Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chipembedzo Chidzabweretsa Mtendere wa Dziko lonse?

Kodi Chipembedzo Chidzabweretsa Mtendere wa Dziko lonse?

Kodi Chipembedzo Chidzabweretsa Mtendere wa Dziko lonse?

KUYAMBIRA pa August 28 mpaka pa August 31, 2000, nthumwi zoposa 500 zochokera m’mayiko 73 zinasonkhana ku mzinda wa New York City. Nthumwizo zinakumana pa maofesi a United Nations kukachita “Msonkhano wa Atsogoleri a Zipembedzo ndi a Zauzimu Wokambirana za Mtendere wa Dziko Lonse M’zaka Chikwi.” Atsogoleriwo, omwe ambiri mwa iwo anavala nduŵira, mikanjo yachikasu ndi yakuda, maduku anthenga, anaimira zikhulupiriro miyandamiyanda. Mwa nthumwi zimenezi panali nthumwi za Chibahai, Chibuda, Chihindu, Chijaini, Chishinto, Chisiki, Chisilamu, Chitao, Chiyuda, Chizorowasita, ndi zipembedzo za Gawo la Matchalitchi Achikristu.

Nthumwizo zinakumanirana pa maofesi a United Nations kwamasiku aŵiri oyambirira a msonkhano wa masiku anayiwo. Msonkhanowo sunakonzedwe kapena kulipiriridwa ndi United Nations koma unakonzedwa ndi mabungwe osiyanasiyana. Komabe, bungwe la United Nations limodzi ndi atsogoleri a zipembedzo analankhula za kufunika kogwirira ntchito pamodzi n’cholinga chothetsa umphaŵi, kusankhana mafuko, kuwononga malo okhala, nkhondo, ndiponso zida zankhondo zamphamvu kwambiri.

Nthumwizo zinasaina chikalata chakuti “Pangano la Mtendere wa Dziko Lonse.” Ngakhale kuti chikalatachi chinavomereza kuti ziwawa ndi nkhondo “nthaŵi zina zachitika motsogozedwa ndi chipembedzo,” icho chinanenanso kuti nthumwi zosainazo “zidzathandizana ndi United Nations . . . pantchito yofunafuna mtendere.” Komabe, panalibe mfundo zenizeni zosonyeza mmene zimenezi zingachitikire.

Patsiku lachiŵiri la msonkhanowo, a Bawa Jain, mlembi wamkulu wa msonkhanowo, m’mawu awo amalonje anamaliza mwa kulongosola kuti zaka zingapo zapitazo iwo anaona chithunzi chinachake chojambulidwa pakhoma la maofesi a United Nations. Chithunzicho chinkasonyeza mwamuna wamtali kuposa nyumba ya Maofesi Oyendetsa Ntchito za United Nations. Iye anali kugogoda pa nyumbayo ngati kuti nyumbayo ndiyo chitseko. M’munsi mwa chithunzicho munali mawu akuti: “Kalonga wa Mtendere.” A Jain anati: “[Chithunzicho] chinandikhudza mtima kwambiri nditangochiona. Ndinafunsa anthu osiyanasiyana kuti [chithunzicho] chimatanthauzanji. Ndikuganiza kuti lero ndili ndi yankho lake. Kusonkhana kwa inu nonse pano, atsogoleri a zauzimu ndi a zachipembedzo a padziko lonse, zikundisonyeza bwinobwino kuti [uyu] ndiye kalonga wa mtendere akugogoda pachitseko cha United Nations.”

Baibulo limafotokoza malingaliro osiyana ndi ameneŵa. Limasonyeza kuti Kalonga wa Mtendere ndi Yesu Kristu. Iye adzabweretsa mtendere wa dziko lonse, osati mwa ntchito za atsogoleri a zandale kapena a zachipembedzo a dzikoli, koma mwa Ufumu wa Mulungu. Ndi Ufumu umenewu, womwe ndi boma la Mulungu la kumwamba, womwe udzatha kugwirizanitsa anthu omvera ndi kupangitsa chifuno cha Mulungu kuchitika pa dziko lapansi.​—Yesaya 9:6; Mateyu 6:9, 10.