Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mitsempha Yako Idzalandirapo Moyo”

“Mitsempha Yako Idzalandirapo Moyo”

“Mitsempha Yako Idzalandirapo Moyo”

PALI chikhulupiriro chakuti matenda ambiri a anthu amayamba chifukwa cha kuvutika m’maganizo koyambitsidwa ndi mantha, chisoni, nsanje, mkwiyo, chidani, ndi kudzimva wamlandu. Poona zimenezi, mawu a m’Baibulo akuti, ‘ukaopa Yehova, . . . mitsempha yako idzalandirapo moyo ndi mafupa ako uwisi,’ n’ngotonthoza zedi!​—Miyambo 3:7, 8.

Mafupa ndiwo nsanamira za thupi. Choncho, Baibulo limagwiritsa ntchito liwu lakuti “mafupa” mwa fanizo kutanthauza munthu weniweniyo, makamaka povutika ndi maganizo osautsa kwambiri. Koma kodi ndi motani mmene kuopa Yehova ‘kungapatsire mitsempha yako moyo’?

Akatswiri a Baibulo, amasiyana maganizo pa mawu akuti “mitsempha” m’ndimeyi. Katswiri wina wothirira ndemanga pa Baibulo ananena kuti, chifukwa chakuti “mitsempha” ndiyo ili “m’katikati mwa thupi,” ingaimirenso ziwalo zonse zofunika kwambiri. Wophunzira Baibulo wina anaganiza kuti liwu lakuti “mitsempha” lingatanthauze mchombo, monga mmene lagwiritsidwira ntchito pa Ezekieli 16:4. Ngati zili choncho, ndiye kuti Miyambo 3:8 ingakhale ikutsimikizira kufunika kwa kudalira Mulungu ndi mtima wonse, monga mmene kakhanda komwe sikanabadwe kamadalira mayi wake pa chilichonse chofunika m’thupi lake. Komabe, maganizo ena n’ngakuti m’vesili, “mitsempha” ikhoza kutanthauza minofu ndi minyewa ya thupi. M’nkhaniyi, mbali zimenezi zingakhale zikulekanitsidwa ndi “mafupa” omwe ndi mbali zolimba za thupi.

Kaya tanthauzo lake lenileni n’lotani, chinthu chimodzi n’chotsimikizika: Kuopa kum’khumudwitsa Yehova ndiyo njira yanzeru. Kutsatira miyezo ya Mulungu kungatipangitse kukhala ndi moyo wabwino tsopano. Kuwonjezera apo, kungachititse kuti Yehova atiyanje, ndipo zimenezi zidzatitsogolera ku moyo wosatha wangwiro​—mwakuthupi ndi mwa maganizo​—m’dziko lake latsopano.​—Yesaya 33:24; Chivumbulutso 21:4; 22:2.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Dr. G. Moscoso/​SPL/​Photo Researchers