“Ambuye Anauka Ndithu!”
“Ambuye Anauka Ndithu!”
Tangoganizani chisoni chimene ophunzira a Yesu anali nacho Mbuye wawo ataphedwa. Chiyembekezo chawo chinali ngati mtembo umene Yosefe wa ku Arimateya anauika m’manda. Chiyembekezo choti Yesu adzamasula Ayuda m’goli la Aroma nachonso chinatheratu
NGATI zinthu zikanathera pamenepa, ophunzira a Yesu akanatha monga momwe otsatira anthu ena ambiri odzinenera kukhala Amesiya amathera. Koma Yesu anali wamoyo! Malinga ndi zomwe Malemba amanena, iye anaonekera kwa otsatira ake kangapo konse pambuyo pa imfa yake. Chotero, ena mwa iwo anasonkhezereka kufuula kuti: “Ambuye anauka ndithu!”—Luka 24:34.
Ophunzirawo anayenera kuchirikiza chikhulupiriro chawo mwa Yesu monga Mesiya. Pochita zimenezo, iwo kwenikweni ankatchula za kuuka kwake monga umboni wamphamvu wotsimikiza kuti iye ndiyedi Mesiya. Ndithudi, “atumwi anachita umboni ndi mphamvu yaikulu za kuuka kwa Ambuye Yesu.”—Machitidwe 4:33.
Ngati wina akanapeza umboni wotsimikiza kuti nkhani ya kuuka kwa Yesu inali yonama, mwina mwa kumva wina mwa ophunzira ake akuvomereza kuti inalidi yonama kapena mwa kusonyeza kuti mtembo wa Yesu unakhalabe m’manda, ndiye kuti Chikristu chikanatha pachiyambi pomwepo. Koma sichinatero. Podziŵa kuti Kristu anali wamoyo, ophunzira a Yesu anapita kulikonse kukalengeza za kuuka kwake ndipo anthu miyandamiyanda anakhulupirira Kristu woukitsidwayo.
N’chifukwa chiyani inunso mungakhulupirire kuuka kwa Yesu? Kodi pali umboni wanji wotsimikiza kuti zimenezi zinachitikadi?
N’kupenderanji Maumboni?
Nkhani zonse za m’Mauthenga Abwino anayi zimatchula za kuuka kwa Yesu. (Mateyu 28:1-10; Marko 16:1-8; Luka 24:1-12; Yohane 20:1-29) * Mbali zina za Malemba Achigiriki Achikristu zimatchulanso motsimikiza za kuuka kwa Kristu.
N’zosadabwitsa kuti otsatira a Yesu akhala akulengeza za kuuka kwake. Ngati Mulungu anaukitsadi Yesu, imeneyo ndi nkhani yochititsa chidwi kwambiri yomwe sinachitikepo n’kale lonse padziko lapansi. Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu alikodi. Komanso, zikutanthauza kuti Yesu ali moyo tsopano lino.
Kodi zimenezi zimatikhudza motani? Eya, Yesu anapemphera kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Inde, titha kupeza chidziŵitso chopatsa moyo cha Yesu ndi Atate wake. Mwa kugwiritsa ntchito chidziŵitso choterocho, ngakhale titamwalira ifenso tidzaukitsidwa popeza Yesu anaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Titha kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko lapansi la Paradaiso mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu womwe uli m’manja wa Mwana wake wolemekezekayo Yesu Kristu, Mfumu ya mafumu.—Yesaya 9:6, 7; Luka 23:43; Chivumbulutso 17:14.
Choncho, kufuna kudziŵa ngati Yesu anaukadi n’kofunika kwambiri. Kumakhudza moyo wathu tsopano lino komanso chiyembekezo chathu cham’tsogolo. N’chifukwa chake tikukupemphani kupenda maumboni anayi otsimikiza kuti Yesu anafa ndipo anaukitsidwa.
Yesu Anaferadi Pamtengo
Ena okayikira amanena kuti ngakhale kuti Yesu anapachikidwa, iye sanafe pamtengowo. Iwo amanena kuti anakomoka chabe ndipo anatsitsimuka chifukwa cha kuzizira kwa m’manda. Komabe, buku lililonse losimba za Yesu limene lilipo limatsimikiza kuti m’mandamo anaikamo mtembo wa Yesu.
Popeza kuti Yesu anamupha anthu akuona, panali mboni zomwe zinatsimikizira kuti iye anafera pamtengo pomwepo. Kazembe wankhondo wachiroma yemwe ankatsogolera zonse anatsimikiza kuti Yesu wafa. Kazembeyo anali wodziŵa bwino kwambiri ntchito yake, ndipo inaphatikizapo kuonetsetsa kuti Yesu wafadi. Komanso, bwanamkubwa wachiroma Pontiyo Pilato anapereka mtembo wa Yesu kwa Yosefe wa ku Arimateya kuti akauike m’manda atatsimikiza kaye kuti Yesu wafadi.—Marko 15:39-46.
M’manda Munapezeka Mulibe Kanthu
Ophunzira anatsimikiza koyamba za kuuka kwa Yesu ataona m’manda mulibe kanthu ndipo umboni umenewu palibe amatsutsa mpaka lero. Yesu anamuika m’manda atsopano osagwiritsidwapo ntchito. Mandawo anali pafupi ndi malo opachikirako anthu ndipo panthaŵiyo malowo anali osasoŵa. (Yohane 19:41, 42) Nkhani zonse za m’Mauthenga Abwino zimagwirizana kuti mabwenzi a Yesu atafika kumandako m’maŵa wachiŵiri pambuyo pa imfa yake, mtembowo sanaupeze.—Mateyu 28:1-7; Marko 16:1-7; Luka 24:1-3; Yohane 20:1-10.
Zinalitu zodabwitsa zedi kwa adani a Yesu ndiponso kwa mabwenzi ake kuona kuti m’manda mulibe kanthu. Adani akewo anali atayesetsa kwanthaŵi yaitali kuti Yesu aphedwe ndi kuikidwa m’manda. Atakwaniritsa zolinga zawo, iwo anaonetsetsa kuti aika mlonda ndiponso kutseka mandawo. Komabe, m’maŵa wa tsiku loyamba la mlungu, m’mandamo munalibe kanthu.
Kodi mabwenzi a Yesu anachotsa mtembowo m’mandamo? Sizikanatheka, chifukwa chakuti Mauthenga Abwino amanena kuti iwo anali achisoni kwambiri iye ataphedwa. Komanso, ophunzira ake sakadalolera kuvutika ndiponso kuphedwa chifukwa cha chinthu chomwe akudziŵa kuti n’chabodza.
Nanga ndani anachotsa mtembowo m’manda? Zoti adani a Yesu akadachotsa mtembowo zinali zokayikitsa kwabasi. Komabe, ngakhale akadatero, iwo mwachionekere akadaulula pambuyo pake kuti atsutse zomwe ophunzira ake ankanena kuti Yesu waukitsidwa ndipo ali ndi moyo. Koma zinthu sizinatero chifukwa chakuti anali Mulungu amene anachita zimenezo.
Patapita milungu ingapo, adani a Yesu sanam’tsutse Petro pamene ankachitira umboni kuti: “Amuna inu Aisrayeli, mverani mawu aŵa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa iye pakati pa inu, monga mudziŵa nokha; ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziŵiratu kwa Mulungu, inu mwam’pachika ndi kumupha ndi manja a anthu osayeruzika; yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti iye agwidwe nayo. Pakuti Davide anena za iye, ndinaona Mbuye pamaso panga nthaŵi zonse . . . Ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo. Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Hade, kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivundi.”—Machitidwe 2:22-27.
Ambiri Anamuona Yesu Woukitsidwayo
M’buku la Machitidwe, wolemba Uthenga Wabwino Luka ananena kuti: “Kwa iwonso [atumwi], [Yesu] anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anayi, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu.” (Machitidwe 1:2, 3) Ophunzira ambiri anamuona Yesu woukitsidwayo panthaŵi zosiyanasiyana—m’munda, panjira, pachakudya, komanso m’mbali mwa Nyanja ya Tiberiya.—Mateyu 28:8-10; Luka 24:13-43; Yohane 21:1-23.
Otsutsa amakayikira zoti Yesu anaonekera. Iwo amanena kuti olembawo anangopeka nkhanizo ndiponso amatchulanso mfundo zina zomwe amati zimasiyanasiyana. Komabe, kusiyanasiyana kwa apo ndi apo m’Mauthenga Abwino kumachitira umboni woti panalibe zachinyengo. Kum’dziŵa kwathu Yesu kumawonjezereka pamene wolemba wina alongosola mwatsatanetsatane zinthu zomwe zikugwirizana ndi nkhani ina ya m’zochitika zina za m’moyo wa Kristu wapadziko lapansi.
Kodi amene anamuona Yesu ataukitsidwa ankaona zideruderu chabe? Maganizo onse otereŵa n’ngopanda pake chifukwa chakuti ndi anthu ambiri amene anamuona. Ena mwa anthuŵa anali asodzi, akazi, wogwira ntchito yaboma, ngakhalenso mtumwi Tomasi wokayikirayo yemwe anatsimikiza ataona kaye umboni wosatsutsika woti Yesu waukitsidwadi. (Yohane 20:24-29) Nthaŵi zambiri, ophunzira a Yesu sanali kum’zindikira Mbuye wawo woukitsidwayo. Nthaŵi inayake, anthu opitirira 500 anamuona ndipo ambiri mwa iwo anali akadali moyo pomwe mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chochitikacho monga umboni wotsimikiza za chiukiriro.—1 Akorinto 15:6.
Yesu Wamoyo Akusintha Miyoyo ya Anthu
Kuuka kwa Yesu si nkhani yachibwana yoyenera kungoidziŵa chabe kapena yosangalatsa kumatsutsana ayi. Kudziŵa kokha kuti iye ali Afilipi 2:8-11) Iwo akhulupirira Yesu komanso njira yachipulumutso imene Yehova Mulungu anakonza kudzera m’nsembe ya dipo ya Kristu. (Aroma 5:8) Anthu ameneŵa apezadi chimwemwe chenicheni mwa kuchita chifuniro cha Mulungu ndiponso kukhala mogwirizana ndi zomwe Yesu anaphunzitsa.
moyo kwachititsa anthu kulikonse kusintha miyoyo yawo. Kuyambira m’zaka za zana loyamba, anthu miyandamiyanda atembenuka kusiya kutsutsa Chikristu ndipo afika potsimikiza kuti ndicho chipembedzo choona. Kodi chawasintha n’chiyani? Kuphunzira Malemba ndiko kwawakhutiritsa kuti Mulungu anaukitsira Yesu kumoyo waulemerero wakumwamba monga cholengedwa chauzimu. (Taganizirani zomwe kukhala Mkristu kunkatanthauza m’zaka za zana loyamba. Kunalibe kufunafuna kutchuka, ulamuliro, kapena chuma. M’malo mwake, Akristu oyambirira ambiri ‘analolera mokondwera kulandidwa chuma’ chifukwa cha chikhulupiriro chawo. (Ahebri 10:34) Kukhala Mkristu kunatanthauza moyo wodzipereka komanso wamazunzo chifukwa nthaŵi zambiri mapeto ake kunali kuphedwa.
Asanakhale otsatira a Kristu, ambiri anali ndi mwayi wodzakhala otchuka ndiponso achuma. Saulo wa ku Tariso anaphunzitsidwa ndi mphunzitsi wotchuka kwambiri wachilamulo wotchedwa Gamaliyeli ndipo nayenso anayamba kutchuka pakati pa Ayuda. (Machitidwe 9:1, 2; 22:3; Agalatiya 1:14) Komabe, Saulo anadzakhala mtumwi Paulo. Iye ndi ena ambiri anakana kutchuka ndiponso ulamuliro zimene dzikoli linapereka. N’chifukwa chiyani? Chifukwa chofuna kulengeza uthenga wachiyembekezo chenicheni wochokera pa malonjezo a Mulungu ndiponso pa chiukiriro cha Yesu Kristu. (Akolose 1:28) Iwo analolera kuvutika chifukwa cha zomwe ankadziŵa kuti zinali zoona.
N’chimodzimodzinso anthu miyandamiyanda lerolino. Anthuŵa mungawapeze m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse. Mboni zili zokondwa kwambiri kukuitanani ku chikumbutso cha imfa ya Kristu, chomwe chidzachitike dzuŵa litangoloŵa Lamlungu, pa April 8, 2001. Iwo adzakondwa kwambiri ngati mutadzakhalapo pamwambo umenewu komanso pamisonkhano yawo yophunzira Baibulo yomwe imachitikira ku Nyumba zawo za Ufumu.
Bwanji osaphunzira zambiri, osati pa za imfa kapena kuuka kwa Yesu zokha, komanso za moyo wake ndiponso ziphunzitso zake? Iye akutiitana kuti tidze kwa iye. (Mateyu 11:28-30) Chitanipo kanthu tsopano kuti mupeze chidziŵitso cholondola cha Yehova Mulungu ndi cha Yesu Kristu. Kuchita zimenezo kudzakupezetsani moyo wosatha mu Ufumu wa Mulungu womwe uli m’manja mwa Mwana wake wokondedwayo.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 8 Kuti mupeze umboni wotsimikiza kuti Mauthenga Abwino ndi oona, onani mutu wakuti “Mauthenga Abwino—Mbiri Kapena Nthano?” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2000.
[Zithunzi patsamba 7]
Anthu miyandamiyanda apeza chimwemwe chenicheni monga otsatira a Yesu Kristu
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
Chotengedwa m’Baibulo la Self-Pronouncing Edition of the Holy Bible, lokhala ndi Baibulo la King James ndi mabaibulo a Revised