Kodi Mungakhaledi Achimwemwe?
Kodi Mungakhaledi Achimwemwe?
GEORGE ankamwetulira akamapereka moni kwa wina aliyense. Kwa iye, moyo unali mphatso yamtengo wapatali yoyenera kusangalala nayo. Nsangala ndi chiyembekezo ndizo zinali khalidwe lake ndipo khalidweli linawonjezeka ngakhale atayamba kuvutika ndi ukalamba. George ankadziŵika kuti anali munthu wansangala mpaka patsiku lomwe anamwalira. Kodi ndinu wansangala monga George? Kodi tsiku lililonse m’maliona monga mphatso yoyenera kusangalala nayo? Kapena kodi kuyembekezera tsiku latsopano kumakugwetsani mphwayi kapena kukudetsani nkhaŵa? Kodi chinachake chikukulepheretsani kukhala wachimwemwe?
Chimwemwe chimatanthauza mtendere wamumtima umene umakhala kunthaŵi zonse. Chimwemwe chimadziŵika ndi mtima wokhutira, nsangala, ndiponso kulakalaka kwachibadwa kuti mtendere wamumtima upitirire. Kodi anthu achimwemwe choterocho alikodi?
Masiku ano, anthu amaona kuti munthu angasangalale pokhapokha ngati atakhala wolemera kwambiri. Anthu miyandamiyanda amajijirika kwambiri kuti apeze chuma. Pochita zimenezi, ambiri salabadira anansi awo ndiponso zinthu zina zofunika kwambiri m’moyo. Mofanana ndi chiswe pachulu, iwo nthaŵi zonse amakhala kalikiliki kupita uku ndi uku, kotero kuti amakhala ndi nthaŵi yochepa yoganizira zomwe akuchita komanso yoganizirana wina ndi mnzake. N’chifukwa chake “anthu omwe akupezeka ndi matenda a kuvutika maganizo akuchulukirachulukira,” inatero nyuzipepala yotchedwa Los Angeles Times. Nyuzipepalayo inatinso, “anthu tsopano akuyamba kudwala matendaŵa adakali aang’ono kwambiri. . . . Ndipo mankhwala oletsa kuvutika maganizo akuyenda malonda kwambiri.” Anthu miyandamiyanda amamwa mankhwala oletsedwa kapena moŵa kuti aiŵale mavuto. M’mayiko ena, anthu amangogula zinthu mwachisawawa akakhala kuti akuvutika maganizo. Kafukufuku
wina ku Britain wasonyeza kuti, “akazi ndiwo amakonda kugula zinthu monga njira yothetsera kuvutika maganizo. Akazi amene amagula zinthu poyesa kuthetsa kuvutika maganizo anali ochuluka kuŵirikiza katatu poyerekezera ndi chiŵerengero cha amuna,” inatero nyuzipepala ya ku Britain yotchedwa The Guardian.Komabe, chimwemwe chenicheni sichipezeka m’sitolo, m’chakumwa chaukali, m’mibulu yamankhwala, m’jekeseni, kapena mu akaunti ya ku banki. Chimwemwe n’chaulere osati chogulitsa ayi. Kodi mphatso yamtengo wapatali imeneyi tingaipeze kuti? M’nkhani yotsatirayi tifotokoza zimenezi.