Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Funafunani Yehova Lisanadze Tsiku la Mkwiyo Wake

Funafunani Yehova Lisanadze Tsiku la Mkwiyo Wake

Funafunani Yehova Lisanadze Tsiku la Mkwiyo Wake

“Funani Yehova . . . funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”​—ZEFANIYA 2:3.

1. Kodi mkhalidwe wauzimu wa Yuda unali wotani pamene Zefaniya amayamba ntchito yake yolosera?

ZEFANIYA anayamba ntchito yake yolosera panthaŵi yovuta kwambiri m’mbiri ya Yuda. Mkhalidwe wauzimu wa mtunduwo unali utaipiratu. M’malo modalira Yehova, anthuwo ankatembenukira kwa ansembe achikunja ndi okhulupirira nyenyezi kuti awathandize. Kulambira Baala, limodzi ndi miyambo yake yokhudzana ndi mphamvu zobereketsa, zinali pwirikiti m’dzikomo. Atsogoleri a dzikolo​—akalonga, zinduna, ndi oweruza​—anali kupondereza anthu amene amafunikira kumawateteza. (Zefaniya 1:9; 3:3) N’chifukwa chaketu Yehova anaganiza ‘zotambasulira dzanja lake’ pa Yuda ndi Yerusalemu n’cholinga chowawononga!​—Zefaniya 1:4.

2. Kodi atumiki a Mulungu okhulupirika m’Yuda anali n’chiyembekezo chotani?

2 Komabe, ngakhale kuti mkhalidwe unali woipa chotero, panali kachiyembekezo ndithu. Yosiya, mwana wa Amoni, ndiye tsopano anali pampando wachifumu. Ngakhale kuti anali mnyamata wamng’ono kwambiri, Yosiya anali ndi chikondi chenicheni pa Yehova. Ngati mfumu yatsopanoyo inabwezeretsa kulambira koyera m’dziko la Yuda, chinalitu chinthu cholimbikitsa mtima kwabasi kwa ochepa omwe anali kutumikira Mulungu mokhulupirika! Mwina enanso anasonkhezereka ndi kugwirizana nawo ndi kudzatetezeka patsiku la mkwiyo wa Yehova.

Zofunika Kuti Tidzapulumuke

3, 4. Kodi n’zofunika zitatu ziti zomwe munthu ayenera kukwaniritsa kuti adzapulumuke pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova”?

3 Kodi zinalidi zotheka kuti anthu ena n’kupulumukadi patsiku la mkwiyo wa Yehova? Inde, malinga ngati anakwaniritsa zofunika zitatu zotchulidwa pa Zefaniya 2:2, 3. Pamene tikuŵerenga mavesi ameneŵa, tiyeni tipende zofunika zimenezi mwapadera. Zefaniya analemba kuti: “Lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”

4 Choncho, kuti munthu apulumuke anafunikira (1) kufunafuna Yehova, (2) kufunafuna chilungamo, ndi (3) kufunafuna chifatso. Zofunika zimenezi tiyenera kuzilabadira kwambiri lerolino. Chifukwa chiyani? Chifukwa monga momwe Yuda ndi Yerusalemu anayang’anizirana ndi tsiku lachiweruzo m’zaka za m’ma 600 B.C.E., Yehova Mulungu adzathana ndi mayiko opanga gawo la Matchalitchi Achikristu, komanso anthu oipa onse, patsiku la ‘chisautso chachikulu’ likudzalo. (Mateyu 24:21) Aliyense wofuna kudzabisika panthaŵiyo ayenera kuchitapo kanthu tsopano lino. Motani? Mwa kufunafuna Yehova, kufunafuna chilungamo, ndi kufunafuna chifatso, madzi asanafike m’khosi!

5. Kodi ‘kufunafuna Yehova’ kumaphatikizapo chiyani lerolino?

5 Mwina munganene kuti: ‘Komatu ndine mtumiki wa Mulungu wodzipatulira ndi wobatizidwa, mmodzi wa Mboni za Yehova. Kodi sindinazikwaniritse kale zofunikazo?’ Kwenikweni, pali zambiri osati kungodzipatulira chabe kwa Yehova. Israyeli unali mtundu wodzipatulira, koma m’masiku a Zefaniya, anthu a Yuda sanali kuchita zinthu monga anthu odzipatulira. Zotsatirapo zinali zakuti mtunduwo unakanidwa. ‘Kufunafuna Yehova’ lerolino kumaphatikizapo kupalana naye ubwenzi wabwino ndi kuusunga mwa kugwirizana ndi gulu lake lapadziko lapansi. Kumatanthauza kudziŵa mmene Mulungu amaonera zinthu ndi kulabadira maganizo ake. Timafunafuna Yehova pamene tiphunzira Mawu ake mosamalitsa, kuwasinkhasinkha ndi kutsatira malangizo ake m’moyo wathu. Pamene tikufunafunanso chitsogozo cha Yehova m’pemphero lochokera pansi pamtima ndi kutsatira chitsogozo cha mzimu wake woyera, ubwenzi wathu ndi Yehova umazama, ndipo timasonkhezereka kum’tumikira ‘ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse.’​—Deuteronomo 6:5; Agalatiya 5:22-25; Afilipi 4:6, 7; Chivumbulutso 4:11.

6. Kodi ‘chilungamo timachifunafuna’ motani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zotheka ngakhale m’dziko lino?

6 Chofunika chachiŵiri chotchulidwa pa Zefaniya 2:3 ndicho ‘kufunafuna chilungamo.’ Ambiri a ife tinasintha zambiri m’moyo wathu kuti tiyenerere ubatizo wachikristu, komabe tiyenera kupitirizabe kuchirikiza miyezo yolungama ya Mulungu m’moyo wathu wonse. Ena omwe anayamba bwino m’mbali imeneyi alola kuchitidwa maŵanga ndi dzikoli. Kufunafuna chilungamo n’kovuta, chifukwa chakuti tazingidwa ndi anthu amene amaona chiwerewere, kunama, ndi machimo ena monga makhalidwe ololeka. Komabe, chilakolako champhamvu cha kukondweretsa Yehova chitha kugonjetsa chikhumbo chilichonse chofuna kusangalatsa dziko mwa kuyesa kutengera zochitika za dzikoli. Dziko la Yuda linataya chiyanjo cha Mulungu chifukwa chotsanzira mayiko osaopa Mulungu oyandikana nawo. Chotero, m’malo motsanzira dzikoli, tiyeni tikhale “akutsanza a Mulungu,” tikumakulitsa ‘umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo ndi m’chiyero cha choonadi.’​—Aefeso 4:24; 5:1.

7. Kodi ‘chifatso timachifunafuna’ motani?

7 Mfundo yachitatu imene Zefaniya 2:3 akutchula ndi yakuti ngati tikufuna kudzabisika m’tsiku la mkwiyo wa Yehova, tiyenera ‘kufunafuna chifatso.’ Tsiku ndi tsiku, timakumana ndi amuna, akazi, ndi achinyamata osadziŵa chilichonse ponena za chifatso. Kwa iwo, kuleza mtima ndi kupusa. Kugonjera amakuona ngati mantha. Amachita zinthu molamula, mwadyera, ndiponso momva zaokha. Amafuna kuti wina asaloŵerere pa zimene amaziona kukhala “ufulu” wawo ndi zokonda zawo, zivute zitani. Zingakhaletu zomvetsa chisoni kwabasi ngati maganizo ena oterowo angatiyambukire ifenso! Ino ndi nthaŵi ‘yofunafuna chifatso.’ Motani? Mwa kugonjera Mulungu, kutsatira malangizo ake modzichepetsa ndi kuchita mogwirizana ndi chifuniro chake.

N’chifukwa Chiyani Akuti “Kapena” Mudzabisika?

8. Kodi kugwiritsa ntchito mawu akuti “kapena” pa Zefaniya 2:3 kukusonyeza chiyani?

8 Onani kuti Zefaniya 2:3 akunena kuti: “Kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” N’chifukwa chiyani akugwiritsa ntchito mawu akuti “kapena” polankhula ndi ‘ofatsa onse a m’dziko’? Inde, ofatsa amenewo anatenga masitepe abwino, koma sanafunikire kudzidalira. Anali asanafike kumapeto a moyo wawo ali okhulupirika. Zinali zotheka kuti ena mwa iwo akanagwa m’tchimo. N’chimodzimodzinso kwa ife. Yesu anati: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Inde, kupulumuka tsiku la mkwiyo wa Yehova kudzadalira kupitiriza kwathu kuchita chimene chili choyenera kwa iye. Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kuchita zimenezo?

9. Kodi n’zinthu zoyenera ziti zomwe Mfumu Yosiya yachinyamatayo inachita?

9 Zikuoneka kuti pomvera mawu a Zefaniya, Mfumu Yosiya, inasonkhezereka ‘kufunafuna Yehova.’ Malemba amati: “Atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziŵiri [Yosiya] akali mnyamata [wazaka pafupifupi 16], anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake.” (2 Mbiri 34:3) Yosiya anapitirizanso ‘kufunafuna chilungamo’ pakuti timaŵerenga kuti: “Atakhala zaka khumi ndi chimodzi [pamene Yosiya anali ndi zaka pafupifupi 20] anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuchotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga. Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake.” (2 Mbiri 34:3, 4) Yosiya ‘anafunafunanso chifatso,’ anachita zinthu modzichepetsa kuti akondweretse Yehova mwa kuyeretsa dzikolo pothetsa kupembedza mafano ndi zochitika zina za chipembedzo chonyenga. Ofatsa ena ayenera kuti anasangalala kwabasi poona zimenezi!

10. Kodi chinachitika n’chiyani mu Yuda m’chaka cha 607 B.C.E., koma ndani anapulumuka?

10 Mu ulamuliro wa Yosiya, Ayuda ambiri anabwerera kwa Yehova. Koma mfumuyo itamwalira, ambiri anabwereranso ku njira zawo zakale​—ku zochita zosaloleka kwa Mulungu. Monga momwe Yehova anali ataneneratu, Ababulo anagonjetsa Yuda ndi kuwononga likulu lake, Yerusalemu, mu 607 B.C.E. Komabe, sikuti amenewo anali mapeto a zonse. Mneneri Yeremiya, Ebedi-Meleki Mkusi, am’nyumba ya Yonadabu, ndi ena okhulupirika kwa Mulungu anabisika pa tsiku limenelo la mkwiyo wa Yehova.​—Yeremiya 35:18, 19; 39:11, 12, 15-18.

Adani a Mulungu Inu​—Samalani!

11. N’chifukwa chiyani kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu lerolino kuli kovuta, koma kodi adani a anthu a Yehova ayenera kulingalira chiyani?

11 Pamene tikudikirira tsiku la mkwiyo wa Yehova pa dongosolo lino loipali, ‘timagwa m’mayesero a mitundumitundu.’ (Yakobo 1:2) M’mayiko ambiri amene amati amalemekeza ufulu wakupembedza, atsogoleri achipembedzo achiwembu agwiritsa ntchito mphamvu zawo ponyengerera akuluakulu a boma kuti azunze anthu a Mulungu. Anthu achipongwe akhala akunenera mabodza Mboni za Yehova, kuwatcha “kagulu kampatuko koopsa.” Mulungu akudziŵa bwino zomwe akuchitazo​—ndipo sadzatha kuthaŵa chiweruzo chake. Adani a Mulungu ameneŵa ayenera kulingalira zimene zinaonekera ena omwe ankadana ndi anthu ake kalero monga Afilisti. Ulosi umati: “Pakuti Gaza adzasiyidwa, ndi Asikeloni adzakhala bwinja; adzaingitsa Asidodi usana, ndi Ekroni adzazulidwa.” Mizinda ya Afilisti ya Gaza, Asikeloni, Asidodi, ndi Ekroni inali kudzawonongedwa kotheratu.​—Zefaniya 2:4-7.

12. N’chiyani chinachitikira Filistiya, Moabu, ndi Amoni?

12 Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Ndinamva kutonza kwa Moabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire awo.” (Zefaniya 2:8) Zoona, Igupto ndi Itiopiya anagonjetsedwa ndi Ababulo. Koma kodi chiweruzo cha Mulungu chinali chotani kwa Moabu ndi Amoni, mitundu yochokera mwa Loti, mwana wa mphwake wa Abrahamu? Yehova ananeneratu kuti: “Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora.” Mosiyana ndi makolo awo achikaziwo​—ana aakazi aŵiri a Loti, omwe anapulumuka chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora​—Moabu ndi Amoni onyadawo sanabisike paziweruzo za Mulungu. (Zefaniya 2:9-12; Genesis 19:16, 23-26, 36-38) Nanga mtundu wa Afilisti uja uli kuti lerolino limodzi ndi mizinda yake? Bwanji mizinda yotchukayo ya Moabu ndi Amoni? Ngakhale mutafufuza chotani, simungaipeze.

13. Kodi ofukula m’mabwinja anapeza chiyani ku Nineve?

13 M’masiku a Zefaniya, Ufumu wa Asuri unali pachimake pa ulamuliro wake. Katswiri wina wofukula za m’mabwinja, Austen Layard, polongosola mbali imodzi ya nyumba yachifumu imene anafukula m’likulu la Asuri la Nineve analemba kuti: “Masiling’i akudenga . . . anawapanga kuchita tizigawotizigawo, ndi kujambulapo maluŵa, kapena nyama zosiyanasiyana. Tizigawo tina anatikometsera ndi zopangidwa kuchokera ku minyanga, kachigawo kalikonse atakakongoletsa m’mphepete mwakemu. Mitanda yakudenga ndi m’mbali mwa zipindazo, anakongoletsamo ndi golidi ndi siliva; ndipo anagwiritsa ntchito mitengo yosoŵa kwambiri, monga mkungudza.” Komabe, malinga n’kunena kwa ulosi wa Zefaniya, Asuri anali kudzawonongedwa ndipo likulu lake, Nineve, linali ‘kudzasanduka bwinja.’​—Zefaniya 2:13.

14. Kodi ulosi wa Zefaniya unakwaniritsidwa motani pa Nineve?

14 Patangopita zaka 15 kuchokera pamene Zefaniya analankhula ulosi umenewu, Nineve wamphamvuyo anawonongedwa, malo ake achifumu anasanduka bwinja lokhalokha. Inde, mzinda wonyadawo unatsala bwinja lokhalokha. Ukulu wa chiwonongekocho unanenedweratu bwino lomwe m’mawu aŵa: “Vuwo ndi nungu zidzakhala m’mitu ya nsanamira zake; adzaimba mawu awo m’mazenera; paziundo padzakhala chipasuko.” (Zefaniya 2:14, 15) Nyumba zolemekezeka za Nineve zinasanduka malo ongoyenera kukhala nungu ndi vuwo. Makwalala a mzindawo anangoti zii, osamvekamonso mawu otsatsa malonda, kapena kufuula kwa asilikali, ngakhalenso kupembedza kwa ansembe. M’misewu yake yaikuluyo, mmene kale munali piringupiringu wa anthu, munangomveka kuimba kwachisoni komvekera pazenera. Mwina kuimba kobuma kwa mbalame kapena kuwomba kwa mphepo yodutsa mmenemo. Ndi mmenenso adani onse a Mulungu ati adzathere psiti!

15. Kodi tingaphunzirenji pa zomwe zinachitikira Filistiya, Moabu, Amoni, ndi Asuri?

15 Kodi tikuphunziranji pa zimene zinachitikira Moabu, Amoni, Filistiya, ndi Asuri? Izi: Monga atumiki a Yehova, adani athu tisawaope m’pang’ono pomwe. Mulungu akuona zimene otsutsa anthu ake akuchita. Yehova anathana ndi adani ake mmbuyomo, ndipo chiweruzo chake chidzafikanso pa dziko lonse lokhalamo anthu lerolino. Koma opulumuka adzakhalapo​—‘khamu lalikulu lochokera m’mitundu yonse.’ (Chivumbulutso 7:9) Mukhoza kukhala pakati pawo​—koma pokhapokha ngati mupitiriza kufunafuna Yehova, kufunafuna chilungamo, ndi kufunafuna chifatso.

Tsoka kwa Ochimwa Odzitukumula!

16. Kodi ulosi wa Zefaniya umati chiyani ponena za akalonga ndi atsogoleri achipembedzo a Yuda, nanga n’chifukwa chiyani mawu ameneŵa akuyenerera Matchalitchi Achikristu?

16 Ulosi wa Zefaniyawo ukukhudzanso Yuda ndi Yerusalemu. Zefaniya 3:1, 2 akuti: “Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza! Sanamvera mawu, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wake.” Ha, linalitu tsoka lalikulu kuti sanalabadire njira zimene Yehova anayesera kulangizira anthu ake! Choipitsitsa kwenikweni chinali nkhanza za akalonga, zinduna, ndi oweruza. Zefaniya anadzudzula mwamphamvu kupanda manyazi kwa atsogoleri achipembedzo, akumati: “Aneneri ake ndiwo anthu a matukutuku ndi onyenga; ansembe awo anaipsa malo opatulika, napotoza chilamulo.” (Zefaniya 3:3, 4) Mawu ameneŵa akuyenereratu bwino lomwe mkhalidwe wa aneneri ndi ansembe a Matchalitchi Achikristu lerolino! Modzitukumula, iwo achotsa dzina la Mulungu m’mabaibulo awo ndipo aphunzitsa ziphunzitso zosonyeza molakwika Uyo amene amati amam’lambira.

17. Kaya anthu amvetsere kapena ayi, n’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kulengeza uthenga wabwino?

17 Moganizira anthu ake akale, Yehova anawachenjeza za zimene anali kudzachita. Anatumiza atumiki ake aneneri​—Zefaniya ndi Yeremiya, limodzinso ndi ena​—kuti akalimbikitse anthuwo kulapa. Inde, “Yehova . . . sadzachita chosalungama, m’mawa ndi m’mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasoŵa kanthu.” Kodi anthuwo anachitanji? “Koma wosalungama sa[na]dziŵa manyazi,” anatero Zefaniya. (Zefaniya 3:5) Chenjezo lofananalo likuperekedwa panthaŵi inonso. Ngati ndinu wofalitsa wa uthenga wabwino, ndiye kuti mukuchita nawo ntchito yochenjeza imeneyi. Choncho lengezanibe uthenga wabwino osaleka! Kaya anthu amve kapena akane, utumiki wanu udzakhalabe wopambana pamaso pa Mulungu malinga ngati mukuuchita mokhulupirika; palibe chifukwa chakuti muchitire manyazi pamene mukuchita ntchito ya Mulungu mwachangu.

18. Kodi Zefaniya 3:6 adzakwaniritsidwa motani?

18 Chiweruzo cha Yehova sichidzakhala cha Matchalitchi Achikristu okha ayi. Chidzudzulo cha Yehova chikuphatikizanso mitundu yonse yapadziko lapansi. Iye akuti: “Ndawononga amitundu; nsanja zawo za kungondya n’zabwinja, ndapasula misewu yawo, palibe wopitapo; midzi yawo yawonongeka.” (Zefaniya 3:6) Chotero mawu ameneŵa ndi odalirika kwambiri, mwakuti Yehova akulankhula za chiwonongekocho ngati kuti chachitika kale. Kodi n’chiyani chinachitikira mizinda ya Filistiya, Moabu, ndi Amoni? Nanga bwanji likulu la Asuri, Nineve? Chiwonongeko chawo chili chenjezo limene mitundu lerolino iyenera kutengerapo chitsanzo. Mulungu sanyozeka.

Pitirizanibe Kufunafuna Yehova

19. Kodi tingafunse mafunso ati othandiza kulingalira?

19 M’tsiku la Zefaniya mkwiyo wa Mulungu unayakira onse ‘ovunditsa machitidwe awo onse.’ (Zefaniya 3:7) Zofananazo zichitikanso m’nthaŵi yathu. Kodi mukuona umboni wakuti tsiku la mkwiyo wa Yehova lili pafupi? Kodi mukupitirizabe ‘kufunafuna Yehova’ mwa kuŵerenga Mawu ake nthaŵi zonse​—tsiku ndi tsiku? Kodi ‘mukufunafuna chilungamo’ mwa kukhala wa khalidwe loyera mogwirizana ndi miyezo ya Mulungu? Ndiponso kodi ‘mukufunafuna chifatso’ mwa kuonetsa mtima wodekha, mwa kugonjera kwa Mulungu ndi makonzedwe ake a chipulumutso?

20. Kodi ndi mafunso ati amene tidzakambirana m’nkhani yotsiriza ya nkhani zotsatanazi za ulosi wa Zefaniya?

20 Ngati tipitiriza kufunafuna Yehova, chilungamo, ndi chifatso, mokhulupirika, tingayembekezere kusangalala ndi madalitso ochuluka tsopano lino​—inde, ngakhale mu “masiku otsiriza” oyesa chikhulupiriro ano. (2 Timoteo 3:1-5; Miyambo 10:22) Komabe tingafunse kuti, ‘Kodi pakali pano tikudalitsidwa m’njira yotani monga atumiki amakono a Yehova, ndipo ndi madalitso otani am’tsogolo amene ulosi wa Zefaniya ukutchula kuti adzagwera amene adzabisika m’tsiku la mkwiyo wa Yehova lomwe likuyandikira mofulumirali?’

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi anthu amam’funafuna motani Yehova?

• Kodi ‘kufunafuna chilungamo’ kumaphatikizapo chiyani?

• Kodi ‘chifatso tingachifunefune’ motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe ‘kufunafuna Yehova, chilungamo, ndi chifatso’?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mukufunafuna Yehova mwa kuphunzira Baibulo ndi kupemphera kuchokera pansi pa mtima?

[Chithunzi patsamba 21]

Chifukwa chakuti akupitiriza kufunafuna Yehova, khamu lalikulu lidzapulumuka tsiku la mkwiyo wake