Latvia Alabadira Uthenga Wabwino
Olengeza Ufumu Akusimba
Latvia Alabadira Uthenga Wabwino
BAIBULO limasonyeza bwino lomwe kuti ndi chifuno cha Mulungu kuti “anthu amtundu uliwonse apulumuke nafike pa chidziŵitso cholondola cha choonadi.” (1 Timoteo 2:4, NW) Anthu omwe kwazaka zambiri akhala akumanidwa mwayi womva uthenga wabwino, tsopano akuumva! Ku Latvia, monganso m’madera ena a dziko lapansi, anthu a misinkhu yonse ndiponso mitundu yosiyanasiyana akulabadira uthengawu, malinga ndi mmene zochitika zotsatirazi zikusonyezera.
• Mu Rēzekne, tawuni ya kum’maŵa kwa Latvia, mayi wina limodzi ndi mwana wake wamkazi wausinkhu wa unamwali anafunsira njira kwa mayi wina mu msewu. Atawalozera, mayiyo, yemwe anali wa Mboni za Yehova, anawaitanira ku misonkhano ya Mboni.
Chifukwa chakuti onse aŵiriwo, mayiyo limodzi ndi mwana wakeyo anali okonda zachipembedzo, iwo anaganiza zopita ku msonkhanowo. Ali panjira, iwo anapangana kuti ngati akapeze chinachake chosayenera pa msonkhanowo, akachoke nthaŵi yomweyo. M’malomwake, msonkhanowo unali wosangalatsa kwambiri moti maganizo oti achoke sanawabwerere n’komwe. Anavomera kuphunzira Baibulo ndipo anayamba kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse. M’miyezi itatu yokha, iwo anasonyeza kufunitsitsa kwawo kuti azichita nawo ntchito yolalikira ndiponso kuyembekezera kuti abatizidwe.
• Mu mzinda wina kumadzulo kwa Latvia, Mboni ina inakumana ndi Anna wazaka 85, amene anasonyeza chidwi chenicheni ndi kuvomera phunziro la Baibulo. Mwana wake wamkazi limodzi ndi abale ake anam’tsutsa kwambiri. Koma Anna sanalole zimenezo kapena ukalamba wake ndiponso kufooka kwa thanzi lake kum’lepheretsa kupitiriza kuphunzira Baibulo.
Tsiku lina, Anna anauza mwana wake wamkazi kuti akukabatizidwa. “Ngati mubatizidwe, ndikakusiyani ku nyumba yosungirako okalamba,” anatero mwana wake wamkaziyo. Komabe, kuopseza kumeneku sikunam’gwetse mphwayi Anna. Chifukwa chakuti anali wokalamba, iye anabatizidwira m’nyumba mwake.
Kodi mwana wake wamkaziyo anatani ndi zimenezi? Anasintha maganizo ake, ndipo anawakonzera chakudya chapadera amayi ake pambuyo pa ubatizowo. Ndiyeno anafunsa amayi akewo kuti, “Tsopano popeza kuti mwabatizidwa, kodi mukumva bwanji?” Yankho la Anna? “Ngati wongobadwa kumene!”
• Mu December 1998, Mboni ziŵiri zinakumana ndi msilikali wina wopuma pantchito wa dziko lomwe linali Soviet Union. Chifukwa choti ankakhulupirira kuti kuli Mlengi, iye anavomera phunziro la Baibulo, ndipo kenako mkazi wake anayamba kuphunzira naye limodzi. Anapita patsogolo mofulumira kwambiri ndipo posapita nthaŵi yaitali anakhala ofalitsa osabatizidwa. M’chilimwe chotsatira, mwamuna yemwe kale anali msilikaliyo anabatizidwa. Kukondetsetsa zinthu zauzimu kwa banja limeneli kwakhala chilimbikitso kwa onse mu mpingo. Komanso, anagwira ntchito zolimba pokonzanso nyumba ina ya m’dera lawolo kuti ikhale Nyumba ya Ufumu yabwino kwambiri.