Opaleshoni Yopanda Magazi—“Njira Yamakono Yochizira”
Opaleshoni Yopanda Magazi—“Njira Yamakono Yochizira”
PA MUTU wakuti “Opaleshoni ‘Yopanda Magazi,’” magazini yotchedwa Maclean’s inati, madokotala ku Canada akhala “akupeza njira zatsopano zomwe, m’zaka zisanu zapitazi, zachititsa kuti yomwe amati ndi opaleshoni yopanda magazi ikhale njira yamakono yochizira.” Brian Muirhead, katswiri wa zochititsa dzanzi pa Health Sciences Centre ku Winnipeg, ndi mmodzi mwa madokotala amenewo. Kodi n’chiyani chinam’chititsa kufufuza njira zochizira popanda magazi?
Mu 1986, Dr. Muirhead anagwira ntchito yovuta kwambiri yochita opaleshoni mwamuna wina wa zaka 70 yemwe anali ndi chilonda chochucha magazi. Chifukwa cha zikhulupiriro zake zozikidwa pa Baibulo monga mmodzi wa Mboni za Yehova, mwamunayu anapempha chithandizo chomwe sichinafunikire kumuika magazi. (Machitidwe 15:28, 29) Dr. Muirhead “anagwiritsa ntchito njira yomwe siinkagwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri, njira yoika madzi a mchere m’thupi mwa wodwalayo n’cholinga choti magazi azithamanga kwambiri,” inatero magazini ya Maclean’s. “Njira imeneyo inathandiza kwambiri, ndipo inalimbikitsa zomwe a Muirhead ankakhulupirira kwambiri kuti ‘tinanyanyira kuika magazi anthu ochuluka. Ndinaganiza kuti tsopano n’kofunika kugwiritsa ntchito njira zina.’”
Kufunika kwa opaleshoni yopanda magazi “kunakula chifukwa chakuti anthu ali ndi nkhaŵa ponena za kumene kuzipezeka magazi m’tsogolomu, ndiponso chifukwa chakuti odwala amachita mantha kuti angatenge mavairasi a matenda chifukwa choikidwa magazi.” Mothandizidwa ndi kafukufuku wochitidwa ndi madokotala amakono, Mboni za Yehova limodzi ndi anthu enanso ambiri apindula. “Kuwonjezera pa kuchepetsa kufunika koika anthu magazi nthaŵi zambiri, maopaleshoni opanda magazi amachepetsa ngozi yotenga matenda kuchokera ku magazi oipitsidwa ngakhale kuti ngoziyo ndi yaying’ono,” inatero magazini ya Maclean’s. Komabe, ngakhale magazi “osaipitsidwa” angaperekenso matenda mwa kupondereza kwa kanthaŵi kochepa mphamvu ya chitetezo ya m’matupi a odwala.
Kodi n’chiyani chimachititsa Mboni za Yehova kuumirira chithandizo chamankhwala chopanda magazi? Mungakonde kuŵerenga bulosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? Mboni za Yehova zidzasangalala kukugaŵirani bulosha limeneli.