Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupeŵa Zoopsa

Kupeŵa Zoopsa

Kupeŵa Zoopsa

“Palibe chinthu chomwe mungachite patsiku, ngakhale kugona, chomwe sichingaike moyo wanu pachiswe.”​—Magazini yotchedwa Discover.

MOYO aufanizira ndi kuyenda m’dera lomwe atcheramo mabomba chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri kuvulala kapena imfa zingachitike nthaŵi iliyonse mwadzidzidzi. Dziko lililonse lili ndi zinthu zomwe limada nazo nkhaŵa kwambiri. Zina mwa zinthuzi ndi monga ngozi zapamsewu, nkhondo zapachiŵeniŵeni, AIDS, kansa, matenda a mtima, ndiponso zina zambiri. Mwachitsanzo, mu Africa, kumwera kwa chipululu cha Sahara, AIDS ndiyo yapha anthu kwambiri. M’chaka chaposachedwapa, matendaŵa “apha anthu 2.2 miliyoni, kuŵirikiza kakhumi chiŵerengero cha anthu ofa pankhondo zonse zapachiŵeniŵeni mu Africa,” inatero magazini yotchedwa U.S. News & World Report.

Padakali pano, dziko lapansi likuwononga ndalama mabiliyoni ambiri pofuna kutalikitsa moyo komanso kuchepetsa matenda ndi kulumala. Mfundo zambiri zomwe dziko limalimbikitsa monga kudya bwino, kumwa moyenera, ndiponso maseŵera olimbitsa thupi, zingathandize ndithu. Komabe, pali gwero limodzi la chidziŵitso chodalirika pankhani iliyonse yofunika m’moyo lomwe lingakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo wabwino ndiponso wotetezeka kwambiri. Gwero limeneli ndi Baibulo. Ilo lili ndi mfundo zothandiza kuthetsa mavuto osiyanasiyana okhudza umoyo wathu ndiponso kakhalidwe kathu. N’zoona kuti Baibulo silimatchula mwatsatanetsatane zofunika kuchita pavuto lililonse. Komabe, limapereka mfundo zabwino koposa zotithandiza pankhani za kadyedwe, kulimbitsa thupi, kaganizidwe, kugonana, ndiponso kagwiritsidwe ntchito ka zoledzeretsa, fodya, mankhwala osokoneza bongo omwe amati amasangulutsa munthu, ndi zina zambiri.

Kwa anthu ambiri moyo n’ngwosautsanso chifukwa cha chuma chosadalirikachi. Pankhani imeneyinso, Baibulo limatithandiza kwambiri. Sikuti ilo limangolimbikitsa kaonedwe kabwino ka ndalama kokha kapena kugwiritsa bwino ntchito ndalamazo, komanso limafotokoza mmene tingakhalire antchito abwino kapena mabwana abwino. Mwachidule, Baibulo ndilo chitsogozo chabwino, osati pankhani zachuma kapena zaumoyo zokha, komanso pa moyo weniweniwo. Kodi mungakonde kudziŵa mmene Baibulo lingathandizire lerolino? Ngati ndi choncho, ŵerenganibe chonde.