Anthu Obwezeretsedwa a Yehova Akum’tamanda Padziko Lonse Lapansi
Anthu Obwezeretsedwa a Yehova Akum’tamanda Padziko Lonse Lapansi
“Ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [“chinenero choyera,” NW], kuti onseŵa aitanire pa dzina la Yehova.”—ZEFANIYA 3:9.
1. N’chifukwa chiyani mauthenga achiŵeruzo anakwaniritsidwa pa Yuda ndi mitundu ina?
NDI mauthenga achiweruzo amphamvu kwabasi amene Yehova anauzira Zefaniya kuti awalengeze! Mawu achiŵeruzo amenewo anakwaniritsidwa pa dziko la Yuda ndi likulu lake, Yerusalemu, chifukwa atsogoleri ndi anthu ake sanali kuchita chifuniro cha Yehova. Mitundu yoyandikana naye, monga Filistiya, Moabu, ndi Amoni, inakumananso ndi mkwiyo wa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chotsutsa anthu a Yehova mwankhanza kwa zaka mazana ambiri. Pachifukwa chofananacho, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Asuri unali kudzawonongedwa, osakhalaponso.
2. Kodi zikusonyeza kuti ndani amene ankauzidwa mawu a pa Zefaniya 3:8?
2 Komabe, analipo anthu ena a mitima yowongoka m’dziko la Yuda panthaŵiyo. Iwowo anayembekezera mwachidwi chiweruzo cha Mulungu pa oipawo ndipo zikuoneka kuti ndiwo anali kuuzidwa mawu akuti: “Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira Ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima Ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndiko mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.”—Zefaniya 3:8.
“Chinenero Choyera” cha Yani?
3. Kodi Zefaniya anauziridwa uthenga wotani wa chiyembekezo umene anafunikira kuti aupereke?
3 Inde, Zefaniya analengezadi mauthenga a Yehova achiweruzo. Koma mneneriyu anauziridwanso kuti aphatikizepo uthenga wabwino wa chiyembekezo—umene unali wolimbikitsa kwambiri kwa amene anakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Monga kwalembedwa pa Zefaniya 3:9, Yehova analengeza kuti: “Pamenepo ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [chinenero choyera ], kuti onseŵa aitanire pa dzina la Yehova kum’tumikira ndi mtima umodzi.”
4, 5. (a) N’chiyani chomwe chinachitikira osalungama? (b) Kodi ndani anapindula ndi zimenezo, nanga n’chifukwa chiyani?
Zefaniya 3:11) Choncho odzikuza amene ankanyansidwa ndi malamulo a Mulungu ndi kuchita zinthu zosemphana ndi chilungamo, anali kudzachotsedwa. Ndiyeno ndani anapindula ndi zimenezi? Zefaniya 3:12, 13 amati: “[Ine Yehova] ndidzasiya pakati pako anthu ozunzika ndi osauka, ndipo iwo adzakhulupirira dzina la Yehova. Otsala a Israyeli sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwawo simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.”
4 Koma analipo anthu amene sanayenera kulandira nawo mlomo woyerawo, kapena kuti chinenero choyeracho. Ulosiwo umanena za amenewo kuti: “Ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwawo.” (5 Otsalira okhulupirika a mu Yuda wakale, akanapindula. Chifukwa chiyani? Chifukwa anali ozunzika ndi osauka, kapena kuti odzichepetsa ndi ofatsa, malinga ndi Chihebri choyambirira. Iwo anachita mogwirizana ndi mawu akuti: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:3.
6. Kodi chinachitika n’chiyani pa kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wa Zefaniya?
6 Pakukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wa Zefaniya, Mulungu analanga Yuda wosakhulupirikayo mwa kulola Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Babulo, kuugonjetsa ndi kuutengera kuukapolo mu 607 B.C.E. Ena, kuphatikizapo mneneri Yeremiya anapulumuka, ndipo enanso anakhalabe okhulupirika kwa Yehova kuukapoloko. M’chaka cha 539 B.C.E., Babulo anagwetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi olamulidwa ndi Mfumu Koresi. Patapita zaka pafupifupi ziŵiri, Koresi anapereka lamulo limene linalola otsala a Israyeli kubwerera kudziko lakwawo. M’kupita kwa nthaŵi, kachisi ku Yerusalemu anamangidwanso, ndipo ansembe analinso okonzeka kuphunzitsa anthu Chilamulo. (Malaki 2:7) Choncho Yehova analemeretsa otsala obwezeretsedwawo—malinga ngati anakhalabe okhulupirika.
7, 8. Kodi mawu aulosi a pa Zefaniya 3:14-17 akunena za yani, ndipo n’chifukwa chiyani mukutero?
7 Zefaniya ananeneratu za amene akasangalala ndi kubwezeretsako kuti: “Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni, fuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu. Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa. Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usaopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m’chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.”—Zefaniya 3:14-17.
8 Mawu aulosi amenewo akunena za otsala osonkhanitsidwa kutuluka muukapolo wa ku Babulo ndi kubwezedwa kudziko lakwawo. Zimenezi zafotokozedwa momveka bwino pa Zefaniya 3:18-20, pamenepo timaŵerenga kuti: “Ndidzasonkhanitsa iwo akulirira msonkhano woikika, ndiwo a mwa iwe, amene akatundu ake anawakhalira mtonzo. Taonani, nthaŵi yomweyo ndidzachita nawo onse akuzunza iwe; ndipo ndidzapulumutsa wotsimphinayo, ndi kusonkhanitsa wopitikitsidwayo; ndipo ndidzawaika akhale chilemekezo ndi dzina, iwo amene manyazi awo anali m’dziko lonse. Nthaŵi yomweyo ndidzakuloŵetsani, ndi nthaŵi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.”
9. Kodi Yehova anadzipangira motani dzina kudzera mwa Yuda?
9 Tangoganizani kudabwa kwake, ndi kusokonezeka maganizo kumene kunagwira anthu a mitundu yozungulira omwe ankadana ndi anthu a Mulungu! Anthu okhala mu Yuda anali atatengedwa kuukapolo ndi Babulo wamphamvuyo, popanda chiyembekezo chakuti angakabwereko. Komanso, dziko lawo linangotsala bwinja lokhalokha. Koma mwa mphamvu ya Mulungu, iwo anabwezeretsedwa kudziko lakwawo patapita zaka 70, pamene mitundu yachidaniyo inali kupita ku chiwonongeko. Ndithudi, Yehova anadzipangira dzina mwa kubwezeretsa otsala okhulupirikawo! Anawapanga ‘akhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu.’ Kubwezeretsedwa kumeneku kunadzetsadi chitamando chachikulu kwa Yehova ndi kwa amene analengeza za dzina lake!
Kulambira Yehova Kukwezeka
10, 11. Kodi kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi wa Zefaniya wa kubwezeretsa kunayenera kuchitika liti, ndipo tikudziŵa motani zimenezi?
10 Kubwezeretsedwa kwinanso kunachitika m’zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu, pamene Yesu anasonkhanitsa otsala a Israyeli ku kulambira koona. Zimenezi zinachitira chithunzi zimene zinalinkudza, pakuti kukwaniritsidwa kwakukulu kwa kubwezeretsedwako kunali m’tsogolo. Ulosi wa Mika unaneneratu kuti: “Kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda, ndi mitundu ya anthu idzayendako.”—Mika 4:1.
11 Kodi zimenezi zikachitika liti? Monga momwe ulosiwo ukunenera, “masiku otsiriza”—inde, m’kati mwa “masiku otsiriza” ano. (2 Timoteo 3:1) Zimenezi zinayenera kuchitika dongosolo loipali la zinthu lisanathe, pamene mitundu ikulambirabe milungu yonyenga. Mika 4:5 amati: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake.” Nanga bwanji ponena za olambira oona? Ulosi wa Mika ukuyankha kuti: “Ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.”
12. Kodi kulambira koona kwakwezeka motani m’masiku otsiriza ano?
12 Choncho, m’masiku ano otsiriza, “phiri la
nyumba ya Yehova [la]khazikika pamwamba pa mapiri.” Kulambira Yehova koona kokwezeka kwabwezeretsedwa, kwakhazikika zolimba, ndi kukwezeka pamwamba pa zipembedzo zina zonse. Ndipo, monga momwe ulosi wa Mika unaneneratu, anthu ambiri adzamukako. Awo olambira moona ‘adzayenda m’dzina la Yehova Mulungu [wawo] ku nthaŵi yomka muyaya.’13, 14. Kodi dziko lino linaloŵa liti mu “masiku otsiriza,” ndipo kwakhala kukuchitika chiyani kuchokera nthaŵiyo chokhudza kulambira koona?
13 Zochitika zokwaniritsa ulosi wa Baibulo zimasonyeza kuti dzikoli linaloŵa m’gawo lomalizira la “masiku otsiriza” m’chaka cha 1914. (Marko 13:4-10) Mbiri imasonyeza kuti panthaŵiyo Yehova anayamba kusonkhanitsa ndi cholinga cha kulambira koona, otsala okhulupirika a odzozedwa omwe anali ndi chiyembekezo chopita kumwamba. Pambuyo pa zimenezo, kusonkhanitsa “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe”—omwe ali ndi chiyembekezo chokhala padziko lapansi kosatha kunayamba.—Chivumbulutso 7:9.
14 Chichitikireni nkhondo yoyamba ya padziko lonse mpaka lero, kulambira Yehova kochitidwa ndi anthu odziŵika ndi dzina lake kwapita patsogolo mwamphamvu motsogoleredwa ndi iye. Kuchokera pa masauzande ochepa pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, alambiri a Yehova tsopano akuthamangira m’ma 6 miliyoni, osonkhana m’mipingo yokwanira 91,000 m’mayiko 235. Chaka ndi chaka, olengeza Ufumu ameneŵa amathera maola opitirira 1 biliyoni kutamanda Mulungu poyera. N’zoonekeratu kuti Mboni za Yehova zimenezi n’zimene zikukwaniritsa mawu aulosi a Yesu akuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
15. Kodi Zefaniya 2:3 akukwaniritsidwa motani panopa?
15 Zefaniya 3:17 amati: “Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa.” Kupita patsogolo kwauzimu kumene atumiki a Yehova akusangalala nako m’masiku ano otsiriza n’chifukwa chakuti Yehovayo ‘ali pakati pawo’ monga Mulungu wawo wamphamvuyonse. Zili choncho lerolino monganso momwe zinalili pakubwezeretsedwa kwa Yuda wakaleyo, mu 537 B.C.E. Chotero tingaone mmene Zefaniya 2:3 akukwaniritsidwira mokulira m’nthaŵi yathu ino. Lembali limati: ‘Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko.’ Mu 537 B.C.E., mawuwo akuti “nonse” anaphatikizapo otsala onse a Ayuda omwe anabwerera kwawo kuchokera kuukapolo ku Babulo. Koma tsopano akuimira ofatsa a m’mitundu yonse kuzungulira dziko lonse lapansi, aja omwe akulabadira ntchito yolalikira yapadziko lonse ndi amene akukhamukira ku “phiri la nyumba ya Yehova.”
Kulambira Koona Kukupita Patsogolo
16. Kodi adani athu amachitanji akaona kupita patsogolo kwa atumiki a Yehova m’nthaŵi zamakono zino?
16 Chitapita chaka cha 537 B.C.E., ambiri m’mitundu yozungulira anadabwa poona atumiki a Mulungu obwerera kwawo amenewo akubwezeretsa kulambira koona. Komabe, kubwezeretsa kumeneko kunali pamlingo waung’ono Yohane 12:19.
chabe. Tangolingalirani zimene ena—ngakhalenso adani a anthu a Mulungu—akunena tsopano poona kuwonjezeka ndi kupita patsogolo kodabwitsa kwa atumiki a Yehova m’masiku athu ano. Mosakayikira, ena mwa adani ameneŵa akumva mmene anamvera Afarisi ataona mmene anthu anakhamukira kwa Yesu. Iwo anafuula kuti: “Onani dziko litsata pambuyo pake pa Iye.”—17. Kodi wolemba mabuku wina anati chiyani ponena za Mboni za Yehova, ndipo n’kuwonjezereka kotani komwe kwachitika?
17 M’buku lake lakuti These Also Believe, (Aŵanso Amakhulupirira) Pulofesa Charles S. Braden anati: ‘Mboni za Yehova zafika paliponse m’dziko lapansi ndi ntchito yawo yochitira umboni. Kunena zoona, palibe chipembedzo n’chimodzi chomwe padziko lapansi chimene chakhala chokangalika ndi cholimbikira poyesetsa kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu kuposa Mboni za Yehova. Mwachionekere, gulu limeneli lidzakulirakulirabe.’ Ananenadi zoona! Pamene amalemba mawu amenewo zaka 50 zapitazo, kunali Mboni ngati 300,000 zokha zomwe zinali kulalikira padziko lonse. Kodi ameneyu akanati chiyani lerolino, pamene chiŵerengero cha alaliki chapanthaŵiyo tsopano chaŵirikiza nthaŵi pafupifupi makumi aŵiri—kufika pafupifupi 6 miliyoni?
18. Kodi chinenero choyera n’chiyani, ndipo kodi Mulungu wachipereka kwa yani?
18 Kudzera mwa mneneri wake, Mulungu analonjeza kuti: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu mlomo woyera [chinenero choyera ] kuti onseŵa aitanire pa dzina la Yehova kum’tumikira ndi mtima umodzi.” (Zefaniya 3:9) M’masiku otsiriza ano, ndi Mboni za Yehova zimene zikuitanira pa dzina la Yehova, zimenenso zikum’tumikira mogwirizana m’chomangira chosaduka cha chikondi—inde, “ndi mtima umodzi.” Ndi iwoŵa amene Yehova wawapatsa chinenero choyera kapena kuti mlomo woyera. Chinenero choyera chimenechi chikuphatikizapo kumvetsa bwino zoona zake ponena za Mulungu ndi zofuna zake. Ndi Yehova yekha amene amathandiza kumvetsa bwino kotereku, ndipo amatero kudzera mwa mzimu wake woyera. (1 Akorinto 2:10) Kodi mzimu wake woyera waupereka kwa ndani? Waupereka kwa okhawo “akumvera iye” monga wolamulira. (Machitidwe 5:32) Mboni za Yehova zokha n’zofunitsitsa kumvera Mulungu monga Wolamulira m’chilichonse. Ndiye chifukwa chake zimalandira mzimu wa Mulungu ndi kulankhula chinenero choyera, zoona zenizeni ponena za Yehova ndi zofuna zake zodabwitsa. Zimagwiritsa ntchito chinenero choyera chimenechi potamanda Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi pamlingo waukulu ndi womakulakulabe.
19. Kodi kulankhula chinenero choyera kumaphatikizapo chiyani?
19 Kulankhula chinenero choyera sindiko kungokhulupirira choonadi ndi kuchiphunzitsa kwa ena kokha, koma kuti aliyense agwirizanitse makhalidwe ake ndi malamulo komanso malangizo a Mulungu. Akristu odzozedwa atsogolera kufunafuna Yehova ndi kulankhula chinenero choyera. Tangoganizani zimene iwo akwaniritsa! Ngakhale kuti tsopano chiŵerengero cha odzozedwa chatsika moti otsala sakukwanira 8,700, komabe a “nkhosa zina” pafupifupi 6 miliyoni, akutsanzira chikhulupiriro chawo pofunafuna Yehova ndi kulankhula chinenero choyera. Chiŵerengero chimenechi cha akhamu lalikulu ochokera m’mitundu yonse n’chimene chikukulirakulira. Ameneŵa amakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu, akuchita utumiki wopatulika m’bwalo la padziko lapansi la kachisi wauzimu wa Mulungu, ndipo adzapulumuka “m’chisautso chachikulu” chomwe posachedwa pompa chidzafikira dziko losalungamali.—Chivumbulutso 7:9, 14, 15.
20. Kodi n’chiyani chomwe odzozedwa okhulupirika komanso amene amapanga khamu lalikulu akuyembekezera?
2 Petro 3:13) Yesu Kristu, ndi a 144,000 odzozedwa oukitsidwira ku moyo wakumwamba kukatumikira monga mafumu ndi ansembe limodzi ndi Kristu, amapanga boma latsopano lolamulira dziko lapansi. (Aroma 8:16, 17; Chivumbulutso 7:4; 20:6) Opulumuka chisautso chachikulu adzayamba kukonza dziko lapansi kuti likhale paradaiso ndipo adzapitirizabe kulankhula chinenero choyera chopatsidwa ndi Mulungu. Kwenikweni, mawu aŵa amanena za iwowo kuti: “Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu. M’chilungamo iwe udzakhazikitsidwa.”—Yesaya 54:13, 14.
20 Khamu lalikulu lidzaloŵetsedwa m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. (Ntchito Yophunzitsa Yaikulu Koposa M’mbiri
21, 22. (a) Monga momwe Machitidwe 24:15 akusonyezera, ndani amene adzafunikira kuphunzitsidwa chinenero choyera? (b) Kodi ndi ntchito yophunzitsa yosayerekezeka iti yomwe idzachitike padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu?
21 Gulu lalikulu kwambiri lomwe lidzapatsidwa mwayi wophunzira chinenero choyera m’dziko latsopano ndi amene amawatchula pa Machitidwe 24:15, pamene pamati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” M’zaka za m’mbuyomu, anthu mabiliyoni ambiri anakhalapo ndi moyo ndi kumwalira opanda chidziŵitso cholondola chonena za Yehova. Mwa njira yadongosolo, iye adzawabwezeretsa ku moyo. Ndipo oukitsidwa amenewo adzafunikira kuphunzitsidwa chinenero choyera.
22 Udzakhalatu mwayi wosaneneka kuchita nawo ntchito yophunzitsa yaikulu imeneyo! Ndithudi, idzakhala ntchito yophunzitsa yopambana m’mbiri yonse ya anthu. Ndipo idzachitikira mu ulamuliro wabwino koposa wa Kristu Yesu monga mfumu ya Ufumuwo. M’kupita kwanthaŵi, anthu adzaona kukwaniritsidwa kwa Yesaya 11:9, amene amati: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”
23. N’chifukwa chiyani munganene kuti tili ndi mwayi waukulu monga anthu a Yehova?
23 Tilitu ndi mwayi m’masiku ano otsiriza, wokonzekera nthaŵi yochititsa chidwi imeneyo pamene dziko lapansi lidzadzazadi ndi odziŵa Yehova! Ndipo tilinso ndi mwayi waukulu pakali pano wokhala anthu a Mulungu, omwe akudzionera okha kukwaniritsidwa kwa mawu aulosi olembedwa pa Zefaniya 3:20! Pamenepo tikupeza chilimbikitso cha Yehova chakuti: “Ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi.”
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ulosi wa Zefaniya wa kubwezeretsa wakwaniritsidwa motani?
• Kodi kulambira koona kwapita patsogolo motani m’masiku ano otsiriza?
• Ndi ntchito yaikulu iti yophunzitsa yomwe idzachitika m’dziko latsopano?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 25]
Anthu a Yehova anabwerera kwawo kukabwezeretsa kulambira koyera. Kodi mukudziŵa tanthauzo la izi lerolino?
[Zithunzi patsamba 26]
Mwa kulankhula “chinenero choyera,” Mboni za Yehova zimapereka uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo kwa anthu