Udani Woyenera ndi Wosayenera
Udani Woyenera ndi Wosayenera
BAIBULO limatsutsa amene amasonyeza udani kwa mnzake. Komanso, limanena za udani umene atumiki a Mulungu ayenera kukhala nawo.
Kuti timvetsetse mmene Mulungu amaonera udani, tiyenera kuzindikira kuti m’Malemba, mawu akuti “udani” ali ndi matanthauzo angapo. Angatanthauze mkwiyo waukulu, wa kusafunira wina zabwino kopitirizabe, komwe kaŵirikaŵiri kumaphatikizapo njiru. Udani umenewo ungakule kufikira pofuna kuvulaza munthu wina. “Udani” ungatanthauzenso kuipidwa kwambiri ndi chinthu kapena munthu popanda cholinga chofuna kumuvulaza, koma kuyesetsa kupeza chinthucho kapena munthuyo chifukwa cha kunyansidwa naye. Komanso, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “udani” kutanthauza kukonda pang’ono.—Genesis 29:31, 33; Deuteronomo 21:15, 16.
Udani Wosayenera
Lamulo la Mulungu kwa Aisrayeli linati: “Usamamuda mbale wako mumtima mwako.” (Levitiko 19:17) Chimodzi mwa zofunika kwa munthu yemwe wathaŵira ku midzi yopulumukirako pofuna chitetezo chifukwa cha kupha munthu mwangozi, chinali chakuti analibe udani ndi wophedwayo.—Deuteronomo 19:4, 11-13.
Lamulo la Yesu lakuti munthu akonde adani ake, n’logwirizana kwambiri ndi chiphunzitso cha m’Malemba Achihebri. (Mateyu 5:44) Yobu, munthu wokhulupirika anazindikira kuti kukakhala kulakwa ngati iye akasangalala m’njira iliyonse chifukwa cha kuvutika kwa amene anali kumuda kwambiri. (Yobu 31:29) Chilamulo cha Mose chinapatsa Aisrayeli udindo wa kuthandiza Aisrayeli anzawo omwe amawaona monga adani awo. (Eksodo 23:4, 5) M’malo mwa kusangalala ndi kuvutika kwa mdani wawo, atumiki a Mulungu akulangizidwa kuti: “Mdani wako akamva njala um’dyetse, Akamva ludzu um’mwetse madzi.”—Miyambo 25:21.
Malingaliro akuti adani ayenera kudedwa, anali pakati pa malingaliro omwe aphunzitsi a miyambo yachiyuda anaphatikiza ku chilamulo cha Mulungu. Chifukwa chakuti Chilamulo chinalangiza Aisrayeli kukonda anansi awo, aphunzitsi ameneŵa anaganiza kuti izi zikutanthauza kuti anayeneranso kuda adani awo. (Levitiko 19:18) Mawu akuti “bwenzi” ndi “mnansi” anayamba kuwaona monga onena za Ayuda okha basi, pamene anthu ena onse anali kuwaona monga adani. Poona mmene anali kugwiritsira ntchito mawu akuti “mnansi” ndiponso chikhalidwe chawo chomwe chinkalimbikitsa kudana ndi anthu a mitundu ina, n’zosavuta kumvetsa chifukwa chake anaphatikiza Mawu awoawo akuti, “ndi kumuda mdani wako” pa lamulo la Mulungu.—Mateyu 5:43.
Mosiyana ndi zimenezo, Mkristu ayenera kukonda adani ake, anthu amene amamuda. Chikondi chimenechi, (m’Chigiriki, a·gaʹpe) si kungotengeka maganizo chifukwa cha kuzoloŵerana, monga mmene ambiri
amaganizira, koma lili khalidwe kapena kuti chikhalidwe cha kukonda anthu, monga udindo ndiponso chinthu choyenera, kufunafuna ubwino wa ena moona mtima pa zinthu zoyenera.Chikondi cha a·gaʹpe chimakwirira udani, sichilola munthu kunyalanyaza mfundo zoyenera zachikhalidwe chifukwa cha maudani, koma kuchitira anthu mokoma mtima. Kwa omwe mosazindikira amatsutsa moyo wake wachikristu ndiponso kum’zunza, mtumiki wa Mulungu adzawapempherera oterowo kuti maso awo atseguke kotero kuti aone choonadi cha Mulungu ndiponso zolinga Zake.—Mateyu 5:44.
Peŵani Udani Wosayenera
Pamene akhala Akristu, anthu amene kale anali kudana amakondana. (Tito 3:3) Amene amada mbale wake akadali mumdima, ndipo lingakhale bodza ndithu atanena kuti amakonda Mulungu. Munthu wodana ndi mbale wake n’ngwofanana ndi wakupha munthu.—1 Yohane 4:20; 3:15.
Kutengeka maganizo pa chikondi ndi pa udani, kungapangitse munthu kuchita mopambanitsa, monga mmene zinachitikira kwa Davide ponena za mwana wake Abisalomu. (2 Samueli 18:33; 19:1-6) Choncho, “wolekerera mwanake osam’menya amuda; koma wom’konda am’yambize kum’langa.”—Miyambo 13:24.
Mwa kulemekeza ufulu wa ena wofuna kukhala paokha ndi kusonyeza kuwaganizira mwachikondi, munthu angapewe kukhala wodedwa mosayenera. N’chifukwa chake pali langizo lakuti: “Phazi lako liloŵe m’nyumba ya mnzako kamodzikamodzi; kuti angatope nawe ndi kukuda.”—Miyambo 25:17.
Udani Woyenera
Pazochitika zina ndiponso nthaŵi zina, n’koyenera kusonyeza udani. Pali “mphindi ya kukonda ndi mphindi ya kudana.” (Mlaliki 3:1, 8) Ngakhale ponena za Yehova, Baibulo limati anamuda Esau. (Malaki 1:2, 3) Koma zimenezi sizitanthauza kuti Mulungu amada munthu popanda chifukwa chenicheni. Esau anadzionetsera yekha kuti anali wosayenera chikondi cha Yehova mwa kunyoza cholandira chake cha kukhala woyamba kubadwa mwakuchigulitsa, zomwe zinasonyezanso kusayamikira malonjezo ndi madalitso a Mulungu. Kuwonjezera apo, anakonza za kupha mbale wake Yakobo.—Genesis 25:32-34; 27:41-43; Ahebri 12:14-16.
Posonyeza kukhulupirika koona kwa Yehova, atumiki ake amada chomwe iye amachida ndiponso omwe iye amawada. Wamasalmo analemba kuti: “Kodi sindidana nawo iwo akudana ndi Inu, Yehova, ndipo kodi sindimva nawo chisoni iwo akuukira Inu? Ndidana nawo ndi udani weniweni: ndiwayesa adani.”—Salmo 139:21, 22.
Koma udani umenewu sufuna kuvulaza ena ndipo sufanana ndi mtopola kapena njiru. M’malo mwake, ndiko kukanitsitsa choipa, kupewa choipa ndiponso anthu amene amada Yehova kwambiri. (Aroma 12:9, 17, 19) Moyenera, Akristu amada amene ali adani otsimikizirika a Mulungu, monga Mdyerekezi ndi ziwanda zake, kuphatikizanso anthu amene asankha kukhala otsutsana ndi Yehova mwadala.
Ngakhale kuti Akristu sakonda amene asandutsa chisomo cha Mulungu kukhala chifukwa chochitira zosayenera, iwo sada anthu omwe achimwa amene ali oyenerera kusonyezedwa chifundo. M’malo mwa kudana ndi wochimwa yemwe walapa, amadana ndi mchitidwe wa choipawo, inde, amadana ngakhalenso ndi “malaya ochitidwa mawanga ndi thupi.”—Yuda 4, 23.