira 500 basi . . . Aliyense wosankhidwa ayenera kukhala mtumiki wanthaŵi zonse wa Sosaite kapena membala wotumikira pa kagulu [mpingo] ka Mboni za Yehova ndipo ayenera kusonyeza mzimu wa Ambuye.”

Kuchokera nthaŵi imeneyo, madailekitala a Sosaite anafunikira kuvoteredwa ndi anthu odzipereka kotheratu kwa Yehova, mosaŵerengera chithandizo cha ndalama zimene ankapereka zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu. Zimenezi zinagwirizana ndi kuyenga komwe kunali m’kati koloseredwa pa Yesaya 60:17, pomwe timaŵerenga kuti: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Potchula “akapitawo” ndi “oyang’anira ntchito,” ulosi umenewu umanena za kuwongolera zinthu m’kayendetsedwe ka ntchito m’gulu la anthu a Yehova.

Sitepe lofunika kwambiri limeneli loloŵetsa gulu pamzera wateokalase linafika kumapeto kwa “masiku zikwi ziŵiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku,” otchulidwa pa Danieli 8:14. Panthaŵiyo, ‘malo opatulika anayesedwa olungama.’

Komabe, utapita msonkhano wapachaka wosaiŵalikawo mu 1944, panatsalabe funso lofunika kwambiri. Popeza kuti panthaŵiyo Bungwe Lolamulira linalinso ngati bungwe la madailekitala la mamembala seveni la ku Pennsylvania, kodi zinatanthauza kuti kunali kosatheka kuti mamembala a Bungwe Lolamulira akhale Akristu odzozedwa opitirira seveni? Ndiponso, popeza kuti madailekitala amachita kuvoteredwa ndi mamembala a bungwelo, kodi mamembala a bungwelo anali kuvotera mamembala a Bungwe Lolamulira pamsonkhano wapachaka uliwonse? Kodi madailekitala ndi maofesala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania ndi mamembala a Bungwe Lolamulira ndi anthu amodzimodzi, kapena ndi osiyana?

Msonkhano Wapachaka Winanso Wosaiŵalika

Mafunso ameneŵa anayankhidwa pamsonkhano wapachaka umene unachitika pa October 1, 1971. Pamsonkhanowo, mmodzi wa olankhula ananena kuti bungwe lolamulira la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” linayamba kukhalapo zaka mazana ambiri isanabwere Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. (Mateyu 24:45-47) Bungwe lolamulira linakhazikitsidwa pa Pentekoste wa 33 C.E., zaka 1,800, lisanakhale bungwe lalamulo la ku Pennsylvania. Poyamba, bungwe lolamulira linali ndi amuna 12, osati 7 ayi. Mwachionekere, chiŵerengero chawo chinadzawonjezedwa, chifukwa “atumwi ndi akulu” ndiwo anali atsogoleri ku Yerusalemu.​—Machitidwe 15:2.

Mu 1971 wolankhula mmodzimodziyo anafotokoza kuti mamembala a Watch Tower Society sakanatha kuvotera mamembala odzozedwa a Bungwe Lolamulira. Chifukwa chiyani? Iye anati: “Chifukwa ‘bungwe lolamulira la ‘gulu’ la kapolo silisankhidwa ndi munthu aliyense. Limasankhidwa ndi . . . Yesu Kristu, Mutu wa mpingo weniweni wachikristu komanso Ambuye ndi Mbuye wa gulu la ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.’” Pamenepo, n’zoonekeratu kuti mamembala a Bungwe Lolamulira sangachite kuvoteredwa paudindo ndi mamembala a bungwe lalamulo lililonse.

Popitiriza, wolankhulayo ananena mawu ofunikira kwambiri akuti: “Bungwe lolamulira lilibe maofesala ngati aja a Bungwe la Madailekitala, monga pulezidenti, wachiŵiri kwa pulezidenti, mlembi-msungichuma ndi wachiŵiri kwa mlembi-msungichuma. Limangokhala ndi tcheyamani basi.” Kwa zaka zambiri, pulezidenti wa bungwe la ku Pennsylvania analinso membala wamkulu wa Bungwe Lolamulira. Izi sizikhalanso choncho. Ngakhale kuti ali osiyana m’chidziŵitso ndi maluso, mamembala a Bungwe Lolamulira ndi ofanana paudindo. Wolankhulayo anawonjezera kuti: “Membala aliyense wa bungwe lolamulira akhoza kukhala tcheyamani wa bungwelo ngakhale asali pulezidenti wa . . . Sosaite . . . Zimangodalira dongosolo la utcheyamani umene umazungulira kwa onse m’bungwe lolamulira.”

Pamsonkhano wapachaka wosaiŵalika umenewo mu 1971, kusiyana kunaoneka bwino lomwe pakati pa mamembala odzozedwa ndi mzimu a Bungwe Lolamulira ndi madailekitala a bungwe lalamulo la ku Pennsylvania. Chikhalirechobe, mamembala a Bungwe Lolamulira anapitiriza kutumikira monga madailekitala ndi maofesala a Sosaite. Komabe, funso lerolino n’lakuti: Kodi pali chifukwa cha m’Malemba chilichonse chimene madailekitala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania ayenera kukhaliranso mamembala a Bungwe Lolamulira?

Yankho ndi lakuti ayi. Bungwe lalamulo la ku Pennsylvania si ndilo bungwe lalamulo lokha limene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito. Aliponso ena. Lina ndi lija la Watchtower Bible and Tract Society of New York, Incorporated. Limayendetsa ntchito yathu mu United States. Mwachionekere, dalitso la Yehova lakhala pa bungwe limenelo, ngakhale kuti ambiri mwa madailekitala ndi maofesala ake ndi a “nkhosa zina.” Lina ndi la International Bible Students Association, limene limagwiritsidwa ntchito mu Britain. Palinso mabungwe ena omwe amagwiritsidwa ntchito kupititsa patsogolo chuma cha Ufumu m’mayiko ena. Mabungwe onsewo amathandiza mogwirizana ndipo amachita mbali yofunika kuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse lapansi. Zilibe kanthu ndi malo kumene mabungwewo ali kapena amene akutumikira monga madailekitala kapena maofesala, iwo amatsogoleredwa mwateokalase ndipo amagwiritsidwa ntchito ndi Bungwe Lolamulira. Choncho, mabungwe oterowo anapatsidwa ntchito imene akuichita popititsa patsogolo chuma cha Ufumu.

N’zotithandiza pokhala ndi mabungwe alamulo. Mwa kutero, timamvera malamulo a m’dziko, malinga ndi zimene Mawu a Mulungu amafuna. (Yeremiya 32:11; Aroma 13:1) Mabungwe alamulo amathandiza pantchito yofalitsa uthenga wa Ufumu mwa kusindikiza mabaibulo, mabuku, magazini, mabulosha, ndi zinthu zina. Mabungwe oterowo amathandizanso posamalira nkhani zokhudzana ndi mapepala a malo, chithandizo pakagwa tsoka, kupeza malo ochitira misonkhano yaikulu, ndi zina zotero. Timayamikira kwambiri mautumiki a mabungwe amenewo.

Dzina la Yehova Likwezedwa

Mu 1944, Mfundo 2 ya m’chikalata cha mgwirizano cha Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania inasinthidwa pofuna kulimbikitsa zolinga za bungweli. Malinga ndi chikalatacho, zolinga za Sosaite zikuphatikizapo cholinga chachikulu ichi: “Kulalikira uthenga wa ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu Yesu ku mitundu yonse kuti ukhale umboni wa dzina lake, mawu ake ndi ulemerero wa YEHOVA Mulungu Wamphamvuyonse.”

Chiyambire 1926, ‘kapolo wokhulupirika’ wakweza dzina la Yehova. Makamaka chaka cha 1931 chinali chapadera kwambiri, pamene Ophunzira Baibulo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10-12) Zofalitsa za Sosaite zimene zatchukitsa kwambiri dzina la Mulungu zimaphatikizapo mabuku monga akuti Jehovah (1934), “Let Your Name Be Sanctified (Dzina Lanu Liyeretsedwe)” (1961), ndi lakuti “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”​—How? (Amitundu Adzadziŵa Kuti Ine Ndine Yehova​—Motani?) (1971).

Mwapadera, tiyenera kutchulanso Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, limene linafalitsidwa lathunthu m’Chingelezi mu 1960. Ilo lili ndi dzina la Yehova monse mopezekamo Tetragrammaton (zilembo zinayi za dzina la Mulungu) m’Malemba Achihebri. Baibulo limeneli lilinso ndi dzina la Mulungu m’malo 237 m’Malemba Achigiriki Achikristu mmene popenda mwachidwi anaona kuti linafunikamo. Tili oyamikira kwambiri poona kuti, m’njira zambiri, Yehova walola “kapolo” ameneyo ndi Bungwe lake Lolamulira kugwiritsa ntchito zipangizo zawo zofalitsira komanso mabungwe alamulo kubukitsa dzina lake padziko lonse lapansi!

Kufalitsa Mawu a Mulungu Kupita Patsogolo

Anthu a Yehova achitira umboni dzina lake mosalekeza ndipo akweza Mawu ake mwa kufalitsa ndi kugaŵira mamiliyoni a mabuku ozikidwa pa Baibulo limodzinso ndi mabaibulo enieniwo. Kumayambiriro kwa ma 1900, Watch Tower Society inakhala ndi ulamuliro wonse wa Baibulo lolembedwa ndi Benjamin Wilson, lokhala ndi zinenero ziŵiri, Chigiriki ndi Chingelezi, la Malemba Achigiriki Achikristu, lotchedwa The Emphatic Diaglott. Sosaite inafalitsanso Baibulo la Ophunzira Baibulo la King James Version, limene linalinso ndi mawu owonjezera okwanira masamba 500. Mu 1942 inafalitsa Baibulo la King James Version lokhala ndi malemba owonjezera m’madanga apakati. Kenako mu 1944, Sosaite inayamba kusindikiza Baibulo lotchedwa American Standard Version la 1901, limene limatchula dzina la Mulungu. Dzina la Yehova linalinso mbali yaikulu m’Baibulo lotchedwa The Bible in Living English, lolembedwa ndi Stephen T. Byington, limene linafalitsidwa ndi Sosaite mu 1972.

Mabungwe alamulo ogwiritsidwa ntchito ndi Mboni za Yehova ndiwo akhala akuthandiza kusindikiza ndi kufalitsa mabaibulo onsewo. Komabe, chimene chakhala chapadera kwambiri ndiwo mgwirizano pakati pa bungwe la Watch Tower Society ndi kagulu ka Mboni za Yehova zodzozedwa zimene zimapanga Komiti Yoyang’anira Kumasulira Baibulo la New World Translation. Tikusangalala kuona kuti, pofika lero, Baibulo lasindikizidwa, lonse lathunthu kapena mbali yake, m’makope opitirira 106,400,000, m’zinenero 38. Indedi, bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, lilidi bungwe la Baibulo!

‘Kapolo wokhulupirika wakhazikidwa kusamalira zinthu zonse za Mbuye wake.’ Zinthuzo zimaphatikizapo nyumba ndi zipangizo zonse zakulikulu ku New York State, U.S.A., ndi maofesi ake anthambi okwanira 110 omwe akugwira ntchito tsopano padziko lonse. Mamembala a gulu la kapolo akudziŵa kuti adzafunsidwa za mmene anagwiritsira ntchito zinthu zimene zaikizidwa kwa iwo. (Mateyu 25:14-30) Komabe, izi siziletsa ‘kapoloyo’ kulola oyang’anira oyeneretsedwa a “nkhosa zina” kuti asamalire maudindo a zamalamulo ndi akayendetsedwe ka ntchito. Ndi iko komwe, kuteroko kumalola mamembala a Bungwe Lolamulira kupereka nthaŵi yochuluka “m’kupemphera, ndi kutumikira mawu.”​—Machitidwe 6:4.

Malinga ngati mikhalidwe ya dzikoli ikulolabe, Bungwe Lolamulira, loimira “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” lidzapitirizabe kugwiritsa ntchito mabungwe alamulo. Mabungwewo ndi othandiza, koma sikuti popanda iwo zinthu sizingayende. Ngati bungwe lalamulo lithetsedwa ndi lamulo la boma, ntchito yolalikira idzapitirirabe. Ngakhale pakali pano, m’mayiko amene ntchito yathu ndi yoletsedwa ndipo tilibeko mabungwe alamulo owagwiritsa ntchito kumeneko, uthenga wa Ufumu ukulalikidwabe, ophunzira akupezedwabe, ndipo chiwonjezeko chateokalase chikupitabe patsogolo. Zimenezo zikuchitika chifukwa Mboni za Yehova zimadzala ndi kuthirira, ndipo ‘Mulungu amapitiriza kumakulitsa.’​—1 Akorinto 3:6, 7.

Pamene tiyang’ana m’tsogolo, tili ndi chidaliro chakuti Yehova adzasamalira zosoŵa zauzimu ndi zakuthupi za anthu ake. Iye limodzi ndi Mwana wake, Yesu Kristu, adzapitiriza kupereka utsogoleri ndi chithandizo zochokera kumwamba zofunikira kuti ntchito yolalikira Ufumu imalizike. Inde, chilichonse chimene timatha kuchita monga atumiki a Mulungu sichitheka ‘ndi khamu la nkhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi mzimu wa Yehova.’ (Zekariya 4:6) Chotero timapempherera chithandizo cha Mulungu, chifukwa timadziŵa kuti mwa mphamvu imene Yehova amapereka, tidzakhoza kutsiriza ntchito imene watipatsa kuti tiichite m’nthaŵi ino ya mapeto!