Mwambo Womwe Simuyenera Kuphonya
Mwambo Womwe Simuyenera Kuphonya
“Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro” zimachokera kwa Mulungu, Atate wathu wakumwamba.—Yakobo 1:17.
MPHATSO yaikulu kwambiri yomwe wapereka kwa anthu ochimwa ndiyo makonzedwe akuti anthuwo apulumutsidwe mwa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. Imfa ya Yesu, Momboli wathu, inapangitsa moyo wosatha padziko lapansi kukhala wotheka. Pa Luka 22:19, timalamulidwa kukumbukira imfa yake.
Mboni za Yehova zikukupemphani mwachikondi kuti mukakhale nazo pamodzi posunga lamulo la Yesu limeneli. Mwambo wapachaka umenewu udzachitika dzuŵa litaloŵa padeti logwirizana ndi Nisani 14 pa kalendala yoyendera mwezi ya Baibulo, lomwe ndi Lamlungu, April 8, 2001. Sungani deti limeneli kuti musadzaiŵale. Mboni za Yehova za m’dera lanu zingakuuzeni malo ake enieni ndi nthaŵi.