Momwe Tingakulitsire Khalidwe Labwino
Momwe Tingakulitsire Khalidwe Labwino
MABUKU amakono omasulira mawu, amati “khalidwe labwino” ndilo “kupambana kwa makhalidwe; ubwino.” Khalidwe labwino ndilo “kuchita zinthu ndi kulingalira moyenera; ndilo ubwino wa kakhalidwe.” Marvin R. Vincent, wolemba mabuku omasulira mawu anati lingaliro lake lenileni loyambirira la mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “khalidwe labwino” limatanthauza “ubwino wamtundu wina uliwonse.” Chotero, n’zosadabwitsa kuti nthaŵi zina mikhalidwe monga nzeru, kulimba mtima, kudziletsa, chilungamo, chifundo, kulimbikira, kuona mtima, kudzichepetsa, ndi kukhulupirika yayamikiridwa kukhala makhalidwe abwino. Khalidwe labwino alifotokozanso kuti ndilo “kugwirizana ndi muyezo wachilungamo.”
Kodi ndi muyezo wayani wa kupambana, ubwino, ndi chilungamo womwe tiyenera kugwirizana nawo? “Malinga ndi anthu okhulupirira maganizo aumunthu pa makhalidwe,” inatero magazini ya Newsweek, “kukayikira komwe gulu lokana zachikale linayambitsa kwachititsa kuti nkhani yonse yokhudza chabwino ndi choipa ionedwe malinga ndi zokonda za munthu, zofuna za mtima wake, kapena zomwe amakonda pachikhalidwe chawo.” Koma kodi zokonda za munthu ndiyo njira yokhutiritsa yodziŵira chabwino ndi choipa? Ayi. Kuti tikulitse khalidwe labwino, tifunikira muyezo wodalirika wa chabwino ndi choipa—muyezo womwe tingayezere kachitidwe kena kake, maganizo, kapena khalidwe linalake kuti tidziŵe ngati ndi labwino kapena loipa.
Gwero Lokha Loona la Miyezo ya Makhalidwe Abwino
Pali Gwero limodzi lokha loona la miyezo ya makhalidwe abwino—Mlengi wa anthu, Yehova Mulungu. Atangolenga munthu woyambayo, Adamu, Yehova Mulungu anaikira munthuyo lamulo ili: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa Genesis 2:16, 17) Yehova Mulungu anapatsa mtengowo dzina lapadera limenelo kusonyeza kuti iye yekha ndiye ali ndi ufulu wonse wouza zolengedwa zake chomwe chili chabwino ndi choipa. Chotero miyezo ya Mulungu ya chabwino ndi choipa inakhala maziko a chiweruzo, kapena choyezera, zochita za munthu, maganizo ake, ndi mikhalidwe yake. Popanda miyezo ngati imeneyo sitikanatha kusiyanitsa molondola chabwino ndi choipa.
usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Lamulo lokhudza mtengo wodziŵitsa chabwino ndi choipa linapatsa Adamu ndi Hava mwayi wosankha—kumvera kapena kusamvera. Kwa iwo, khalidwe labwino linatanthauza kumvera lamulo limenelo. M’kupita kwa nthaŵi, Yehova anapitiriza kuvumbula zomwe zimam’sangalatsa ndi zimene sizim’sangalatsa, ndipo analemba zimenezi m’Baibulo kaamba ka ife. Choncho, kukulitsa khalidwe labwino kumafuna kugwirizana kwathu ndi miyezo yolungama ya Yehova yotchulidwa m’Malemba.
Idziŵeni Bwino Lomwe Miyezo ya Mulungu
Popeza kuti Yehova Mulungu waika miyezo ya chabwino ndi choipa ndipo waivumbula m’Baibulo, kodi sitiyenera kuidziŵa bwino lomwe? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
Mwachitsanzo, talingalirani zomwe zinam’chitikira Kunihito, wotchulidwa m’nkhani yatha ija. Anamvedwa molakwa pamene anali kusonyeza kudzichepetsa monga momwe amachitira pachikhalidwe chakwawo. Pambuyo pake, kupenda mosamalitsa miyezo ya m’Malemba kunam’thandiza kuchita zinthu mosamala kwambiri. N’zoona kuti Baibulo limalimbikitsa kudzichepetsa, ndipo limadzudzula kudzidalira mopambanitsa ndi kudzikuza. (Miyambo 11:2; Mika 6:8) Komabe, pofotokoza ziyeneretso za woyenerera “udindo wa woyang’anira,” mtumwi Paulo anatchula za ‘kukhumba [“kukalamira,” NW]’ udindo umenewo. (1 Timoteo 3:1) “Kukalamira” kumeneku kuyenera kuchitidwa mosadzitukumula kapena kudzikuza komanso mopanda kudzipeputsiratu mosafunikira.
Kodi Baibulo limati bwanji ponena za khalidwe lopambana pankhani za malonda? Kugwiritsa ntchito njira zokayikitsa kapena kutsata njira zotsutsana ndi malamulo aboma komanso malamulo a msonkho n’kofala kwambiri lerolino m’nkhani za malonda. Komabe mosasamala kanthu zomwe ena amachita, muyezo wa Baibulo umafuna kuti ‘tikhale nawo makhalidwe abwino [“oona mtima m’zonse,” NW].’ (Ahebri 13:18) Choncho, timakulitsa khalidwe labwino mwa kuchita moona mtima ndi mosakondera ndi olemba anzawo ntchito, olembedwa ntchito, makasitomala, ndi maboma a m’dziko. (Deuteronomo 25:13-16; Aroma 13:1; Tito 2:9, 10) Ndithudi kuona mtima kumalimbikitsa kukhulupirirana ndi kufunirana zabwino. Ndipo kulemberana zomwe tagwirizana kaŵirikaŵiri kumathandiza kupeŵa kusamvetsetsana ndi zovuta zomwe zingabuke chifukwa cha ‘zakugwa m’nthaŵi yake’ [“zochitika zosadziŵika,” NW].—Mlaliki 9:11; Yakobo 4:13, 14.
Nkhani ya kavalidwe ndi kudzikongoletsa ndi mbali ina yomwenso tifunikira kukulitsa khalidwe labwino. Kavalidwe n’kosiyanasiyana malinga ndi chikhalidwe, ndipo tingasonkhezereke mwamphamvu kuti tisaphonye masitayelo amakono akavalidwe. Koma n’chifukwa chiyani tingafune kutsatira sitayelo kapena fashoni iliyonse yatsopano? Baibulo limatichenjeza kuti “musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.” (Aroma 12:2) M’malo mopanga malamulo, mtumwi Paulo analemba mouziridwa kuti: “Akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali; komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu).” (1 Timoteo 2:9, 10) Muyezo wosavuta umenewu umagwira ntchito kwa amuna ndi akazi omwe. Inde, n’zotheka kuvala masitayelo osiyanasiyana osangalatsa malinga ndi chikhalidwe chathu kapena malinga n’zomwe ifeyo patokha timakonda.
Baibulo limatchulanso makhalidwe oipa omwe Mulungu amatsutsa mwamphamvu. Pa 1 Akorinto 6:9, 10, timaŵerenga chenjezo lakuti: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.” Lemba limeneli linathandiza Maria, watchulidwa poyamba uja, kuona kuti malinga ndi muyezo wa khalidwe lopambana womwe Mlengi anakhazikitsa, ubwenzi wake ndi Juan sunali woyenera ndi kuti anayenera kuuthetsa kuti akhale wovomerezeka kwa Mulungu. Mwachionekere, kuti tikulitse khalidwe labwino, tifunikira kuidziŵa bwino lomwe miyezo ya Yehova.
Phunzirani ndi Mtima
Khalidwe labwino sikungopeŵa chabe choipa. Lili ndi mphamvu yake. Munthu wakhalidwe labwino ali ndi ubwino wake. Pulofesa wina anati: “Khalidwe labwino lifunikira kuliphunzira ndi mtima komanso ndi mutu.” Chotero, kukulitsa khalidwe labwino kumafuna zambiri osati chabe kungodziŵa bwino Mawu a Mulungu. Kumafuna kusinkhasinkha zomwe zalembedwa mmenemo kuti mitima yathu idzazidwe ndi kuyamikira Yehova ndi kutisonkhezera kugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Malemba m’moyo wathu.
“Ha! Ndikondadi chilamulo chanu.” Anafuula motero wamasalmo. “Ndilingiriramo ine tsiku lonse.” (Salmo 119:97) Ndipo Mfumu Davide analemba kuti: “Ndikumbukira masiku a kale lomwe; zija [Mulungu] mudazichita ndilingirirapo; ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.” (Salmo 143:5) Nafenso tiyenera kupanga kusinkhasinkha mwapemphero kukhala mbali yofunika kwambiri pa kuphunzira kwathu Baibulo ndi zofalitsa zophunzitsa Baibulo.
Zoona, kupatula nthaŵi yophunzira mwakhama ndi kusinkhasinkha kungakhale kovuta. Komabe ngati tikufuna kukhala ndi khalidwe labwino tifunikira kupatula nthaŵi kuchokera ku ntchito zina. (Aefeso 5:15, 16) Aaron, wazaka 24, amapatula nthaŵi yoteroyo tsiku lililonse mwa kudzuka mofulumirirapo ndi mphindi 30 kuposa momwe amachitira kale. Iye akusimba kuti: “Poyamba, ndinkangoŵerenga Baibulo mphindi 30 zonsezo. Koma posachedwapa ndazindikira kufunika kwa kusinkhasinkha. Chotero pano ndimagwiritsa ntchito pafupifupi theka la nthaŵi imeneyo kusinkhasinkha zomwe ndaŵerengazo. Zimenezi zandipindulitsa kwambiri.” Kusinkhasinkha kungachitike panthaŵi ina yapadera. Poimbira Yehova nyimbo zotamanda, Davide anati: ‘Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndilingalira za Inu maulonda a usiku.’ (Salmo 63:6) Ndipo Baibulo limati: “Isake anatuluka kulingalira m’munda madzulo.”—Genesis 24:63.
Kusinkhasinkha n’kofunika kwambiri pokulitsa khalidwe labwino, chifukwa chakuti kumatithandiza kumva mmene Yehova amamvera ndi kuchititsa maganizo ake kufanana ndi athu. Mwachitsanzo, Maria anadziŵa kuti Mulungu amaletsa dama. Koma kuti ‘adane nacho choipa; ndi kugwirizana nacho chabwino,’ anafunikira kusinkhasinkha malemba ofunika a m’Baibulo. (Aroma 12:9) Anathandizidwa kuona kufunika kosintha ataŵerenga Akolose 3:5, lomwe limatilimbikitsa ‘kufetsa ziŵalozo; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi [“chilakolako cha kugonana,” NW], chilakolako choipa, ndi chisiriro.’ Maria anayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndiyenera kufetsa chilakolako chiti cha kugonana? Kodi ndiyenera kupeŵa chiyani chomwe chingadzutse zilakolako zodetsa? Kodi ndifunikira kusintha mmene ndimachitira ndi anyamata?’
Kusinkhasinkha kumaphatikizapo kulingalira zotsatira za zochita zinazake. Paulo akulimbikitsa Akristu kupeŵa dama ndi kuti akhale odziletsa kuti “wina asafike popweteka mbale wake ndi kumusokonezera ufulu wake.” (1 Atesalonika 4:3-7, NW) Mafunso abwino kuwalingalira ndi akuti: ‘Kodi ndikachita zimenezi ndidzivulaza motani, nanga banja langa, kapena ena? Kodi zidzandikhudza motani mwauzimu, m’maganizo, ndi kuthupi? Kodi chinachitika n’chiyani kwa ena omwe anaswa malamulo a Mulungu m’mbuyomu?’ Kusinkhasinkha kotereku kunalimbitsa kwambiri Maria, ndipo kungateronso kwa ife.
Tengerani Phunziro pa Zitsanzo
Kodi khalidwe labwino lingaphunzitsidwe m’kalasi? Funso limeneli lathetsa nzeru akatswiri ambiri kwa zaka zambiri. Plato, Mgiriki wafilosofi, anali kuganiza kuti lingatero. Kumbali ina, Aristotle ankaganiza kuti khalidwe labwino ungalipeze mwa kuchita zinthu zabwino. Mtolankhani wina anafotokoza mwachidule kukambirana komwe kunalipo pankhani imeneyi motere: “Mwachidule, sitingaphunzire makhalidwe abwino patokha. Ndiponso sangaphunzitsidwe kuchokera m’mabuku ophunzira. Khalidwe labwino limapezeka mwa kukhala ndi anthu pamudzi . . . omwe amalimbikitsa anthu kukhala ndi khalidwe labwino ndi kuwafupa.” Komano n’kuti komwe tingapeze anthu akhalidwe labwinodi? Ngakhale kuti zikhalidwe zina zimapereka zitsanzo zina za khalidwe labwino, monga m’nthano zawo zonena za ngwazi, Baibulo lili ndi zitsanzo zenizeni zochuluka.
Chitsanzo chodziŵika bwino cha khalidwe labwino n’cha Yehova. Iye nthaŵi zonse amachita zinthu mwaubwino ndiponso amachita chilungamo ndi chabwino. Tingakulitse khalidwe labwino mwa kukhala “akutsanza a Mulungu.” (Aefeso 5:1) Ndipo Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, ‘anatisiyira chitsanzo kuti tikalondole mapazi ake.’ (1 Petro 2:21) Kuwonjezera pamenepo, m’Baibulo muli nkhani za anthu ambiri okhulupirika, monga Abrahamu, Sara, Yosefe, Rute, Yobu, Danieli ndi Ahebri anzake atatu aja. Sitiyenera kuiŵalanso zitsanzo za khalidwe labwino za atumiki amakono a Yehova.
Tingakhoze
Kodi tingathedi kuchita zomwe Mulungu amati khalidwe labwino? Popeza kuti tinalandira kupanda ungwiro monga choloŵa, nthaŵi zina m’kati mwathu mungabuke chinkhondo chochititsa mantha pakati pa maganizo ndi thupi—kwinaku kufuna kuchita chabwino kwinaku kutsata zizoloŵezi zathu zauchimo. (Aroma 5:12; 7:13-23) Koma ndi thandizo la Mulungu tingapambane pankhondo imeneyo. (Aroma 7:24, 25) Yehova watipatsa Mawu ake ndi zofalitsa zophunzitsa Baibulo. Mwa kuphunzira Malemba mwakhama ndi kuwasinkhasinkha mwapemphero, tingakhale oyera mumtima. Mumtima woyera woterowo m’machokera malingaliro, mawu, ndi zochita zabwino. (Luka 6:45) Kutengera zitsanzo za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, tingakulitse umunthu waumulungu. Ndipotu tingaphunzire zochuluka kwa anthu omwe akutumikira Mulungu mokhulupirika lerolino.
Mtumwi Paulo analimbikitsa oŵerenga ake ‘kupitirizabe kulingalira’ khalidwe labwino ndi zinthu zina zotamandika. Mosakayika, kuchita zimenezi kudzatidzetsera madalitso a Mulungu. (Afilipi 4:8, 9) Ndi thandizo la Yehova, tikhoza kukulitsa khalidwe labwino.
[Chithunzi patsamba 6]
Phatikizani kusinkhasinkha pa phunziro lanu la Baibulo
[Chithunzi patsamba 7]
Kulitsani umunthu waumulungu mwa kutsanzira Kristu Yesu