Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Oyenerera ku Kenya

Kufunafuna Oyenerera ku Kenya

Kufunafuna Oyenerera ku Kenya

KENYA ndi dziko lomwe lili ndi zinthu zachilengedwe zokongola kwambiri. Nkhalango zobiriŵira, zigwa zazikulu, zipululu zotentha kwambiri, ndiponso mapiri okutidwa ndi chipale chofeŵa, zimakongoletsa dziko losangalatsali. M’dzikoli mulinso nyama zotchedwa nyumbu zopitirira miliyoni imodzi komanso zipembere zomwe anthu akuzipha kwambiri. Mutha kukaonanso khwimbi la nyamalikiti zikudutsa m’zigwa zaudzu okhaokha.

Kulinso zolengedwa zochuluka zamlengalenga monga ziwombankhanga zamphamvu zomwe zimalengama m’malele ndiponso mbalame zokongola kwabasi zomwe zimaimba nyimbo zosangalatsa. Komanso osaiŵala njovu ndi mikango yochititsa chidwiyo. Ndithudi, zinthu zokongola ndiponso nyimbo zokoma za mbalame m’dziko la Kenya n’zosaiŵalika.

Komanso, mawu ena amamveka m’dziko lonse lokongolali. Mawu ameneŵa ndi a anthu miyandamiyanda olengeza uthenga wachiyembekezo. (Yesaya 52:7) Uthenga umenewu umapita kwa anthu a mitundu ndi zinenero zoposa 40. M’njira imeneyi, Kenya ndi dziko lokongolanso kwambiri mwauzimu.

Anthu ambiri a ku Kenya amakonda kupembedza ndipo amafunitsitsa kukambirana nkhani zauzimu. Ngakhale zili choncho, kupeza anthu oti mulankhule nawo n’kovuta kwambiri chifukwa chakuti m’dziko la Kenya, monganso m’mayiko ena ambiri, zinthu zikusintha.

Mavuto azachuma akakamiza anthu ambiri kusintha miyoyo yawo. Akazi omwe pachikhalidwe ankagwira ntchito zapakhomo, tsopano akupezeka m’maofesi, kapena m’mphepete mwa misewu akugulitsa zipatso, ndiwo zamasamba, nsomba, ndiponso madengu. Amuna amagwira ntchito nthaŵi yaitali kuyesa kupeza zosoŵa za mabanja awo. Ngakhale ana nawonso amangoyendayenda m’misewu kugulitsa mtedza wokazinga ndiponso mazira ophika. Zotsatira zake n’zakuti anthu ochepa ndiwo amapezeka panyumba masana onse. Zimenezi zachititsa kuti olengeza uthenga wabwino wa Ufumu nawonso asinthe.

Mipingo ya Mboni za Yehova inalangizidwa kuika maganizo kwambiri kwa anthu amene sapezeka panyumba. Anthu amene amayendayenda kugwira ntchito zawo zatsiku n’tsiku, komanso mabwenzi, achibale, amalonda, ndi ogwira nawo ntchito. Ndipo abale anachitadi zimenezo, kumalankhula ndi anthu kulikonse komwe angapezeke. (Mateyu 10:11) Kodi khama lawo lofikira anthu kulikonse labala zipatso? Inde, latero! Talingalirani zitsanzo zina izi.

Achibale Amene Timawakonda Kwambiri

Mzinda wa Nairobi womwe ndi likulu la dziko la Kenya muli anthu pafupifupi mamiliyoni atatu. Chakum’maŵa kwa mzindawu kunkakhala mkulu wina wa asilikali yemwe anapuma pantchito. Kwanthaŵi yaitali iye ankadana kwambiri ndi Mboni za Yehova ngakhale kuti mwana wake anali Mboni. Mu February, msilikali wopuma pantchitoyo anayenda ulendo wa makilomita 160 kupita ku tauni ina yotchedwa Nakuru m’chigwa cha Rift Valley komwe kunkakhala mwana wakeyo. M’kati mwa kuchezako, mwanayo anawapatsa bambo akewo mphatso yomwe inali buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * Bambowo analandira ndipo ananyamuka.

Atafika kumudzi, mkuluyo anapereka bukulo kwa mkazi wake, yemwe anayamba kuliŵerenga mosadziŵa kuti linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Pang’ono ndi pang’ono, choonadi cha Baibulo chinayamba kum’gwira mtima, ndipo ankauza mwamuna wake zomwe waŵerenga. Pofuna kungodziŵa zinthu, mwamunayonso anayamba kuŵerenga bukulo. Atazindikira amene anafalitsa bukulo, iwo anaona kuti sanali kuuzidwa zoona zake zokhudza Mboni za Yehova. Iwo anakaonana ndi Mboni ina ya m’deralo ndipo anayamba kuphunzira Baibulo. Ataŵerenga bukulo paokha, iwo anazindikira kuti kusuta kapena kugulitsa fodya n’kosemphana ndi chikristu. (Mateyu 22:39; 2 Akorinto 7:1) Mosazengereza, anawononga ndudu zonse za fodya m’sitolo yawo. Patapita miyezi ingapo, iwo anali oyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa, ndipo pasanapite nthaŵi anabatizidwa pamsonkhano wachigawo.

M’zinyalala Mutuluka Chuma

M’madera ena a m’boma la Nairobi, muli midzi yomwe m’makhala anthu mazana zikwi zambiri. Kumeneku kuli mizera yambirimbiri ya nyumba zomata, zamitengo yokhayokha, ndiponso zamalata okhaokha. Ntchito ikamasoŵa m’makampani ndi m’mafakitale, anthu amagwira ntchito zina. Antchito otchedwa Jua Kali, (mawu a m’Chiswahili kutanthauza dzuŵa lotentha kwambiri) amagwira ntchito padzuŵa lalikali kumakonza nkhwayira kuchokera ku matayala akale a galimoto. Amakonzanso nyali pogwiritsa ntchito tizitini topanda ntchito. Ena amafunafuna mapepala, zitini, ndiponso mabotolo m’miyulu ya zinyalala komanso m’mabini kuti akazikonzenso.

Kodi m’zinyalala mungatuluke chuma? Inde! Mbale wina akukumbukira kuti: “Munthu wina wamwamuna wojintcha, wosasamba, ndiponso wosapesa, anafika pa Nyumba yathu ya Msonkhano atanyamula thumba lalikulu la pulasitiki lodzaza ndi nyuzipepala komanso magazini zong’ambikang’ambika. Atandiuza kuti dzina lake ndi William, iye anafunsa kuti: ‘Kodi muli ndi makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda?’ Ndinali wamantha, ndipo sindinkadziŵa kuti cholinga chake n’chiyani. N’tamuonetsa makope asanu a magaziniwo, iye anawasanthula limodzi ndi limodzi kenako anati: ‘Nditenga onseŵa.’ Ndinadabwa, ndipo ndinabwerera m’chipinda changa n’kubweretsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. * Ndinamuonetsa chithunzi cha Paradaiso ndipo ndinamuuza kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Kenako, ndinam’pempha ndimvekere: ‘William, bwanji ubwere maŵa kuti tidzayambe kuphunzira Baibulo?’ Iye anabweradi!

“Lamlungu linalake iye anabwera ku msonkhano kwanthaŵi yoyamba. Tsiku limenelo ine ndinali kukamba nkhani yapoyera. William atangoloŵa, anayang’ana anthu omwe anali mmenemo, n’kuyang’ananso ine kupulatifomu, basi n’kutuluka mu holoyo. N’tam’funsa pambuyo pake chifukwa chomwe anachitira zimenezo. Mwamanyazi, iye anayankha kuti: “Anthu mmenemuja anali otchena kwambiri ndipo ndinachita manyazi.’

“William atapita patsogolo n’kuphunzira kwake, choonadi cha m’Baibulo chinayamba kusintha moyo wake. Anasamba, kumeta tsitsi lake, kuvala zovala zabwino zochapa, ndipo posakhalitsa anayamba kubwera kumisonkhano nthaŵi ndi nthaŵi. Buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha litatulutsidwa, tinayamba kuliphunzira. Panthaŵiyo n’kuti iye atakambapo kale nkhani ziŵiri za m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndipo anali wofalitsa wosabatizidwa. Ndinali wokondwa kwambiri kumulandira monga mbale wanga wauzimu pamene anabatizidwa pamsonkhano watsiku limodzi.”

Kodi n’kuti kumene William anaonera kuti magazini a Nsanja ya Olonda n’ngofunika? “Ndinapeza makope ena a magaziniŵa pa mapepala otayidwa kudzala.” Inde, Iye anapeza chuma m’njira yapadera kwambiri!

Kuchitira Umboni Kuntchito

Kodi m’makhala achangu nthaŵi zonse kugwiritsa ntchito mipata yochitira umboni wamwamwayi kuntchito kwanu? James, yemwe ndi mkulu mumpingo wa Nairobi, anadziŵa choonadi cha Baibulo m’njira imeneyi. Ndipo nayenso wakhala waluso kwambiri pogwiritsa ntchito njirayi kulankhula ndi anthu ena. Mwachitsanzo, nthaŵi ina James anaona wogwira naye ntchito akuloŵa muofesi atavala baji lolembedwa kuti “Yesu Amapulumutsa.” Motsanzira mlaliki Filipo, James anam’funsa mnzakeyo kuti: “Kodi m’madziŵa tanthauzo la mawu amenewo?” (Machitidwe 8:30) Funso limenelo linachititsa kuti ayambe kukambirana. Phunziro la Baibulo linayamba, ndipo kenako munthuyo anabatizidwa. Kodi James zakhala zikumuyendera bwino kwa anthu enanso? Lekani afotokoze yekha:

“Tom ndi ine tinkagwira ntchito pa kampani imodzi. Nthaŵi zambiri tinkakwera limodzi basi yakuntchito kwathu. Tsiku lina m’maŵa, tinakhala pampando umodzi. Ndinkaŵerenga buku lathu linalake, ndipo ndinaligwira m’njira yoti Tom azitha kuona bwinobwino. Monga mmene ndimayembekezera, iye anachita nalo chidwi kwambiri ndipo ndinam’bwereka bukulo mosangalala. Zomwe anaŵerengazo zinam’gwira mtima kwambiri moti anavomera kuti tiziphunzira Baibulo. Tsopano iye pamodzi ndi mkazi wake ndi atumiki a Yehova obatizidwa.”

James akupitiriza kuti: “Kaŵirikaŵiri kukampani kwathu panthaŵi ya nkhomaliro kumakhala macheza abwino kwambiri. Pamacheza ngati ameneŵa m’pamene ndinakumana ndi Ephraim ndi Walter koma panthaŵi zosiyana. Onse aŵiri ankadziŵa kuti ndine wa Mboni. Ephraim ankafuna kudziŵa chifukwa chimene anthu amadana kwambiri ndi Mboni za Yehova. Walter ankafuna kudziŵa kusiyana kwa Mboni ndi zipembedzo zina. Onse aŵiri anakhutira kwambiri ndi mayankho ochokera m’Malemba omwe ndinapereka ndipo anavomera kuti tiziphunzira. Ephraim anaphunzira mofulumira kwambiri. M’kupita kwanthaŵi, iye pamodzi ndi mkazi wake anapatulira miyoyo yawo kwa Yehova. Tsopano iye ndi mkulu ndipo mkazi wake ndi mpainiya wokhazikika. Mosiyana ndi zimenezo, Walter anatsutsidwa kwambiri mpaka anataya buku lake lophunzirira. Komabe, chifukwa cha khama langa, iye anayambanso kuphunzira. Nayenso tsopano akusangalala ndi mwayi wotumikira monga mkulu.” Onse pamodzi, anthu okwana 11 akhala Akristu oona chifukwa chakuti James anagwiritsa ntchito mipata yochitira umboni wamwamwayi kuntchito kwake.

Zotsatira Zochititsa Chidwi Koposa

M’mudzi wina waung’ono m’mphepete mwa nyanja ya Victoria, anthu anasonkhana pamwambo wamaliro. Pagululo panali Mboni ina yokalamba. Iyo inayandikira mphunzitsi wina wamkazi wotchedwa Dolly ndipo anam’fotokozera za anthu akufa ndiponso za chifuno cha Yehova chochotseratu imfa. Ataona chidwi chake, mbaleyo anatsimikizira mphunzitsiyo amvekere: “Ukabwerera kutauni yakwanu, mmodzi mwa amishonale athu adzakupeza ndipo adzakuphunzitsa Baibulo.”

Tauni yakwawo kwa Dolly ndi mzinda wachitatu pa mizinda yaikulu koposa ku Kenya. Panthaŵiyo n’kuti amishonale anayi okha akugwira ntchito mumzindawo. Mbale wokalambayo sanadziŵitse n’komwe mmishonale wina aliyense kuti akaonane ndi Dolly. Iye anali chabe ndi chikhulupiriro chonse kuti zinthu zidzachitika motero. Ndipo zinaterodi! Posapita nthaŵi, mlongo wina yemwe ndi mmishonale anakumana ndi Dolly ndipo anayamba kuphunzira naye. Tsopano Dolly anabatizidwa, ndipo mwana wake wamng’ono wamkazi analembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase komanso ana ake amuna aŵiri anabatizidwa. Iye analinso wosangalala kuchita nawo Sukulu ya Utumiki Waupainiya.

Kusamalira Kuchuluka kwa Anthu

Kuikirapo mtima pa kuchita umboni wamwamwayi kwachititsa kuti anthu ena zikwi zambiri amve uthenga wabwino ku Kenya. Tsopano ofalitsa opitirira 15,000 akuchita ntchito yofunika imeneyi, ndipo oposa 41,000 anali nawo pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu chaka chatha. M’dziko lonse la Kenya, anthu ofika pamisonkhano nthaŵi zambiri amakhala ochuluka kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu. Chifukwa cha zimenezi pakufunika Nyumba za Ufumu zambiri.

Nyumba za Ufumu zikumangidwa m’mizinda yaikulu ndiponso kumidzi. Imodzi mwa nyumba zimenezi ili m’boma la Samburu, lomwe lili kwalokha mtunda wamakilomita 320 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Nairobi. Mu 1934, tauniyo anaitcha kuti Maralal, mawu a m’Chisamburu otanthauza “kunyezimira, chifukwa chakuti nyumba yoyamba yamalata imeneyi inkanyezimira ndi dzuŵa. Patatha zaka 62 nyumba ina yamalata inamangidwa ku Maralal. Nayonso “ikunyezimira” ndiponso “kuwala” chifukwa chakuti ndiyo malo a kulambira koona m’deralo.

Ofalitsa okwana 15 anayetsetsa kwambiri kumanga Nyumba ya Ufumu yoyamba m’dera lakumidzi limeneli ku Kenya. Ndalama zinali zochepa moti abale anadalira zipangizo wamba zakomweko. Anamanga khoma ndi nsichi ndiyeno n’kulimata ndi dothi lofiira. Khomalo analisalaza ndipo kenako analikulungiza kapena kuti kulitsutsuta pogwiritsa ntchito ndowe za ng’ombe zosakaniza ndi phulusa. Zimenezi zinachititsa khomalo kukhalabe lolimba kwa zaka zambiri.

Kuti apeze nsichi za nyumbayo, abale anatenga chilolezo chodula mitengo. Koma nkhalango yapafupi inali pamtunda wa makilomita khumi. Abale ndi alongo ankapita kunkhalangoyo kukadula mitengo n’kuisadza bwinobwino. Kenako ankainyamula kupita nayo komwe ankamanga nyumbayo. Nthaŵi ina akuchokera ku nkhalangoko, wapolisi anawaimitsa abalewo n’kunena kuti chilolezo chawocho chinali chosayenera. Wapolisiyo anauza mpainiya wapadera kuti wamangidwa chifukwa chodula mitengo. Mlongo wina wodziŵika kwambiri m’deralo komanso kwa apolisiwo, ananena kuti: “Ngati mwamanga mbale wathu, ndiye kuti mumange tonse chifukwa tonsefe timadula mitengo!” Kenako wapolisiyo anawauza onse kuti apite.

M’nkhalangomo munalinso nyama zolusa moti kuyendamo kunali koopsa. Tsiku lina, mlongo wina ankadula mtengo ndipo mtengowo utagwa pansi, iye anaona nyama ikudumpha kenako inathaŵa. Ikudutsa iye sanaionetsetse bwino, ndipo ankaganiza kuti ndi mphoyo, koma kenako ataona mapazi ake anadziŵa kuti unali mkango! Ngakhale kuti panali zoopsa zoterezi, abale anamaliza holoyo ndipo ‘ikunyezimira’ ndi kutamanditsa Yehova.

Pa February 1, 1963, linali tsiku lalikulu m’mbiri yateokalase ya dziko la Kenya. Patsikuli m’pamene anatsegulira ofesi ya nthambi yomwe inali nyumba imodzi chabe yaikulu mamita 7.4. Pa October 25, 1997, linalinso tsiku lina losaiŵalika m’mbiri yateokalase m’dziko la Kenya. Patsikuli anapatulira malo a Beteli aakulu mamita 7,800! Ntchito yomanga maloŵa inatha patapita zaka zitatu. Antchito ongodzipereka ochokera m’mayiko 25 anasandutsa malo amatope komanso a thengo ameneŵa kukhala malo okongola kwambiri a nthambi komwe kumakhala anthu a banja la Beteli okwana 80.

Mpake kukondwera ndi zomwe Yehova wachitira anthu ake. Tikuthokoza Yehova kwambiri chifukwa chosonkhezera mitima ya atumiki ake kuti afutukule ndi kulimbikitsa ntchito yofunafuna oyenerera ku Kenya zomwe zachititsa kuti dzikolo likhale lokongola mwauzimu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

^ ndime 13 Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.