Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yenderani Limodzi ndi Gulu la Yehova

Yenderani Limodzi ndi Gulu la Yehova

Yenderani Limodzi ndi Gulu la Yehova

‘Mulungu wa mtendere . . . [akupatseni, NW] . . . chinthu chilichonse chabwino, kuti muchite chifuniro chake.’​—AHEBRI 13:20, 21.

1. Kodi padziko lonse lapansi pali anthu angati, nanga ndi angati omwe ali m’zipembedzo zosiyanasiyana?

M’CHAKA cha 1999, chiŵerengero cha anthu padziko lonse lapansi chinakwana mabiliyoni asanu ndi limodzi! Buku lotchedwa The World Almanac likusonyeza kuti mwa chiŵerengero chimenechi anthu ngati 1,165,000,000 ndi Asilamu; 1,030,000,000 ndi Aroma Katolika; 762,000,000 ndi Ahindu; 354,000,000 ndi Abuda; 316,000,000 ndi Apulotesitanti; ndipo 214,000,000 ndi a zipembedzo za Orthodox.

2. Kodi tinganenenji za mkhalidwe wachipembedzo womwe ulipo lerolino?

2 Poona kugaŵanika ndi kusokonezeka kwa zipembedzo komwe kwafala lerolino, kodi tingati anthu mamiliyoni onseŵa akuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu? Ayi, “pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Kumbali ina, bwanji nanga za ubale wapadziko lonse wa atumiki a Yehova? (1 Petro 2:17) Kufufuza mosamalitsa kwasonyeza kuti ‘Mulungu wamtendere wawapatsa chinthu chilichonse chabwino kuti achite chifuniro chake.’​—Ahebri 13:20, 21.

3. Kodi chinachitika n’chiyani mu Yerusalemu pa Pentekoste mu 33 C.E., nanga n’chifukwa chiyani?

3 Mwachidziŵikire, chiŵerengero cha omwe akugwirizana ndi Mboni za Yehova si ndicho chizindikiro chodziŵira ngati akuyanjidwa ndi Mulungu; ndiponso kuchuluka kwa chiŵerengero si ndiko kumene kumakondweretsa Mulungu. Sanasankhe Aisrayeli chifukwa chakuti anali ‘ochuluka koposa mitundu yonse ya anthu.’ Kwenikweni, iwo anali ‘ochepa.’ (Deuteronomo 7:7) Koma chifukwa chakuti Israyeli anasonyeza kusakhulupirika, pa Pentekoste mu 33 C.E., Yehova anasamutsira chiyanjo chake ku mpingo watsopano wopangidwa ndi otsatira a Yesu Kristu. Iwo anali odzozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova ndipo mwachangu anapita kukauza ena za choonadi cha Mulungu ndi Kristu.​—Machitidwe 2:41, 42.

Kupitabe Patsogolo

4. N’chifukwa chiyani munganene kuti mpingo woyambirira wachikristu unkapita patsogolo mosalekeza?

4 M’zaka za zana loyamba, mpingo wachikristu unali kupitabe patsogolo mosaleka, kutsegula magawo atsopano, kupanga ophunzira, ndi kuwonjezera kumvetsa kwawo zifuniro za Mulungu. Akristu oyambirirawo anayendera limodzi ndi kuunika kwauzimu kovumbulidwa m’makalata ouziridwa ndi Mulungu. Polimbikitsidwa ndi atumwi komanso ena omwe anali kuwachezera, anakwaniritsa utumiki wawo. Zimenezi zalembedwa bwino lomwe m’Malemba Achigiriki Achikristu.​—Machitidwe 10:21, 22; 13:46, 47; 2 Timoteo 1:13; 4:5; Ahebri 6:1-3; 2 Petro 3:17, 18.

5. N’chifukwa chiyani gulu la Mulungu likupita patsogolo lerolino, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuyendera nalo limodzi?

5 Mofanana ndi Akristu oyambirirawo, Mboni za Yehova zamakono zawonjezeka kuchokera pamene zinayamba monga kagulu kakang’ono. (Zekariya 4:8-10) Kuyambira cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1800 pakhala umboni woonekeratu wakuti mzimu wa Mulungu uli pagulu lake. Chifukwa chakuti sitinadalire mphamvu za anthu, koma m’chitsogozo cha mzimu woyera, tapitirizabe kupita patsogolo m’kamvedwe kathu ka Malemba ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. (Zekariya 4:6) Tsopano popeza kuti tili “m’masiku otsiriza,” n’kofunika kuti tipitirizebe kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova lopita patsogololi. (2 Timoteo 3:1-5) Kuchita zimenezo kumatithandiza kukhalabe n’chiyembekezo champhamvu ndi kutenga nawo mbali m’ntchito yochitira umboni za Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu chimaliziro cha dongosolo lino la zinthu chisanafike.​—Mateyu 24:3-14.

6, 7. Kodi tidzapenda mbali zitatu ziti za mmene gulu la Yehova lapitira patsogolo?

6 M’gulu lathuli muli ena omwe anayamba kugwirizana ndi gulu la Yehova m’zaka za m’ma 1920, 1930, ndi m’ma 1940. M’zaka zoyambirira zimenezo, ndani wa ife amene akanayerekeza n’komwe kuti gululi lidzakula mochititsa chidwi ndi kupita patsogolo moŵirikiza mpaka m’nthaŵi yathu ino? Talingalirani za zinthu zikuluzikulu zomwe zachitika m’mbiri yathu yamakono! Ndithudi, n’kopindulitsa mwauzimu kukumbukira zomwe Yehova wachita kudzera mwa anthu ake olinganizika mwateokalase.

7 Kalero, Davide mawu anam’thera atasinkhasinkha ntchito zodabwitsa za Yehova. Iye anati: “Ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziŵerenga.” (Salmo 40:5) Nafenso timalephera kuziŵerenga. Timalephera kusimba ntchito zochuluka ndi zotamandika zomwe Yehova wazichita m’tsiku lathu. Komabe, tiyeni tipende mbali zitatu m’zimene gulu la Yehova lapita patsogolo: (1) kuunika kwauzimu kopita patsogolo, (2) utumiki wowongoleredwa ndi wofutukuka, komanso (3) kusintha kwapanthaŵi yake m’kachitidwe ka zinthu m’gulu.

Kuyamikira Kuunika Kwauzimu

8. Mogwirizana ndi Miyambo 4:18, kodi kuunika kwauzimu kwatithandiza kuzindikira chiyani chokhudza Ufumu?

8 Kunena za kuunika kwauzimu komkabe m’tsogolo, taonadi zoona zake za lemba la Miyambo 4:18. Lembali limati: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kumkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.” Ndifetu oyamikira kwabasi chifukwa taona kuunika kwauzimu kukumka kuŵaliraŵalirabe! Mfundo yaikulu pa msonkhano waukulu womwe unachitikira ku Cedar Point, Ohio, m’chaka cha 1919, inali Ufumu wa Mulungu. Yehova akugwiritsa ntchito Ufumuwo kuyeretsa dzina lake ndi kukweza ulamuliro wake. Kwenikweni, kuunika kwauzimu kwatithandiza kuzindikira kuti kuchokera ku Genesis kukafika ku Chivumbulutso, Baibulo limachitira umboni chifuno cha Yehova choyeretsa dzina lake kudzera mu Ufumu wolamulidwa ndi Mwana wake. Mmenemo muli chiyembekezo champhamvu kwa onse okonda chilungamo.​—Mateyu 12:18, 21.

9, 10. M’zaka za m’ma 1920, kodi anaphunzira chiyani ponena za Ufumu ndi za magulu aŵiri otsutsana, ndipo zimenezi zathandiza motani?

9 Pamsonkhano winanso waukulu ku Cedar Point m’chaka cha 1922, mlendo wapadera, J. F. Rutherford, analimbikitsa anthu a Mulungu kuti “lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi Ufumu wake.” M’nkhani yakuti “Kubadwa kwa Mtundu,” yofalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925, munali chidziŵitso chakuya chokhudza maulosi omwe ananeneratu za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu m’chaka cha 1914. Zinadziŵikanso m’zaka za m’ma 1920 kuti pali magulu aŵiri otsutsana​—la Yehova ndi la Satana. Nkhondo ili m’kati pakati pa aŵiriŵa, ndipo tidzakhala m’gulu lopambana kokha ngati tingayendere limodzi ndi gulu la Yehova.

10 Kodi kuunika kwauzimu kumeneku kwatithandiza motani? Popeza kuti Ufumu wa Mulungu ndi Mfumu Yesu Kristu sali mbali ya dziko lapansi, nafenso sitingakhale mbali ya dziko. Mwa kukhalabe olekana ndi dziko, timasonyeza kuti tili kumbali ya choonadi. (Yohane 17:16; 18:37) Tikamaona mavuto osaneneka omwe akuta dongosolo loipali, tilitu oyamikira zedi kuti sitili mbali ya gulu la Satana! Ndipotu ndife amwayi kwabasi pokhala otetezeka mwauzimu m’kati mwa gulu la Yehova!

11. Ndi dzina liti la m’Malemba lomwe anthu a Mulungu anatenga m’chaka cha 1931?

11 Pamsonkhano waukulu womwe unachitikira ku Columbus, Ohio, m’chaka cha 1931, lemba la Yesaya 43:10-12, linagwiritsidwa ntchito moyenera. Ophunzira Baibulo anatenga dzina lapadera lakuti Mboni za Yehova. Ndi mwayitu waukulu kwabasi kudziŵikitsa dzina la Mulungu kotero kuti ena akaitanire padzinalo ndi kudzapulumuka!​—Salmo 83:18; Aroma 10:13.

12. N’kuunika kotani kwauzimu kokhudza khamu lalikulu komwe kunaperekedwa mu 1935?

12 Zaka za m’ma 1930 zisanafike, ambiri mwa anthu a Mulungu sanali otsimikizira kwenikweni za chiyembekezo chawo cha moyo wam’tsogolo. Ena ankaganiza za moyo wakumwamba koma ankachita chidwi kwambiri ndi ziphunzitso za m’Baibulo za dziko lapansi la paradaiso. Pamsonkhano waukulu womwe unachitikira ku Washington, D.C., m’chaka cha 1935, zinali zochititsa chidwi kumva kuti namtindi wa anthu, kapena kuti khamu lalikulu, la pa Chivumbulutso chaputala 7, ndi gulu lokhala ndi chiyembekezo cha moyo wapadziko lapansi pompano. Chiyambire nthaŵiyo, kusonkhanitsa khamu lalikulu kwapita patsogolo mofulumira kwambiri. Kodi sitikuyamikira kuti khamu lalikulu tikutha kulidziŵa bwino? Kuona anthu ochuluka akusonkhanitsidwa kuchokera m’mitundu, m’mafuko, ndi m’zinenero zonse kumatisonkhezera kugwira ntchito mwachamuna pamene tikuyendera limodzi ndi gulu la Yehova.

13. Ndi nkhani yaikulu iti yomwe inagogomezedwa pa msonkhano waukulu ku St. Louis mu 1941?

13 Nkhani yaikulu yomwe ikukhudza mtundu wa anthu anaigogomeza pamsonkhano waukulu ku St. Louis, Missouri, m’chaka cha 1941. Ndi yokhudza ulamuliro kapena kuti ufumu wam’chilengedwe chonse. Imeneyi ndi nkhani yomwe iyenera kuthetsedwa mwamsanga, ndipo tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha pamene zimenezo zidzachitike likuyandikira mofulumira ndithu! Nkhani inanso yomwe inagogomezedwa mu 1941 inali nkhani yofanana nayo yokhudza kukhulupirika, yomwe imalola aliyense wa ife kusonyeza mbali yomwe ali mu ufumu wa Mulungu.

14. Pamsonkhano wa mayiko mu 1950, kodi anaphunzira chiyani ponena za akalonga otchulidwa pa Yesaya 32:1, 2?

14 Pamsonkhano wa mayiko wa mu 1950 ku New York City, akalonga a pa Yesaya 32:1, 2 analongosoledwa bwino kwambiri. Zinali zokhudza mtima pamene Mbale Frederick Franz anakamba nkhani imeneyi ndi kufotokoza kuti amene adzakhale akalonga m’dziko lapansi latsopano ali pakati pathu. Pamsonkhano umenewo ndi m’misonkhano inanso yotsatira, kuunika kwauzimu kwakhala kukuŵaliraŵalirabe. (Salmo 97:11) Tikuthokozatu zedi kuti njira yathu ‘ikunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuŵala kufikira usana woti mbe!’

Kupita Patsogolo Muutumiki Wathu

15, 16. (a) Kodi tinapita motani patsogolo muutumiki wathu m’zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930? (b) N’zofalitsa ziti zomwe zasonkhezera utumiki wachikristu m’zaka zaposachedwapa?

15 Njira yachiŵiri imene gulu la Yehova lapitira patsogolo ikukhudza ntchito yathu yaikulu​—kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20; Marko 13:10) Kuti tikwaniritse ntchito imeneyi, gululi lakhala likugogomeza mobwerezabwereza kufunika kofutukula utumiki wathu. M’chaka cha 1922, Akristu onse analimbikitsidwa kuchita nawo ntchito yolalikira. Unali udindo wa wina aliyense kuwalitsa kuunika kwake ndi kukhala ndi mbali m’kuchitira umboni choonadi. (Mateyu 5:14-16) Mu 1927, panakhala dongosolo lakuti Lamlungu lipatulidwe kukhala tsiku la utumiki wakumunda. Kuyambira mu February 1940, sizinali zachilendo kuona Mboni m’misewu ya m’magawo amalonda zikugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Consolation (tsopano Galamukani!).

16 Kabuku kotchedwa Model Study (Chitsanzo cha Phunziro) kanatulutsidwa m’chaka cha 1937, komwe kanagogomeza kwambiri kufunika kopanga maulendo obwereza kuti tiphunzitse anthu ena choonadi cha Baibulo. M’zaka zotsatira, ntchito yophunzitsa Baibulo inaikidwa patsogolo kwambiri. Mbali imeneyi ya utumiki inasonkhezeredwa kwambiri ndi kutuluka kwa buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” mu 1946 ndi buku lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya mu 1968. Tsopano, tikugwiritsa ntchito buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kuphunzira mabuku ameneŵa kumayala maziko abwino popanga ophunzira.

Kupita Patsogolo Mogwirizana ndi Kusintha M’kachitidwe ka Zinthu M’gulu

17. Mogwirizana ndi Yesaya 60:17, kodi gulu la Yehova lapita motani patsogolo?

17 Mbali yachitatu yomwe gulu la Yehova lapita patsogolo ikukhudza kuwongolera kachitidwe ka zinthu m’gulu. Malinga ndi Yesaya 60:17, Yehova analonjeza kuti: “M’malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m’malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m’malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m’malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” Potsatira ulosi umenewu, pachitika zinthu zina zothandiza kuwongolera uyang’aniro wa ntchito yolalikira Ufumu ndi kawetedwe ka nkhosa.

18, 19. Kodi n’kusintha kotani kwa kachitidwe ka zinthu komwe kwachitika m’gulu m’kupita kwa zaka?

18 M’chaka cha 1919 wotsogolera utumiki anaikidwa mumpingo uliwonse umene unali wokonzeka kuchita utumiki wakumunda. Zimenezi zinawonjezera changu cha ntchito ya m’munda. Masankho a akulu ndi otumikira m’mipingo anasiyidwa mu 1932. Kumeneku kunali kutsazikana ndi kuchita zinthu za mumpingo m’njira ya demokalase. Kusintha kwinanso kosaiŵalika kunachitika mu 1938 pamene atumiki onse a mumpingo anayamba kuikidwa mogwirizana kwambiri ndi makonzedwe a kuikidwa mwateokalase omwe mpingo woyambirira wachikristu unkatsata. (Machitidwe 14:23; 1 Timoteo 4:14) Mu 1972 oyang’anira ndi atumiki otumikira anaikidwa m’maudindo, monga momwe amuna otero ankaikidwira pakati pa Akristu oyambirira. M’malo moti mwamuna mmodzi yekha atumikire monga woyang’anira mpingo, Afilipi 1:1 limodzinso ndi malemba ena akusonyeza kuti awo amene ali ndi ziyeneretso za m’Malemba za oyang’anira ndi amene amapanga bungwe la akulu.​—Machitidwe 20:28; Aefeso 4:11, 12.

19 M’chaka cha 1975 makonzedwe akuti makomiti a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova aziyang’anira ntchito yapadziko lonse ya gulu la Mulungu anayamba kugwira ntchito. Makomiti a Nthambi anaikidwa kuti aziyang’anira ntchito m’magawo awo. Kuyambira pamenepo, pakhala kuyesetsa kufeŵetsa ntchito kulikulu ndi m’nthambi za Watch Tower Society pofuna ‘kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.’ (Afilipi 1:9, 10, NW) Maudindo amene abusa aang’ono a Kristu ali nawo akuphatikizapo kutsogolera ntchito yolalikira, kuphunzitsa mumpingo, ndi kuŵeta bwino gulu la nkhosa za Mulungu.​—1 Timoteo 4:16; Ahebri 13:7, 17; 1 Petro 5:2, 3.

Utsogoleri Wachamuna wa Yesu

20. Kodi kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova kumafuna kuti tizindikire chiyani ponena za malo a Yesu?

20 Kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova lopita patsogolo kumafuna kuti tizindikire udindo wopatsidwa ndi Mulungu wa Yesu Kristu monga “mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:22, 23) Mfundo inanso yofunika ndi ya pa Yesaya 55:4, pomwe timaŵerenga kuti: “Taonani, [ine Yehova] ndam’pereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.” Ndithudi Yesu akuidziŵa bwino ntchito yotsogolera. Akudziŵanso nkhosa zake ndi zochita zawo. Kwenikweni, atapenda mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiyamina, iye akunena kasanu konse kuti: “Ndidziŵa ntchito zako.” (Chivumbulutso 2:2, 19; 3:1, 8, 15) Yesu amadziŵanso zosoŵa zathu, monga momwe Atate wake, Yehova, amachitira. Asanapereke Pemphero Lachitsanzo, Yesu anati: “Atate wanu adziŵa zomwe muzisoŵa, inu musanayambe kupempha iye.”​—Mateyu 6:8-13.

21. Kodi utsogoleri wa Yesu ukuchitidwa motani mumpingo wachikristu?

21 Kodi utsogoleri wa Yesu ukuchitidwa motani? Njira imodzi, akutsogolera kudzera mwa oyang’anira achikristu, “mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8) Chivumbulutso 1:16 chikusonyeza oyang’anira odzozedwa ali m’dzanja lamanja la Kristu, akutsogoleredwa ndi iye. Lerolino, Yesu akutsogolera makonzedwe okhala ndi akulu, mosasamala kanthu kuti amuna ameneŵa ali n’chiyembekezo chopita kumwamba kapena chapadziko lapansi. Monga momwe nkhani yoyamba ija yafotokozera, n’ngoikidwa ndi mzimu woyera mogwirizana ndi ziyeneretso za m’Malemba. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) M’zaka za zana loyamba, gulu la amuna achikulire m’Yerusalemu linapanga bungwe lolamulira lomwe linali kuyang’anira mipingo ndi ntchito yolalikira Ufumu. Njira yofananayo ikutsatiridwa lerolino m’gulu la Yehova.

Yenderani Limodzi!

22. Kodi Bungwe Lolamulira limapereka thandizo lotani?

22 Zinthu zonse zokhudza Ufumu padziko lapansi zaikizidwa m’manja mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” woimiridwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. (Mateyu 24:45-47) Udindo waukulu wa Bungwe Lolamulira ndiwo kupereka malangizo auzimu ndi utsogoleri m’mpingo wachikristu. (Machitidwe 6:1-6) Komabe, olambira anzathu akagwa m’tsoka lachilengedwe, Bungwe Lolamulira limapempha bungwe limodzi lalamulo kapena angapo kuti apereke thandizo ndi kukonzetsa kapena kumanga nyumba zowonongeka komanso Nyumba za Ufumu. Ngati Akristu ena akusautsidwa kapena kuzunzidwa, kuyesetsa kumakhalapo kuti alimbikitsidwe mwauzimu. Ndiponso “m’nthaŵi ya mavuto,” amachita zilizonse zotheka kuti ntchito yolalikira ipitebe patsogolo.​—2 Timoteo 4:1, 2, NW.

23, 24. Mosasamala kanthu zomwe zimagwera anthu ake, kodi Yehova amapereka chiyani nthaŵi zonse, ndipo kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji?

23 Kaya ndi mkhalidwe wotani umene ungagwere anthu a Yehova, iye amaperekabe chakudya chauzimu ndi utsogoleri wofunikira nthaŵi zonse. Mulungu amazindikiritsanso ndi kupereka nzeru kwa abale audindo kuti akonzekere kupita patsogolo ndi kuwongolera kowonjezeka m’gulu lateokalaseli. (Deuteronomo 34:9; Aefeso 1:16, 17) Zivute zitani, Yehova amapereka zonse zimene tikufunikira kuti tikwaniritse ntchito yomwe tapatsidwa yopanga ophunzira ndi kuchita utumiki wathu padziko lonse lapansi.​—2 Timoteo 4:5.

24 Tili n’chikhulupiriro chonse kuti Yehova sadzasiya anthu ake okhulupirika; adzaŵapulumutsa pa “chisautso chachikulu” chikudzachi. (Chivumbulutso 7:9-14; Salmo 94:14; 2 Petro 2:9) Tili ndi zifukwa zabwino zokhalirabe ndi chidaliro chomwe tinali nacho pachiyambi mpaka titafika kumapeto. (Ahebri 3:14) Chotero titsimikizetu mtima kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova.

Kodi Mungayankhe Motani?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti gulu la Yehova likupitabe patsogolo?

• Kodi pali umboni wotani wakuti anthu a Mulungu akusangalala ndi kuunika kwauzimu komkabe m’tsogolo?

• Kodi kusintha kwakhalapo motani muutumiki wachikristu?

• Kodi n’kusintha kwapanthaŵi yake kotani komwe kwachitika m’kayendetsedwe ka zinthu m’gulu la atumiki a Yehova?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Mofanana ndi Davide, nafenso sitingathe kuŵerenga ntchito zonse zodabwitsa za Yehova

[Chithunzi patsamba 18]

Nkhosa za Mulungu zapindula ndi kusintha kwa panthaŵi yake kwa kayendetsedwe ka zinthu m’gulu