Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutha Kupeza Madalitso a Ufumu

Mutha Kupeza Madalitso a Ufumu

Mutha Kupeza Madalitso a Ufumu

MTUMWI wachikristu Paulo ankadziŵa zinenero zikuluzikulu zingapo za m’nthaŵi yake. Anali atalandira maphunziro amene masiku ano tingati ndi a ku yunivesite. Anali ndi ufulu wonse wopatsidwa kwa nzika za Roma. (Machitidwe 21:37-40; 22:3, 28) Pokhala ndi zinthu ngati zimenezi akanatha kukhala wolemera ndi wotchuka. Koma iye anati: “Zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa chitayiko chifukwa cha Kristu . . . ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.” (Afilipi 3:7, 8) Kodi Paulo ananeneranji zimenezo?

Poyamba Paulo ankadziŵika ndi dzina lakuti Saulo wa ku Tariso komanso monga wozunza “otsata Njirayo.” Koma anadzakhala wokhulupirira atalandira masomphenya a Yesu woukitsidwayo wokhala mu ulemerero. (Machitidwe 9:1-19) Kwa Paulo, zimene zinam’chitikirazi paulendo wake wa ku Damasiko zinam’tsimikizira kotheratu kuti Yesu analidi Mesiya wolonjezedwayo, kapena kuti Kristu, wolamulira wam’tsogolo wa Ufumu wolonjezedwawo. Zinapangitsanso Paulo kusinthiratu moyo wake, monga momwe tikuonera m’mawu ake amphamvu m’ndime yoyambayo. Kunena kwina, pokhala woona mtima, Paulo analapa.​—Agalatiya 1:13-16.

M’Baibulo, mneni wakuti “lapa” kaŵirikaŵiri anatembenuzidwa kuchokera ku mawu achigiriki amene kwenikweni amatanthauza “kudziŵa pambuyo pake,” zimene zili zosiyana ndi “kudziŵiratu.” Chotero, kulapa kumatanthauza kusintha malingaliro ako, mtima, kapena cholinga, kusiyiratu njira zako zakale ndi kuziona kukhala zosayenera. (Machitidwe 3:19; Chivumbulutso 2:5) Paulo sanaone zimene zinam’chitikira panjira yopita ku Damasiko monga chochitika wamba chogwira mtima kapenanso ngati chokumana nacho wamba chauzimu. Kwa iye zinam’thandiza kuzindikira kuti njira yake yoyambayo, yosadziŵa Kristu, inali yopanda pake. Anazindikiranso kuti ngati akufuna kupindula ndi chidziŵitso chake chatsopanocho chonena za Kristu, ayenera kuchitapo kanthu kuti awongolere moyo wake.​—Aroma 2:4; Aefeso 4:24.

Kusintha Kumene Kunadzetsa Madalitso

Poyamba, zimene Paulo anali kudziŵa za Mulungu anaziphunzira kwakukulukulu kwa Afarisi, pokhala anali mmodzi wa iwo. Zikhulupiriro zawo zinali mafilosofi ndi miyambo ya anthu zosakanikirana kwambiri. Chifukwa chodana ndi zipembedzo zina, Paulo anagwiritsa ntchito changu chake ndi nyonga zake molakwa. Ngakhale ankaganiza kuti akutumikira Mulungu, kwenikweni anali kulimbana naye.​—Afilipi 3:5, 6.

Atalandira chidziŵitso cholondola cha Kristu ndi ntchito yake pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu, Paulo anaona kuti anayenera kusankhapo chimodzi: Kodi akhalebe Mfarisi ndi kukhalabe pamalo aulemu apamwamba, kapena kodi asinthe moyo wake ndi kuyamba kuchita zilizonse zofunika kuti akhale wovomerezeka kwa Mulungu? Paulo anasankha bwino, popeza anati: “Uthenga wabwino sundichititsa manyazi; pakuti uli mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira kuyambira Myuda, ndiponso Mhelene.” (Aroma 1:16) Paulo anakhala mlaliki wachangu wa uthenga wabwino wonena za Kristu ndi Ufumu.

Patapita zaka zambiri, Paulo anauza Akristu anzake kuti: “Ine sindiŵerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira; koma chinthu chimodzi ndichichita; poiŵaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 3:13, 14) Paulo anapindula ndi uthenga wabwino chifukwa chakuti anakwanitsa kusiya zimene zinali kum’patula kwa Mulungu ndipo ndi mtima wonse analunjika zolinga zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

Kodi Inuyo Mukanatani?

Mwina uthenga wabwino wa Ufumu mwaumva posachedwapa. Kodi nkhani yonena za kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wangwiro ikukusangalatsani? Iyeneradi kutero, chifukwa tonsefe mwachibadwa timafuna kukhala ndi moyo wamtendere ndi wosungika. Baibulo limanena kuti Mulungu “waika zamuyaya” m’mitima yathu. (Mlaliki 3:11) Chotero n’chibadwa chathu kulakalaka nthaŵi pamene anthu adzakhala ndi moyo wosatha mu mtendere komanso mwachimwemwe. Ndipo ndicho chiyembekezo chimene uthenga wabwino wa Ufumu ukupereka.

Komano kuti inuyo mukhale n’chiyembekezo chimenechi, muyenera kufufuza kuti mudziŵe zimene uthenga wabwino ukunena. Mtumwi Paulo anatilangiza kuti: “Mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Chotero, mofanana ndi Paulo, mutapeza chidziŵitso chimenecho ndi kuchimvetsa, musankhepo chimodzi.

Komabe, zingatheke kuti muli kale ndi zikhulupiriro zina za tsogolo lanu. Kumbukirani kuti Saulo asanakhale mtumwi Paulo anali ndi zikhulupiriro zake pa za Mulungu. Koma m’malo moyembekeza Mulungu kutitsegula maso mwa chozizwitsa, bwanji osaipenda mosamala nkhaniyi? Dzifunseni kuti: ‘Kodi kunena zoona ndikudziŵa kuti chifuniro cha Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi n’chiyani? Kodi ndingapereke umboni wotani pochirikiza zimene ndimakhulupirira? Umboni wangawo titati tiufufuze mogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu, Baibulo, kodi ungapezeke kukhaladi woona?’ Palibe vuto ndi kufufuza zikhulupiriro zanu zachipembedzo mwa njira imeneyi. Ndipotu muyeneradi kuchita zimenezi chifukwa chakuti Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.” (1 Atesalonika 5:21) Pajatu kuvomerezedwa ndi Mulungu ndicho chinthu chofunika kwambiri.​—Yohane 17:3; 1 Timoteo 2:3, 4.

Atsogoleri achipembedzo angatilonjeze tsogolo losatha. Koma lonjezo limenelo silidzatithandiza kupeza madalitso a Ufumu wa Mulungu, pokhapokha ngati n’lozikidwa pa zimene Baibulo limaphunzitsa. Mu Ulaliki wake wotchukawo wa pa Phiri, Yesu anachenjeza mwamphamvu kuti: “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”​—Mateyu 7:21.

Taonani mmene Yesu akugogomezera kuchita chifuniro cha Atate wake monga muyezo wolandirira madalitso a Ufumu wa Mulungu. M’mawu ena, zinthu zooneka ngati zaumulungu zingakhale zosavomerezeka kwa Mulungu. Inde, Yesu anatinso: “Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafuulira iwo, Sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Chotero, n’zoonekeratu kuti chinthu chofunika kwambiri ndicho kuonetsetsa kuti tikumvetsa bwino lomwe zimene uthenga wabwino wa Ufumu ukunena kenako n’kuchita zomwezo.​—Mateyu 7:24, 25.

Thandizo Lilipo

Kwa zaka zoposa 100, Mboni za Yehova zakhala zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Mwa kufalitsa mabuku ndiponso mwa mawu a pakamwa, akuthandiza anthu padziko lonse lapansi kupeza chidziŵitso cholondola chofotokoza Ufumuwo, madalitso amene udzadzetsa, ndi zimene munthu ayenera kuchita kuti apeze madalitso amenewo.

Tikukulimbikitsani kulabadira uthenga umene Mboni za Yehova zikulalikira. Mwa kulandira uthenga wabwino ndi kuchita zimene ukunena, mungalandire madalitso aakulu kwabasi osati nthaŵi ino yokha komanso m’tsogolo pamene Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi.​—1 Timoteo 4:8.

Chitanipo kanthu tsopano lino, chifukwa chakuti madalitso a Ufumu wa Mulungu ali pafupi!

[Zithunzi patsamba 7]

Mwa kufalitsa mabuku ndiponso mwa mawu apakamwa, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu