Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumvera—Kodi Ndi Phunziro Lofunika Paubwana?

Kumvera—Kodi Ndi Phunziro Lofunika Paubwana?

Kumvera​—Kodi Ndi Phunziro Lofunika Paubwana?

“MAKOLO Amafuna Anthu Odzidalira, Osati Makanda Omangomvera.” Unatero mutu wa nyuzipepala ina. Nkhani imeneyi inachokera pa zotsatira za kufufuza kumene kunachitika ku New Zealand, komwe kunasonyeza kuti “anthu 22 [okha] pa anthu 100 alionse omwe anafunsidwapo ndiwo ankalingalira kuti ana ayenera kuphunzitsidwa kumvera.” Kufufuzako kunapezanso kuti makolo lerolino amakhulupirira kuti n’kofunika kwambiri kuphunzitsa ana nkhani monga za makhalidwe abwino, kudziimira pawekha, ndiponso kudalirika.

M’nyengo ino ya kudzidalira ndiponso dyera, m’posadabwitsa kuti anthu ambiri amakayikira za kukhala womvera ndiponso kuphunzitsa ana kukhala omvera. Komano kodi mfundo yoti ana akhale omvera iyenera kungolingaliridwa ngati yamakedzana ndi yachikale? Kapena kodi kumvera ndi limodzi mwa maphunziro ofunika omwe ana ayenera kulandira ndi kupindula nawo? Koposa zonse, kodi Yehova Mulungu, Woyambitsa makonzedwe a banja, amaona bwanji za kumvera makolo, ndipo ena mwa mapindu a kumvera makolo ndi ati?​—Machitidwe 17:28; Aefeso 3:14, 15.

“Ichi N’chabwino”

Ku mpingo wa Akristu a m’zaka za zana loyamba wa ku Efeso, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino.” (Aefeso 6:1) Chotero, chifukwa chachikulu chomvera makolo n’chakuti kumvera n’kogwirizana ndi miyezo ya Mulungu ya chinthu chabwino. Monga momwe Paulo analembera, “ichi n’chabwino.”

Mogwirizana ndi zimenezi, timadziŵa kuti Mawu a Mulungu amafotokoza malangizo achikondi a makolo kukhala okongola kwambiri, “korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako,” ndiponso kukhala chinthu chinachake ‘chokondweretsa Ambuye.’ (Miyambo 1:8, 9; Akolose 3:20) Mosiyana kwambiri ndi zimenezi, kusamvera makolo kumadzetsa udani ndi Mulungu.​—Aroma 1:30, 32.

“Kuti Kukhale Bwino ndi Iŵe”

Paulo anatchula ubwino wina wa kumvera pamene analemba kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), kuti kukhale bwino ndi iŵe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:2, 3; Eksodo 20:12) Kodi ndi motani mmene kumvera makolo kungabweretsere munthu zinthu zokoma?

Choyamba, kodi si zoona kuti makolo anakhalapo kale ndiponso amadziŵa zinthu zambiri? Ngakhale kuti sangadziŵe zambiri pankhani za kompyuta kapena maphunziro ena a kusukulu, iwo amadziŵa zambiri pankhani za moyo ndiponso mmene tingathetsere mavuto m’moyo. Pamene, achinyamata salingalira bwinobwino chifukwa nzeru zoterozo zimadza mwa kukhala wokhwima m’maganizo. Motero, iwo amakhala opupuluma posankha zinthu zoti achite, nthaŵi zambiri anzawo amawasonkhezera kuti achite zinthu zoopsa, ndipo zimangowavulaza. Moyenerera, Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” Kodi mankhwala ake n’chiyani? “Nthyole yom’langira idzauingitsira kutali.”​—Miyambo 22:15.

Mapindu a kumvera sikuti amangothera pa unansi wa kholo ndi mwana. Kuti anthu agwire ntchito mopanda zopinga komanso mwaphindu, payenera kukhala mgwirizano, womwe umafuna kumvera. Mwachitsanzo, mu ukwati, kukhala wokonzeka kugonja ndiko kumabweretsa mtendere, mgwirizano, ndi chimwemwe, kusiyana ndi kukhala munthu wolamulira ndi wosaganizira za ufulu ndi zolingalira za ena. Pantchito, m’pofunika kuti wolembedwa ntchito akhale wogonjera pofuna kuti ntchito iliyonse iyende bwino. Pa za malamulo a boma, kumvera sikuti kumangom’pulumutsa munthu kuti asalandire chilango koma kumadzetsanso chitetezo.​—Aroma 13:1-7; Aefeso 5:21-25; 6:5-8.

Achinyamata omwe samvera olamulira kaŵirikaŵiri sagwirizana ndi ena. Mosiyana ndi zimenezi, phunziro la kumvera lolandiridwa paubwana lingakhale lopindulitsa kwa moyo wonse wa munthu. Ndi mwayi waukulu kwambiri kuphunzira kumvera paubwana!

Mphoto Yaikulu ya Kumvera

Kumvera sikuti kumangodzetsa unansi wachimwemwe pabanja ndiponso mapindu anthaŵi yaitali okha koma kumamanganso maziko a unansi wabwino kwambiri kuposa unansi uliwonse​—womwe ndi unansi wa munthu ndi Mlengi wake. Monga “Mlengi” yemwe ali ndi “chitsime cha moyo,” Yehova Mulungu ndi woyenerera kuti timumvere kotheratu.​—Mlaliki 12:1; Salmo 36:9.

Liwu lakuti “mvera” logwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana limapezeka nthaŵi zambiri m’Baibulo. Komanso, pali malemba zikwizikwi onena za malamulo, ndi ziweruzo za Mulungu zomwe zimafuna kugonjera. Sitidabwa kuti Mulungu amaona kumvera monga chiyeneretso chopezera chiyanjo chake. Inde, kumvera ndi kofunika kwambiri kuti tikhale pa unansi ndi Yehova. (1 Samueli 15:22) N’zomvetsa chisoni kuti anthu mwachibadwa amakhala osamvera. “Ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake,” limatero Baibulo. (Genesis 8:21) Chotero, kumvera kuyenera kuphunziridwa osati paubwana pokha koma kwa moyo wonse. Kutero kumadzetsa mphoto yaikulu kwambiri.

Kumbukirani kuti, malinga ndi momwe mtumwi Paulo analembera, lamulo la kumvera makolo lili ndi lonjezo la mbali ziŵiri, lomwe ndi ‘kuti kukhale bwino ndi iŵe ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaitali padziko.’ Chitsimikizo cha lonjezo limeneli timachipeza pa Miyambo 3:1, 2: “Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.” Mphoto yaikulu ya anthu omvera ndiyo kukhala pa unansi ndi Yehova lerolino ndiponso moyo wosatha m’dziko latsopano la mtendere.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

[Zithunzi pamasamba 30, 31]

Kumvera kumadzetsa unansi wachimwemwe m’banja, pantchito, ndiponso ndi Yehova