Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chisangalalo kwa Oyenda M’kuunika

Chisangalalo kwa Oyenda M’kuunika

Chisangalalo kwa Oyenda M’kuunika

“Tiyeni, tiyende m’kuwala kwa Yehova.”​—YESAYA 2:5.

1, 2. (a) Kodi kuunika n’kofunika motani? (b) N’chifukwa chiyani chenjezo lakuti mdima udzaphimba dziko lapansi n’loopsa?

YEHOVA ndiye Gwero la kuunika. Baibulo limamutcha ‘Wopatsa dzuŵa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi nyenyezi kuti aunikire usiku.’ (Yeremiya 31:35; Salmo 8:3) Ndiye analenga dzuŵa lathuli lomwe kwenikweni tingati ndi ng’anjo yonyeketsa imene imatulutsa mphamvu zochuluka. Zina mwa mphamvuzi ndizo kuwala ndi kutentha kwake. Kachigawo kochepa kwambiri ka mphamvu zimenezi kamene kamatifika monga kuwala kamachirikiza moyo padziko lapansi lino. Popanda dzuŵa limeneli, si bwenzi tili pano. Dziko lapansi likanakhala lopanda chamoyo chilichonse.

2 Ndi mfundo imeneyo m’maganizo, tingathe kumvetsa kufunika kwa mkhalidwe womwe mneneri Yesaya anaufotokoza. Iye anati: “Taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:2) Komatu mdima wotchulidwa pano si mdima weniweni. Yesaya sanatanthauze kuti tsiku linalake dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zidzaleka kuwala. (Salmo 89:36, 37; 136:7-9) M’malo mwake, anali kunena za mdima wauzimu. Komatu mdima wauzimu n’ngwochititsa mantha. Sitingakhale moyo kwa nthaŵi yaitali popanda kuunika kwauzimu monga momwe sitingakhalire popanda kuwala kwa dzuŵa.​—Luka 1:79.

3. Polingalira mawu a Yesaya, kodi Akristu ayenera kuchitanji?

3 Polingalira zimenezi, n’zodetsa nkhaŵa kwambiri kuona kuti mawu a Yesaya, ngakhale kuti anakwaniritsidwa kale pa Yuda wakale, akukwaniritsidwa mokulira lerolino. Inde, m’nthaŵi yathu ino dzikoli lili m’mdima wauzimu. Mumkhalidwe woopsa ngati umenewu, kuunika kwauzimu n’kofunika kwambiri. N’chifukwa chake kuli kofunika kuti Akristu amvere chilimbikitso cha Yesu chakuti: “Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu.” (Mateyu 5:16) Akristu okhulupirika angaunike mumdima wa anthu odzichepetsa, kuwapatsa mwayi wodzalandira moyo wosatha.​—Yohane 8:12.

Nthaŵi za Mdima M’Israyeli

4. Kodi mawu aulosi a Yesaya anakwaniritsidwa liti kwanthaŵi yoyamba, koma kodi zinthu zinali kale motani m’nthaŵi yake?

4 Mawu a Yesaya onena za mdima wokuta dziko anakwaniritsidwa kwa nthaŵi yoyamba Yuda atasanduka wabwinja ndipo anthu ake ali ku ukapolo ku Babulo. Komabe, zimenezo zisanachitike, m’tsiku la Yesaya mbali yaikulu ya mtunduwo inali kale mumdima wauzimu. Zimenezi zinam’sonkhezera kuchonderera anthu amtundu wake kuti: “Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m’kuwala kwa Yehova!”​—Yesaya 2:5; 5:20.

5, 6. Kodi n’zinthu ziti zimene zinachititsa kuti kukhale mdima m’tsiku la Yesaya?

5 Yesaya analosera mu Yuda “masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.” (Yesaya 1:1) Inali nthaŵi yovuta kwambiri ya chipwirikiti m’zandale, chinyengo m’zipembedzo, ziphuphu poweruza milandu, ndi kupondereza osauka. Ngakhale pamene mafumu okhulupirika monga Yotamu amalamulira, maguwa ansembe a milungu yonyenga sanali osoŵa m’mapiri ambiri. Mu ulamuliro wa mafumu osakhulupirika, zinthu zinanyanya kuipa. Mwachitsanzo, Mfumu yoipa Ahazi anafika popereka mwana wake nsembe kwa mulungu Moleki. Unalitu umbuli umenewo!​—2 Mafumu 15:32-34; 16:2-4.

6 Maunansi awo ndi mayiko ena anafikanso poipa. Moabu, Edomu, ndi Filistiya anaopseza kwambiri Yuda m’malire ake. Ufumu wakumpoto wa Israyeli unali paudani waukulu ndi Yuda ngakhale kuti anali pachibale. Cha kumpoto kwenikweni, Suriya anaopseza Yuda ndi kum’soŵetsa mtendere. Woopsa kwambiri anali Asuri wankhanzayo, yemwe nthaŵi zonse anali kufunafuna njira zokulitsira mphamvu za ulamuliro wake. M’nthaŵi yomwe Yesaya amalosera, Asuri anagonjetsa dziko lonse la Israyeli ndipo anatsala pang’ono kuwonongeratu Yuda. Nthaŵi inayake Asuri analanda mizinda yonse yamalinga m’Yuda kupatula Yerusalemu yekha.​—Yesaya 1:7, 8; 36:1.

7. Kodi Israyeli ndi Yuda anasankha njira yotani, ndipo Yehova anachitanji?

7 Anthu a pangano la Mulungu anagwa m’masoka amenewo chifukwa chakuti Israyeli ndi Yuda sanamvere Mulungu. Mofanana ndi amene akutchulidwa m’buku la Miyambo, ameneŵa ‘anasiya mayendedwe olungama, nayenda m’njira za mdima.’ (Miyambo 2:13) Komabe, ngakhale kuti Yehova anakwiya ndi anthu ake, iye sanawanyalanyaze kotheratu. M’malo mwake, anautsa Yesaya ndi aneneri ena kuti akapereke kuunika kwauzimu m’dzikomo kwa aliyense amene ankafunabe kutumikira Yehova mokhulupirika. Ndithudi, kuunika kumene aneneri ameneŵa anapereka kunali kwa mtengo wapatali zedi. Kunali kopatsa moyo.

Nthaŵi za Mdima Lerolino

8, 9. N’zinthu ziti zimene zikuchititsa kuti dziko likhale mumdima lerolino?

8 Zochitika za m’nthaŵi ya Yesaya zikufanana kwambiri ndi zimene zikuchitika lerolino. M’nthaŵi yathu ino, anthu otsogolera akana Yehova ndi Mfumu yake yokwezeka, Yesu Kristu. (Salmo 2:2, 3) Atsogoleri achipembedzo m’Matchalitchi Achikristu aphimba m’maso nkhosa zawo. Atsogoleri ameneŵa amati akutumikira Mulungu, koma kwenikweni ambiri a iwo amachirikiza milungu ya dziko lino​—kusankhana mitundu, kulimbikitsa kwambiri nkhondo, kukonda chuma, ndi kukonda anthu otchuka​—kuwonjezera pa kuphunzitsa ziphunzitso zachikunja.

9 M’malo ambiri, zipembedzo za m’gawo la Matchalitchi Achikristu zaloŵerera m’nkhondo ndi m’zipolowe zapachiweniweni zopululutsa anthu amafuko ena komanso m’zoopsa zina. Chinanso, m’malo molimbikitsa makhalidwe abwino a m’Baibulo, matchalitchi ambiri akuwanyalanyaza kapena akuchirikiza mwakhama mikhalidwe yosayenera monga dama ndi kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Chifukwa cha kunyalanyaza miyezo ya m’Baibulo kotereku, anthu a m’Matchalitchi Achikristu ali ngati anthu omwe wamasalmo wakale ankawanena kuti: “Sadziŵa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.” (Salmo 82:5) Ndithudi, mofanana ndi Yuda wakale, Matchalitchi Achikristu nawonso ali mumdima wandiweyani.​—Chivumbulutso 8:12.

10. Kodi kuunika kukuwala motani mumdima lerolino, nanga odzichepetsa amapindula motani?

10 M’mdima umenewu, Yehova akuunikira odzichepetsa. Akuchita zimenezi pogwiritsa ntchito atumiki ake odzozedwa padziko lapansi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo ameneŵa ‘akuwala monga zounikira m’dziko lapansi.’ (Mateyu 24:45; Afilipi 2:15) Gulu la kapolo limenelo, mothandizana ndi anzawo miyandamiyanda a “nkhosa zina,” akupereka kuunika kwauzimu kuchokera m’Mawu a Mulungu, Baibulo. (Yohane 10:16) M’dziko lamdima lino, kuunika kumeneku kumapereka chiyembekezo kwa odzichepetsa, kumawathandiza kukhala paubwenzi ndi Mulungu, ndiponso kumawathandiza kupeŵa mbuna zauzimu. Kuwala kumeneku n’kwamtengo wapatali, ndi kopatsa moyo.

“Ndidzatamanda Dzina Lanu”

11. Kodi Yehova anafotokoza za chiyani m’tsiku la Yesaya?

11 Kodi Yehova anapereka malangizo otani m’masiku amdima amene Yesaya anakhalamo ndiponso pambuyo pake mdimawo utaŵirikiza kwambiri m’nthaŵi yomwe Ababulo amatengera mtundu wa Yehova ku ukapolo? Kuwonjezera pa kupereka malangizo a makhalidwe abwino, iye anafotokoza pasadakhale momveka bwino mmene adzakwaniritsira zifuno zake zokhudza anthu ake. Mwachitsanzo, talingalirani za maulosi ochititsa chidwi m’buku la Yesaya chaputala 25 mpaka chaputala 27. Mawu a m’machaputala ameneŵa akusonyeza mmene Yehova anachitira zinthu m’nthaŵiyo komanso mmene amazichitira lerolino.

12. Kodi ndi mawu ati ochokera pansi pa mtima amene Yesaya ananena?

12 Choyamba, Yesaya akulengeza kuti: “Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu.” Ndithudi kutamanda kumeneku n’kochokera pansi pa mtima! Koma n’chiyani chinam’sonkhezera mneneriyu kupemphera mwa mtunduwu? Mfundo yaikulu akuivumbula m’mbali yachiŵiri ya vesili. Pamenepo tikuŵerenga kuti: “Chifukwa [inu Yehova] mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m’zoonadi.”​—Yesaya 25:1.

13. (a) Kodi Yesaya anadziŵa chiyani chimene chinalimbikitsa chidaliro chake mwa Yehova? (b) Kodi chitsanzo cha Yesaya chingatiphunzitse chiyani?

13 Podzafika m’nthaŵi ya Yesaya, Yehova anali atachitira mtundu wa Israyeli zinthu zambiri zodabwitsa, ndipo zimenezi zinali zitalembedwa. N’zodziŵikiratu kuti Yesaya anali kuzidziŵa bwino zolembedwazo. Mwachitsanzo, iye anadziŵa kuti Yehova anatulutsa anthu ake ku ukapolo ku Igupto ndi kuwapulumutsa ku mkwiyo wa gulu lankhondo la Farao pa Nyanja Yofiira. Anadziŵa kuti Yehova anatsogolera anthu ake m’chipululu ndi kuwaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Salmo 136:1, 10-26) Mbiri zakale ngati zimenezo zinasonyeza kuti Yehova Mulungu ndi wokhulupirika ndi wodalirika. ‘Uphungu’ wake​—zofuna zake zonse​—zimakwaniritsidwa. Chidziŵitso cholondola chomwe Mulungu anapatsa Yesaya chinam’limbikitsa kupitirizabe kuyenda m’kuunika. Chotero iye anali chitsanzo chabwino kwa ife. Ngati timaphunzira Mawu olembedwa a Mulungu mosamala ndi kugwiritsa ntchito zomwe taphunzirazo m’moyo wathu, nafenso tidzakhalabe m’kuunika.​—Salmo 119:105; 2 Akorinto 4:6.

Mudzi Wawonongedwa

14. Kodi ndi chiyani chomwe chinanenedweratu ponena za mudzi, ndipo mwachionekere kodi mudzi umenewu unali uti?

14 Chitsanzo cha uphungu wa Mulungu tikuchipeza pa Yesaya 25:2, pamene timaŵerenga kuti: “Chifukwa Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse.” Kodi mudzi umenewu n’chiyani? N’zodziŵikiratu kuti Yesaya anali kulosera za Babulo. Ndithudi, inafika nthaŵi pamene Babulo anasanduka muunda wa miyala.

15. Ndi “mudzi waukulu” uti umene ulipo lerolino, ndipo n’chiyani chidzachitikire mudzi umenewu?

15 Kodi pali mudzi wina lerolino wofanana ndi umene Yesaya anatchula? Inde ulipo. Buku la Chivumbulutso limanena za “mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.” (Chivumbulutso 17:18) Mudzi waukulu umenewu ndiwo ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 17:5) Lerolino, mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu ndiyo Matchalitchi Achikristu, omwe atsogoleri ake achipembedzo akutsogolera potsutsa ntchito ya anthu a Yehova yolalikira Ufumu. (Mateyu 24:14) Komabe, mofanana ndi Babulo wakale, Babulo Wamkulu nayenso awonongedwa posachedwapa, ndipo sadzaukanso.

16, 17. Kodi adani a Yehova anam’lemekeza motani m’nthaŵi yakale komanso m’nthaŵi zamakono zino?

16 Kodi Yesaya analoseranso zotani ponena za “mudzi walinga” umenewu? Yesaya anauza Yehova kuti: “Anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mudzi wa mitundu yakuopsa udzakuopani inu.” (Yesaya 25:3) Kodi mzinda wankhanza umenewu, “mudzi wa mitundu yakuopsa,” unalemekeza motani Yehova? Eya, kumbukirani zomwe zinachitikira Nebukadinezara, mfumu yamphamvu ya Babulo. Zitam’chitikira zinthu zodabwitsa zomwe zinasonyeza kufooka kwake, anakakamizika kuvomereza kuti Yehova ndiye wamkulu ndikuti Iye ndi Wamphamvuyonse. (Danieli 4:34, 35) Pamene Yehova asonyeza mphamvu yake, adani ake nawonso amaumirizika kuvomereza ntchito zake zamphamvu, ngakhale kuti amatero monyinyirika.

17 Kodi Babulo Wamkulu anaumirizikapo kuvomereza ntchito zamphamvu za Yehova? Inde. Nkhondo yoyamba yapadziko lonse ili m’kati, atumiki odzozedwa a Yehova analalikira m’masautso. M’chaka cha 1918 anapita kuukapolo wauzimu maofesala otsogolera Watch Tower Society ataikidwa m’ndende. Ntchito yolinganizika bwino yolalikira inaima. Kenako, m’chaka cha 1919, Yehova anawabwezeretsa ndi kuwalimbikitsa ndi mzimu wake, ndiyeno anapita kukakwaniritsa ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu amitundu yonse. (Marko 13:10) Zonsezi zinali zitaloseredwa kale m’buku la Chivumbulutso, monganso mmene zimenezi zinakhudzira otsutsawo. Ameneŵa “anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa m’Mwamba.” (Chivumbulutso 11:3, 7, 11-13) Si kuti onsewo anatembenuka mtima, koma kuti anaumirizika kuzindikira ntchito zodabwitsa za Yehova pa chochitikachi, monga momwe Yesaya anali ataneneratu.

“Linga la Aumphawi”

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani otsutsa alephera kuchotsa kukhulupirika kwa anthu a Yehova? (b) Kodi “nyimbo ya akuopsa” idzaletseka motani?

18 Tsopano potembenukira ku chifundo chimene Yehova amaonetsera anthu oyenda m’kuunika, Yesaya akuuza Yehova kuti: “Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m’kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuŵa, pamene kuwomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuwomba chemba. Monga kutentha m’malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsa idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuŵa.”​—Yesaya 25:4, 5.

19 Kuchokera m’chaka cha 1919 anthu ankhanza ayesetsa mulimonse mmene akanathera kuti achotse kukhulupirika kwa alambiri oona, koma alephera. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yehova ndiye linga ndi kothaŵirako anthu ake. Amapereka mpumulo m’kati mwa masautso owawitsa ndipo ali ngati linga lolimba kobisalirako mkuntho wa chitsutso. Ife amene tikuyenda m’kuunika kwa Mulungu tikuyang’ana m’tsogolo ndi chidaliro chonse ku nthaŵi yomwe “nyimbo ya akuopsa idzaletseka.” Inde, tikuyembekezera mwachidwi tsiku lomwe adani a Yehova adzatha psiti.

20, 21. Kodi Yehova wakonza phwando lotani, nanga kodi phwando limenelo lidzaphatikizapo chiyani m’dziko latsopano?

20 Yehova amachita zambiri zoposa kungoteteza atumiki ake. Amawagaŵira zosoŵa zawo monga Atate wawo wachikondi. Atalanditsa anthu ake kwa Babulo Wamkulu mu 1919, anawakonzera phwando la chilakiko, chakudya chauzimu cha mwana alirenji. Zimenezi zinaloseredwa pa Yesaya 25:6, pamene timaŵerenga kuti: “Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” Ha, ndifetu odala kudya nawo chakudya chonona pa phwando limenelo! (Mateyu 4:4) ‘Pagome la Yehova’ padzazadi chakudya chonona kuti tidye. (1 Akorinto 10:21) Kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” tapatsidwa chilichonse chimene tingafune chokhudza mbali yauzimu.

21 Ndipotu phwando lokonzedwa ndi Mulungu limeneli lili n’zambiri. Madyerero auzimu amene tsopano tikusangalala nawo amatikumbutsa za kuchuluka kwa chakudya chakuthupi chimene chidzakhalapo m’dziko latsopano limene Mulungu watilonjeza. Panthaŵiyo, “phwando la zinthu zonona” lidzaphatikizapo chakudya chakuthupi chamwana alirenji. Palibe aliyense amene adzamva njala yachakudya chakuthupi kapena chauzimu. Idzakhala nthaŵi ya chisangalalo chadzaoneni kwa okhulupirira anzathu amene tsopano akuvutika ndi “njala” yoloseredwa yomwe ndi mbali ya “chizindikiro” cha kukhalapo kwa Yesu! (Mateyu 24:3, 7) Kwa iwo, mawu a wamasalmo n’golimbikitsa kwambiri. Iye anati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”​—Salmo 72:16.

22, 23. (a) Kodi ndi “nsalu,” kapena “chophimba,” chotani chimene chidzachotsedwa, ndipo motani? (b) Kodi ‘chitonzo cha anthu a Yehova’ chidzachotsedwa motani?

22 Tsopano mvetserani lonjezo losangalatsa kwambiri. Poyerekeza uchimo ndi imfa ngati “nsalu,” kapena “chophimba,” Yesaya anati: “[Yehova] adzawononga m’phiri limeneli chophimba nkhope chovundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsalu yokuta amitundu onse.” (Yesaya 25:7) Tangoganizani! Uchimo ndi imfa, zimene zasautsa mtundu wa anthu monga bulangete lokhuthala lolepheretsa anthu kupuma bwino, sizidzakhalaponso. Tikulakalakadi tsikulo pamene nsembe ya dipo ya Yesu idzagwira ntchito yake mokwanira popindulitsa anthu onse omvera ndi okhulupirika!​—Chivumbulutso 21:3, 4.

23 Ponena za nthaŵi yosangalatsa imeneyo, mneneri wouziridwayo akutitsimikizira kuti: “[Mulungu] wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.” (Yesaya 25:8) Palibe amene adzafa imfa yachibadwa kapena kulira chifukwa chakuti wokondedwa wake wafa. Ha, kusangalatsa kwake eti mmene zinthu zidzasinthire! Kuwonjezera pamenepo, kulikonse padziko lapansi sipadzamvekanso chitonzo ndi mabodza amene Mulungu ndi atumiki ake awapirira kwa nthaŵi yaitali. Chifukwa chiyani sadzamveka? Chifukwa Yehova adzachotsa gwero la mabodzawo​—atate wa bodza, Satana Mdyerekezi limodzi ndi mbewu yonse ya Satana.​—Yohane 8:44.

24. Kodi amene amayenda m’kuunika amachitanji akaona ntchito zamphamvu zimene Yehova akuwachitira?

24 Polingalira mphamvu zodabwitsa zimene Yehova adzaonetsa m’njira imeneyi, awo amene akuyenda m’kuunika akusonkhezereka kufuula kuti: “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tam’lindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tam’lindirira Iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.” (Yesaya 25:9) Posachedwapa, anthu olungama adzakondwa kwabasi. Mdima udzachotsedwa kotheratu, ndipo okhulupirika adzasangalala m’kuunika kwa Yehova kunthaŵi za nthaŵi. Kodi tingayembekezerenso zina zoposa izi? Ndithudi ayi!

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani kuyenda m’kuunika kuli kofunika lerolino?

• N’chifukwa chiyani Yesaya anatamanda dzina la Yehova?

• N’chifukwa chiyani adani sadzachotsa kukhulupirika kwa anthu a Mulungu?

• Kodi oyenda m’kuunika akuyembekezera madalitso ochuluka otani?

[Mafunso]

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Anthu okhala mu Yuda ankapereka ana awo nsembe kwa Moleki

[Zithunzi patsamba 15]

Kudziŵa zochita zamphamvu za Yehova kunam’sonkhezera Yesaya kutamanda dzina la Yehova

[Chithunzi patsamba 16]

Olungama adzakondwa m’kuunika kwa Yehova kunthaŵi za nthaŵi