Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Oyang’anira ndi Atumiki Otumikira Amaikidwa Mwateokalase

Oyang’anira ndi Atumiki Otumikira Amaikidwa Mwateokalase

Oyang’anira ndi Atumiki Otumikira Amaikidwa Mwateokalase

“Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira.”​—MACHITIDWE 20:28.

1, 2. Kodi Yesaya 60:22 akukwaniritsidwa motani?

YEHOVA analosera kalero kuti chinachake chosaiŵalika chikachitika m’nthaŵi yamapeto. Kudzera mwa mneneri Yesaya, ananeneratu kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake.”​—Yesaya 60:22.

2 Kodi pali umboni wakuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa lerolino? Inde, ulipo! M’zaka za m’ma 1870, mpingo umodzi wa anthu a Yehova unakhazikitsidwa ku Allegheny, Pennsylvania, m’dziko la United States of America. Kuchokera kuchiyambi chaching’ono chimenecho, mwatuluka mipingo masauzande ambiri ndipo ikumka nichulukabe padziko lonse lapansi. Miyandamiyanda ya olengeza Ufumu​—mtundu wamphamvu​—tsopano akugwirizana ndi mipingo yoposa 91,000 m’mayiko 235 kuzungulira dziko lonse. Mosakayikira, umenewu ndi umboni wakuti Yehova akupititsa patsogolo ntchito yosonkhanitsa olambira oona “chisautso chachikulu,” chomwe tsopano chayandikira kwambiri chisanayambe.​—Mateyu 24:21; Chivumbulutso 7:9-14.

3. Kodi kubatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera” kumatanthauzanji?

3 Atadzipatulira kwa Yehova, ndiponso mogwirizana ndi malangizo a Yesu, miyandamiyanda ya anthu ameneŵa anabatizidwa “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera.” (Mateyu 28:19) Kubatizidwa “m’dzina la Atate” kukutanthauza kuti anthu odzipatulira ameneŵa amamuona Yehova monga Atate wawo wakumwamba ndi Wopatsa Moyo ndipo amagonjera ulamuliro wake. Kubatizidwa ‘m’dzina la Mwana’ kumasonyeza kuti akuvomereza kuti Yesu Kristu ndiye Momboli wawo, Mtsogoleri, ndi Mfumu yawo. Amadziŵanso mbali yofunika yomwe mzimu woyera wa Mulungu, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, umachita potsogolera moyo wawo. Zimenezi zimasonyeza kuti anabatizidwa ‘m’dzina la mzimu woyera.’

4. Kodi atumiki achikristu amaikidwa motani?

4 Pa ubatizo wawo, ophunzira atsopanoŵa amaikidwa monga atumiki a Yehova Mulungu. Kodi amawaika ndani? Mawu a pa 2 Akorinto 3:5 akugwiranso ntchito pa iwoŵa. Mawuŵa amati: “Kukwanira kwathu [monga atumiki] kuchokera kwa Mulungu.” Sangalakalake n’komwe ulemu wina waukulu woposa kuikidwa ndi Yehova Mulungu mwiniyo! Atabatizidwa, adzapitiriza kukula mwauzimu monga atumiki a “uthenga wabwino” ngati adzalola kutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu ndi kupitiriza kuchita zomwe mawu ake akunena.​—Mateyu 24:14; Machitidwe 9:31.

Kuikidwa Mwateokalase​—Osati Mwademokalase

5. Kodi oyang’anira ndi atumiki otumikira achikristu amasankhidwa mwademokalase? Fotokozani.

5 Uyang’aniro woyenerera wochitidwa ndi oyang’anira oyeneretsedwa komanso thandizo loyenera la atumiki otumikira n’zofunika posamalira zosoŵa zauzimu za atumiki okangalika omwe chiŵerengero chawo chikumka n’chiwonjezeka. (Afilipi 1:1) Kodi amuna auzimu ameneŵa amaikidwa motani? Samaikidwa potsata njira zomwe Matchalitchi Achikristu amatsata. Mwachitsanzo, oyang’anira achikristu sasankhidwa mwademokalase, kapena kuti mwa kupeza mavoti ambiri kuchokera kwa anthu a mumpingo wawo. M’malo mwake, amaikidwa m’maudindo ameneŵa mwateokalase. Kodi zimenezi zikutanthauzanji?

6. (a) Kodi teokalase yeniyeni n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani kuikidwa kwa oyang’anira ndi atumiki otumikira kuli kwa teokalase?

6 Kunena mwachidule, teokalase yeniyeni ndi ulamuliro wa Mulungu. Modzifunira, Mboni za Yehova zimagonjera ulamuliro wake ndipo zimachitira zinthu limodzi n’cholinga chochita chifuno cha Mulungu. (Salmo 143:10; Mateyu 6:9, 10) Kuikidwa kwa oyang’anira achikristu, kapena akulu, ndi atumiki otumikira n’kwateokalase chifukwa chakuti kuvomereza ndi kuika amunaŵa m’maudindo ameneŵa kumachitika mogwirizana ndi makonzedwe a Mulungu operekedwa m’Malemba Opatulika. Ndipotu monga “mutu wa pa zonse,” Yehova ali ndi ufulu wonse wolinganiza zinthu kuti gulu lake liziyenda monga momwe akufunira.​—1 Mbiri 29:11; Salmo 97:9.

7. Kodi Mboni za Yehova zimalamuliridwa motani?

7 Mosiyana ndi magulu ambiri achipembedzo m’Gawo la Matchalitchi Achikristu, Mboni za Yehova sizipanga zokha mtundu wa boma lauzimu lomwe likuwayang’anira. Akristu okhulupirika ameneŵa amayesetsa kumamatira ku miyezo ya Yehova. Oyang’anira awo samaikidwa m’maudindo amenewo ndi mtundu winawake wa utsogoleri wampingo, bungwe la atsogoleri amaudindo akuluakulu m’matchalitchi, kapena gulu losankhidwa la atsogoleri achipembedzo. Ngati ena m’mbali yadzikoli akufuna kuloŵerera m’nkhani ya maikidwe ameneŵa, anthu a Yehova amakana kugonja. Molimbika, sasunthika m’malo awo ofotokozedwa bwino lomwe ndi atumwi m’zaka za zana loyamba pamene anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Chotero, Mboni zimamvera Mulungu m’zinthu zonse. (Ahebri 12:9; Yakobo 4:7) Kutsatira dongosolo la teokalase kumadzetsa chiyanjo cha Mulungu.

8. Kodi zochitika za demokalase ndi za teokalase n’zosiyana motani?

8 Monga atumiki a Wateokalase Wamkulu, Yehova, tiyenera kudziŵa kusiyana m’zochitika za demokalase ndi za teokalase. Mu demokalase, chiŵerengero cha opikisana chimafunikira chikhale chofanana m’magulu onse opikisanawo. Nthaŵi zambiri opikisanawo amadziŵika chifukwa chochita misonkhano yokopa anthu ndipo wopeza mavoti ambiri ndi amene amalandira udindowo. Kuika munthu paudindo mwateokalase si kumaloŵetsa iliyonse ya njira zimenezi. Maudindo ameneŵa sachokera kwa anthu; ndiponso sachokera ku mabungwe ena ake ovomerezeka mwalamulo. Ponena za kuikidwa kwake ndi Yesu komanso Yehova monga “mtumwi wa anthu amitundu,” mwachionekere Paulo anauza Agalatiya kuti anaikidwa ‘mosachokera kwa anthu, kapena mwa munthu, koma mwa Yesu Kristu, ndi Mulungu Atate, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.’​—Aroma 11:13; Agalatiya 1:1.

Kuikidwa ndi Mzimu Woyera

9. Kodi Machitidwe 20:28 amati chiyani za kuikidwa kwa oyang’anira achikristu?

9 Paulo anakumbutsa oyang’anira a ku Efeso kuti anaikidwa ndi Mulungu mwa mzimu woyera. Iye anati: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang’anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.” (Machitidwe 20:28, NW) Oyang’anira achikristu amenewo anafunikira kupitiriza kutsogoleredwa ndi mzimu woyera pogwira ntchito yawo monga abusa a gulu la nkhosa za Mulungu. Ngati mwamuna woikidwa pa udindo anapezeka kuti sanali kukwaniritsanso miyezo yaumulungu, m’nthaŵi yake mzimu woyera unali kutsogolera kuti achotsedwe paudindo wakewo.

10. Kodi m’motani mmene mzimu woyera umachitira mbali yofunika kwambiri poika munthu paudindo mwateokalase?

10 Kodi m’motani momwe mzimu woyera umachitira mbali yofunika kwambiri? Choyamba, malemba omwe amapereka ziyeneretso za oyang’anira auzimu anauziridwa ndi mzimu woyera. M’makalata ake omwe analembera Timoteo ndi Tito, Paulo anatchulamo miyezo yoti oyang’anira ndi atumiki otumikira akwaniritse. Zonse pamodzi, iye anatchula ziyeneretso zosiyanasiyana ngati 16. Mwachitsanzo, oyang’anira anayenera kukhala amuna opanda chilema, odzisunga, odziletsa, olongosoka, okonda kuchereza alendo, okhoza kuphunzitsa, ndi osonyeza chitsanzo chabwino monga mitu ya mabanja. Anafunikira kukhala osamwetsa mowa, anayenera kukhala osakonda ndalama, ndipo anafunikira kudziletsa. Mofananamo, amuna omwe anali kukalamira utumiki wotumikira nawonso anafunikira kukwaniritsa miyezo yapamwamba.​—1 Timoteo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9.

11. Kodi zina mwa ziyeneretso zimene amuna omwe akukalamira maudindo m’mpingo ayenera kukwanitsa ndi ziti?

11 Kupenda ziyeneretso zimenezi kumasonyeza kuti otsogolera pakulambira Yehova ayenera kukhala zitsanzo zabwino m’mikhalidwe yachikristu. Amuna omwe akukalamira maudindo mumpingo ayenera kusonyeza kuti mzimu woyera ukugwira ntchito pa iwo. (2 Timoteo 1:14) Ziyenera kuonekeratu kuti mzimu wa Mulungu ukubala zipatso mwa amuna ameneŵa za “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso (“kudziletsa,” NW).” (Agalatiya 5:22, 23) Zipatso zimenezi zidzaonekera momwe adzachitira ndi okhulupirira anzawo komanso ndi anthu ena. Inde, ena angapambane posonyeza zipatso zina za mzimu, pamene ena angakwaniritse ziyeneretso zina zofunika kwa oyang’anira pamlingo waukulu kwambiri. Komabe, zochita m’moyo wa tsiku ndi tsiku wa onse ofuna kuikidwa monga oyang’anira kapena atumiki otumikira, ziyenera kusonyeza kuti ali amuna auzimu, okwaniritsa zofunika za m’Mawu a Mulungu.

12. Kodi ndani amene tingati aikidwa ndi mzimu woyera?

12 Polimbikitsa ena kuti akhale omutsanza, Paulo ankachita zimenezo momasuka chifukwa chakuti iyeyo anali kutsanzira Yesu Kristu, yemwe ‘anatisiyira chitsanzo kuti tikalondole mapazi ake.’ (1 Petro 2:21; 1 Akorinto 11:1) Onse amene angakhale atakwaniritsa zofunika za m’Malemba, panthaŵi ya kuikidwa kwawo monga oyang’anira kapena atumiki otumikira, pamenepo tingati aikidwa ndi mzimu woyera.

13. Kodi mzimu woyera umathandiza motani awo amene akuvomereza amuna oti atumikire mumpingo?

13 Palinso chinthu china chomwe chimasonyeza momwe mzimu woyera umagwirira ntchito povomereza ndi kuika oyang’anira. Yesu anati ‘Atate wa kumwamba amapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye.’ (Luka 11:13) Chotero pamene akulu m’mpingo wathuwo akumana kuti avomereze amuna m’maudindo ampingo, amapempherera mzimu wa Mulungu kuti uwatsogolere. Zivomerezo zawozo zimazikika m’zomwe zatchulidwa m’Mawu ouziridwa a Mulungu, ndipo mzimu woyera umawathandiza kuzindikira ngati munthu amene akulingalira zomuika paudindoyo akukwaniritsadi ziyeneretso za m’Malemba. Awo amene akupereka zivomerezo sayenera kusonkhezeredwa ndi maonekedwe akunja, maphunziro a munthu, kapena maluso ake achibadwa. Chachikulu, iwo ayenera kuonetsetsa ngati munthuyo ali wauzimu, amene anthu ena mumpingomo adzamasuka kumufikira kuti afunsire uphungu wauzimu.

14. Kodi tikuphunziranji pa Machitidwe 6:1-3?

14 Ngakhale kuti bungwe la akulu limathandizana ndi oyang’anira oyendayenda povomereza abale kuti akhale akulu kapena atumiki otumikira, kuikidwa kwenikweni kumachitidwa mogwirizana ndi chitsanzo choperekedwa m’zaka za zana loyamba. Nthaŵi inayake, kunafunika amuna oyeneretsedwa mwauzimu oti asamalire ntchito yofunika. Bungwe lolamulira linapereka malangizo aŵa: “Yang’anani mwa inu amuna asanu ndi aŵiri a mbiri yabwino, odzala ndi mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.” (Machitidwe 6:1-3) Ngakhale kuti amuna omwe analandira malangizoŵa ndi amene anapereka zivomerezo, koma kuika kunachitidwa ndi amuna omwe anali ndi udindo wochita zimenezo ku Yerusalemu. Njira yofananayo imatsatiridwanso lerolino.

15. Kodi Bungwe Lolamulira limaphatikizidwa motani m’nkhani yoika amuna m’maudindo?

15 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova limaika mwachindunji mamembala onse a m’Komiti ya Nthambi. Polingalira kuti ndani amene angapatsidwe udindo waukulu ngati umenewu, Bungwe Lolamulira limakumbukira mawu a Yesu akuti: “Kwa munthu aliyense adam’patsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.” (Luka 12:48) Kuwonjezera pa kuika mamembala a Komiti ya Nthambi, Bungwe Lolamulira limaika akulu a pa Beteli ndi oyang’anira oyendayenda. Komabe, limapereka udindo umenewu kwa abale okhulupirika kuti aike anthu m’maudindo ena m’malo mwa Bungwe Lolamulira. Zimenezinso zili ndi chitsanzo cha m’Malemba.

‘Uike Akulu, Monga Ndinakulamulira’

16. N’chifukwa chiyani Paulo anasiya Tito ku Krete, ndipo zimenezi zikusonyezanji ponena za kuika anthu m’maudindo mwateokalase lerolino?

16 Paulo anauza wogwira naye ntchito Tito kuti: “Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe m’Krete, kuti ukalongosole zosoŵa, nukaike akulu m’midzi yonse, monga ndinakulamulira.” (Tito 1:5) Kenako Paulo anatchula ziyeneretso zomwe Tito anayenera kuyang’ana mwa amuna omwe akanayenerera kuikidwa m’maudindo amenewo. Chotero lerolino, Bungwe Lolamulira limaika abale oyeneretsedwa panthambi kuti aliimire poika akulu ndi atumiki otumikira. Abale omwe amachita zinthu moimira Bungwe Lolamulirawo amachita mosamala kwambiri kuti amvetse bwino ndi kutsatira malangizo a m’Malemba oikira anthu m’maudindo ameneŵa. Choncho, amuna oyenerera amaikidwa kuti atumikire m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse mwa malangizo ochokera ku Bungwe Lolamulira.

17. Kodi ofesi ya nthambi imayendetsa motani zivomerezo za kuikidwa kwa oyang’anira ndi atumiki otumikira?

17 Zivomerezo za kuikidwa kwa oyang’anira ndi atumiki otumikira akazitumiza ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society, amuna odziŵa bwino ntchito yawo amadalira mzimu wa Mulungu kuwatsogolera pamene akuika anthu m’maudindo. Amuna ameneŵa amadziŵa kuti akuŵerengeredwa mlandu, amazindikira kuti sayenera kufulumira kuika manja awo pa munthu aliyense, poopa kuti angagaŵane naye machimo ake.​—1 Timoteo 5:22.

18, 19. (a) Kodi ena amadziŵitsidwa motani za kuikidwa kwawo? (b) Kodi dongosolo lonse lovomereza ndi kuika munthu paudindo limachitika motani?

18 Ena amadziŵitsidwa za kuikidwa kwawo kudzera m’kalata yokhala ndi chidindo kuchokera ku bungwe lalamulo. Kalata yotereyi ingagwiritsidwe ntchito kuika abale oposa mmodzi m’maudindo mumpingo.

19 Kuikidwa kwa teokalase n’kochokera kwa Yehova kudzera mwa Mwana wake ndi njira yake ya Mulungu yooneka yapadziko lapansi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi Bungwe lake Lolamulira. (Mateyu 24:45-47) Dongosolo lonse la kuvomereza ndi kuika kumeneku limayendetsedwa, kapena kutsogoleredwa ndi mzimu woyera. Izi zili choncho chifukwa chakuti ziyeneretso zake zaperekedwa m’Mawu a Mulungu, omwe n’ngouziridwa ndi mzimu woyera, ndipo munthu woikidwayo amasonyeza kuti akubala zipatso za mzimu. Chotero, tiyenera kuona kuti mzimu woyera ndiwo umaika munthu pa udindo uliwonse. Monga momwe oyang’anira ndi atumiki otumikira ankaikidwira mwateokalase m’zaka za zana loyamba, lerolino amaikidwanso mwateokalase.

Kuyamikira Utsogoleri wa Yehova

20. N’chifukwa chiyani nafenso tili ndi malingaliro ngati a Davide olembedwa pa Salmo 133:1?

20 M’nthaŵi ino pamene zinthu zikupita patsogolo mwauzimu ndi kuwonjezeka kwa teokalase m’ntchito yolalikira Ufumu, tikuyamikira kwambiri kuti Yehova ndiye ali ndi udindo wonse woika oyang’anira ndi atumiki otumikira. Makonzedwe a m’Malemba ameneŵa amatithandiza kusungabe miyezo yapamwamba ya Mulungu ya chilungamo pakati pathu monga Mboni za Yehova. Komanso, mzimu wachikristu ndi kuyesetsa mwakhama kwa amuna ameneŵa kumachirikiza kwambiri mtendere wathu wodabwitsa ndi mgwirizano wathu monga atumiki a Yehova. Chotero ife, monga wamasalmo Davide, tasonkhezereka kufuula kuti: “Onani, n’kokoma ndi kokondweretsa ndithu kuti abale akhale pamodzi!”​—Salmo 133:1.

21. Kodi Yesaya 60:17 akukwaniritsidwa motani lerolino?

21 Tikuyamikiratu zedi kuti Yehova akutitsogolera kudzera m’Mawu ndi mzimu wake woyera! Ndipotu mawu a pa Yesaya 60:17 n’ngatanthauzo kwabasi. Mawuwo amati: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Pamene njira za teokalase zagwiritsidwa ntchito mwa dongosolo lake ndi mopita patsogolo pakati pa Mboni za Yehova, taona madalitso amtunduwu m’gulu lonse la Mulungu la padziko lapansi.

22. Kodi moyenerera tikuyamikira chiyani, ndipo kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji?

22 Tikuyamikira kwambiri makonzedwe ateokalase omwe akugwira ntchito pakati pathu. Ndipo tikuthokoza kwambiri ntchito yovuta koma yokhutiritsa yomwe oyang’anira ndi atumiki otumikira oikidwa mwateokalase akuigwira. Tikutamanda ndi mtima wonse Atate wathu wachikondi wakumwamba, yemwe watipatsa chuma chauzimu ndipo watipatsa madalitso ochuluka. (Miyambo 10:22) Chotero, titsimikizetu mtima kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova. Koposa zonse, tiyeni tipitirizebe kutumikira limodzi mogwirizana kaamba ka ulemu, chitamando, ndi ulemerero wa dzina lalikulu ndi loyera la Yehova.

Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti oyang’anira ndi atumiki otumikira amaikidwa mwateokalase, osati mwademokalase?

• Kodi amuna amaudindo achikristu amaikidwa motani ndi mzimu woyera?

• Kodi Bungwe Lolamulira limaphatikizidwa motani poika oyang’anira ndi atumiki otumikira?

• Ponena za kuikidwa mwateokalase, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 15]

Akulu ndi atumiki otumikira ali ndi mwayi wotumikira monga oikidwa mwateokalase