Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dokotala wa Maso Afesa Mbewu

Dokotala wa Maso Afesa Mbewu

Dokotala wa Maso Afesa Mbewu

Kodi khama la dokotala wa maso ku Lviv m’dziko la Ukraine, likukhudzana motani ndi kukhazikitsidwa kwa mpingo wachirasha wa Mboni za Yehova ku Haifa m’dziko la Israel, pamtunda wa makilomita 2,000, kudutsa mayiko angapo? Nkhani imeneyi ikusonyeza kuona kwa mawu a m’Baibulo a pa Mlaliki 11:6: “Mamaŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino.”

NKHANI yathu ikuyambira mu 1990 pamene Ella, mtsikana wachiyuda anali kukhala ku Lviv. Ella ndi banja lawo, anali kukonzekera kusamukira ku Israel. Atatsala pang’ono kunyamuka, Ella anafunika kukaonana ndi dokotala wa maso yemwe anali wa Mboni za Yehova. Panthaŵiyo, ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Ukraine. Komabe, dokotalayo sanazengereze kukambirana ndi Ella zikhulupiriro zake za m’Baibulo. Ella anadabwa kumva kuti Mulungu ali ndi dzina. Zimenezi zinam’chititsa chidwi, ndipo anakambirana za m’Baibulo bwino lomwe.

Ella anasangalala kwambiri ndi kukambiranako ndipo anapempha kuti adzateronso mlungu wotsatira ndi m’tsogolomo mwake. Chidwi chake chinali kukula, koma panali vuto. Nthaŵi yoti banja lawo lisamukire ku Israel inali kuyandikira msanga. Panali zambiri zoti Ella aphunzire! Kuti agwiritse ntchito mopindulitsa nthaŵi yotsalayo, anapempha kuti aziphunzira Baibulo tsiku lililonse mpaka atanyamuka. Ngakhale kuti Ella sanapitireze kuphunzira atafika ku Israel, mbewu ya choonadi inali itamera mu mtima mwake. Pakutha pa chaka, anali akuphunziranso Baibulo mwakhama.

Nkhondo inayamba ku Persian Gulf, ndipo dziko la Iraq linali kuponya mabomba ku dziko la Israel. Nkhani imeneyi ndiyo inali kukambidwa kaŵirikaŵiri. Tsiku lina mu golosale, Ella anamva banja lina longobwera kumene lolankhula Chirasha, likukambirana nkhaniyi. Ngakhale kuti iye anali kuphunzirabe Baibulo, anakumana ndi banjalo ndi kukambirana nalo za lonjezo la Baibulo la dziko lamtendere. Zotsatira zake zinali zakuti, agogo aakazi a Galina; amayi Natasha; ana awo wamwamuna Sasha (Ariel); ndi wamkazi Ilana, onse anayamba kuphunzira Baibulo pamodzi ndi Ella.

Ngakhale kuti anakumana ndi ziyeso zambiri, Sasha ndiye anali woyamba kubatizidwa m’banjamo. Mosaganizira kuti iye anali wophunzira wanzeru kwambiri, anachotsedwa sukulu chifukwa chakuti chikumbumtima chake chachikristu, sichikanamulola kuchita nawo maphunziro a zankhondo omwe anali mbali ya maphunziro pa sukulupo. (Yesaya 2:2-4) Mlandu wa Sasha unafika ku Bwalo Lalikulu la milandu la Israel ku Jerusalem lomwe mosangalatsa, linalamula kuti Sasha abwezeretsedwe pa sukulu kuti amalize temu ya sukulu. Mlanduwu unafalitsidwa m’dziko lonselo. Chifukwa cha zimenezi, Aisrayeli ambiri anadziŵa zikhulupiriro za Mboni za Yehova. *

Atangomaliza sukulu yake yasekondale, Sasha anayamba utumiki wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova. Tsopano, iye ndi mpainiya wapadera ndiponso mkulu mumpingo. Mlongo wakenso wamng’ono, Ilana anayamba utumiki wanthaŵi zonse. Amayi awo ndi agogo awo aakazi, anabatizidwa monga Mboni. Mbewu yomwe dokotala wa maso anafesa inali kuberekabe zipatso!

Ella anapitabe patsogolo mwauzimu ndipo posapita nthaŵi anayamba kulalikira nyumba ndi nyumba. Pakhomo loyambirira, anakumana ndi Faina yemwe anali atangobwera kumene kuchokera ku Ukraine. Faina anali kuvutika ndi maganizo. Pambuyo pake Ella anadzadziŵa kuti atatsala pang’ono kugogoda pakhomo pa Faina, mayi wovutika maganizo ameneyu anali akupemphera kwa Mulungu kuti: “Sindikukudziŵani, koma ngati mukundimva, ndithandizeni.” Iye ndi Ella, anakambirana zolimbikitsa. Faina anafunsa mafunso ambiri ndipo mosamala, anaganizira mayankho a Ella. M’kupita kwa nthaŵi, anakhutira kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Anasintha ndandanda yake ya maphunziro a ku yunivesite n’cholinga choti azikhala ndi nthaŵi yokwanira ya kumpingo ndi ku ntchito yolalikira. M’mwezi wa May 1994, Faina anabatizidwa. Nayenso anayamba utumiki wa upainiya, ndipo anali kudzithandiza mwa kugwira ntchito ya maola ochepa ya makompyuta.

Pamene anali kulalikira mu November 1994, mwadzidzidzi Ella anafooka kwambiri. Anapita kuchipatala komwe atamuyeza, anapeza kuti anali ndi chilonda m’mimba chomwe chinali kutulutsa magazi. Pofika madzulo, mlingo wa hemoglobin m’magazi a Ella unali utachepa kufika pa 7.2. Mkulu mu mpingo wa Ella, yemwe ndi tcheyamani wa Komiti Yolankhulana ndi Chipatala (HLC), anapatsa madokotala njira zambirimbiri zochiritsira popanda kugwiritsa ntchito magazi. * Opaleshoni inachitika bwinobwino popanda kumuika magazi ndipo Ella anachira bwinobwino.​—Machitidwe 15:28, 29.

Karl, dokotala wa Ella yemwe ndi m’Yuda wobadwira ku Germany, anachita chidwi kwambiri. Kenako anakumbukira kuti makolo ake, omwe anapulumuka chipululutso cha Nazi, anadziŵa Mboni za Yehova ku ndende. Karl anafunsa mafunso ambiri. Ngakhale kuti anali wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yake ya udokotala, Karl anapatula nthaŵi kuti aziphunzira Baibulo nthaŵi zonse. M’chaka chotsatira anali kupezeka pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu yachikristu.

Kodi chachitika n’chiyani ndi mbewu yofesedwa ndi dokotala wa maso uja? Taona kale zomwe zinachitikira Sasha ndi banja lake. Kunena za Ella, iye ndi mpainiya wapadera. Mwana wake Eina, anayamba ntchito yake ya upainiya atangomaliza sukulu ya sekondale. Nayenso Faina ndi mpainiya wapadera. Kunena za Karl dokotala wa matenda a akazi, tsopano ndi Mboni yobatizidwa ndiponso mtumiki wotumikira, akugawira odwala ake ndi anthu ena mphamvu yochiritsa ya choonadi cha Baibulo.

Kagulu kakang’ono ka anthu olankhula Chirasha komwe kanayamba monga mbali ya mpingo wachihebri wa Haifa, tsopano wakhala mpingo wokangalika wa Chirasha womwe uli ndi ofalitsa Ufumu oposa 120. Chifukwa china cha kuwonjezereka kumeneku n’chakuti dokotala wa maso ku Lviv anagwiritsa ntchito mwayi womwe anali nawo kufesa mbewu!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Kuti mudziŵe zambiri, onani Galamukani!, ya Chingelezi ya November 8, 1994 masamba 12-15.

^ ndime 9 Makomiti Olankhulana ndi Chipatala (HLC), amaimira Mboni za Yehova padziko lonse, ndi kuthandiza kukhazikitsa mgwirizano pakati pa odwala ndi achipatala. Amaperekanso njira zina zochiritsira zopezeka pa kufufuza kwatsopano kwa zamankhwala.

[Mapu patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

UKRAINE

ISRAEL

[Mawu a Chitunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Zithunzi patsamba 30]

Ella ndi mwana wake Eina

[Chithunzi patsamba 31]

Gulu lachimwemwe la Mboni zolankhula Chirasha ku Haifa. Kuyambira kumanzere kupita kumanja: Sasha, Ilana, Natasha, Galina, Faina, Ella, Eina, ndi Karl