Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungapezere Chimwemwe Chenicheni

Mmene Mungapezere Chimwemwe Chenicheni

Mmene Mungapezere Chimwemwe Chenicheni

MTSOGOLERI wachipembedzo chachibuda wotchedwa Dalai Lama ananena kuti: “Ndimakhulupirira kuti cholinga chenicheni cha moyo wathu ndicho kufunafuna chimwemwe.” Kenako ananena kuti amakhulupirira kuti chimwemwe chingapezeke mwa kuphunzitsa, kapena kuwongolera maganizo ndi mtima.” Ananenanso kuti, “maganizo ndiwo chinthu chofunika kwambiri kuti tipeze chimwemwe chenicheni.” Iye amaona kuti kukhulupirira Mulungu kulibe ntchito. *

Mosiyana ndi zimenezo, taganizirani za Yesu amene ankakhulupirira kwambiri Mulungu ndiponso yemwe zophunzitsa zake zagwira mtima anthu mamiliyoni mazanamazana kwa zaka zambiri. Yesu ankafuna kuti anthu azisangalala. Iye anayamba Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri ndi mawu asanu ndi anayi omwe anayamba mwakuti: “Achimwemwe ali . . . ” (Mateyu 5:1-12, NW) Paulaliki womwewo, iye anaphunzitsa anthu kupenda, kuyeretsa, ndiponso kuwongolera maganizo ndi mitima yawo. Anawauza kuti asakhale ndi malingaliro achiwawa, akhalidwe loipa kapena odzikonda, koma kuti akhale ndi malingaliro amtendere, oyera, ndiponso mtima wachikondi. (Mateyu 5:21, 22, 27, 28; 6:19-21) Monga momwe mmodzi wa ophunzira ake analangizira, tiyenera kupitiriza ‘kulingalira’ zinthu ‘zoona, zolemekezeka, zolungama, zoyera, zokongola, ndiponso zokoma.’​—Afilipi 4:8.

Yesu ankadziŵa kuti chimwemwe chenicheni chimafuna mgwirizano. Anthufe mwachibadwa timakonda kucheza ndi anzathu. Choncho, sitingasangalaledi ngati titakhala patokha kapena ngati nthaŵi ndi nthaŵi timakangana ndi anzathu omwe tikukhala nawo. Tingakhale achimwemwe pokhapokha ngati timakondedwa komanso ngati timakonda anzathu. Yesu anaphunzitsa kuti, unansi wathu ndi Mulungu ndiwo maziko achikondi choterocho. Pankhaniyi, zomwe Yesu anaphunzitsa zikusiyana ndi zomwe Dalai Lama anaphunzitsa, chifukwa chakuti Yesu anaphunzitsa kuti anthu sangasangalale popanda kudalira Mulungu. N’chifukwa chiyani zili choncho?​—Mateyu 4:4; 22:37-39.

Ganizirani Zosoŵa Zanu Zauzimu

Yesu ananena kuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) N’chifukwa chiyani Yesu ananena zimenezi? N’chifukwa chakuti mosiyana ndi nyama, anthufe timafuna zinthu zauzimu. Popeza kuti tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, titha kukulitsa mikhalidwe yake monga chikondi, chilungamo, chifundo, ndiponso nzeru kum’lingo winawake. (Genesis 1:27; Mika 6:8; 1 Yohane 4:8) Zosoŵa zathu zauzimu zimaphatikizapo kufunika kokhala ndi cholinga m’miyoyo yathu.

Kodi tingakwaniritse motani zosoŵa zauzimu zimenezi? Sitingakwaniritse mwa kusinkhasinkha kapena kudzipenda chabe. M’malo mwake, Yesu ananena kuti: “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Onani kuti Yesu ananena kuti Mulungu ndiye gwero la “mawu onse” ofunika kuti tikhale ndi moyo. Mulungu yekha ndiye angatithandize kuyankha mafunso ena. Kudziŵa zimenezi n’kofunika kwambiri makamaka tsopano pamene ziphunzitso zokhudza cholinga cha moyo ndiponso njira zopezera chimwemwe zafala kwambiri. Masitolo ogulitsa mabuku adzaza ndi mabuku omwe amalonjeza thanzi, chuma, ndiponso chimwemwe kwa oŵerenga. Pa Intaneti palinso malo ankhani zokhudza chimwemwe zokhazokha.

Komabe, maganizo a anthu pankhani zimenezi kaŵirikaŵiri amakhala osokeretsa. Nthaŵi zambiri nkhani zoterezi zimangolimbikitsa dyera kapena kudzitukumula. Nkhanizo zimachokera pa nzeru komanso luntha lopereŵera ndipo nthaŵi zambiri zimachokera m’malo achinyengo. Mwachitsanzo, chizoloŵezi chomwe chikufala kwambiri kwa olemba mabuku amalangizo ndicho kulemba mfundo zawozo kuchokera pa chiphunzitso cha sayansi yachisinthiko yophatikizana ndi sayansi ya maganizo ndi chikhalidwe. Chiphunzitsocho chimanena kuti mwina munthu anatengera maganizo a nyama yomwe amati ndiko anachokera. Zoona zake n’zakuti, njira zilizonse zopezera chimwemwe zomwe n’zochokera pa chiphunzitso chomwe chimanyalanyaza Mlengi n’zosayenera ndipo zimagwiritsa mwala. Mneneri wakale ananena kuti: “Anzeru ali ndi manyazi, . . . akana mawu a Yehova ali nayo nzeru yotani?”​—Yeremiya 8:9.

Yehova Mulungu amadziŵa mmene anatipangira ndiponso zomwe zingatisangalatsedi. Iye amadziŵanso chomwe anaikira munthu padziko lapansi komanso zomwe zili m’tsogolo ndipo amatiuza nkhani zimenezi m’Baibulo. Zomwe amavumbula m’buku louziridwa limeneli zimachititsa anthu amaganizo abwino kulabadira komanso zimawadzetsera chimwemwe. (Luka 10:21; Yohane 8:32) Zimenezi n’zimene zinachitikira ophunzira aŵiri a Yesu. Iwo anakhumudwa kwambiri iye ataphedwa. Koma atamva kuchokera kwa Yesu woukitsidwayo za udindo wake m’chifuno cha Mulungu chopulumutsa anthu, iwo anati: “Mtima wathu sunali wotentha m’kati mwathu nanga mmene analankhula nafe m’njira, mmene anatitsegulira malembo?”​—Luka 24:32.

Chimwemwe choterocho chimakula ngati tilola choonadi cha m’Baibulo kutsogolera moyo wathu. Pamenepa, chimwemwe tingachifanizire ndi utawaleza. Umaoneka pokhapokha ngati nyengo ili yoyenera, koma umaoneka bwino kwambiri mwinanso kukula kukhala utawaleza uŵiri ngati nyengo ili yoyenera mwapadera. Tsopano tiyeni tione zitsanzo zingapo za mmene kugwiritsa ntchito ziphunzitso za m’Baibulo kungawonjezere chimwemwe.

Musafune Zambiri M’moyo Wanu

Choyamba, taganizirani za langizo la Yesu pankhani yachuma. Atachenjeza za kufuna chuma monga chinthu chachikulu m’moyo, iye anatchula mawu apadera. Iye anati: “Chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala loŵalitsidwa.” (Mateyu 6:19-22) Kwenikweni iye ankatanthauza kuti ngati tikufunafuna chuma, ulamuliro, kapena zinthu zina zomwe anthu ena amalakalaka, ndiye kuti tidzalephera kupeza zinthu zofunika kwambiri. N’chifukwa chake Yesu nthaŵi ina ananena kuti, “moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.” (Luka 12:15) Ngati tiika patsogolo zinthu zofunikadi monga unansi wathu ndi Mulungu, zosoŵa za banja, ndi zina zotero, ndiye kuti “diso” lathu lidzakhala la “kumodzi” lopenya bwino.

Dziŵani kuti, Yesu sanali kulimbikitsa moyo wosasangalala kapena wodzimana monkitsa. Ndiiko komwe, Yesu mwiniyo sanali wosasangalala kapena wodzimana monkitsa. (Mateyu 11:19; Yohane 2:1-11) M’malo mwake, iye anaphunzitsa kuti, anthu amene amaona mwayi wopeza chuma kukhala woposa moyo, sadzapeza moyo.

Ponenapo za anthu ena omwe amakhala achuma kwambiri adakali aang’ono, wasayansi yamaganizo wina ku San Francisco, U.S.A. ananena kuti, kwa anthu otereŵa ndalama ndizo “zimawachititsa kuvutika maganizo ndiponso kusokonezeka mutu.” Iye anawonjezera kuti, anthu otereŵa “amagula nyumba ziŵiri kapena zitatu, galimoto, ndiponso zinthu zina. Ndipo ngati zimenezi sizikuwabweretsera chimwemwe, iwo amavutika maganizo ndipo sadziŵa chochita ndi miyoyo yawo.” Mosiyana ndi zimenezo, anthu amene amatsatira langizo la Yesu losafuna chuma chochuluka, akumapatsa mpata zinthu zauzimu ndiwo angakhaledi achimwemwe.

Tom, mmisiri womanga nyumba yemwe akukhala ku Hawaii, anadzipereka kukathandiza kumanga nyumba zolambiriramo pazilumba za Pacific komwe anthu alibe chuma chochuluka. Tom anaona kanthu kena mwa anthu odzichepetsawo. Iye anati: “Abale ndi alongo anga achikristu pa zilumbazo anali osangalaladi. Iwo anandithandiza kuona kuti ndalama kapena katundu sindizo chinsinsi chopezera chimwemwe.” Iye anaonanso kuti anthu odzipereka omwe ankagwira naye ntchito anali okhutira kwambiri. Tom ananena kuti: “Iwo akanatha kupeza ndalama zambiri, koma anasankha kuika zinthu zauzimu patsogolo kwinaku n’kumapitiriza kukhala moyo wosafuna zambiri. Atachita chidwi ndi zitsanzo zimenezi, Tom nayenso anayamba kukhala moyo wosafuna zambiri n’cholinga choti azipeza nthaŵi yochuluka yosamalira zinthu zauzimu ndiponso banja lake. Zimenezi zam’pindulira kwambiri.

Chimwemwe Ndiponso Kudzilemekeza

Kudzilemekeza n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale wachimwemwe. Chifukwa cha zofooka zobwera ndi kupanda ungwiro, ena amadzikayikira ndipo kwa anthu ambiri maganizo otereŵa amayamba adakali aang’ono. Nthaŵi zina kungakhaledi kovuta kuthetsa maganizo ozika mizu otereŵa, komabe, zimenezi zitha kutheka. Chinsinsi chake chagona pa kugwiritsa ntchito Mawu a Mulungu basi.

Baibulo limafotokoza mmene Mlengi amamvera za anthufe. Kodi si zoona kuti mmene iye amationera ndicho chinthu chofunika kwambiri kuposa mmene munthu aliyense ngakhale enife timadzionera? Mulungu amationa mopanda tsankho chifukwa cha chikondi chake. Iye amadziŵa zomwe tikuganiza komanso zomwe tingaganize. (1 Samueli 16:7; 1 Yohane 4:8) Komanso, iye amaona amene akufuna kum’kondweretsa monga anthu apadera, inde, okondedwa kwambiri, ngakhale atakhala ndi zofooka zotani.​—Danieli 9:23; Hagai 2:7.

N’zoona kuti Mulungu sanyalanyaza zofooka zathu ndiponso tchimo lililonse lomwe timachita. Iye amayembekezera kuti tiziyesetsa kuchita zabwino, ndipo iye amatichirikiza tikamatero. (Luka 13:24) Komabe, Baibulo limanena kuti: “Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.” Limanenanso kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.”​—Salmo 103:13; 130:3, 4.

Choncho, phunzirani kukhala wooneka bwino kwa Yehova. Kudziŵa kuti iye amakonda ndiponso kukhulupirira amene amam’konda ngakhale atamadziona ngati wonyozeka, kungawonjezere kwambiri chimwemwe cha munthu aliyense.​—1 Yohane 3:19, 20.

Chimwemwe Chimafuna Chiyembekezo

Chiphunzitso chomwe chafala posachedwapa chotchedwa sayansi ya maganizo abwino, chimatchula chidaliro chomwe akuti chimakula munthu akamaganiza bwino ndiponso kuika mtima pa mphamvu zake. Chidaliro chimenechi akuti chingachititse munthu kukhala wachimwemwe. Oŵerengeka chabe angakane kuti kukhala ndi chidaliro cha moyo ndiponso cham’tsogolo kumawonjezera chimwemwe chathu. Komabe, chidaliro choterocho chiyenera kukhala ndi maziko oona osati kungolakalaka chabe zitatero. Komanso, sikuti chidaliro pachokha kapena kuganiza bwino zidzachotsa nkhondo, njala, matenda, kuipitsa dziko, ukalamba, kapena imfa​—zinthu zomwe zimalepheretsa anthu kukhala achimwemwe. Komabe, chidaliro chili ndi ntchito yake yoyenera.

N’zochititsa chidwi kuti Baibulo siligwiritsa ntchito mawu akuti chidaliro, m’malo mwake, limagwiritsa ntchito mawu amphamvu kwambiri akuti chiyembekezo. Buku lotanthauzira mawu lotchedwa Vine’s Complete Expository Dictionary limatanthauzira mawu akuti “chiyembekezo” monga mmene Baibulo limawagwiritsira ntchito kukhala “kudikira moyenera ndiponso motsimikizira, . . . kuyembekezera zinthu zabwino mokondwera.” Mmene mawuŵa amagwirira ntchito m’Baibulo, amaposa kungokhala chabe ndi chidaliro pa chinachake. Amaphatikizapo maziko a chiyembekezocho. (Aefeso 4:4; 1 Petro 1:3) Mwachitsanzo, chiyembekezo cha Akristu n’chakuti mavuto onse omwe atchulidwa m’ndime ili pamwambayi adzatha posachedwapa. (Salmo 37:9-11, 29) Koma chiyembekezocho chimaphatikizapo zambiri.

Akristu akuyembekezera nthaŵi imene anthu okhulupirika adzakhale ndi moyo wangwiro padziko lapansi la Paradaiso. (Luka 23:42, 43) Kuwonjezera pa chiyembekezo chimenechi, Chivumbulutso 21:3, 4 amati: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake. . . . Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”

Aliyense amene akuyembekezera kudzakhala ndi tsogolo lotero ali ndi zifukwa zokwanira zokhalira wosangalala, ngakhale zinthu sizikuyenda bwino tsopano. (Yakobo 1:12) Choncho, bwanji osalifufuza Baibulo kuti muone chifukwa chimene mungakhulupirire zimenezi. Limbitsani chiyembekezo chanu mwa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Kuchita zimenezi kudzakupindulitsani mwauzimu, kukuthandizani kupeŵa zinthu zomwe zimalanda anthu chimwemwe komanso mudzakhala okhutira kwambiri. Inde, chinsinsi chachikulu cha chimwemwe chenicheni ndicho kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mlaliki 12:13) Moyo wotsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo ndiwo wosangalatsa chifukwa Yesu ananena kuti: ‘Achimwemwe iwo akumva mawu a Mulungu, nawasunga.’​—Luka 11:28.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Abuda sakhulupirira Mulungu.

[Zithunzi patsamba 5]

Chimwemwe sichingapezeke mwa kupeza chuma chochuluka, kukhala pawekha, kapena kudalira nzeru zopereŵera za anthu

[Chithunzi patsamba 6]

Moyo womvera Mawu a Mulungu ndiwo wosangalatsa

[Chithunzi patsamba 7]

Chiyembekezo chachikristu chimachititsa munthu kukhala wosangalala