Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsiku la Yehova Lopereka Chiŵeruzo Layandikira!

Tsiku la Yehova Lopereka Chiŵeruzo Layandikira!

Tsiku la Yehova Lopereka Chiŵeruzo Layandikira!

“Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi, lifulumira kudza.”​—ZEFANIYA 1:14.

1. Kodi Mulungu anapereka chenjezo lotani kudzera mwa Zefaniya?

YEHOVA MULUNGU wangotsala pang’ono kuti athane ndi anthu oipa. Mvetserani! Iye akuchenjeza kuti: “Ndidzatha munthu . . . ndidzawononga anthu kuwachotsa panthaka.” (Zefaniya 1:3) Ambuye Mfumu Yehova analankhula mawu amenewo kudzera mwa mneneri wake Zefaniya, mwinamwake mdzukulu wa mdzukulu wa Mfumu Hezekiya wokhulupirikayo. Chilengezo chimenecho, choperekedwa m’masiku a Mfumu Yosiya wabwinoyo, sichinawakomere anthu “oipa” a m’dziko la Yuda.

2. N’chifukwa chiyani zomwe anachita Yosiya sizinalepheretse kufika kwa tsiku la Yehova lopereka chiweruzo?

2 Mosakayikira, kulosera kwa Zefaniya kunachititsa Yosiya wachinyamatayo kuzindikira kwambiri za kufunika kochotsa kulambira konyansa m’dziko la Yuda. Komabe, zimene mfumu inachita poyesetsa kufafaniza chipembedzo chonyenga m’dzikolo sizinathetse kuipa konse pakati pa anthuwo kapena kufafaniza machimo a agogo ake aamuna, Mfumu Manase, amene “anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa.” (2 Mafumu 24:3, 4; 2 Mbiri 34:3) Chotero, tsiku la Yehova lopereka chiŵeruzo linali kudzafika ndithu.

3. Tingatsimikizire motani kuti kupulumuka “tsiku la mkwiyo wa Yehova” n’kotheka?

3 Komabe, panayenera kudzapezeka opulumuka pa tsiku lochititsa mantha limenelo. Chotero, mneneri wa Mulungu analimbikitsa kuti: “Lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zefaniya 2:2, 3) Pamene tikuganizira za chiyembekezo chodzapulumuka tsiku la Yehova lopereka chiweruzo, tiyeni tipende buku la m’Baibulo la Zefaniya. Bukuli linalembedwa mu Yuda chisanafike chaka cha 648 B.C.E., ndipo lili mbali ya “mawu a chinenero” a Mulungu amene tonsefe tiyenera kuwalabadira ndi mtima wonse.​—2 Petro 1:19.

Yehova Atambasula Dzanja Lake

4, 5. Kodi Zefaniya 1:1-3 anakwaniritsidwa motani pa oipa mu Yuda?

4 “Mawu a Yehova” kwa Zefaniya akuyamba ndi chenjezo lomwe talitchula kale lija. Mulungu akulengeza kuti: “Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova. Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m’mlengalenga, ndi nsomba za m’nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzawononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.”​—Zefaniya 1:1-3.

5 Inde, Yehova anali kudzathetsa kuipa konse m’dziko la Yuda. Kodi Mulungu anali kudzagwiritsa ntchito ndani “kuzichotsa [zonse] panthaka”? Popeza kuti Zefaniya mwachionekere anapereka ulosiwu kumayambiriro kwa ulamuliro wa Mfumu Yosiya, umene unayamba mu 659 B.C.E., mawu aulosi amenewo anakwaniritsidwa pa chiwonongeko cha Yuda ndi likulu lake, Yerusalemu, m’manja mwa Ababulo mu 607 B.C.E. Panthaŵi imeneyo, ‘anawatha onse’ oipa mu Yuda.

6-8. N’chiyani chomwe chinaloseredwa pa Zefaniya 1:4-6, nanga kodi ulosi umenewo unakwaniritsidwa motani mu Yuda wakale?

6 Poneneratu zomwe Mulungu adzachitira olambira onyenga, Zefaniya 1:4-6 akuti: “Ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m’Yerusalemu; ndipo ndidzawononga otsala a Baala kuwachotsa m’malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe; ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu; ndi iwo akubwerera osam’tsata Yehova; ndi osam’funa Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.”

7 Yehova anatambasula dzanja lake pokantha anthu a m’Yuda ndi m’Yerusalemu. Iye anatsimikiza kupha alambiri a mulungu wa Akanani, Baala, wa mphamvu za kubereka. Milungu yosiyanasiyana amaitcha Abaala chifukwa olambira ake anali kukhulupirira kuti ili ndi mphamvu m’madera akutiakuti. Mwachitsanzo, panali Baala yemwe Amoabu ndi Amidyani amam’lambira pa Phiri la Peori. (Numeri 25:1, 3, 6) M’Yuda monse, Yehova anali kudzadula ansembe a Baala, limodzinso ndi ansembe achilevi osakhulupirika amene anali kuphwanya chilamulo cha Mulungu mwa kuyanjana ndi ansembe amenewo.​—Eksodo 20:2, 3.

8 Mulungu analinso kudzadula aja ‘akulambira khamu lakumwamba,’ mwachionekere kutanthauza okhulupirira nyenyezi ndi olambira dzuŵa. (2 Mafumu 23:11; Yeremiya 19:13; 32:29) Mkwiyo wa Mulungu unalinso kudzayakira aja oyesa kusakaniza kulambira koona ndi chipembedzo chonyenga mwa ‘kulumbira kwa Yehova ndi kulumbiranso kwa mfumu.’ N’kutheka kuti mfumu imeneyi akutanthauza Moleki, mulungu wamkulu wa Aamori. Kulambira Moleki kunkaphatikizapo kupereka nsembe ana.​—1 Mafumu 11:5; Yeremiya 32:35.

Mapeto a Matchalitchi Achikristu Ali Pafupi!

9. (a) Kodi Matchalitchi Achikristu ali ndi mlandu wotani? (b) Mosiyana ndi anthu osakhulupirira a mu Yuda, kodi ife tiyenera kutsimikiza mtima kuchitanji?

9 Zonsezi zikutikumbutsa za Matchalitchi Achikristu, omwe aloŵerera m’kulambira konyenga ndi kukhulupirira nyenyezi. Ndipotu zomwe Matchalitchi Achikristuwo akuchita zopereka nsembe miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri m’nkhondo zochirikizidwa ndi atsogoleri achipembedzo, n’chinthu chonyansa kwabasi! Tisakhaletu ngati Ayuda osakhulupirika aja, omwe ‘anabwerera osam’tsata Yehova,’ tisagwe mphwayi ndi kusam’funafunanso iye kapena chitsogozo chake. M’malo mwake, tiyeni tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu.

10. Kodi mungafotokoze motani tanthauzo laulosi la Zefaniya 1:7?

10 Mawu otsatira a mneneriyu akuyenerera ochimwa a m’Yuda ndi oipa a m’nthaŵi yathu. Zefaniya 1:7 akuti: “Khalani chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.” Mwachionekere, ‘oitanidwawo’ anali Akasidi, adani a Yuda. ‘Nsembeyo’ inali Yuda yemweyo, kuphatikizapo likulu lake. Chotero Zefaniya analengeza cholinga cha Mulungu cha kuwononga Yerusalemu, ndiponso ulosi umenewu ukunenanso za kuwonongedwa kwa Matchalitchi Achikristu. Kwenikweni, pamene tsiku la Mulungu lopereka chiweruzo layandikira chonchi, dziko lonse liyenera ‘kukhala chete pamaso pa Mfumu Ambuye Yehova’ ndi kumvetsera zimene akunena kudzera mwa “kagulu ka nkhosa” ka otsatira a Yesu odzozedwa ndi anzawo a “nkhosa zina.” (Luka 12:32; Yohane 10:16) Chiwonongeko chili pafupi kwa onse omwe sadzamvera ndi onse amene mwa kusamverako akupandukira ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.​—Salmo 2:1, 2.

Posachedwapa​—Tsiku la Kuchema Lifika!

11. Kodi tanthauzo lalikulu la Zefaniya 1:8-11 n’lotani?

11 Ponena za tsiku la Yehova, Zefaniya 1:8-11 akuwonjezera kuti: “Kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo. Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiunda, nadzaza nyumba ya mbuye wawo ndi chiŵaŵa ndi chinyengo. Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera ku chipata cha nsomba, ndi kuchema kochokera ku dera lachiŵiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera, kuzitunda. Chemani okhala m’chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva awonongeka.”

12. Kodi ena akupezeka bwanji “akuvala chovala chachilendo”?

12 Mfumu Yosiya anali kudzaloŵedwa m’malo ndi Yehoahazi, Yoyakimu, ndi Yoyakini. Kenako panali kudzafika ulamuliro wa Zedekiya, umene timaukumbukira ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Ngakhale kuti anayang’anizana ndi tsoka limenelo, zikuoneka kuti ena anafuna kupanga ubwenzi ndi mitundu yoyandikana nayo mwa ‘kuvala chovala chachilendo.’ Mofananamo, ambiri lero amadzionetsera m’njira zosiyanasiyana kuti sali kumbali ya gulu la Yehova. Popeza kuti adzionetsera kukhala mbali ya gulu la Satana, adzalangidwa.

13. Mogwirizana ndi ulosi wa Zefaniya, kodi n’chiyani chinayenera kuchitika Ababulo ataukira Yerusalemu?

13 “Tsiku ilo” loŵerengera mlandu Yuda limafanana ndi tsiku la Yehova lopereka chiweruzo kwa adani ake, pothetsa kuipa konse, ndi kusonyeza ukulu wake. Pamene Ababulo adzaukira Yerusalemu, kuchema kunali kudzamveka kuchokera kuchipata cha Nsomba. Mwina chinatchedwa choncho chifukwa chinali pafupi ndi msika wa nsomba. (Nehemiya 13:16) Magulu a Babulo akaloŵera kuchigawo chotchedwa dera lachiŵiri, ndipo “kugamuka kwakukulu kochokera ku zitunda” kungatanthauze phokoso la Akasidi omwe akufika. Panayenera kudzamveka “kuchema” kwa anthu a ku chigwa, mwinamwake kumtunda kwa Chigwa cha Tiropeoni. Kodi anayenera kudzachema chifukwa chiyani? Chifukwa malonda awo, kuphatikizapo a “onsewo osenza siliva,” anali kudzathera pomwepo.

14. Kodi Mulungu anali kudzachitanji posanthula anthu odzitcha olambira ake?

14 Kodi Yehova adzachitanji posanthula anthu omwe amati n’ngolambira ake? Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Kudzachitika nthaŵi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m’mitima mwawo, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa. Ndipo zolemera zawo zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zawo zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzawoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.”​—Zefaniya 1:12, 13.

15. (a) N’chiyani chomwe chinali kudzachitikira ansembe ampatuko a mu Yerusalemu? (b) Kodi olambira onyenga amakono chidzawachitikire n’chiyani?

15 Ansembe ampatuko a ku Yerusalemu ankasakaniza kulambira Yehova ndi chipembedzo chonyenga. Ngakhale kuti ankaona ngati anali otetezeka, Mulungu anawavumbula poyera ngati kuti anawaunika ndi nyali zoŵala kwambiri zimene zinaŵalira mumdima wauzimu momwe iwo anali atabisalamo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene akathaŵa chiweruzo ndi chilango cha Mulungu. Ampatuko opusawo anakhazikika pansi ngati masese m’chipanda cha moŵa. Sanafune chilengezo chilichonse cha kuloŵerera kwa Mulungu m’zochita za anthu kuwasokoneza, koma sakanatha kuthaŵa kuweruzidwa ndi Mulungu. Onse ochirikiza chipembedzo chonyenga lerolino sadzathanso kuthaŵa, kuphatikizapo mamembala a Matchalitchi Achikristu, komanso anthu ena omwe apatuka pakulambira Yehova. Pokana kuti ameneŵa sali “masiku otsiriza,” m’mitima yawo amati, ‘Yehova sadzachita chokoma, kapena kuchita choipa.’ Ati umbuli wake eti!​—2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4, 10.

16. N’chiyani chimene chinali kudzachitika pamene Mulungu akupereka chiweruzo pa Yuda, ndipo kodi kudziŵa zimenezo kuyenera kutikhudza motani?

16 Ampatuko a Yuda anachenjezedwa kuti Ababulo adzafunkha chuma chawo, adzapasula nyumba zawo, ndi kutenga zipatso za minda yawo yamphesa. Chuma chakuthupi chinali chopanda pake pamene Mulungu anapereka chiweruzo chake pa Yuda. Zidzakhalanso momwemo pamene tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lifika padongosolo la zinthu lilipoli. Choncho, tiyeni tikhale ndi kaonedwe ka zinthu kauzimu ndi ‘kukundika chuma chathu kumwamba’ mwa kutsogoza kutumikira Yehova m’miyoyo yathu!​—Mateyu 6:19-21, 33.

“Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”

17. Malinga ndi Zefaniya 1:14-16, kodi tsiku la Yehova lopereka chiweruzo layandikira motani?

17 Kodi tsiku la Yehova lopereka chiweruzo layandikira motani? Malinga ndi Zefaniya 1:14-16, Mulungu akupereka chitsimikizo ichi: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mawu a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo moŵaŵa mtima. Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la masauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii, tsiku la lipenga ndi lakufuulira midzi yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungondya.”

18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kulingalira kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lili kutali?

18 Ansembe ochimwa a Yuda, akalonga, ndi anthu ena anachenjezedwa kuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” Kwa Yuda ‘tsiku la Yehova linali kufulumira kwambiri kudza.’ Chimodzimodzinso m’nthaŵi zathu zino, munthu asaganize kuti chiweruzo cha Yehova pa anthu oipa chidakali kutali. M’malo mwake, monga momwe Mulungu anachitirapo kanthu mwamsanga pa Yuda, ‘adzafulumizanso’ tsiku lake lopereka chiŵeruzo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Idzakhalatu nthaŵi yoŵaŵa kwabasi kwa onse osalabadira machenjezo a Yehova operekedwa ndi Mboni zake komanso kwa olephera kuvomereza kulambira koona!

19, 20. (a) Kodi kunachitika zotani pamene Mulungu anapereka mkwiyo wake pa Yuda ndi Yerusalemu? (b) Polingalira za kuwononga mosankha komwe kudzachitikira dongosolo lino la zinthu, kodi pakubuka mafunso otani?

19 Tsiku la mkwiyo wa Mulungu pa Yuda ndi Yerusalemu, linali “tsiku la masauko ndi lopsinja.” Oukira achibabulo anadzetsa mavuto ochuluka kwa anthu a Yuda, kuphatikizapo kusauka kwa maganizo poyang’anizana ndi imfa ndi chiwonongeko. “Tsiku la bwinja, ndi chipasuko” limenelo linali tsiku la mdima, mitambo, ndi chisisira, mwinamwake osati mophiphiritsa mokha komanso kwenikweni, chifukwa utsi ndi mitembo zinali paliponse. Linali “tsiku la lipenga ndi kufuulira,” koma machenjezowo anaperekedwa mosaphula kanthu.

20 Alonda a Yerusalemu anagwira njakata Ababulo atayamba kuswa ndi zida zawo “nsanja zazitali zakungondya.” M’tsiku lathu, chitetezo cha dziko lamakonoli chidzakhala chopanda pake polimbana ndi zida zimene zili m’malo a Mulungu ozisungiramo kumwamba, zimene wakonzekera kuzigwiritsa ntchito mwamsanga powononga chomwe adzasankha kuchiwononga. Kodi mukuyembekeza kudzapulumuka? Kodi mwaima mwamphamvu kumbali ya Yehova, amene ‘amasunga onse akukondana naye; koma wowononga oipa onse?’​—Salmo 145:20.

21, 22. Kodi Zefaniya 1:17, 18 adzakwaniritsidwa motani m’tsiku lathu?

21 Lilitu tsiku la chiweruzo lochititsa mantha kwabasi loloseredwa pa Zefaniya 1:17, 18! “Ndidzatengera anthu zowapsinja,” akutero Yehova Mulungu, ndipo “adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wawo udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yawo idzanga ndowe. Ngakhale siliva wawo, ngakhale golidi wawo sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m’dziko.”

22 Monga anachitira m’masiku a Zefaniya, Yehova adzadzetsera zopsinja kwa “onse okhala m’dziko,” okana kumvera chenjezo lake. Chifukwa amachimwira Mulungu, adzayenda mothedwa nzeru ngati akhungu, osatha kupeza chipulumutso. Patsiku la Yehova lopereka chiweruzo, mwazi wawo “udzatsanulidwa ngati fumbi,” monga chinthu chopanda ntchito. Adzafa imfa yonyozeka kwabasi, chifukwa Mulungu adzamwaza mitembo yawo​—ngakhale zam’mimba​—za oipaŵa padziko lonse lapansi, ngati “ndowe.”

23. Ngakhale kuti ochita zoipa sadzatha kuthaŵa “tsiku la mkwiyo wa Yehova,” kodi ulosi wa Zefaniya ukupereka chiyembekezo chotani?

23 Palibe aliyense amene angapulumutse olimbana ndi Mulungu komanso anthu ake. Siliva ngakhale golidi sanathe kupulumutsa ochimwa a mu Yudawo. Momwemonso, chuma chobisika ndi ziphuphu sizidzateteza kapena kupulumutsa Matchalitchi Achikristu ndi dongosolo lonse loipali pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Patsiku limenelo la chiweruzo, “dziko lonse lidzatha” ndi moto wa changu cha Mulungu pamene adzasesa kotheratu oipa onse. Popeza kuti tili n’chikhulupiriro m’mawu aulosi a Mulungu, ndife otsimikizira kuti tsopano tili m’kati mwenimweni mwa “nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) Tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lili pafupi, ndipo posachedwapa adzabwezera adani ake. Komabe, ulosi wa Zefaniya ukupereka chiyembekezo cha chipulumutso. Tsono, kodi chofunika n’chiyani kuti tikabisike pa tsiku la ukali wa Yehova?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ulosi wa Zefaniya unakwaniritsidwa motani pa Yuda ndi Yerusalemu?

• N’chiyani chomwe chidzachitikira Matchalitchi Achikristu ndi oipa onse a m’tsiku lathu?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kulingalira kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo lidakali kutali?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Zefaniya analengeza molimba mtima kuti tsiku la Yehova lopereka chiweruzo linali pafupi

[Mawu a Chithunzi]

Kuchokera mu Self-Pronouncing Edition of the Holy Bible, lokhala ndi King James komanso Revised versions

[Chithunzi patsamba 15]

Tsiku la Yehova linafikira Yuda ndi Yerusalemu ataukiridwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E.

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi mukuyembekeza kudzapulumuka pamene Yehova adzawononga oipa?