Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwapanga Choonadi Kukhala Chanuchanu?

Kodi Mwapanga Choonadi Kukhala Chanuchanu?

Kodi Mwapanga Choonadi Kukhala Chanuchanu?

“Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”​—AROMA 12:2.

1, 2. N’chifukwa chiyani kukhala Mkristu weniweni kuli kovuta lerolino?

KUKHALA Mkristu weniweni m’masiku otsiriza ano​—“nthaŵi zoŵaŵitsa” zino​—si chinthu chapafupi. (2 Timoteo 3:1) Mfundo n’njakuti, munthu ayenera kugonjetsa dziko kuti athe kutsatira chitsanzo cha Kristu. (1 Yohane 5:4) Kumbukirani zomwe Yesu ananena zokhudza njira yachikristu: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.” Iye ananenanso kuti: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku, nanditsate Ine.”​—Mateyu 7:13, 14; Luka 9:23.

2 Tikapeza njira yopapatiza ya kumoyo, chothetsa nzeru china chachikristu ndicho kukhalabe m’njirayo. N’chifukwa chiyani chimenecho chili chothetsa nzeru? N’chifukwa chakuti kudzipatulira kwathu ndi ubatizo wathu zinam’sonkhezera Satana kulunjikitsa misampha yake yamachenjera pa ife. (Aefeso 6:11) Amaona zoofoka zathu ndi kufunafuna njira zoti agwiritse ntchito kufooka kwathuko poyesa kuipitsa mkhalidwe wathu wauzimu. Ndiiko komwe, anayesa kugwetsa Yesu, choncho kodi ife angangotisiya?​—Mateyu 4:1-11.

Misampha Yaukatswiri ya Satana

3. Kodi Satana anaika motani chikayikiro m’malingaliro a Hava?

3 Msampha umodzi womwe Satana amagwiritsa ntchito ndiwo kuika chikayikiro m’malingaliro athu. Amayang’ana mbali zofooka m’zovala zathu zankhondo yauzimu. Pachiyambi penipeni, anagwiritsa ntchito machenjera amenewo kwa Hava, pomufunsa kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” (Genesis 3:1) M’mawu ena, Satana anali kunena kuti, ‘kodi n’zothekadi kuti Mulungu akanachita kukuletsani choncho? N’zoona Mulungu angakuletseni chinthu chabwino ngati chimenecho? Oo! Mulungu anadziŵa kuti tsiku lomwe mudzadya chipatso cha mtengo umenewu maso anu adzatseguka ndithu ndipo mudzafanana ndi Mulungu, mudzadziŵa zabwino ndi zoipa!’ Satana anadzala mbewu ya chikayikiro ndipo anayembekezera kuti imere.​—Genesis 3:5.

4. Kodi ena lerolino angamakayikire za chiyani?

4 Kodi Satana amagwiritsa ntchito motani machenjera ameneŵa lerolino? Ngati titanyalanyaza kuŵerenga Baibulo, phunziro lathu laumwini, mapemphero athu, komanso utumiki wathu wachikristu ndi misonkhano, ndiye kuti tidzapereka mpata woti ena asonkhezere zikayikiro mwa ife. Mwachitsanzo: “Kodi timadziŵa motani kuti ichi n’choonadi monga momwe Yesu anaphunzitsira?” “Kodi ano alidi masiku otsiriza? Ndiiko komwe, tili kale m’zaka za m’ma 2000.” Kodi Armagedo ilidi pafupi, kapena kodi idakali kutali?” Ngati kukayikira kwamtunduwu kungabuke, kodi tingachitenji kuti tikuthetse?

5, 6. Kodi tiyenera kuchitanji ngati titayamba kukayikira?

5 Yakobo anapereka uphungu wothandiza pamene analemba kuti: “Koma wina wa inu ikam’soŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzam’patsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wa mitima iŵiri akhala wosinkhasinkha pa njira zake zonse.”​—Yakobo 1:5-8.

6 Chotero, kodi tiyenera kuchitanji? Ngati pali mafunso kapena kukayikira kulikonse, tiyenera ‘kupempha kwa Mulungu’ m’pemphero kuti atipatse chikhulupiriro ndi kutithandiza kuzindikira komanso kuti alimbikitse khama lathu lochita phunziro laumwini. Tingapemphenso thandizo kwa ena omwe ali olimba m’chikhulupiriro, osakayika konse kuti Yehova adzatipatsa chichirikizo chofunikacho. Yakobo anatinso: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu. Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” Inde, kukayikira kwathuko kudzatha pamene tikuyandikira kwa Mulungu kudzera m’phunziro ndi pemphero.​—Yakobo 4:7, 8.

7, 8. Kodi ndi mfundo zina ziti zomwe tingadziŵire kulambira komwe Yesu anaphunzitsa, ndipo ndani omwe amakwaniritsa mfundo zimenezo?

7 Mwachitsanzo, titenge funso lakuti: Kodi timadziŵa motani kuti kulambira kwathu ndiko kumene Yesu anaphunzitsa? Kuti tiyankhe funso limeneli, kodi tiyenera kupenda mfundo ziti? Baibulo limafotokoza kuti Akristu oona ayenera kukhala ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. (Yohane 13:34, 35) Ayenera kuyeretsa dzina la Mulungu, lakuti Yehova. (Yesaya 12:4, 5; Mateyu 6:9) Ndipo ayenera kudziŵikitsa dzina limenelo.​—Eksodo 3:15; Yohane 17:26.

8 Chizindikiro chinanso cha kulambira koona ndicho kulemekeza Mawu a Mulungu, Baibulo. Ilo ndi buku lapadera lomwe limavumbula umunthu wa Mulungu ndi zifuno zake. (Yohane 17:17; 2 Timoteo 3:16, 17) Kuwonjezera pamenepo, Akristu oona amalengeza Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokhacho cha munthu cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. (Marko 13:10; Chivumbulutso 21:1-4) Saloŵerera m’ndale zachinyengo zadzikoli ndi njira yake yoipitsitsa ya moyo. (Yohane 15:19; Yakobo 1:27; 4:4) Ndani lerolino omwe akwaniritsa zimenezi? Umboni ukusonyeza kuti pali yankho limodzi lokha​—Mboni za Yehova.

Bwanji Ngati Tikukayikirabe?

9, 10. Kodi tingachitenji kuti tithetse kukayikira ngati kukupitirizabe?

9 Bwanji ngati tikuona kuti tikukayikira kwambiri? Kodi pamenepa tingachitenji? Mfumu yanzeru Solomo ikupereka yankho lakuti: ‘Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kupfuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kum’dziŵadi Mulungu.’​Miyambo 2:1-5.

10 Amenewo si malingaliro odabwitsa kodi? Ngati tikufunitsitsa kutchera khutu ku nzeru ya Mulungu moona mtima, ‘tidzam’dziŵadi Mulungu.’ Inde, tingam’dziŵedi Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse ngati tikufunitsitsa kulandira ndi kusunga mawu ake. Zimenezo zikutanthauza kutembenukira kwa Yehova m’pemphero komanso mwa phunziro laumwini. Chuma chobisika cha Mawu ake chingathetse kukayikira kulikonse ndi kutithandiza kuona kuŵala kwa choonadi.

11. Kodi mnyamata wa Elisa anasonyeza motani kukayikira?

11 Chitsanzo chabwino cha momwe pemphero linathandizira mtumiki wamantha ndi wokayikira wa Mulungu tingachipeze pa 2 Mafumu 6:11-18. Mnyamata wa Elisa sanathe kuona zinthu mwauzimu. Sanathe kuzindikira kuti panali gulu lankhondo lakumwamba lomwe likanatha kuthandiza mneneri wa Mulungu, amene anali atazingidwa ndi gulu la nkhondo la Aaramu. Mwamantha mnyamatayo anafuula nati: “Kalanga ine, mbuye wanga! tichitenji?” Kodi Elisa anati bwanji? “Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Koma kodi mnyamatayo akanakhulupirira motani? Gulu lankhondo lakumwambalo sanali kuliona.

12. (a) Kodi kukayikira kwa mnyamatayo kunatha bwanji? (b) Kodi tingathetse motani kukayikira kulikonse kumene tingakhale nako?

12 “Elisa anapemphera, nati, Yehova, mum’tsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anam’tsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magareta amoto akum’zinga Elisa.” Pachochitikacho Yehova anam’chititsa mnyamatayo kuona magulu ankhondo akumwamba omwe anali kutetezera Elisa. Komabe, sitiyenera kuyembekezera thandizo laumulungu lofananalo lerolino. Kumbukirani kuti mnyamata wa mneneri uja analibe Baibulo lathunthu lomwe akanatha kuphunzira kuti alimbitse chikhulupiriro chake. Ife tili nalo Baibulo. Ngati titaligwiritsa ntchito mokwanira, chikhulupiriro chathu chingalimbitsidwe mofananamo. Mwachitsanzo, tingathe kulingalira za nkhani zambiri zomwe zimafotokoza Yehova ali m’bwalo lake lamilandu kumwamba. Zimenezi zidzachotsa kukayikira kulikonse koti Yehova ali ndi gulu lakumwamba lothandiza atumiki ake m’ntchito yophunzitsa yapadziko lonse lerolino.​—Yesaya 6:1-4; Ezekieli 1:4-28; Danieli 7:9, 10; Chivumbulutso 4:1-11; 14:6, 7.

Chenjerani ndi Misampha ya Satana!

13. Kodi Satana amayesa kufooketsa kagwiridwe kathu ka choonadi m’njira ziti?

13 Kodi njira zina za Satana zofooketsera uzimu wathu ndiponso kugwiritsitsa kwathu choonadi ndi ziti? Imodzi mwa njirazi ndiyo chiwerewere, chamtundu uliwonse mwa mitundu yake yonse. M’dziko lamakono lotchuka ndi chiwerewereli, chomwe amachitcha chibwenzi pakati pa mwamuna ndi mkazi (kutanthauza chimasomaso) kapena kuti kugonana usiku umodzi wokha (kuchita dama mosalabadira chilichonse) kwangokhala chizoloŵezi chatsiku ndi tsiku ku mbadwo wongofuna zosangalatsawu. Mafilimu, ma TV, ndi mavidiyo amachirikiza kwambiri moyo umenewu. Zolaula zafala kwambiri m’zoulutsira nkhani, makamaka pa Intaneti. Oonerera zimenezi pofuna kungodziŵa zomwe zimachitika ali pachiyeso.​—1 Atesalonika 4:3-5; Yakobo 1:13-15.

14. N’chifukwa chiyani Akristu ena agwa m’misampha ya Satana?

14 Akristu ena agonjera chidwi chawo chofuna kudziŵa zambiri ndipo aipitsa malingaliro ndi mitima yawo mwa kuonerera zithunzi zolaula zamaliseche kapena zosonyeza anthu akugonana. Alola kugwa m’misampha yokopa ya Satana. Kuchita zimenezo kaŵirikaŵiri kwachititsa ena kufooka mwauzimu. Otereŵa alephera kukhalabe ‘makanda m’choipa.’ Sanafikire pa ‘kukhala aakulu misinkhu mu luso la kuzindikira.’ (1 Akorinto 14:20) Chaka chilichonse, anthu masauzande ambiri amavulala chifukwa cholephera kutsatira malangizo komanso miyezo ya m’Mawu a Mulungu. Anyalanyaza kuvala ndi kukhalabe chivalire “zida zonse za Mulungu.”​—Aefeso 6:10-13; Akolose 3:5-10; 1 Timoteo 1:18, 19.

Sungani Chomwe Tili Nacho

15. N’chifukwa chiyani ena zingawavute kusunga choloŵa chawo chauzimu?

15 “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani,” anatero Yesu. (Yohane 8:32) Mboni zambiri zinachita kusiya moyo wawo wakale ndi kuchoka m’zipembedzo zawo zakale. Pachifukwa chimenecho, angazindikire mwamsanga ufulu womwe choonadi chimadzetsa. Mosiyana ndi zimenezo, achinyamata ena omwe aleredwa ndi makolo omwe ali kale m’choonadi zingawavute kusunga choloŵa chawo chauzimu. Sanakhalepo m’chipembedzo chonyenga kapena kukhala mbali yadzikoli lomwe limalimbikitsa kwambiri kufuna zosangalatsa, kumwa mankhwala osokoneza bongo, ndi chisembwere. Zotsatira zake zingakhale zakuti, iwoŵa angalephere kuona kusiyana koonekeratu kwa paradaiso wathu wauzimu ndi dziko loipa la Satanali. Ena angafike pogonjera chiyeso chakuti alaŵeko poizoni wadzikoli pofuna kuona zomwe akumanidwa!​—1 Yohane 2:15-17; Chivumbulutso 18:1-5.

16. (a) Kodi tingadzifunse mafunso ati? (b) Kodi tikuphunzitsidwa ndi kulimbikitsidwa kuchita chiyani?

16 Kodi timafunikira kutentha zala zathu kuti tidziŵe mmene zimaŵaŵira? Kodi sitingaphunzire kuopsa kwake kuchokera kwa ena omwe zinawachitikira? Kodi tifunikira kuchita ‘kukunkhulira m’thope’ la dzikoli kuti tione ngati tikumanidwa chinachake? (2 Petro 2:20-22) Petro anakumbutsa Akristu a m’zaka za zana loyamba omwe kale anali mbali ya dziko la Satana kuti: “Nthaŵi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka.” Ndithudi sitifunikira kugwa ‘m’kusefukira komwe kwa chitayiko’ chadzikoli kuti tione mmene moyo ungakhalire wopanda tanthauzo. (1 Petro 4:3, 4) M’malo mwake, timaphunzitsidwa miyezo ya Yehova yapamwamba ya makhalidwe ku Nyumba zathu za Ufumu, komwe ndi malo ophunzirirako Baibulo. Ndipo tikulimbikitsidwa kugwiritsa ntchito mphamvu zathu za kulingalira kusonyeza kuti tili ndi choonadi ndikuti tapanga choonadicho kukhala chathuchathu.​—Yoswa 1:8; Aroma 12:1, 2; 2 Timoteo 3:14-17.

Dzina Lathu Sichizindikiro Chabe

17. Kodi tingakhale motani Mboni za Yehova zogwira mtima?

17 Ngati titapanga choonadi kukhala chathuchathu, tidzayesetsa kuuza ena za choonadicho pa mpata uliwonse woyenera. Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu omwe sakusonyeza chidwi tidzayesa kuwaumiriza kuti adziŵe choonadi ayi. (Mateyu 7:6) Koma kuti sitidzazengereza kudzidziŵikitsa kuti ndife Mboni za Yehova. Ngati munthu angasonyeze chidwi pang’ono chabe mwa kufunsa funso lochokera pansi pamtima kapena mwa kulandira chofalitsa chothandiza pophunzira Baibulo, tidzakhala okonzeka kumuuza chiyembekezo chathu. Inde, zimenezi zingafune kuti nthaŵi zonse tizikhala ndi mabuku kulikonse komwe tingakhale​—kaya ndi kunyumba, kuntchito, kusukulu, kusitolo, kapena kumalo osangalalirako.​—1 Petro 3:15.

18. Kodi kudzidziŵikitsa bwino lomwe kuti ndife Akristu kungatipindulitse motani m’moyo wathu?

18 Mwa kudzidziŵikitsa kuti ndife Akristu, timalimbitsa chitetezo chathu pa kuukira kulikonse koipitsitsa kwa Satana. Ngati kuntchito kwathu kuli madyerero a tsiku lobadwa, Khirisimasi, kapena mpikisano wamwayi, anzathu ogwira nawo ntchito kaŵirikaŵiri adzati, “Musavutike naye ameneyu. Ndi wa Mboni za Yehova.” Pachifukwa chofananacho, anthu adzachepetsa kukamba nkhani zolaula ife tilipo. Chotero, kudziŵitsa ena za chikhulupiriro chathu chachikristu n’kopindulitsa kwambiri m’moyo wathu, monganso momwe mtumwi Petro anasonyezera kuti: “Ndipo ndani iye amene adzakuchitirani choipa, ngati muchita nacho changu chinthu chabwino? Komatu ngatinso mukamva zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, odala, inu.”​—1 Petro 3:13, 14.

19. Kodi tikudziŵa bwanji kuti tili m’kati mwenimweni mwa masiku otsiriza?

19 Phindu lina lopanga choonadi kukhala chathuchathu n’lakuti tidzakhala otsimikizira kuti ano alidi masiku otsiriza a dongosolo lino lazinthu. Tidzadziŵa kuti ambiri mwa maulosi a m’Baibulo akufika pachimake m’nthaŵi yathu ino. * Chenjezo la Paulo lakuti “masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa” latsimikizika mokwanira ndi zochitika zochititsa mantha m’zaka 100 zapitazi. (2 Timoteo 3:1-5; Marko 13:3-37) Nkhani ina m’nyuzipepala yaposachedwapa yosimba zochitika m’zaka za m’ma 1900 inali ndi mutu wakuti “Tidzaikumbukira Monga Nyengo ya Nkhalwe.” Nkhaniyo inati: “Chaka cha 1999 ndicho chinapambana pa kuphana mwaumbanda m’chigawo chotsiriza cha zaka 100 zotchuka kwambiri ndi kuphana mwa uchigaŵenga.”

20. Kodi ino ndi nthaŵi yoti tichitenji?

20 Ino si nthaŵi yozengereza. Madalitso a Yehova n’ngwoonekeratu m’ntchito yaikulu koposa yophunzitsa Baibulo yomwe ikuchitika padziko lonse monga umboni kumitundu yonse. (Mateyu 24:14) Pangani choonadi kukhala chanuchanu, ndipo uzani ena za choonadicho. Tsogolo lanu losatha likudalira pa zomwe mukuchita tsopano lino. Tikachita manja lende sitidzalandira madalitso a Yehova. (Luka 9:62) M’malo mwake, ino ndiyo nthaŵi yakuti ‘mukhale okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.’​—1 Akorinto 15:58.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Onani Nsanja ya Olonda, ya January 15, 2000, masamba 12-14. Ndime 13-18 zikupereka maumboni asanu ndi umodzi okhutiritsa osonyeza kuti takhala m’masiku otsiriza chiyambire 1914.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi tingathetse motani kukayikira?

• Kodi tingaphunzirenji kuchokera pa chitsanzo cha mnyamata wa Elisa?

• Kodi tiyenera kukhala atcheru nthaŵi zonse kuletsa ziyeso ziti zamakhalidwe?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kudzidziŵikitsa bwino lomwe kuti ndife Mboni za Yehova?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse ndi kupemphera zingatithandize kuthetsa kukayikira

[Chithunzi patsamba 11]

Masomphenya anathetsa kukayikira konse kwa mnyamata wa Elisa

[Chithunzi patsamba 12]

Timaphunzitsidwa miyezo yapamwamba ya Yehova ya makhalidwe pa Nyumba za Ufumu monga iyi ya ku Benin