Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ntchito Yaukatswiri”

“Ntchito Yaukatswiri”

Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu

“Ntchito Yaukatswiri”

KUYAMBIRA pachiyambi pa zochita zawo zamakono, Mboni za Yehova zakhala ndi chidwi kwambiri ndi wina mwa maulosi a Yesu Kristu wakuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Pomwe chaka cha 1914​—chiyambi cha “masiku otsiriza”​—chinali kuyandikira, Ophunzira Baibulo oona mtima motsimikiza anayamba ndawala yophunzitsa ya m’Malemba Opatulika yomwe inali isanachitikepo m’mbuyomo.​—2 Timoteo 3:1.

Pofuna kukwaniritsa cholinga chawo cholengeza uthenga wabwino padziko lonse, atumiki a Yehova ameneŵa anagwiritsa ntchito njira yomwe inali yatsopano, yotsimikizika ndiponso yomveka bwino. Kuti tidziŵe zambiri, tiyeni tibwererenso m’nthaŵiyo.

Njira Yatsopano Yolengezera Uthenga Wabwino

Uno ndi mwezi wa January 1914. Yerekezerani kuti muli mumzinda wa New York City ndipo mwakhala m’gulu la anthu 5,000 mu holo yomwe magetsi awazimitsa. Patsogolo panu pali chinsalu chachikulu choonetserapo kanema. Munthu wina waimvi wovala mkanjo akuonekera pa chinsalucho. Munaonererapo kale akanema opanda mawu, koma munthu amene mukuonayo akulankhula ndipo mukumva zomwe akulankhulazo. Muli pamwambo wokhazikitsa chipangizo chinachake chopangidwa mwaluso zedi, ndipo uthenga wake n’ngwapadera kwambiri. Amene akulankhulayo ndi Charles Taze Russell, pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, ndipo limeneli ndi “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe.”

Kuti afikire anthu ambiri, C. T. Russell anazindikira kuti kugwiritsa ntchito akanema kungathandize kwambiri. Choncho, mu 1912, iye anayamba kukonza “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe.” M’kupita kwanthaŵi, seŵerolo linadzakhala la zithunzi zosayenda ndi zoyenda za pa filimu yamaola asanu ndi atatu ya zithunzi zokongola ndiponso zotulutsa mawu.

Popeza linakonzedwa kuti lionetsedwe m’zigawo zinayi, “Seŵero la Pakanema” linkaonetsa anthu zochitika kuyambira pa chilengedwe mpaka m’mbiri yonse ya anthu kufikira pachimake penipeni pa chifuno cha Yehova Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu pamapeto a Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. Panatenga zaka zambiri ndithu kuti kugwiritsa ntchito umisiri wofananawo kukhale kopambana m’zamalonda. Komabe, anthu miyandamiyanda anaonerera “Seŵero la Pakanema” kwaulere!

Nyimbo zojambulidwa mwapamwamba komanso nkhani zojambulidwa pa galamafoni zokwana 96 zinakonzedwa kaamba ka “Seŵero la Pakanema.” Zithunzi zosayendazo zinkapangidwa kuchokera ku zithunzi zakale zojambulidwa bwino zomwe zinkaonetsa zochitika m’mbiri ya padziko lonse. Kunalinso kofunika kujambula zithunzi zina zatsopano ndiponso zina zachidule mazana ambiri. Zithunzi zina zosayenda zoonetsa mtundu wake weniweni ndiponso mafilimu ena zinkajambulidwa mosamalitsa pamanja. Ndipo izi zinkachitika mobwerezabwereza, moti m’kupita kwanthaŵi maseŵero azigawo zinayi okwana 20 anapangidwa. Zimenezi zinatheketsa kuti azionetsa chigawo china cha “Seŵero la Pakanema” m’mizinda 80 yosiyanasiyana patsiku!

Zochitika Mseri

Kodi zinkachitika mseri n’zotani panthaŵi yoonetsa “Seŵero la Pakanema”? “Seŵerolo linkayamba ndi kuonetsa Mbale Russell,” anatero Wophunzira Baibulo wotchedwa Alice Hoffman. “Amati akaonekera pa chinsalu chakanemacho, milomo yake n’kuyamba kugwedera, galamafoni inkatsegulidwa . . . ndipo akatero tinkamvetsera mawu ake.”

Ponenapo za kujambula zochitika kofulumirako, Zola Hoffman anakumbukira kuti: “Ndinakhala dwii kudabwa pomwe tinkaonerera masiku a ntchito ya kulenga. Tinaona ndi maso athu maluŵa akumasula pang’onopang’ono.”

Wokonda nyimbo wina wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova wotchedwa Karl F. Klein anawonjezera kuti: “Panthaŵi imodzimodziyo pamene zithunzi zimenezi zinkaonetsedwa, chapansipansi pankamvekanso nyimbo zabwino kwambiri monga yakuti Narcissus ndiponso yakuti Humoreske.”

Panalinso zinthu zina zosaiŵalika. “Nthaŵi zina, tinkaonanso zinthu zochititsa mantha,” anakumbukira motero Clayton J. Woodworth, Jr. “Nthaŵi inayake, nyimbo ina inkayimba kuti ‘Thaŵirani ku Mapiri Anu ngati Mbalame’, ndipo pa chinsalu chakanema panaoneka nyama yaikulu zedi yotchedwa Gigantosaurus, nyama yaikulutu kwabasi yomwe inaliko Chigumula chisanachitike”!

Kuwonjezera pa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” panapangidwanso seŵero lina lazigawo ziŵiri lotchedwa “Seŵero la Eureka.” (Onani bokosi) Chigawo chimodzi chinali ndi nkhani zojambulidwa komanso nyimbo. Chigawo chinacho chinali ndi nyimbo komanso zithunzi zosayenda. Ngakhale kuti “Seŵero la Eureka” linalibe zithunzi zoyenda, seŵerolo ankalikonda kwambiri kumadera komwe kunali anthu ochepa.

Chida Champhamvu Chochitira Umboni

Pomwe chaka cha 1914 chimatha, “Seŵero la Pakanema” linali litaonetsedwa kwa anthu opitirira 9,000,000 a ku North America, Ulaya ndiponso a ku Australia. Ngakhale kuti chiŵerengero chawo chinali chochepa, Ophunzira Baibulo sanasoŵe chidaliro cholimba chofunikacho kuti alengeze uthenga wabwino pogwiritsa ntchito chida chatsopanocho. Iwo anapereka mokondwera ndalama zolipirira malo abwino kuti akaonetsereko maseŵeroŵa. Motero “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe” linachita ntchito yaikulu kwambiri podziŵitsa anthu Mawu a Mulungu ndiponso zifuno zake.

M’kalata yake yopita kwa C. T. Russell, munthu wina analemba kuti: “Moyo wanga unasitha kotheratu n’tangoonera koyamba Seŵero lanu; kapena ndinene kuti, zomwe ndinkadziŵa kuchokera m’Baibulo zinasintha kotheratu.” Mayi wina wapabanja ananenanso kuti: “M’pang’onong’ono chikhulupiriro changa m’zachipembedzo chikadasweka chipanda ‘Seŵero la Pakanema la Chilengedwe’ lomwe analionetsa kuno m’chilimwe chapitachi. . .  . Tsopano ndili ndi mtendere umene dziko silingaupereke ndiponso umene sindingautaye chifukwa cha ulemerero wake wonse.”

Demetrius Papageorge yemwe wakhala nthaŵi yaitali akugwira ntchito pa malikulu a Sosaite anathirira ndemanga amvekere: “Tikaganizira za chiŵerengero chochepa cha Ophunzira Baibulo ndiponso kuchepa kwa ndalama zomwe zinalipo, ‘Seŵero la Pakanema’ linalidi ntchito yaukatswiri. Ntchitoyo inkachirikizidwadi ndi mzimu wa Yehova!”

[Bokosi/​Zithunzi pamasamba 8, 9]

“Seŵero la Eureka”

Patapita miyezi isanu ndi itatu chikhazikitsireni “Seŵero la Pakanema,” Sosaite inaona kufunika kopanganso seŵero lina lomwe linatchedwa kuti “Seŵero la Eureka.” Pamene kwinaku “Seŵero la Pakanema” lathunthu ankapitiriza kulionetsa m’mizinda ikuluikulu, zigawo za seŵero la “Eureka” zinkaperekanso uthenga womwewo kumadera akumidzi. Chigawo chimodzi cha “Seŵero la Eureka” ankati chinkapatsa “alongo mwayi wapadera” wolalikira. N’chifukwa chiyani ankanena choncho? Chifukwa chakuti chikwama cha malekodi a pa galamafoni a seŵeroli chinkalemera makilogalamu 14 okha basi. N’zoona kuti pankafunikanso kunyamula galamafoni kuti akaonetse seŵeroli.