Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi

Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi

Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu

Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi

“MWANANGA, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miyambo 27:11) Pempho labwinoli likusonyeza kuti zolengedwa zanzeru za Mulungu zitha kukondweretsa mtima wa Yehova mwakukhala zokhulupirika kwa iye. (Zefaniya 3:17) Komabe, Satana, wotonzayo, ali wotsimikiza kuswa umphumphu wa amene amatumikira Yehova.​—Yobu 1:10, 11.

Satana wakwiyira kwambiri anthu a Yehova makamaka kuyambira kumayambiriro a zaka za m’ma 1900, pamene anaponyedwa padziko lapansi kum’chotsa kumwamba. (Chivumbulutso 12:10, 12) Komabe, Akristu oona aima “amphumphu ndi otsimikiza kotheratu” ndipo akhalabe okhulupirika kwa Mulungu. (Akolose 4:12) Tiyeni mwachidule tione chitsanzo chimodzi cha kukhulupirika koteroko. Chitsanzochi n’cha Mboni za Yehova ku Germany nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse isanachitike ndiponso nkhondoyo ili m’kati.

Kugwira Ntchito Mwachangu Kunadzetsa Ziyeso za Kukhulupirika

M’ma 1920 ndiponso kumayambiriro a m’ma 1930, Bibelforscher, dzina lomwe Mboni za Yehova panthaŵiyo zinkadziŵika nalo ku Germany zinagaŵira mabuku ambiri ofotokoza Baibulo. Pakati pa 1919 ndi 1933, anagaŵira banja lililonse ku Germany mabuku, timabuku, kapena magazini pafupifupi asanu ndi atatu.

Panthaŵiyo, dziko la Germany ndilo linali ndi chiŵerengero chachikulu cha otsatira a Kristu odzozedwa. Moti mwa anthu 83,941 amene anadya Chakudya Chamadzulo cha Ambuye padziko lonse mu 1933, pafupifupi 30 mwa anthu 100 alionse ankakhala ku Germany. Pasanapite nthaŵi, kukhulupirika kwa Mboni za ku Germany zimenezi kunayesedwa kwambiri. (Chivumbulutso 12:17; 14:12) Anawachotsa ntchito, anawazunza panyumba, anawachotsa sukulu, ndipo kenako zinthu zinafika poipa kwambiri mpaka anayamba kuwamenya, kuwamanga ndi kuwatsekera m’ndende. (Chithunzi choyamba) Zotsatira zake zinali zakuti, m’zaka zoyandikira ku nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, 5 mpaka 10 peresenti ya anthu omwe anaikidwa m’misasa yachibalo anali Mboni za Yehova.

Chifukwa Chimene Anazi Ankazunzira Mboni

Koma kodi n’chifukwa chiyani ulamuliro wa Nazi unkadana kwambiri ndi Mboni za Yehova? M’buku lake lotchedwa Hitler​—1889-1936: Hubris, pulofesa wambiri yakale wotchedwa lan Kershaw ananena kuti Mboni zinazunzidwa chifukwa chokana “zofuna zonse za boma la Nazi.”

Buku lotchedwa Betrayal​—German Churches and the Holocaust, lolembedwa ndi pulofesa wambiri yakale Robert P. Ericksen ndiponso pulofesa wamaphunziro achiyuda Susannah Heschel, linanena kuti Mboni “zinkakana kuchita nawo chiwawa kapena nkhondo. . . . Mboni zinkakhulupirira kuti sibwino kuloŵerera m’ndale. Izi zinatanthauza kuti iwo sakadavotera kapena kuchitira sawatcha Hitler.” Bukulo linawonjezera kuti, zimenezi zinakwiyitsa Anazi ndipo analola kuti Mboni zizunzidwe chifukwa “achipani cha National Socialist sakanalolera zimenezi.”

Zionetsero Zapadziko Lonse Komanso Nkhanza Zadzaoneni

Pa February 9, 1934, Joseph F. Rutherford yemwe ankatsogolera ntchito panthaŵiyo, anatuma mthenga wapadera kukapereka kalata yodandaula kwa Hitler chifukwa cha nkhanza za Anazi. (Chithunzi chachiŵiri) Pa October 7, 1934, pambuyo pa kalata ya Rutherford, Mboni za Yehova m’mayiko 50 kuphatikizapo dziko la Germany zinatumiza kwa Hitler makalata komanso matelegalamu odandaula pafupifupi 20,000.

Anazi atamva izi, anawonjezera kwambiri nkhanza zawo moti pa April 1, 1935, Mboni zinaletsedwa m’dziko lonselo. Ndipo pa August 28, 1936, apolisi a Gestapo anayamba kuchitira Mboni nkhanza zadzaoneni. Komabe, Mboni “zinapitiriza kugaŵira mabuku ndiponso kukhalabe zokhulupirika,” linatero buku lotchedwa Betrayal​—German Churches and the Holocaust.

Mwachitsanzo, pa December 12, 1936, Mboni pafupifupi 3,500 zinagaŵira pamaso pa apolisi a Gestapo makope miyandamiyanda onena za maganizo awo pa nkhanza zomwe ankawachitira. Ponenapo za ndawala imeneyi, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Kunalitu kugonja kwakukulu komanso nkhonya yapamphuno kwa adaniwo moti antchito okhulupirikawo anasangalala kwambiri.”​—Aroma 9:17.

Sanagonje Chifukwa Chozunzidwa!

Anazi anapitirizabe kufunafuna Mboni za Yehova. Pomwe chimafika chaka cha 1939, n’kuti anthu masauzande asanu ndi limodzi atawaika m’ndende, ndipo ena miyandamiyanda atawatumiza ku misasa yachibalo. (Chithunzi chachitatu) Kodi zinthu zinali motani chakumapeto kwa nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse? Mboni pafupifupi 2,000 zomwe zinali m’ndende zinali zitafa ndipo mwa anthu ameneŵa oposa 250 anachita kuwanyonga. Komabe, Pulofesa Ericksen ndiponso Pulofesa Heschel analemba kuti, “Mbali yaikulu, Mboni za Yehova zinakhalabe zokhulupirika pamazunzowo.” Kotero kuti ulamuliro wa Hitler utatha, Mboni miyandamiyanda zinatuluka ku misasa zitapambana.​—Chithunzi chachinayi; Machitidwe 5:38, 39; Aroma 8:35-37.

Kodi chinapatsa mphamvu anthu a Yehova kuti apirire chizunzocho n’chiyani? Adolphe Arnold yemwe anapulumuka ku msasa wachibalo anafotokoza kuti: “Ngakhale utafooka motani, Yehova amaona, amadziŵa mavuto ako, ndiponso amakupatsa nyonga zofunika kuti ugonjetse vutolo ndi kukhalabe wokhulupirika. Iye salephera konse.”

Mawu a mneneri Zefaniya anagwira ntchito kwabasi kwa Akristu okhulupirikawo. Iye ananena kuti: “Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe.” (Zefaniya 3:17) Onse olambira Mulungu woona lerolino atsanziretu chikhulupiriro cha Mboni zokhulupirika zomwe zinasungabe umphumphu pachizunzo cha Nazi ndipo akatero iwonso adzakondweretsa mtima wa Yehova.​—Afilipi 1:12-14.

[Mawu a Chithunzi patsamba 8]

Państwowe Muzeum Oświȩcim-Brzezinka, mwa chilolezo cha USHMM Photo Archives