Ganizirani Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
Ganizirani Ntchito Zodabwitsa za Mulungu
“Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu.”—SALMO 40:5.
1, 2. Kodi tili ndi umboni wotani wa ntchito zodabwitsa za Mulungu, nanga kodi zimenezi ziyenera kutisonkhezera kuchitanji?
PAMENE mukuŵerenga Baibulo, mungaone mosavuta kuti Mulungu anali kuchitira anthu ake akale, Israyeli, zinthu zodabwitsa. (Yoswa 3:5; Salmo 106:7, 21, 22) Komabe, ngakhale kuti panopa Yehova sakuloŵerera m’zochita za anthu monga momwe ankachitira mu Israyeli, tikayang’anayang’ana timaona umboni wochuluka wa ntchito zake zodabwitsa. Choncho tili ndi chifukwa chabwino chonenera limodzi ndi wamasalmo kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24; 148:1-5.
2 Ambiri lerolino amanyalanyaza kapena kukana umboni woonekeratu umenewu wa ntchito za Mlengi. (Aroma 1:20) Komabe, n’kopindulitsa ndi koyenera kuti ife tiwasonyeze ndi kuwatsimikizira za malo athu ndi udindo umene tili nawo kwa Mlengi wathu. Tingapeze thandizo labwino kwambiri pambali imeneyi m’buku la Yobu chaputala 38 mpaka . Pamenepo Yehova anauza Yobu mbali zina za ntchito Zake zodabwitsa. Tiyeni tipende zina mwa zinthu zochititsa chidwi zimene Mulungu anatchula. 41
Ntchito Zamphamvu Komanso Zodabwitsa
3. Kodi ndi mafunso okhudza zinthu ziti amene Mulungu anafunsa pa Yobu 38:22, 23, 25-29?
3 Panthaŵi inayake, Mulungu anam’funsa Yobu kuti: “Kodi unalowa m’zosungiramo chipale chofeŵa? Kapena unapenya zosungiramo matalala, amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo?” Chipale chofeŵa ndi matalala sizachilendo m’madera ambiri padziko lapansi. Mulungu anapitiriza kuti: “Ndani anachikumbira mchera chimvula, kapena njira ya bingu la mphezi, kuvumbitsa mvula pa dziko lopanda anthu, ku chipululu kosakhala munthu, kukhutitsa thengo la kunkhwangwala, ndi kuphukitsa msipu? Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame? Chipale chinatuluka m’mimba ya yani? Ndi chisanu chochokera m’mwamba anachibala ndani?”—Yobu 38:22, 23, 25-29.
4-6. Kodi zimene anthu akudziŵa zokhudza chipale chofeŵa n’zochepa mulingaliro lotani?
4 Anthu ena m’mayiko otukuka, amene amakonda zoyendayenda angaone chipale chofeŵa ngati chowalepheretsa kuchita zinthu. Komabe, ena ambiri amaona kuti chipale chofeŵa n’chosangalatsa, ndi kuti chimachititsa kuti malo ambiri m’nyengo yachisanu akhale ochititsa chidwi ndi opereka mwayi wochita zinthu zina zapadera. Polingalira za mafunso a Mulungu aja, kodi chipale chofeŵa mukuchidziŵa bwino, kapena momwe chimaonekera? Eya, tikudziŵa mmene chipale chofeŵa chochuluka chimaonekera, mwinamwake tinachiona m’zithunzi kapena chifukwa chakuti tinaona chipale chofeŵa chenichenicho. Koma bwanji za kachidutswa kakang’ono ka chipale chofeŵa? Kodi mukudziŵa mmene kamaonekera, mwinamwake mutakapenda mosamalitsa?
5 Anthu ambiri athera zaka zambiri akuphunzira ndi kujambula zidutswa za chipale chofeŵa. Chidutswa cha chipale chofeŵa chingakhale ndi timibulu tofeŵa 100 tamadzi oundana toumbika m’maonekedwe osiyanasiyana okongola kwambiri. Buku lakuti Atmosphere limati: “Sizachilendo kupeza zidutswa za chipale chofeŵa zomwe nthaŵi zonse zimakhala zosiyana, ndipo ngakhale kuti asayansi akunenetsa kuti palibe lamulo lachilengedwe loletsa kupangika kwa zidutswa zofanana, sanapezepo zidutswa ziŵiri zofanana. Kufufuza mozama za tinthu tating’ono kwambiri kunachitidwa ndi . . . Wilson A. Bentley, yemwe anathera zaka zoposa 40 akupenda ndi kujambula zidutswa za chipale chofeŵa pogwiritsa ntchito makina a maikulosikopu koma sanapeze zidutswa ziŵiri zomwe zinali zofanana ndendende.” Ndipo nthaŵi zina zidutswa ziŵiri zitaoneka ngati zofanana, kodi zimenezo zingasinthe kudabwitsa kwa kapangidwe ka zidutswa za chipale chofeŵa m’maonekedwe osiyanasiyana?
6 Kumbukirani funso la Mulungu lija lakuti: “Kodi unalowa m’zosungiramo chipale chofeŵa?” Ambiri amaganiza kuti mitambo ndiyo mosungiramo chipale chofeŵa. Kodi mungaganize nkomwe zopita m’zosungiramo zimenezi kuti mukagaŵe tizidutswa tachipale chofeŵacho m’mitundu yosiyanasiyana ndi kuphunzira mmene timaumbikira? Insaikulopediya ya sayansi imati: “Mpangidwe komanso gwero la poyambira kuundana kwa madzi, zimenenso zimachititsa kuti madontho a madzi a m’mitambo aundane pamlingo wozizira kwambiri wa pafupifupi -40°C, anthu sakuzimvetsabe.”—Salmo 147:16, 17; Yesaya 55:9, 10.
7. Kodi anthu akudziŵa zochuluka motani zokhudza mvula?
7 Bwanji za mvula? Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi mvula ili naye atate? Kapena wabala ndani madontho a mame?” Insaikulopediya ya sayansi yomwe tatchula ija inati: “Chifukwa cha kuchulukitsa kwa zinthu zoyenda m’mlengalenga ndiponso kusiyana kwakukulu kwa nthunzi ndi tizigawo tosiyanasiyana tomwe timapanga mpweya, zikuoneka kuti n’zosatheka kufotokoza bwino mmene mitambo ndi mvula zimapangikira.” Mwachidule, asayansi afotokoza zambiri
zokhudza mvula, koma kwenikweni mvulayo sangathe kuifotokoza mogwira mtima. Komabe, inu mukudziŵa kuti mvula n’njofunika kwambiri, chifukwa imathirira nthaka, kukulitsa mbewu, ndi kuti tithe kukhala ndi moyo mosangalala.8. N’chifukwa chiyani mawu a Paulo olembedwa pa Machitidwe 14:17 ali oyenerera?
8 Kodi simungavomereze mawu ophera mphongo a mtumwi Paulo? Iye analimbikitsa ena kuona m’ntchito zodabwitsa zimenezi umboni wakuti pali Wina amene anazipanga. Ponena za Yehova Mulungu Paulo anati: “Sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.”—Machitidwe 14:17; Salmo 147:8.
9. Kodi ntchito zodabwitsa za Mulungu zimasonyeza motani mphamvu zake zosanenekazo?
9 Mposakayikitsa kuti Wochita ntchito zodabwitsa ndi zopindulitsa zoterezi ali ndi nzeru zosaneneka ndi mphamvu zochuluka. Ponena za mphamvu zake, talingalirani izi: Akuti tsiku lililonse kumagunda mabingu 45,000, ndipo pachaka amagunda oposa 16 miliyoni. Zimenezi zikutanthauza kuti panopa mabingu pafupifupi 2,000 akugunda. Mitambo yamphamvu imene imaphulitsa bingu limodzi imayenda mwaphamvu zofanana ndi mphamvu za mabomba anyukiliya khumi kapena kuposerapo amene anawaphulitsa m’nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse. Zina mwa mphamvu zimenezo mumaziona mu mphezi. Ngakhale kuti mphezi ndi yoopsa, koma kwenikweni imathandiza kupanga mitundu yosiyanasiyana ya mpweya wa nitrogen umene umathandiza kuti dothi likhale lachonde, ndipo mbewu zimaugwiritsa ntchito monga chakudya chake chachilengedwe. Choncho mphezi ndi mphamvu zoonekeratu, komanso n’njopindulitsa kwambiri.—Salmo 104:14, 15.
Kodi Zakukhudzani Motani?
10. Kodi mafunso opezeka pa Yobu 38:33-38 mungawayankhe motani?
10 Yerekezerani kuti inuyo ndinu Yobu, ndipo Mulungu Wamphamvuyonse akukufunsani mafunso. Mosakayika mudzavomereza kuti anthu ambiri saganizira mozama za ntchito zodabwitsa za Mulungu. Yehova akutifunsa mafunso omwe tikuŵerenga Yobu 38:33-38. “Kodi udziŵa malemba a kuthambo? Ukhoza kukhazikitsa ufumu wawo pa dziko lapansi? Kodi udziŵa kukwezera mawu ako kumitambo, kuti madzi ochuluka akukute? Kodi ukhoza kutumiza mphezi kuti zimuke, ndi kunena nawe, ‘Tili pano’? Ndani analonga nzeru m’mitambomo? Ndani waninkha nyenyezi yotsotsoka luntha? Adziŵa ndani kuŵerenga mitambo mwanzeru, ndi kutsanulira michenje ya kuthambo ndani, pokandika fumbi, ndi kuundana zibuma pamodzi?”
pa11, 12. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe zikusonyeza kuti Mulungu ndi Wochita zodabwitsa?
11 Tapenda mfundo zochepa chabe mwa mfundo zomwe Elihu anakambirana ndi Yobu, ndipo taona ena mwa mafunso amene Yehova anafuna kuti Yobu ayankhe “ngati mwamuna.” (Yobu 38:3) Tikunena kuti “ena” chifukwa chakuti m’chaputala 38 ndi 39, Mulungu akutchulanso mbali zina zochititsa chidwi za chilengedwe. Mwachitsanzo, anatchula magulu a nyenyezi zakumwamba. Ndani akudziŵa malamulo ndi malangizo ake onse? (Yobu 38:31-33) Yehova anauzanso Yobu kuti alingalire za nyama monga mkango ndi khungubwi, chinkhoma ndi mbidzi, njati ndi nthiŵatiŵa, kavalo wamphamvu ndi chiwombankhanga. Kenako Mulungu anam’funsa Yobu ngati ndiye anapanga nyama zonsezi mosiyanasiyana, kuzipatsa moyo ndi kuti ziswane. Mudzasangalala kuŵerenga machaputala ameneŵa, makamaka ngati m’makonda akavalo kapena nyama zina.—Salmo 50:10, 11.
12 Mungaŵerengenso Yobu chaputala 40 ndi 41, pamene Yehova akufunsanso Yobu mafunso ena okhudza zolengedwa ziŵiri zapadera. Zimenezi ndi mvuu, yaikulu ndi yamphamvu zedi, komanso ng’ona yoopsa ya mumtsinje wa Nile. Iliyonse mwa nyama zimenezi ndi cholengedwa chodabwitsa chofunika kuchilingalira. Tsopano tiyeni tione mmene zimenezi zingatikhudzire.
13. Kodi mafunso a Mulungu anam’khudza motani Yobu, nanga kodi ifeyo zinthu zimenezi ziyenera kutikhudza motani?
13 Yobu chaputala 42 chikutisonyeza mmene mafunso a Mulunguwo anam’khudzira Yobu. Poyambirira Yobu ankalingalira kwambiri za iye mwini ndi anthu ena. Koma chifukwa chomvera malangizo opezeka m’mafunso a Mulunguwo, Yobu anasintha malingaliro ake. Iye anavomereza kuti: “Ndidziŵa kuti [inu Yehova] mukhoza kuchita zonse, ndi kuti palibe choletsa cholingirira chanu chilichonse. Ndani uyu abisa uphungu wosadziŵa kanthu? Chifukwa chake ndinafotokozera zimene sindinazizindikira, zondidabwitsa, zosazidziŵa ine.” (Yobu 42:2, 3) Inde, atalingalira zodabwitsa za Mulungu, Yobu ananena kuti zinthu zimenezi zinali zozizwitsa zedi kwa iye. Titapenda chilengedwe chozizwitsachi, nafenso tidzagoma ndi nzeru za Mulungu komanso mphamvu zake. Mpaka pati? Kodi nkhani yagona pa kungogoma ndi mphamvu zadzaoneni za Yehova komanso luntha lake basi? Kapena kodi tiyenera kusonkhezereka kuposa pamenepo?
14. Kodi Davide anachitanji poona ntchito zodabwitsa za Mulungu?
14 Mu Salmo 86, Davide anatchulanso zinthu zofananazo. Mu salmo loyambirira iye anati: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.” (Salmo 19:1, 2) Koma Davide anapitiriza kufotokoza. Pa Salmo 86:10, 11, timaŵerenga kuti: “Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa; Inu ndinu Mulungu, nokhanu. Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m’choonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.” Kuopa Mlengi kwa Davide chifukwa cha ntchito Zake zonse zodabwitsa kukuphatikizapo mantha oyenerera aumulungu. Chifukwa chake mukuchidziŵa kale. Davide sanafune kukwiyitsa Wochita zodabwitsa zimenezi. Nafenso sitingafune kum’kwiyitsa.
15. Kodi n’chifukwa chiyani mantha aumulungu a Davide anali oyenerera?
15 Davide ayenera kuti anazindikira kuti popeza Mulungu ali ndi mphamvu zochuluka ndipo amazigwiritsa ntchito momwe angafunire, angathe kuzigwiritsa ntchito pokhaulitsa aliyense amene sakondwera naye. Kwa iwo limenelo limakhala tsoka. Mulungu anafunsa Yobu kuti: “Kodi unalowa m’zosungiramo chipale chofeŵa? Kapena unapenya zosungiramo matalala, amene ndiwasungira tsiku la nsautso, tsiku lakulimbana nkhondo?” Chipale chofeŵa, matalala, mvula yamkuntho, mphepo, ndi mphezi zili m’nkhokwe yake yosungiramo zida. Ndipotu zimenezi ndi mphamvu zachilengedwe zozizwitsa kwabasi!—Yobu 38:22, 23.
16, 17. N’chiyani chikusonyeza mphamvu zochititsa mantha zimene Mulungu alinazo, nanga mphamvu zoterozo anazigwiritsapo ntchito motani m’mbuyomu?
16 Mwinamwake mukukumbukira ngozi inayake
imene inachitika kwanuko chifukwa cha mvula ndi mphepo yamkuntho, kamvulumvulu wamphamvu, mvula yamatalala, kapena kusefukira kwa madzi. Mwachitsanzo, kumapeto kwa chaka cha 1999, mvula ndi mphepo yamkuntho zinawomba kumwera cha kumadzulo kwa Ulaya. Inali yodzidzimutsa ngakhale kwa akatswiri a zanyengo. Mphepo yamkunthoyo inali kuthamanga mtunda wa makilomita 200 pa ola limodzi, ndipo inasasula zikwizikwi za madenga, inagwetsa mitengo ya magetsi, ndi kugubuduza malole akuluakulu. Tangoyerekezani kuti mukuona zimenezo zikuchitika: Mkuntho umenewo unazula kapena kukhadzula mitengo pafupifupi 270 miliyoni, ndipo mitengo 10,000 mwa imeneyi inali ya m’nkhalango ya Versailles mokha, kunja kwa mzinda wa Paris. Mkuntho umenewu unathimitsa magetsi m’nyumba za anthu mamiliyoni ambiri. Chiŵerengero cha omwalira chinali pafupifupi 100. Komatu zonsezi zinachitika m’kanthaŵi kochepa zedi. Zinalidi mphamvu zodabwitsa!17 Wina angati mkuntho ndi chinthu chamwadzidzidzi, chosawongolereka, kapena kulamulirika. Nangano, chingachitike n’chiyani ngati Wamphamvu yonse ameneyu atachita zodabwitsa pogwiritsa ntchito mphamvu zimenezo molamulirika komanso motsogozeka? Anachitapo zofanana ndi zimenezo kalero m’masiku a Abrahamu, yemwe anamva kuti woweruza wa dziko lonse lapansi waona kuipa kosaneneka kwa mizinda iŵiriyo, Sodomu ndi Gomora. Mizindayi inaipa kwambiri mwakuti mfuu ya kudandaula inamveka kwa Mulungu, amene anathandiza olungama onse kuthaŵa pamene mizinda imeneyi inali kuwonongedwa. Mbiri ya chochitikacho imati: “Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba.” Zinalitu zodabwitsa zimenezo, kupulumutsa olungama ndi kuwononga oipa mopambanitsa.—Genesis 19:24.
18. Kodi Yesaya chaputala 25 chimanena za zinthu zodabwitsa ziti?
18 Patapita nthaŵi, Mulungu anapereka chiŵeruzo pa mzinda wakale wa Babulo. Mwinamwake umenewu ndiwo mudzi wotchulidwa pa Yesaya chaputala 25. Mulungu ananeneratu kuti mudzi winawake udzakhala bwinja. Iye anati: “Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse.” (Yesaya 25:2) Amene masiku ano amakacheza kumene kunali Babulo wakale amavomereza kuti zimenezi zinachitikadi. Kodi kuwonongedwa kwa Babulo kunangochitika mwangozi? Ayi. Koma tingavomerezane ndi zimene Yesaya ananena kuti: “Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa, ngakhale zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m’zoonadi.”—Yesaya 25:1.
Zinthu Zodabwitsa M’tsogolomu
19, 20. Kodi tikuyembekezera kuti Yesaya 25:6-8 adzakwaniritsidwa motani?
19 Mulungu anakwaniritsa ulosi uli pamwambawu m’mbuyomu, ndipo adzachitanso zodabwitsa m’tsogolo. M’nkhani yomweyi, pamene Yesaya akutchula “zinthu zodabwitsa” za Mulungu, tikupezamo ulosi wodalirika umene udzakwaniritsidwa m’tsogolo, monga momwe ulosi wokhudza chiŵeruzo cha Babulo unakwaniritsidwira. Kodi ndi ‘chinthu chodabwitsa’ chotani chimene chalonjezedwa? Yesaya 25:6 amati: “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.”
20 Mosakayika ulosi umenewu udzakwaniritsidwa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza m’tsogolomu. Panthaŵiyo, mavuto onse amene akuvutitsa anthu ambiri panopa adzatheratu. Kwenikweni, ulosi wa pa Yesaya 25:7, 8 ukutitsimikizira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake zokhoza kulenga zinthu pamene adzachita chimodzi mwa zinthu zodabwitsa zosaiŵalika. Lembali limati: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.” Pambuyo pake mtumwi Paulo anatchulanso mawu ochokera m’mavesi ameneŵa ndi kuwagwiritsa ntchito potchula mfundo yakuti Mulungu adzabwezeretsa akufa ku moyo, inde kuukitsa akufa. Imeneyi idzakhaladi ntchito yodabwitsa kwabasi!—1 Akorinto 15:51-54.
21. Kodi n’zodabwitsa zotani zimene Mulungu adzachitire akufa?
21 Chifukwa china chimene misozi yachisoni idzathera n’chakuti matenda onse a anthu adzatheratu. Pamene Yesu anali padziko lapansi, anachiritsa anthu ambiri—akhungu anayamba kuona, ogontha anayamba kumva, opuwala anachira. Yohane 5:5-9 amanena kuti anachiritsa munthu amene anali wopuwala kwa zaka 38. Amene anaona izi zikuchitika anaganiza kuti zimenezi n’zozizwitsa, kapena kuti ntchito zodabwitsa. Ndipo zinalidi choncho! Komabe, Yesu anawauza kuti adzazizwa kwambiri pamene adzaukitsa akufa. Anawauza kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”—Yohane 5:28, 29.
22. N’chifukwa chiyani aumphaŵi ndi ozunzika ayenera kuyang’ana m’tsogolo ndi chiyembekezo?
22 N’zodziŵikiratu kuti zimenezi zidzachitika zivute zitani chifukwa chakuti wolonjezayo ndi Yehova. Ndife otsimikizira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu zobwezeretsa zinthu ndi kuzilamulira mwanzeru, ndipo zotsatira zake zidzakhala zodabwitsa. Salmo 72 limanena zimene adzachite kudzera mwa Mwana wake yemwenso ndi Mfumu. Panthaŵiyo olungama adzachuluka. Mtendere udzachuluka. Mulungu adzapulumutsa aumphaŵi ndi ozunzika. Iye akulonjeza kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebano [wakale]: ndipo iwo a m’mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.”—Salmo 72:16.
23. Kodi zodabwitsa za Mulungu ziyenera kutisonkhezera kuchitanji?
23 Ndithudi, tili n’chifukwa cholingalirira ntchito zonse zodabwitsa za Yehova—zomwe anachita m’mbuyomo, zomwe akuchita lerolino, komanso zimene adzachite posachedwapa. “Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, amene achita zodabwiza yekhayo: Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nawo ulemerero wake. Amen, ndi Amen.” (Salmo 72:18, 19) Tiyeni nthaŵi zonse tikambirane zimenezi ndi achibale anthu komanso ndi anthu ena. Inde, tiyeni ‘tifotokozere ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.’—Salmo 78:3, 4; 96:3, 4.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi mafunso amene anaperekedwa kwa Yobu akusonyeza motani kupereŵera kwa nzeru za anthu?
• Kodi ndi zitsanzo ziti za ntchito zodabwitsa za Mulungu zotchulidwa pa Yobu chaputala 37-41 zimene zakugometsani?
• Kodi tiyenera kuchitanji pambuyo polingalira zina mwa ntchito zodabwitsa za Mulungu?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 10]
Kodi kusiyana kochititsa chidwi kwa zidutswa za chipale chofeŵa ndi mphamvu zochititsa mantha za mphezi zakupatsani malingaliro otani?
[Mawu a Chithunzi]
snowcrystals.net
[Zithunzi patsamba 13]
Nthaŵi zonse pamene mukukambirana, kambanipo za ntchito zodabwitsa za Mulungu