Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchirikizidwa ndi Yehova Masiku Anga Onse

Kuchirikizidwa ndi Yehova Masiku Anga Onse

Mbiri ya Moyo Wanga

Kuchirikizidwa ndi Yehova Masiku Anga Onse

YOSIMBIDWA NDI FORREST LEE

Apolisi anali atangotilanda kumene magalamafoni ndi mabuku athu ofotokoza Baibulo. Nkhondo yachiŵiri yadziko lonse, inapatsa anthu otsutsa mwayi wokakamiza wolamulira wamkulu wa dziko la Canada, kuika lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Izi zinachitika pa July 4, 1940.

SITINAFOOLEDWE ndi zimene zinachitikazo. M’malo mwake, tinatenga mabuku ena omwe tinasunga ndi kupitirizabe kulalikira. Sindidzaiwala mawu omwe bambo anga ananena panthaŵiyo kuti: “Sitisiya wamba kulalikira. Yehova watilamula kuti tilalikire.” Panthaŵiyo n’kuti ndili kamnyamata kojijirika ka zaka khumi. Komabe ngakhale lerolino, kutsimikiza ndi kufunitsitsa kwa bambo pa utumiki, kumandikumbutsabe mmene Mulungu wathu Yehova, amalimbikitsira omwe amam’khulupirira.

Nthaŵi yotsatira imene apolisi anatidodometsa, sanatenge mabuku athu okha, komanso anatenga bambo kukawaika m’ndende, kusiya amayi okha ndi ana anayi. Zimenezi zinachitika mu September 1940 ku Saskatchewan. Posapita nthaŵi, ndinachotsedwa sukulu chifukwa cha kutsatira chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo, ndi kukana kupanga sawatcha ku mbendera kapena kuimba nawo nyimbo ya mtundu. Kupitiriza kuphunzira sukulu ndili panyumba, kunandipatsa mpata waukulu ndipo ndinalalikira nawo kwambiri.

Mu 1948, alaliki a nthaŵi zonse a Mboni za Yehova otchedwa apainiya, anapemphedwa kusamukira ku madera a m’mphepete mwa nyanja kum’maŵa kwa Canada. Choncho ndinapita kukalalikira ku Halifax m’chigawo cha Nova Scotia, ndi ku Cape Wolfe, pachilumba cha Prince Edward. Chaka chotsatira, ndinavomera kukatumikira kwa milungu iŵiri pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Toronto. Milungu iŵiri imeneyo, inawonjezeka kufika zaka zoposa zisanu n’chimodzi za utumiki wopindulitsa. Kenako, ndinakumana ndi Myrna, amenenso anali wokonda Yehova, ndipo tinakwatirana mu December 1955. Tinakhazikika ku Milton, m’chigawo cha Ontario, ndipo mwamsanga, mpingo watsopano unakhazikitsidwa kumeneko. Chipinda chapansi cha nyumba yathu chinakhala Nyumba ya Ufumu.

Kulakalaka Kukulitsa Utumiki Wathu

M’zaka zotsatira tinabereka ana asanu ndi mmodzi motsatizana kwambiri. Mwana wathu wamkazi Miriam ndiye woyamba. Kenako panabadwa Charmaine, Mark, Annette, Grant, ndi womalizira Glen. Nthaŵi zambiri pochokera kuntchito, ndinkapeza anaŵa atakhala pansi mozungulira moto, mayi wawo Myrna akuwaŵerengera Baibulo, kufotokoza nkhani za m’Baibulo ndi kukhomereza kukonda Yehova m’mitima mwawo. Chifukwa cha thandizo lake lachikondi, ana athu onse analidziŵa Baibulo mokwanira akadali aang’ono.

Changu cha bambo pa kulalikira, n’chitsanzo chosaiŵalika m’maganizo ndi mu mtima mwanga. (Miyambo 22:6) Choncho, mu 1968, pamene mabanja a Mboni za Yehova anapemphedwa kusamukira ku madera a pakati ndi kumwera kwa America kukathandiza ntchito yolalikira, banja lathu linalakalaka kupita. Panthaŵiyo misinkhu ya ana athu inali kuyambira zaka 5 mpaka 13, ndipo sitinkadziŵa Chisipanya ngakhale pang’ono. Potsatira malangizo omwe anaperekedwa, ndinapita ku mayiko angapo kukaona ngati tingathe kukhalako. Nditabwerera, tinapemphera monga banja posankha komwe tingapite ndipo tinasankha kusamukira ku Nicaragua.

Kutumikira ku Nicaragua

Pofika mu October 1970 tinali ku malo athu atsopano, ndipo pasanathe milungu iŵiri, ndinapatsidwa mbali yaing’ono pa msonkhano wa mpingo. Ndinavutika polankhula Chisipanya chophunzirira ndipo pomaliza, ndinaitana mpingo wonse kuti ubwere kunyumba kwathu kudzakonzekera cerveza Loŵeruka m’maŵa nthaŵi ya 9:30 a.m. Ndinkafuna kunena kuti servicio, kutanthauza kukalalikira, koma m’malo mwake ndinali kuitanira aliyense ku moŵa. Kuphunzira chilankhulo, kunalidi kovuta!

Poyamba, ndinkalemba m’manja zomwe ndikufuna kukanena ndi kumaziyeseza popita pakhomo. Nthaŵi zina ndimati: “Ndi buku ili, mungaphunzire Baibulo kwaulere panyumba panu.” Munthu wina amene anavomera, pambuyo pake anati anabwera kumsonkhano kuti adzaone zomwe ndinkafuna kumuuza. Munthu ameneyu, anakhala Mboni ya Yehova. N’zoonekeratu kuti ndi Mulungu amene amakulitsa mbewu za choonadi m’mitima yodzichepetsa monga mmene mtumwi Paulo anaonera!​—1 Akorinto 3:7.

Titakhala zaka pafupifupi ziŵiri mu mzinda wa Managua womwe ndi likulu la dzikolo, tinapemphedwa kusamukira kumwera kwa Nicaragua. Kumeneko tinagwira ntchito ndi mpingo wa ku Rivas ndi magulu ena a patalipatali a anthu ochita chidwi. Pedro Peña, Mboni yachikulire ndi yokhulupirika, inapita nane kukachezera magulu ameneŵa. Lina linali pachilumba cha m’nyanja ya Nicaragua, pomwe panali banja limodzi lokha la Mboni za Yehova.

Ngakhale kuti banjali silinali lopeza bwino, linayesetsa kwambiri kusonyeza kuyamikira ulendo wathu. Titafika cha kumadzulo, tinapeza atatikonzera kale chakudya. Tinakhalako mlungu umodzi, ndipo anthu ambiri okondedwa ndi okonda Baibulo, anatigaŵira chakudya. Tinasangalala kwambiri kuti anthu 101 anasonkhana nafe Lamlungu pa nkhani ya Baibulo.

Pa ulendo wina wokachezera gulu lina m’dera la kumapiri kumalire ndi dziko la Costa Rica, ndinaona kuti mphamvu ya Yehova inatichirikiza. Tsiku loti tinyamuke, Pedro anabwera kudzanditenga. Koma ndinali kugona chifukwa ndinadwala malungo. Ndinamuuza Pedro kuti, “Sindipita.” Ataika dzanja lake pamphumi panga anati: “Wadwaladi kwambiri, koma uyenera kupita! Abale akudikira.” Ndiyeno, anapemphera mochokera pansi pa mtima komwe sindinamvepo.

Kenako ndinati: “Katenge fresco (chakumwa cha zipatso) umwe. Ndikonzeka posachedwa.” Mabanja aŵiri a Mboni okhala kumeneko, anatisamalira bwino kwambiri. Tsiku lotsatira tinapita nawo kukalalikira ngakhale kuti ndinali wofookabe chifukwa cha malungo. Zinalitu zolimbikitsa kuti anthu oposa 100 anafika pamsonkhano wa Lamlungu!

Kusamukanso

Mu 1975 tinabereka mwana wa chisanu ndi chiŵiri Vaughn. Chaka chotsatira, tinabwerera ku Canada chifukwa cha vuto la zachuma. Kuchoka ku Nicaragua kunali kovuta chifukwa tinaona kuti Yehova anali kutisunga. Panthaŵi imene timachoka, anthu oposa 500 a m’gawo la mpingo wathu anali kusonkhana nafe.

M’mbuyomo, pamene ine ndi mwana wathu wamkazi Miriam tinasankhidwa kukhala apainiya apadera ku Nicaragua, Miriam anandifunsa kuti: “Bambo, ngati mungadzabwerere ku Canada, kodi zingatheke kuti ndidzakhale konkuno?” Ndinalibe malingaliro aliwonse ofuna kubwerera, ndiye ndinati: “Inde ndi choncho kumene!” Choncho pamene tinachoka, Miriam anatsala kuti apitirize ntchito yake yolalikira. Pambuyo pake anakwatiwa ndi Andrew Reed. Mu 1984 analowa nawo kalasi nambala 77 ya Gileadi, sukulu yaumishonale ya Mboni za Yehova, yomwe panthaŵiyo inali ku Brooklyn, mu mzinda wa New York. Tsopano Miriam akutumikira ndi mwamuna wake ku Dominican Republic, kukwaniritsa chikhumbo chake chimene amishonale abwino anam’patsa ku Nicaragua.

Pakali pano mawu a bambo akuti, “sitisiya wamba kulalikira,” amandigwirabe mtima. Pofika mu 1981 tinapeza ndalama zokwanira kuti tibwererenso ku madera a pakati pa America. Nthaŵi ino, tinasamukira ku Costa Rica. Tikutumikira kumeneko, tinapemphedwa kuthandiza kumanga ofesi yanthambi yatsopano. Koma mu 1985, mwana wathu wamwamuna Grant anafunikira chithandizo cha mankhwala, choncho tinabwerera ku Canada. Glen anatsalira ku Costa Rica pantchito yomanga ofesi yanthambi, pamene Annette ndi Charmaine anali kutumikira monga apainiya apadera. Ife amene tinachoka ku Costa Rica tinalibiretu maganizo akuti sitidzapitakonso.

Kukumana ndi Mavuto

Pa September 17, 1993, kunacha kowala bwino ndi dzuŵa. Ine ndi mwana wathu wamkulu wamwamuna Mark, tinali pamwamba kukonza denga. Tinali kugwira ntchito limodzi ndiponso kucheza nkhani zauzimu monga mwa nthaŵi zonse. Kenako, ndinaterereka n’kugwera pansi. Pamene ndimatsitsimuka, ndinangoona magetsi owala ndi anthu ovala zoyera. Ndinali m’chipinda cha odwala mwakayakaya kuchipatala.

Chifukwa cha zomwe Baibulo limanena, mawu anga oyamba anali akuti: “Musandiike magazi, musandiike magazi!” (Machitidwe 15:28, 29) Zinali zolimbikitsa kwambiri kumva Charmaine akunena kuti: “Osadandaula bambo, tonse tilipo.” Pambuyo pake ndinamva kuti madokotala anali ataona khadi langa loletsa magazi moti sipanakhalenso nkhani yondiika magazi. Ndinali nditathyoka khosi ndipo thupi lonse linali litaferatu, sindinathe ngakhale kupuma pandekha.

Pakuti sindinathenso kuchita kanthu, ndinafunikira kuchirikizidwa ndi Yehova kuposa kale lonse. Paipi yondithandiza kupuma inanditseka mmero, chotero sindinathe kulankhula. Anthu amangoyang’ana milomo yanga kuti amve zimene ndikunena.

Panafunika ndalama zambiri. Pakuti mkazi wanga ndi ana anga ambiri anali mu utumiki wanthaŵi zonse, ndinaganiza kuti mwina angosiya utumiki kuti afunefune ndalamazo. Koma Mark anapeza ntchito, ndipo m’miyezi itatu yokha anatha kupeza ndalama zondilipirira. Choncho, onse anatha kupitiriza utumiki wa nthaŵi zonse kupatulapo ine ndi mkazi wanga.

Makadi ndi makalata ambirimbiri ondifunira zabwino ochokera ku mayiko asanu ndi limodzi, anadzaza pamakoma m’chipinda changa kuchipatala. Yehova analidi kundichirikiza. Nawonso mpingo unatithandiza kwambiri ndi chakudya m’miyezi isanu ndi theka yomwe ndinali m’chipinda cha anthu odwala mwakayakaya. Masana aliwonse, mkulu mumpingo wachikristu anali kucheza nane. Anali kundiŵerengera Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo ndiponso kundikambira nkhani zolimbikitsa. Anthu aŵiri a m’banja lathu anali kukonzekera nane limodzi misonkhano ya mpingo, choncho sindinaphonye chakudya chofunika kwambiri chauzimu.

Pamene ndinali m’chipatala, abale anakonza kuti ndikakhale nawo patsiku la msonkhano wapadera. Achipatala anatipatsa nesi ndi dokotala woona za kupuma kuti akakhale nane tsiku lonse. Zinalitu zokondweretsa kwambiri kukhalanso ndi abale ndi alongo achikristu! Sindidzaiwala pamene anthu mazanamazana anapanga mzera kuti andipatse moni.

Kukhalabe Wauzimu

Patatha pafupifupi chaka nditavulala, tinabwerera kunyumba ngakhale kuti ndimafunikirabe chisamaliro nthaŵi zonse. Pogwiritsa ntchito galimoto yokonzedwa mwapadera, ndimapita kumisonkhano ndipo sindilephera kaŵirikaŵiri. Ndiyenera kuvomereza ndithu kuti pamafunika kulimba. Kuchokera pamene ndinabwerera kunyumba sindinaphonyepo msonkhano wachigawo.

Pambuyo pake, mu February 1997, ndinayambanso kulankhula koma pang’ono. Manesi ena amayamikira ndikamawauza chiyembekezo changa cha m’Baibulo. Nesi wina anandiŵerengera buku lonse la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, ndi zofalitsa zina za Watch Tower. Ndimagwiritsa ntchito kamtengo polembera anthu mauthenga pa kompyuta. Ngakhale kuti kutaipa ndi kamtengo n’kotopetsa, n’zopindulitsa kupitirizabe utumiki.

Ndimavutika kwambiri ndi kupweteka kwa mitsempha. Koma ndimaona kuti pamene ndikuuza ena choonadi cha Baibulo kapena pamene wina akundiŵerengera ndimapeza mpumulo. Nthaŵi zina ndimalalikira mu msewu ndi mkazi wanga yemwe amathandiza kumasulira zomwe ndanena pakafunika thandizo. Nthaŵi zina, ndatumikirapo monga mpainiya wothandiza. Kutumikira monga mkulu mu mpingo wachikristu kumandipatsa chimwemwe makamaka pamene abale andipeza pamisonkhano kapena kunyumba ndipo ndawathandiza ndi kuwalimbikitsa.

Ndikuvomera kuti n’kosavuta kukhala wovutika maganizo. Ndiye ndikangoyamba kuvutika maganizo, nthaŵi yomweyo ndimapemphera kuti ndikhale wachimwemwe. Usiku ndi usana ndimapemphera kuti Yehova apitirize kundilimbikitsa. Munthu akandilembera kalata kapena kudzandiona, amandilimbikitsa. Kuŵerenga Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! kumandipatsa maganizo olimbikitsa. Nthaŵi zina manesi osiyanasiyana amandiŵerengera magaziniŵa. Kuchokera pamene ndinavulala, ndamvetsera kuŵerenga kwa Baibulo lonse pakaseti nthaŵi zisanu ndi ziŵiri. Izi ndi zina mwa njira zosiyanasiyana zimene Yehova wandichirikizira.​—Salmo 41:3.

Kusintha kwa zinthu m’moyo wanga, kwandipatsa nthaŵi yochuluka yolingalira mmene Mlangizi wathu Wamkulu Yehova, amatiphunzitsira kwa moyo wonse. Amatiphunzitsa zoona zenizeni za zofuna ndi zolinga zake, kum’tumikira mwatanthauzo, malangizo a mmene tingakhalire ndi chimwemwe m’banja, ndiponso nzeru yodziŵa zimene tingachite tikakhala m’mavuto. Yehova wandidalitsa pondipatsa mkazi wokhulupirika ndi wosangalatsa. Ana anganso andithandiza mokhulupirika, ndipo n’zosangalatsa kuti onse anakhalapo atumiki a nthaŵi zonse. Pa March 11, 2000, mwana wathu Mark ndi mkazi wake Allyson, anamaliza maphunziro awo m’kalasi la nambala 108 la Sukulu ya Gileadi ndipo anatumizidwa ku Nicaragua. Ine ndi mkazi wanga tinakakhala nawo pa mwambo wa omaliza maphunzirowo. Kuchokera pansi pa mtima ndinganene kuti mavuto asintha moyo wanga koma osati mtima wanga.​—Salmo 127:3, 4.

Ndikuthokoza Yehova chifukwa cha nzeru zomwe zandithandiza kupatsira banja langa choloŵa chauzimu chomwe ndinalandira. Ndikulimbikitsidwa kuona ana anga akutumikira Mlengi wawo ndi mtima wofanana ndi wa bambo anga omwe anati, “Sitisiya wamba kulalikira. Yehova watilamula kuti tilalikire.” Zoonadi, Yehova wandichirikiza ine ndi banja langa masiku onse.

[Chithunzi patsamba 24]

Bambo, achimwene anga, ndi mlongo wanga pafupi ndi nyumba yathu yopangolo yomwe timagwiritsa ntchito masiku aupainiya. Ine ndili kumanja

[Chithunzi patsamba 26]

Ndi mkazi wanga Myrna

[Chithunzi patsamba 26]

Chithunzi chaposachedwapa cha banja lathu

[Chithunzi patsamba 27]

Ndimalalikirabe mwa kulemba makalata