Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipulumutso kwa Osankha Kuunika

Chipulumutso kwa Osankha Kuunika

Chipulumutso kwa Osankha Kuunika

“Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani?”​—SALMO 27:1.

1. Kodi n’zinthu ziti zopatsa moyo zomwe Yehova wapereka?

YEHOVA ndiye Gwero la kuwala kwa dzuŵa kumene kumachirikiza moyo padziko lapansi. (Genesis 1:2, 14) Iye alinso Mlengi wa kuunika kwauzimu, kumene kumachotsa mdima wakupha wa dziko la Satanali. (Yesaya 60:2; 2 Akorinto 4:6; Aefeso 5:8-11; 6:12) Awo amene asankha kuunika anganene zomwe wamasalmo ananena kuti: “Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani?” (Salmo 27:1a) Komabe, monga momwe zinalili m’nthaŵi ya Yesu, amene akukonda mdima sakuyembekezera china chilichonse koma chiweruzo basi.​—Yohane 1:9-11; 3:19-21.

2. M’nthaŵi yakale, n’chiyani chomwe chinachitikira okana kuunika kwa Yehova, komanso omwe anamvera mawu ake?

2 M’masiku a Yesaya, ochuluka mwa anthu a pangano la Yehova anakana kuunika. Zotsatira zake zinali zakuti Yesaya anaona kuwonongedwa kwa ufumu wakumpoto wa mtundu wa Israyeli. Ndipo mu 607 B.C.E., Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa ndikuti anthu okhala mu Yuda anawatengera kuukapolo. Komabe, omwe anamvera mawu a Yehova analimbitsidwa kuti athe kupeŵa mpatuko wa m’nthaŵi imeneyo. Ponena za chaka cha 607 B.C.E., Yehova analonjeza kuti onse amene akam’mvera akapulumuka. (Yeremiya 21:8, 9) Lerolino, ife amene timakonda kuunika tingathe kuphunzira zochuluka kuchokera ku zomwe zinachitika kalelo.​—Aefeso 5:5.

Chisangalalo kwa Okhala M’kuunika

3. Lerolino, kodi tingakhale otsimikizira za chiyani, ndi “mtundu wolungama” uti umene timaukonda, ndipo ndi “mudzi wolimba” uti umene “mtundu” umenewu uli nawo?

3 “Ife tili ndi mudzi wolimba. [Mulungu] adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga. Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zoonadi ulowemo.” (Yesaya 26:1, 2) Awa ndi mawu achisangalalo a anthu okhulupirira Yehova. M’tsiku la Yesaya, Ayuda okhulupirika anayang’ana kwa Yehova monga Gwero lokhalo loona la chitetezo, osati kwa milungu yonyenga ya anthu ena m’dzikomo. Lerolino timam’daliranso Yehova mofananamo. Komanso timakonda “mtundu wolungama” wa Yehova​—“Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Mateyu 21:43) Yehova nayenso amaukonda mtundu umenewu chifukwa cha kukhulupirika kwake. Ndi madalitso ake, Israyeli wa Mulungu ali ndi “mudzi wolimba,” gulu lokhala ngati mudzi limene limachirikiza ndi kuteteza mtundu umenewu.

4. Kodi tiyenera kukulitsa mtima wotani?

4 Awo amene ali ‘m’mudzi’ umenewu akudziŵa bwino kuti ‘[Yehova] adzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa umakhulupirira [Yehova].’ Yehova amachirikiza anthu amene amam’khulupirira ndi mtima wawo wonse ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake za khalidwe lolungama. Chotero, anthu okhulupirika mu Yuda anamvera chenjezo la Yesaya lakuti: “Khulupirirani Yehova nthaŵi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.” (Yesaya 26:3, 4; Salmo 9:10; 37:3; Miyambo 3:5) Awo amene ali ndi mtima umenewu amayang’ana kwa “Ambuye Yehova” monga Thanthwe lokhalo lobisalirako. Amakhala naye mu “mtendere weniweni.”​—Afilipi 1:2; 4:6, 7.

Adani a Mulungu Adzatsitsidwa

5, 6. (a) Kodi Babulo wakale anatsitsidwa motani? (b) Kodi “Babulo Wamkulu” anatsitsidwa m’njira iti?

5 Bwanji ngati okhulupirira Yehova azunzidwa? Sayenera kuopa. Yehova amalolera kuti zinthu zotero zichitike kwa kanthaŵi kochepa, koma pambuyo pake amadzetsa mpumulo, ndipo ozunzawo amawaweruza. (2 Atesalonika 1:4-7; 2 Timoteo 1:8-10) Lingalirani zimene zinachitikira “mudzi wa pamsanje.” Yesaya amati: “[Yehova] watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje; iye wautsitsa, wautsitsira pansi; waugwetsa pansi pa fumbi. Phazi lidzaupondereza pansi; ngakhale mapazi a aumphaŵi, ndi mapondedwe a osoŵa.” (Yesaya 26:5, 6) Mudzi wa pamsanje wotchulidwa pano mwinamwake ndi Babulo. Ndithudi mzinda umenewu unazunza anthu a Mulungu. Koma kodi n’chiyani chinachitikira Babulo? M’chaka cha 539 B.C.E, unagonja kwa Amedi ndi Aperisi. Zochititsa manyazi bwanji!

6 M’tsiku lathu lino mawu aulosi a Yesaya akufotokoza momveka zomwe zachitikira “Babulo Wamkulu” chiyambire 1919. Mzinda wokwezeka umenewo unagwa mochititsa manyazi m’chaka chimenecho pamene unaumirizika kumasula anthu a Yehova kuchokera kuukapolo wauzimu. (Chivumbulutso 14:8) Zomwe zinachitika pambuyo pake zinalinso zochititsa manyazi kwambiri. Kagulu kakang’ono kameneko ka Akristu kanayamba ‘kupondereza pansi’ amene anawagwira ukapolowo. M’chaka cha 1922 anayamba kulengeza kudza kwa mapeto a Matchalitchi Achikristu, kulengeza za kuwomba malipenga kwa angelo anayi konenedwa pa Chivumbulutso 8:7-12 ndi masoka atatu oloseredwa pa Chivumbulutso 9:1–11:15.

“Njira ya Wolungama Ili Njira Yoongoka”

7. Kodi amene amatembenukira ku kuunika kwa Yehova amalandira chitsogozo chotani, ndipo kodi amayembekezera yani, nanga amakonda chiyani?

7 Yehova amapulumutsa onse otsata kuunika kwake, ndipo amatsogolera njira zawo, monga momwe Yesaya akusonyezera kuti: “Njira ya wolungama ili njira yoongoka; Inu amene muli woongoka, mukonza njira ya wolungama. Inde m’njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu.” (Yesaya 26:7, 8) Yehova ndi Mulungu wolungama, ndipo awo amene amam’lambira ayenera kutsatira miyezo yake yolungama. Akachita zimenezo, Yehova amawatsogolera, ndi kuwongola njira yawo. Mwa kumvera malangizo ake, odzichepetsa ameneŵa amasonyeza kuti ali ndi chiyembekezo mwa Yehova ndikuti ndi mtima wonse amakonda dzina lake​—“chikumbukiro” chake.​—Eksodo 3:15.

8. Kodi n’chitsanzo cha mtima wabwino chiti chimene Yesaya anasonyeza?

8 Yesaya anakonda dzina la Yehova. Zimenezo n’zoonekeratu m’mawu ake otsatira akuti: “Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9) Yesaya anakhumba Yehova ‘ndi moyo wake’​—ndi mtima wake wonse. Yerekezerani kuti mukumuona mneneri ameneyu akupemphera kwa Yehova usiku kunja kuli zii, popanda phokoso lililonse. Akufotokoza malingaliro ake onse kuchokera pansi pa mtima ndi kufunafuna chitsogozo cha Yehova modzichepetsa. Chitsanzo chabwino kwabasi! Komanso, Yesaya anaphunzira chilungamo kuchokera m’ziweruzo za Yehova. Zimenezi akutikumbutsa nazo kufunika kochita khama nthaŵi zonse, kukhala tcheru kuti tizindikire zofuna za Yehova.

Ena Asankha Mdima

9, 10. Kodi n’zachifundo zotani zimene Yehova anachitira mtundu wake wosakhulupirikawo, koma kodi mtunduwo unachitanji?

9 Yehova anakomera mtima kwambiri Yuda, koma n’zomvetsa chisoni kuti si onse amene analabadira. Mobwerezabwereza, anthu ambiri anasankha kuukira ndi kupanduka m’malo mosankha kuunika kwa choonadi cha Yehova. Yesaya anati: “Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m’dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.”​—Yesaya 26:10.

10 M’tsiku la Yesaya, dzanja la Yehova litateteza Yuda kwa adani ake, anthu ambiri sanakhulupirire zimenezi. Atawapatsa mtendere wake, mtunduwo sunayamikire. Chotero Yehova anangoŵaleka kuti atumikire “ambuye ena,” ndipo pamapeto pake analekerera Ayudawo kuti atengedwe kupita ku ukapolo ku Babulo m’chaka cha 607 B.C.E. (Yesaya 26:11-13) Komabe, patapita nthaŵi otsalira a mtunduwo anabwerera kwawo atazindikira kulakwa kwawo.

11, 12. (a) Kodi omwe anatengera Yuda ku ukapolo anali ndi tsogolo lotani? (b) M’chaka cha 1919 kodi omwe anagwira atumiki odzozedwa a Yehova ukapolo anali ndi tsogolo lotani?

11 Nanga bwanji amene anatengera mtundu wa Yuda ku ukapolowo? Yesaya akuyankha mwaulosi kuti: “Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; pokhala opanda mphamvu mu ifa, sadzauka; chifukwa chake Inu munawazonda, ndi kuwawononga, mwathetsa chikumbukiro chawo chonse.” (Yesaya 26:14, NW) Inde, Babulo atagwa mu 539 B.C.E, analibenso tsogolo lililonse. M’kupita kwa nthaŵi mzindawo unafafanizika. Unali “wopanda mphamvu mu ifa,” ndipo zoti kunali ufumu wamphamvu ndi mbiri chabe yolembedwa m’mabuku. Ndi chenjezotu lamphamvu kwa onse amene aika chiyembekezo chawo m’maulamuliro amphamvu a dziko lino!

12 Mbali zina za ulosi umenewu zinakwaniritsidwa pamene Mulungu analola atumiki ake odzozedwa kupita kuukapolo wauzimu mu 1918 ndiyeno n’kuwaombola mu 1919. Chiyambire m’nthaŵi imeneyo, omwe anawagwira ukapolowo, mokulira Matchalitchi Achikristu, analibe tsogolo lililonse. Koma madalitso amene anthu a Yehova anali kuyembekezera anali ochuluka kwabasi.

“Mwachulukitsa Mtundu”

13, 14. Kodi atumiki odzozedwa a Yehova adalitsidwa motani chiyambire 1919?

13 Mulungu anadalitsa mtima wolapa wa atumiki ake odzozedwa mu 1919 ndi kuwachulukitsa. Choyamba, anasamalira kwambiri za ntchito yosonkhanitsa otsalira otsiriza a Israyeli wa Mulungu, ndipo kenako, anayamba kusonkhanitsa “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” (Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16) Ulosi wa Yesaya unali utaneneratu za madalitso ameneŵa kuti: “Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko. Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.”​—Yesaya 26:15, 16.

14 Lerolino, malire a Israyeli wa Mulungu ali ponseponse padziko lapansi, ndipo khamu lalikulu lomwe lakhala likuwonjezeka tsopano likufika cha m’ma 6 miliyoni. Limeneli ndi khamu la anthu akhama m’ntchito yolalikira uthenga wabwino. (Mateyu 24:14) Ha, madalitsotu a Yehova ameneŵa! Ulemerero umene zimenezi zikudzetsa ku dzina lake n’ngwosaneneka! Dzina limenelo likumveka lerolino m’mayiko 235​—kukwaniritsidwa kosangalatsa kwa lonjezo lake.

15. Kodi ndi kuuka kophiphiritsira kotani kumene kunachitika mu 1919?

15 Ayuda anafunikira thandizo la Yehova kuti athaŵe kuukapolo ku Babulo. Sakanatha kuchita zimenezo mwa iwo okha. (Yesaya 26:17, 18) Mofananamo, kuwomboledwa kwa Israyeli wa Mulungu m’chaka cha 1919 unali umboni wakuti Yehova anali kuwachirikiza. Sizikanachitika popanda iye. Ndipo chochititsa nthumanzi kwambiri chinali kusintha kwa mikhalidwe yawo kumene Yesaya anakuyerekezera ndi kuuka. Iye anati: ‘Akufa anu adzakhala ndi moyo; mtembo wanga adzauukitsa. Ukani muimbe, inu amene mukhala m’fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa [opanda mphamvu mu imfa, NW].’ (Yesaya 26:19; Chivumbulutso 11:7-11) Inde, opanda mphamvu mu imfawo adzabadwanso, titero kunena kwake, kuti adzayambenso kugwira ntchito.

Chitetezo M’nthaŵi Yoopsa

16, 17. (a) Mu 539 B.C.E., kodi Ayuda anafunikira kuchitanji kuti apulumuke pa kugwa kwa Babulo? (b) Kodi ‘zipinda’ n’chiyani lerolino, ndipo kodi zimatipindulitsa motani?

16 Atumiki a Yehova amafuna chitetezo chake nthaŵi zonse. Komabe, posachedwapa adzatambasula dzanja lake kwa nthaŵi yotsiriza kuthana ndi dziko la Satanali, ndipo panthaŵi imeneyi olambira a Yehova adzafunikira thandizo lake kuposa ndi kale lonse. (1 Yohane 5:19) Ponena za nthaŵi yoopsa imeneyo, Yehova akutichenjeza kuti: “Idzani, anthu anga, loŵani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthaŵi kufikira mkwiyo utapita. Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera ku malo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwawo; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.” (Yesaya 26:20, 21; Zefaniya 1:14) Chenjezo limeneli linasonyeza Ayuda mmene angapulumukire pa kugwa kwa Babulo mu 539 B.C.E. Amene anamvera chenjezo limeneli anafunikira kukhala m’nyumba zawo, ndi kutetezeka pamene asilikali olanda dziko anali ponseponse m’misewu.

17 Lerolino, ‘zipinda’ za muulosiwo mwachionekere zikuimira mipingo yochuluka ya anthu a Yehova padziko lonse lapansi. Mipingo imeneyi ndi malo otetezeka ngakhale panopa, ndi malo amene Akristu amapezako chitetezo pakati pa abale awo, mwa kusamalidwa mwachikondi ndi akulu. (Yesaya 32:1, 2; Ahebri 10:24, 25) Zimenezi n’zoonadi makamaka poona mmene mapeto a dongosolo lino la zinthu ayandikirira. Panthaŵi imeneyo omvera okha ndi amene adzapulumuke.​—Zefaniya 2:3.

18. Kodi Yehova adzapha motani “ching’ona chimene chili m’nyanja” posachedwapa?

18 Ponena za nthaŵi imeneyo, Yesaya akulosera kuti: “Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yothamanga, ndi nangumi njoka yopindikapindika; nadzapha ching’ona chimene chili m’nyanja.” (Yesaya 27:1) Kodi “nangumi” m’nthaŵi yathu ino n’chiyani? Mwachidziŵikire, ndi “njoka yakaleyo,” Satana, limodzi ndi dongosolo lake lazinthu loipali, limene akuligwiritsa ntchito polimbana ndi Israyeli wa Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 10, 17; 13:14, 16, 17) M’chaka cha 1919 anthu a Mulungu anachoka m’manja mwa nangumi. Pamapeto pake, nangumi ameneyu adzazimiririka. (Chivumbulutso 19:19-21; 20:1-3, 10) Pamenepo Yehova adzakhala atapha “ching’ona chimene chili m’nyanja.” Padakali pano, chilichonse chimene ching’ona chimenechi chidzayesa kuchitira anthu a Yehova sichidzapambana konse. (Yesaya 54:17) Kuuzidwa zimenezi motsimikizira n’kolimbikitsa kwabasi!

“Munda wa Mphesa Wavinyo”

19. Kodi otsalira ali mumkhalidwe wotani lerolino?

19 Poona kuunika konseku kochokera kwa Yehova, kodi si koyenera kuti tikondwere? Inde, tiyeneradi kukondwera! Yesaya akuchifotokoza bwino kwabasi chimwemwe cha anthu a Yehova pamene akuti: “Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, imbani inu za uwo. Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.” (Yesaya 27:2, 3) Yehova wasamalira ‘munda wake wa mphesa,’ otsalira a Israyeli wa Mulungu, ndiponso wasamalira anzawo ogwira ntchito mwachamuna. (Yohane 15:1-8) Zipatso zodzetsa ulemerero ku dzina lake ndizo zakhala zotsatira zake ndipo zakondweretsa kwambiri atumiki ake padziko lapansi.

20. Kodi Yehova amateteza motani mpingo wachikristu?

20 Tikunyadira kuti mkwiyo umene Yehova anali nawo pa atumiki ake odzozedwa​—umene unam’chititsa kuti awalole kumka kuukapolo wauzimu mu 1918​—watha tsopano. Yehova mwiniyo akuti: “Ndilibe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? ndiziponde ndizitenthe pamodzi. Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nachite nane mtendere; inde, achite nane mtendere.” (Yesaya 27:4, 5) Pofuna kuonetsetsa kuti mphesa zake zikupitiriza kutulutsa vinyo, Yehova wachotsa ndi kutentha zilizonse zomwe zili ngati minga imene ingasokoneze mphesa zake. Chotero, sanalole kuti aliyense asokoneze kupita patsogolo kwa mpingo wachikristu! Aliyense ‘agwire mphamvu za Yehova,’ afunefune chiyanjo ndi chitetezo chake. Mwa kuchita zimenezo, timapanga mtendere ndi Mulungu​—chinthu chofunika kwambiri moti Yesaya anachitchula kaŵiri.​—Salmo 85:1, 2, 8; Aroma 5:1.

21. Kodi m’munda wachonde mwadzaza motani “zipatso”?

21 Madalitso akupitiriza: “M’mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israyeli adzaphuka ndi kuchita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi.” (Yesaya 27:6) Vesi limeneli lakwaniritsidwa kuchokera mu 1919, lapereka umboni wosangalatsa wa mphamvu za Yehova. Akristu odzozedwa adzaza “zipatso” m’dziko, chakudya chauzimu chopatsa thanzi. M’kati mwenimweni mwa dziko loipali, akuteteza miyezo yokwezeka ya Mulungu mosangalala. Ndipo Yehova akupitiriza kuwachulukitsa. Zotsatira zake n’zakuti anzawo miyandamiyanda, a nkhosa zina, ‘akum’tumikira [Mulungu] usana ndi usiku.’ (Chivumbulutso 7:15) Tisaiwaletu mwayi waukulu wakudya nawo “zipatso” ndi kugaŵirako ena!

22. Kodi olandira kuunika amadalitsidwa motani?

22 M’nthaŵi zovuta zino, pamene mdima waphimba dziko ndipo mdima wandiweyani mitundu ya anthu, kodi sitikuthokoza kuti Yehova akuunikira anthu ake mwauzimu? (Yesaya 60:2; Aroma 2:19; 13:12) Kwa onse okulandira, kuunikako kukutanthauza mtendere wamaganizo ndi chisangalalo tsopano lino ndipo m’tsogolo moyo wosatha. Chotero, pa chifukwa chabwino, ife amene timakonda kuunika tikutamanda Yehova ndi mtima wathu wonse ndipo tikunenera limodzi ndi wamasalmo kuti: “Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani? Yembekeza Yehova: limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.”​—Salmo 27:1b, 14.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ozunza anthu a Yehova chidzawachitikira n’chiyani m’tsogolomu?

• Kodi Yesaya ananeneratu za kuwonjezeka kotani?

• Kodi tiyenera kukhala ‘m’zipinda’ ziti, ndipo n’chifukwa chiyani?

• N’chifukwa chiyani Yehova amatamandidwa chifukwa cha mkhalidwe wa anthu ake?

[Mafunso]

[Bokosi patsamba 22]

BUKU LATSOPANO

Mfundo zochuluka zimene zafotokozedwa m’nkhani ziŵiri zophunzirazi zinakambidwa m’nkhani ina pa pulogalamu ya msonkhano wachigawo wa 2000/2001. Chakumapeto kwa nkhaniyo, kunatulutsidwa buku latsopano lamutu wakuti Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse 1. Buku limeneli la masamba 416 likufotokoza vesi ndi vesi machaputala 40 oyambirira a buku la Yesaya.

[Chithunzi patsamba 18]

Olungama okha ndi amene akuloledwa m’gulu la Yehova, ‘mudzi wake wolimba’

[Chithunzi patsamba 19]

Yesaya anafunafuna Yehova “usiku”

[Chithunzi patsamba 21]

Yehova amateteza munda wake wa “mphesa” ndi kuubalitsa zipatso