Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?

Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?

Kodi Ntchito Iyi Ingakhale Yabwino Kwambiri kwa Inu?

NGATI ndinu Mkristu wobatizidwa, mosakayikira kukonda Mulungu kumakupangitsani kuchita chifuniro chake. Ndipo kum’tumikira kuyenera kukhala ntchito yaikulu pamoyo wanu. Ngakhale Yesu Kristu, analamula otsatira ake onse kupanga ophunzira. (Mateyu 28:19, 20) Inde, mwina pakalipano mukugwira ntchito kuti muzipeza zofunika. Koma pokhala wotsatira Yesu ndiponso mmodzi wa Mboni za Yehova, ndinu mtumiki wachikristu yemwe ntchito yolalikira za Ufumu ili yofunika kwambiri pamoyo wanu.​—Mateyu 24:14.

Mwina mukuyandikira zaka 20 kapena mwapyolerapo pang’ono. Muyenera kuti mwalingalira kale mokwanira za ntchito imene mudzagwire pamoyo wanu. Posankha ntchito zomwe mungathe kugwira, mungakonde kusankha imene ingakukhutiritseni.

Tamverani zimene Jørgen wa ku Denmark ananena za ntchito imene anasankha. Anaifotokoza kuti ndi “njira yabwino kwambiri ya moyo yothandiza kuika maganizo onse pantchito yofunika koposa.” Ku Greece, mayi wina wazaka 31 wotchedwa Eva, anati: “Nthaŵi zonse ndimaona kuti moyo wanga ndi watanthauzo, wokhutiritsa, ndi wosangalatsa pouyerekeza ndi wa anzanga.” Kodi ndi ntchito iti yokhutiritsa chonchi? Kodi mungatani kuti muipeze?

Kodi Mulungu Amatsogolera?

Kusankha mtundu wa ntchito kungakhaledi kovuta. Moti ena angalakalake kuti Mulungu awasonyeze chimene akufuna kuti iwo achite pamoyo wawo.

Pamene Mose anali ku Midyani, Yehova anamuuza kuti apite ku Igupto kukatulutsa Aisrayeli ku ukapolo. (Eksodo 3:1-10) Mngelo wa Mulungu anaonekera kwa Gideoni, amene anasankhidwa kuti apulumutse Aisrayeli m’dzanja la Amidyani. (Oweruza 6:11-14) Davide anali kuweta nkhosa pamene Mulungu anauza Samueli kuti akamudzoze kukhala mfumu yotsatira ya Aisrayeli. (1 Samueli 16:1-13) Masiku ano, sitisonyezedwa zochita m’njira imeneyo. M’malo mwake, tifunika kuganizira bwino ndi kusankha mmene tingagwiritsire ntchito mphamvu zomwe Mulungu anatipatsa.

Yehova watsegulira Akristu achinyamata ‘khomo lalikulu la ntchito’ masiku ano. (1 Akorinto 16:9) Motani? M’zaka khumi zapitazo, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chawonjezeka kuchokera pa 2,125,000 mpaka kupitirira 6,000,000 padziko lonse. Kodi ndani amathandiza kugawira mamiliyoni a mabaibulo, mabuku, mabulosha, magazini, ndi mathirakiti zomwe ndi zofunika pamoyo wauzimu ndi pantchito ya padziko lonse yolalikira uthenga wabwino? A m’banja la Beteli padziko lonse ndiwo ali ndi mwayi wa ntchito yokhutiritsa imeneyi.

Moyo Wokhutiritsa

Mawu akuti Beteli amatanthauza ‘Nyumba ya Mulungu.’ Nyumba za Beteli, ndi komwe Akristu odzipereka amene akugwira ntchito ku likulu ndi ku maofesi ena a Watch Tower Society amakhala. (Genesis 28:19) Mabanja a Beteli a masiku ano tingawafanizire ndi ‘mabanja omangidwa ndi nzeru’ omwe maziko ake ndi kukonda Yehova.​—Miyambo 24:3.

Kodi moyo wonga wapabanja ndi wotani pa Beteli? Munthu wina wazaka 25 wa m’banja la Beteli ku Estonia anati: “Ndimasangalala kudzimva kuti ndili pakati pa mabwenzi a Yehova nthaŵi zonse. Ndicho cha mtengo wapatali kwambiri kwa ine pa Beteli.”​—Salmo 15:1, 2.

Tsopano padziko lonse pali anthu pafupifupi 19,500, amene akusangalala ndi mwayi wotumikira pa Beteli. (Salmo 110:3) Ku United States, anthu 46 mwa anthu 100 alionse a pa Beteli, ndi a zaka 19 mpaka 29. Monga Yesaya, nawonso anena kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Ngakhale kuti Yesaya anali atadzipatulira kale kwa Yehova, anadziperekanso kutumikira mowonjezereka. N’zoonekeratu kuti anasiya zofuna zake zina. Amene akutumikira pa Beteli, anasiya nyumba ndi malo omwe anawazoloŵera, ngakhalenso amayi, abambo, abale awo ndi alongo awo ndi anzawo. Iwo anatero mwa kufuna kwawo “chifukwa cha Uthenga Wabwino.”​—Marko 10:29, 30.

Koma kodi ndi madalitso auzimu ati amene amapezeka ku Beteli? Mtsikana wina wa m’banja la Beteli ku Russia anati: “Mwa kukhala wodzipereka, timaphunzira zambiri zomwe zidzatithandiza kukhala ndi moyo m’dziko lapansi latsopano. Kwa ine, madalitso a Yehova ndi ochuluka kwambiri kuposa kudzipereka kwanga.”​—Malaki 3:10.

Moyo pa Beteli

Kodi moyo pa Beteli ndi wotani? A m’banja la Beteli amavomereza kuti n’ngwabwino ndi wokhutiritsa, komanso wosangalatsa. Jens, wazaka 43, akusangalala ndi utumiki wa pa Beteli. Chifukwa chiyani? Iye akuti: “Chifukwa cha kudzimva kuti tikuchita mbali yaikulu m’ntchito yofunika kwambiri. Ndimaona kukula ndi kufunika kwa ntchito ya Yehova.”

Kuyambira Lolemba mpaka Loŵeruka, banja la Beteli limakhala ndi kulambira kwa m’maŵa. Uku n’kukambirana Baibulo komwe mkulu wachidziŵitso amachititsa. Lolemba lililonse madzulo, amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ndipo nthaŵi zina pambuyo pake pamakambidwa nkhani ya m’Malemba yoyenerera banja la Beteli.

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akangofika ku Beteli? Kuti atsopano azoloŵere moyo wa pa Beteli, abale achidziŵitso a m’banjali amakamba nkhani zokhudza mbali zosiyanasiyana za utumiki wa pa Beteli. Pamilungu ingapo m’chaka choyamba, membala watsopano amakhala pa sukulu yabwino kwambiri yom’thandiza kudziŵa Malemba mozamirapo. Mamembala atsopano amasangalalanso ndi pulogalamu yapadera ya kuŵerenga Baibulo. M’chaka choyamba cha utumiki pa Beteli, mamembala atsopano amaŵerenga Baibulo lonse.

Kodi chotsatira cha maphunziro onseŵa n’chiyani? Joshua, wazaka 33 ndipo ali m’banja la Beteli ku Hong Kong, anayankha kuti: “Beteli yandithandiza kuyamikira Yehova mowonjezereka. Ndingayanjane ndi abale ambiri amene atumikira Yehova nthaŵi yaitali. Ndimasangalala kwambiri ndi zochitika zauzimu monga kulambira kwa m’maŵa ndi Phunziro la banja la Nsanja ya Olonda. Komanso ndimakonda kuchita zinthu mwadongosolo ndi moyo wosalira zambiri. Izi zimandichepetsera nkhaŵa pa zinthu zosafunika kwenikweni. Nthaŵi zonse ndapindula mwa kuphunzira kuchita zinthu mwachikristu.”

Anthu a banja la Beteli amagwiritsa ntchito nthaŵi yochuluka ndi khama pantchito yomwe anadzipereka kugwira. Choncho, amagwiritsa ntchito mphamvu ndi nzeru zawo kwenikweni pantchito yomwe apatsidwa pa Beteli. Pali ntchito zambiri zosiyanasiyana. Ena amagwira ntchito yosindikiza kapena kupanga mabuku omwe amatumizidwa ku mipingo yambirimbiri. Ena amagwira ntchito m’khichini, m’chipinda chodyera, kapena kochapira zovala. Komanso pali ntchito zina monga kuyeretsa, kulima, kumanga, ndi zina zambiri. Ena ali ndi udindo wosamalira zipangizo za ntchito m’madipatimenti ameneŵa. Enanso amagwira ntchito za chipatala kapena za muofesi. Ntchito zonse za pa Beteli n’zosangalatsa ndiponso zopindulitsa kwambiri. Ntchito ya pa Beteli ndi yokhutiritsadi chifukwa imapititsa Ufumu patsogolo ndipo anthu amaigwira chifukwa cha kukonda Mulungu.

A m’banja la Beteli amagaŵidwa ku mipingo komwe amaona phindu la ntchito yawo. Amasangalala ndi misonkhano ya mpingo ndiponso kugwira nawo ntchito yolalikira. Chifukwa cha zimenezi, a m’banja la Beteli, apanga ubale wamphamvu ndi abale ndi alongo awo m’mipingo.​—Marko 10:29, 30.

Rita, yemwe ali m’banja la Beteli ku Britain anati: “Mpingo umandisangalatsa kwambiri! Pamisonkhano ndi m’ntchito yolalikira, chikhulupiriro changa chimalimba kwambiri ndikaona abale okondedwa, alongo, ana, ndi achikulire! Zivute zitani amapezekapo. Zimenezi zimandithandiza kulimbikira utumiki wanga pa Beteli.”

Moyo wa pa Beteli si kuti umangokhala ntchito, misonkhano, kukalalikira, ndi kuphunzira ayi. Pamakhalanso nthaŵi za kucheza. Nthaŵi ndi nthaŵi, pamakhala chochitika chotchedwa “Macheza a Banja,” pamene amakhala ndi mwayi wosangalala ndi maluso a ena ndi kumva zinthu zolimbikitsa za m’moyo wa ena amene akutumikira pa Beteli. Amayenderananso wina ndi mnzake ndi kukhala ndi macheza olimbikitsana. Zipangizo zina za maseŵera zingakhalepo, kuphatikizapo malaibulale oŵerengerako ndi kufufuza. Komanso osaiwala kucheza kosangalatsa panthaŵi ya chakudya.

Tom, wa m’banja la Beteli ku Estonia anati: “Pafupi ndi Beteli, pali nyanja ndipo chapafupinso pali nkhalango yokongola komwe ine ndi mkazi wanga timakonda kukayendako. Nthaŵi zina ine ndi anzanga a kumpingo ndi a pa Beteli, timachita maseŵero a gofu, hoke, ndi tenesi. Ndipo nyengo ikakhala yabwino, timakwera njinga.”

Kodi Mungatani Kuti Mukatumikire ku Beteli?

Inde, ku Beteli n’kumene Akristu okhwima amatumikira Yehova mu utumiki wopatulika m’malo mwa okhulupirira anzawo padziko lonse lapansi. Amene amakhala m’banja la Beteli, ayenera kukwaniritsa ziyeneretso zina. Kodi mungatani kuti muyenerere utumiki wa pa Beteli?

Monga Timoteo, amene anatumikira ndi mtumwi Paulo, omwe amavomerezedwa mu utumiki wa pa Beteli, ayenera kukhala ndi mbiri yabwino mu mpingo. (1 Timoteo 1:1) ‘Abale a ku Lustra ndi ku Ikoniyo, anam’chitira umboni wabwino Timoteo.’ (Machitidwe 16:2) Ngakhale anali wamng’ono, Timoteo anadziŵa Malemba ndipo anali wolimba m’choonadi. (2 Timoteo 3:14, 15) Choncho amene amavomerezedwa mu utumiki wa pa Beteli, amawayembekezera kukhala odziŵa Baibulo.

A m’banja la Beteli amafunika kukhala odzipereka. Nayenso Timoteo anali wodzipereka ndi wofunitsitsa kugwira ntchito za Ufumu choyamba kuposa zofuna zake. N’chifukwa chake Paulo anati: “Pakuti ndilibe wina wa mtima womwewo, amene adzasamalira za kwa inu ndi mtima woona. Pakuti onseŵa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu. Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.”​—Afilipi 2:20-22.

Utumiki wa pa Beteli umafunikira amuna ndi akazi auzimu. Zochitika m’banja la Beteli, zimapangitsa anthu a m’banjalo kukula mu uzimu kupyolera mwa kuphunzira Baibulo, kusonkhana ndi Akristu anzathu ndi kulalikira nthaŵi zonse, ndiponso kuyanjana ndi Akristu okhwima. Motero, onse amene ali pa Beteli akuthandizidwa kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Muyende mwa [Yesu Kristu], ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.”​—Akolose 2:6, 7.

Chifukwa cha mtundu wa ntchito ya pa Beteli, amene amavomerezedwa mu utumiki wapamwamba umenewu ayenera kukhala amphamvu ndi a thanzi labwino. Ngati mukuona kuti ndinu woyenera malinga ndi zimene zatchulidwazi, muli ndi zaka 19 kapena kuposerapo, ndipo chaka chapita kuchokera pamene munabatizidwa, tikukulimbikitsani kuti muganizire za utumiki wa pa Beteli.

Tonse Tingathandize

Monga Akristu, mosakayikira tonse timafuna kutsogoza Ufumu choyamba m’moyo wathu ndi kutumikira Yehova ndi mtima wonse. (Mateyu 6:33; Akolose 3:23) Tingalimbikitsenso amene akutumikira ku Beteli kupitiriza utumiki wopatulika kumeneko. Ndipo makamaka abale achinyamata omwe akuyenerera kutumikira pa Beteli ayenera kulimbikitsidwa kuti akalamire mwayi wapamwamba umenewu.

Utumiki wa pa Beteli ndi moyo wokhutiritsa mwauzimu ndipo ingakhaledi ntchito yabwino kwambiri kwa inu. Ndi mmene yakhalira kwa Nick yemwe anayamba kutumikira pa Beteli ali ndi zaka 20. Wakhala akutumikira pa Beteli kwa zaka 10 ndipo akunena kuti: “Ndimapemphera kwa Yehova kaŵirikaŵiri kum’thokoza chifukwa cha kukoma mtima kwake. N’chiyaninso chomwe ndingam’pemphe? Kuno tili ndi Akristu okhulupirika amene akuchita zonse zotheka potumikira Yehova.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 22]

KODI AKULU NDI MAKOLO ANGACHITENJI?

Makamaka akulu ndi oyang’anira oyendayenda ayenera kulimbikitsa achinyamata kufunsira utumiki wa pa Beteli. Posachedwapa, kufufuza pakati pa achinyamata a m’banja la Beteli kwasonyeza kuti 34 peresenti analimbikitsidwa kusankha utumiki wa pa Beteli ndi oyang’anira achikristu. Inde, mwina mpingo wawo ungadandaule chifukwa cha kuchoka kwa anthu othandiza ngati iwowo. Koma ndi bwino kukumbukira kuti ngakhale kuti Timoteo mosakayikira anali kusonyeza chitsanzo chabwino kwa achinyamata a ku Lustra ndi Ikoniyo, akulu a kumeneko sanamuletse kuti akatumikire ndi Paulo. Sanaganize kuti kulola Timoteo kuti apite ndi mtumwi Paulo kungakhale kuluza kwakukulu ku mpingo wawo.​—1 Timoteo 4:14.

Makamakanso makolo achikristu ndiwo ayenera kulimbikitsa ana awo pankhani imeneyi. Pakafukufukuyu, 40 peresenti ya omwe anafunsidwa anati kwenikweni makolo awo ndiwo anawalimbikitsa kuloŵa utumiki wa pa Beteli. Mlongo wina, yemwe wakhala akutumikira pa Beteli kwa zaka zingapo anati: “Moyo wa makolo anga pa utumiki wa Yehova ndiwo unandisonkhezera kwambiri kuyamba utumiki wa pa Beteli. Pokhala monga chitsanzo changa mu utumiki wa nthaŵi zonse, ndinadziŵa kuti uwu ndi moyo wabwino ndi wokhutiritsa kwambiri.”

[Bokosi patsamba 24]

AMAYAMIKIRA UTUMIKI WA PA BETELI

“Ndimanyadira utumiki wa pa Beteli. N’zokhutiritsa kudziŵa kuti ndatumikira Yehova tsiku lonse ndi kuti n’dzateronso maŵa, mkucha, mtondo, mpaka m’tsogolo. Zimenezi zimandipangitsa kukhala ndi chikumbumtima chabwino ndi maganizo abwino.”

“Beteli ndi malo kumene mungagwiritse ntchito nthaŵi yanu yonse ndi nyonga yanu kutumikira Yehova popanda zododometsa. Zimenezi zimapatsa chisangalalo cha mumtima. Komanso mumakhala ndi mwayi wodziŵa mbali zinanso za gulu la Yehova. Mumamva kuti muli oyandikira phata lenileni la gululi, zimene ndi chinthu chokondweretsa kwambiri.”

“Kubwera kuno ku Beteli ndi chochitika chabwino kwambiri pa moyo wanga. Kuno, maphunziro satha. Ndipo maphunziro a kuno si okweza ine, koma Yehova. Kuno ntchito yanga sidzapita pachabe.”

“Kugwiritsa ntchito luso langa pa Beteli kumandikhutiritsa ndipo ndimasangalala kuti ndikutumikira Yehova ndi abale anga.”

“Ntchito yanga yakale sinali yokhutiritsa ndi yokondweretsa chonchi. Kwa zaka zambiri ndakhala ndikulakalaka kugwira ntchito ndi abale ndi alongo ndiponso kuwatumikira. N’chifukwa chake ndinabwera ku Beteli. Ndimakhutira Kwambiri kudziŵa kuti khama langa lidzapindulitsa ena mwauzimu ndi kutamanda Yehova.”